< Ahebri 13 >

1 Pitirizani kukondana monga abale.
Persévérez dans l’amour fraternel.
2 Musayiwale kusamalira alendo, pakuti pochita zimenezi anthu ena anasamalira angelo amene samawadziwa.
N’oubliez pas l’hospitalité; quelques-uns en la pratiquant ont, à leur insu, logé des anges.
3 Muzikumbukira amene ali mʼndende ngati kuti inunso ndi omangidwa, ndiponso amene akusautsidwa ngati inunso mukuvutika.
Souvenez-vous des prisonniers, comme si vous étiez aussi prisonniers; et de ceux qui sont maltraités, comme étant vous aussi dans un corps.
4 Ukwati muziwulemekeza nonse, ndipo mwamuna ndi mkazi azikhala wokhulupirika, pakuti anthu adama ndi achigololo Mulungu adzawalanga.
Que le mariage soit honoré de tous, et le lit conjugal exempt de souillure, car Dieu condamnera les impudiques et les adultères.
5 Mtima wanu usakonde ndalama koma mukhutitsidwe ndi zimene muli nazo, chifukwa Mulungu anati, “Sadzakusiyani, kapena kukutayani konse.”
Que votre conduite soit exempte d’avarice, vous contentant de ce que vous avez; car Dieu lui-même a dit: « Je ne te délaisserai pas et ne t’abandonnerai point »;
6 Kotero ife tikunena molimba mtima kuti, “Ambuye ndiye mthandizi wanga; sindidzachita mantha. Munthu angandichitenji ine?”
de sorte que nous pouvons dire en toute assurance: « Le Seigneur est mon secours, je ne craindrai rien; que pourraient me faire les hommes? »
7 Muzikumbukira atsogoleri anu, amene amakulalikirani Mawu a Mulungu. Ganizirani zamoyo wawo ndipo tsatirani chikhulupiriro chawo.
Souvenez-vous de ceux qui vous conduisent, qui vous ont annoncé la parole de Dieu; et considérant quelle a été l’issue de leur vie, imitez leur foi.
8 Yesu Khristu ndi yemweyo dzulo, lero ndi kunthawi zonse. (aiōn g165)
Jésus-Christ est le même hier et aujourd’hui; il le sera éternellement. (aiōn g165)
9 Musasocheretsedwe ndi ziphunzitso zosiyanasiyana zachilendo. Nʼkwabwino kuti mitima yathu ilimbikitsidwe ndi chisomo osati ndi chakudya, chimene sichipindulitsa iwo amene amachidya.
Ne vous laissez pas entraîner par des doctrines diverses et étrangères, car il vaut mieux affermir son cœur par la grâce, que par des aliments, qui n’ont servi de rien à ceux qui s’y attachent.
10 Ife tili ndi guwa lansembe, ndipo ansembe otumikira mʼtenti cha Ayuda, saloledwa kudya zochokera pamenepo.
Nous avons un autel dont ceux-là n’ont pas le droit de manger qui restent au service du tabernacle.
11 Mkulu wa ansembe amatenga magazi kukapereka nsembe chifukwa cha machimo, koma nyamayo imawotchedwa kunja kwa msasa.
Car pour les animaux dont le sang, expiation du péché, est porté dans le sanctuaire par le grand prêtre, leurs corps sont brûlés hors du camp.
12 Nʼchifukwa chakenso Yesu anafera kunja kwa mzinda kuti ayeretse anthu ake kudzera mʼmagazi ake.
C’est pour cela que Jésus aussi, devant sanctifier le peuple par son sang, a souffert hors de la porte.
13 Tiyeni tsono, tipite kwa iye kunja kwa msasa, titasenza chitonzo chake.
Donc, pour aller à lui, sortons hors du camp, en portant son opprobre.
14 Pakuti ife tilibe mzinda wokhazikika koma tikudikira mzinda umene ukubwera.
Car nous n’avons pas ici-bas de cité permanente, mais nous cherchons celle qui est à venir.
15 Tsono, tiyeni kudzera mwa Yesu tipereke nsembe zachiyamiko kwa Mulungu osalekeza, chipatso cha milomo imene imavomereza dzina lake.
Que ce soit donc par lui que nous offrions sans cesse à Dieu « un sacrifice de louange », c’est-à-dire « le fruit de lèvres » qui célèbrent son nom.
16 Ndipo musayiwale kumachita zabwino ndi kuthandiza ena, pakuti Mulungu amakondwera ndi nsembe zotere.
Et n’oubliez pas la bienfaisance et la libéralité; car Dieu se plaît à de tels sacrifices.
17 Muzimvera atsogoleri anu ndi kugonjera ulamuliro wawo, iwo amakuyangʼanirani monga anthu amene adzayenera kufotokoza za ntchito yawo pamaso pa Mulungu. Muziwamvera kuti agwire ntchito yawo ndi chimwemwe osati molemedwa pakuti izi sizingakupindulireni.
Obéissez à ceux qui vous conduisent, et ayez pour eux de la déférence, car ils veillent sur vos âmes comme devant en rendre compte, — afin qu’ils le fassent avec joie, et non en gémissant; ce qui ne vous serait pas avantageux.
18 Mutipempherere ifenso. Pakuti tikutsimikiza kuti tili ndi chikumbumtima changwiro ndipo timafuna kuchita zinthu zonse mwaulemu.
Priez pour nous; car nous sommes assurés d’avoir une bonne conscience, voulant en toutes choses nous bien conduire.
19 Ine ndikukupemphani kuti mundipempherere kuti Mulungu andibwezere kwa inu msanga.
C’est avec instance que je vous conjure de le faire, afin que je vous sois plus tôt rendu.
20 Mulungu wamtendere, amene kudzera mʼmagazi a pangano lamuyaya anaukitsa Ambuye athu Yesu kwa akufa, amene ndi Mʼbusa wamkulu, (aiōnios g166)
Que le Dieu de la paix, — qui a ramené d’entre les morts celui qui, par le sang d’une alliance éternelle, est devenu le grand Pasteur des brebis, notre Seigneur Jésus, — (aiōnios g166)
21 akupatseni chilichonse chabwino kuti muchite chifuniro chake ndipo Mulungu achite mwa ife, chimene chingamukomere kudzera mwa Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero ku nthawi zanthawi, Ameni. (aiōn g165)
vous rende capables de toute bonne œuvre pour l’accomplissement de sa volonté, en opérant en vous ce qui est agréable à ses yeux, par Jésus-Christ, auquel soit la gloire dans les siècles des siècles! Amen! (aiōn g165)
22 Ndikukupemphani abale kuti mulandire mawu anga achilimbikitso, pakuti ndakulemberani mwachidule.
Je vous prie, frères, d’agréer cette parole d’exhortation, car je vous ai écrit brièvement.
23 Ine ndikufuna kuti inu mudziwe kuti mʼbale wathu Timoteyo wamasulidwa. Ngati iye angafike msanga ndibwera naye kudzakuonani.
Apprenez que notre frère Timothée est relâché; s’il vient assez tôt, j’irai vous voir avec lui.
24 Mupereke moni kwa atsogoleri anu onse ndiponso kwa anthu onse a Mulungu. Abale ochokera ku Italiya akupereka moni.
Saluez tous ceux qui vous conduisent et tous les saints. Les frères d’Italie vous saluent.
25 Chisomo chikhale ndi inu nonse.
Que la grâce soit avec vous tous! Amen!

< Ahebri 13 >