< Ahebri 12 >
1 Tsono popeza ifenso tazunguliridwa ndi gulu lalikulu la mboni, tiyeni titaye chilichonse chimene chimatitchinga, makamaka tchimo limene limatikola mosavuta, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.
τοιγαρουν και ημεις τοσουτον εχοντες περικειμενον ημιν νεφος μαρτυρων ογκον αποθεμενοι παντα και την ευπεριστατον αμαρτιαν δι υπομονης τρεχωμεν τον προκειμενον ημιν αγωνα
2 Tiyeni tiyangʼanitsitse Yesu, amene ndi woyamba ndi wotsiriza wa chikhulupiriro chathu. Chifukwa cha chimwemwe chimene chimamudikira anapirira zowawa zapamtanda. Iye ananyoza manyazi a imfa yotere ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando waufumu wa Mulungu.
αφορωντες εις τον της πιστεως αρχηγον και τελειωτην ιησουν ος αντι της προκειμενης αυτω χαρας υπεμεινεν σταυρον αισχυνης καταφρονησας εν δεξια τε του θρονου του θεου εκαθισεν
3 Muzilingalira za Iye amene anapirira udani waukulu chotere wochokera kwa anthu ochimwa, kuti musafowoke ndi kutaya mtima.
αναλογισασθε γαρ τον τοιαυτην υπομεμενηκοτα υπο των αμαρτωλων εις αυτον αντιλογιαν ινα μη καμητε ταις ψυχαις υμων εκλυομενοι
4 Polimbana ndi uchimo, simunafike mpaka pokhetsa magazi.
ουπω μεχρις αιματος αντικατεστητε προς την αμαρτιαν ανταγωνιζομενοι
5 Kodi mwayiwala mawu olimbitsa mtima aja, amene Mulungu anayankhula kwa inu ngati ana ake? Mawuwo ndi awa: “Mwana wanga, usapeputse kulanga kwa Ambuye ndipo usataye mtima pamene akukudzudzula.
και εκλελησθε της παρακλησεως ητις υμιν ως υιοις διαλεγεται υιε μου μη ολιγωρει παιδειας κυριου μηδε εκλυου υπ αυτου ελεγχομενος
6 Chifukwa Ambuye amadzudzula amene amawakonda ndipo amalanga aliyense amene amamulandira.”
ον γαρ αγαπα κυριος παιδευει μαστιγοι δε παντα υιον ον παραδεχεται
7 Pamene mukupirira masautso monga chilango, Mulungu achitira inu monga ana ake. Kodi ndi mwana wotani amene abambo ake samulanga?
ει παιδειαν υπομενετε ως υιοις υμιν προσφερεται ο θεος τις γαρ εστιν υιος ον ου παιδευει πατηρ
8 Ngati inu simulangidwa, komatu aliyense amalangidwa, ndiye kuti sindinu ana enieni koma amʼchigololo.
ει δε χωρις εστε παιδειας ης μετοχοι γεγονασιν παντες αρα νοθοι εστε και ουχ υιοι
9 Komanso, tonsefe tinali ndi abambo athu otibala amene amatilanga ndipo timawapatsa ulemu. Nanga kodi sitidzagonjera Atate a mizimu yathu kuti tikhale ndi moyo?
ειτα τους μεν της σαρκος ημων πατερας ειχομεν παιδευτας και ενετρεπομεθα ου πολλω μαλλον υποταγησομεθα τω πατρι των πνευματων και ζησομεν
10 Abambo athu ankatilanga kwa kanthawi kochepa monga amaonera kufunika kwake, koma Mulungu amatilanga kuti tipindule, kuti tikhale oyera mtima.
οι μεν γαρ προς ολιγας ημερας κατα το δοκουν αυτοις επαιδευον ο δε επι το συμφερον εις το μεταλαβειν της αγιοτητος αυτου
11 Palibe chilango chimene chimaoneka kuti ndi chabwino pa nthawiyo, komatu chowawa. Koma pambuyo pake, chimabweretsa chipatso chachilungamo ndi mtendere kwa iwo amene aleredwa mwa njira imeneyi.
πασα δε παιδεια προς μεν το παρον ου δοκει χαρας ειναι αλλα λυπης υστερον δε καρπον ειρηνικον τοις δι αυτης γεγυμνασμενοις αποδιδωσιν δικαιοσυνης
12 Nʼchifukwa chake limbitsani manja anu otopa ndi mawondo anu ogowoka.
διο τας παρειμενας χειρας και τα παραλελυμενα γονατα ανορθωσατε
13 Muziyenda mʼnjira zowongoka, kuti iwo amene akukutsatirani ngakhale ndi olumala ndi ofowoka asapunthwe ndi kugwa koma adzilimbikitsidwa.
και τροχιας ορθας ποιησατε τοις ποσιν υμων ινα μη το χωλον εκτραπη ιαθη δε μαλλον
14 Yesetsani kukhala pa mtendere ndi anthu onse ndi kukhala oyera mtima, pakuti popanda chiyero palibe ndi mmodzi yemwe adzaona Ambuye.
ειρηνην διωκετε μετα παντων και τον αγιασμον ου χωρις ουδεις οψεται τον κυριον
15 Yangʼanitsitsani kuti wina aliyense asachiphonye chisomo cha Mulungu ndiponso kuti pasaphuke muzu wamkwiyo umene udzabweretsa mavuto ndi kudetsa ambiri.
επισκοπουντες μη τις υστερων απο της χαριτος του θεου μη τις ριζα πικριας ανω φυουσα ενοχλη και δια ταυτης μιανθωσιν πολλοι
16 Yangʼanitsitsani kuti pasakhale wina wachigololo. Kapena wosapembedza ngati Esau, amene chifukwa cha chakudya cha kamodzi kokha anagulitsa ukulu wake.
μη τις πορνος η βεβηλος ως ησαυ ος αντι βρωσεως μιας απεδοτο τα πρωτοτοκια αυτου
17 Monga inu mukudziwa, pambuyo pake pamene anafuna kuti adalitsidwe anakanidwa. Sanapezenso mpata woti asinthe maganizo, ngakhale anafuna madalitsowo ndi misozi.
ιστε γαρ οτι και μετεπειτα θελων κληρονομησαι την ευλογιαν απεδοκιμασθη μετανοιας γαρ τοπον ουχ ευρεν καιπερ μετα δακρυων εκζητησας αυτην
18 Inu simunafike ku phiri limene mungathe kulikhudza, loyaka moto wa mdima bii, la mphepo yamkuntho;
ου γαρ προσεληλυθατε ψηλαφωμενω ορει και κεκαυμενω πυρι και γνοφω και σκοτω και θυελλη
19 limene pali kulira kwa lipenga, ndiponso kumveka kwa mawu. Anthu amene amamva mawuwo anapempha kuti asawayankhulenso mawu ena.
και σαλπιγγος ηχω και φωνη ρηματων ης οι ακουσαντες παρητησαντο μη προστεθηναι αυτοις λογον
20 Iwo anachita mantha ndi lamulo lija lakuti, “Ngakhale nyama ikangokhudza phirilo, iphedwe ndi miyala.”
ουκ εφερον γαρ το διαστελλομενον καν θηριον θιγη του ορους λιθοβοληθησεται η βολιδι κατατοξευθησεται
21 Maonekedwenso a Mose anali woopsa kwambiri, ngakhale Mose yemwe anati, “Ine ndinachita mantha ndi kunjenjemera.”
και ουτως φοβερον ην το φανταζομενον μωσης ειπεν εκφοβος ειμι και εντρομος
22 Koma inu mwafika ku Phiri la Ziyoni, ku mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wakumwamba. Mwafika mu msonkhano wa angelo osangalala osawerengeka.
αλλα προσεληλυθατε σιων ορει και πολει θεου ζωντος ιερουσαλημ επουρανιω και μυριασιν αγγελων
23 Mwafika mu mpingo wa ana oyamba kubadwa, amene mayina awo analembedwa kumwamba. Inu mwafika kwa Mulungu, woweruza anthu onse, ndiponso kwa mizimu ya anthu olungama ndi osandutsidwa kukhala angwiro.
πανηγυρει και εκκλησια πρωτοτοκων εν ουρανοις απογεγραμμενων και κριτη θεω παντων και πνευμασιν δικαιων τετελειωμενων
24 Kwa Yesu mʼkhalapakati wa pangano latsopano, ndiponso mwafika ku magazi owazidwa amene amayankhula mawu abwino kuposa magazi a Abele.
και διαθηκης νεας μεσιτη ιησου και αιματι ραντισμου κρειττονα λαλουντι παρα τον αβελ
25 Chenjerani kuti musakane kumvera amene akuyankhula nanu. Anthu amene anakana kumvera iye amene anawachenjeza uja pa dziko lapansi pano, sanapulumuke ku chilango ayi, nanga tsono ife tidzapulumuka bwanji ngati tikufulatira wotichenjeza wochokera kumwamba?
βλεπετε μη παραιτησησθε τον λαλουντα ει γαρ εκεινοι ουκ εφυγον τον επι της γης παραιτησαμενοι χρηματιζοντα πολλω μαλλον ημεις οι τον απ ουρανων αποστρεφομενοι
26 Pa nthawiyo mawu ake anagwedeza dziko lapansi, koma tsopano Iye walonjeza kuti, “Kamodzi kenanso ndidzagwedeza osati dziko lapansi lokha komanso thambo.”
ου η φωνη την γην εσαλευσεν τοτε νυν δε επηγγελται λεγων ετι απαξ εγω σειω ου μονον την γην αλλα και τον ουρανον
27 Mawu akuti, “Kamodzi kenanso,” akuonetsa kuchotsedwa kwa zimene zitha kugwedezeka, zonse zolengedwa, kotero kuti zimene sizingatheke kugwedezeka zitsale.
το δε ετι απαξ δηλοι των σαλευομενων την μεταθεσιν ως πεποιημενων ινα μεινη τα μη σαλευομενα
28 Popeza tikulandira ufumu umene sungagwedezeke, tiyeni tikhale oyamika ndi kupembedza Mulungu movomerezeka ndi mwaulemu ndi mantha.
διο βασιλειαν ασαλευτον παραλαμβανοντες εχωμεν χαριν δι ης λατρευωμεν ευαρεστως τω θεω μετα αιδους και ευλαβειας
29 Pakuti Mulungu wathu ndi moto wonyeketsa.
και γαρ ο θεος ημων πυρ καταναλισκον