< Ahebri 10 >
1 Malamulo ndi chithunzithunzi cha zinthu zabwino zimene zikubwera, osati madalitso enieniwo. Pa chifukwa chimenechi sizingatheke konse kuti nsembe zimodzimodzi, zoperekedwa kawirikawiri, kosalekeza ndi chaka ndi chaka, kuti nʼkusandutsa angwiro amene amabwera kudzapembedza.
Umbram enim habens lex futurorum bonorum, non ipsam imaginem rerum: per singulos annos eisdem ipsis hostiis, quas offerunt indesinenter, numquam potest accedentes perfectos facere:
2 Ngati zikanamatero iwowo akanasiya kupereka nsembezo. Pakuti opembedzawo akanamayeretsedwa kamodzi kokha, sibwenzi chikumbumtima chawo chikuwatsutsabe chifukwa cha machimo awo.
alioquin cessassent offerri: ideo quod nullam haberent ultra conscientiam peccati, cultores semel mundati:
3 Koma nsembezo zimawakumbutsa anthuwo machimo awo chaka ndi chaka.
sed in ipsis commemoratio peccatorum per singulos annos fit.
4 Chifukwa nʼkosatheka kuti magazi angʼombe yayimuna ndi mbuzi yayimuna achotse machimo.
impossibile enim est sanguine taurorum et hircorum auferri peccata.
5 Nʼchifukwa chake Khristu atabwera pa dziko lapansi anati, “Simunafune nsembe kapena zopereka, koma thupi munandikonzera.
Ideo ingrediens mundum dicit: Hostiam, et oblationem noluisti: corpus autem aptasti mihi:
6 Simunakondwere nazo nsembe zopsereza ndi nsembe zopereka chifukwa cha tchimo.
holocaustomata pro peccato non tibi placuerunt.
7 Tsono, Ine ndinati, ‘Ndili pano Ine, Inu Mulungu, ndabwera kudzachita zimene mukufuna monga zinalembedwa mʼMalemba.’”
Tunc dixi: Ecce venio: in capite libri scriptum est de me: Ut faciam, Deus, voluntatem tuam.
8 Poyamba Iye anati, “Nsembe kapena zopereka zopsereza ndi nsembe zopereka chifukwa cha tchimo, Inu simunazifune kapena kukondwera nazo.” Ngakhale kuti Malamulo ndiye amanena kuti ziperekedwe.
Superius dicens: Quia hostias, et oblationes, et holocaustomata pro peccato noluisti, nec placita sunt tibi, quae secundum legem offeruntur,
9 Pamenepo Iye anati, “Ndili pano Ine, ndabwera kudzachita zimene mukufuna.” Khristu anachotsa nsembe zoyamba zija kuti mʼmalo mwake ayikemo nsembe za mtundu wachiwiri.
tunc dixi: Ecce venio, ut faciam, Deus, voluntatem tuam: aufert primum, ut sequens statuat.
10 Chifukwa chakuti Yesu Khristu anachita zimene Mulungu anafuna kuti achite, ndife oyeretsedwa ndi nsembe ya thupi lake, limene analipereka kamodzi kokha.
In qua voluntate sanctificati sumus per oblationem corporis Iesu Christi semel.
11 Wansembe aliyense amayimirira tsiku ndi tsiku nʼkutumikira, ndipo amapereka nsembe imodzimodzi mobwerezabwereza, nsembe zimene sizingathe kuchotsa machimo.
Et omnis quidem sacerdos praesto est quotidie ministrans, et easdem saepe offerens hostias, quae numquam possunt auferre peccata:
12 Koma pamene wansembe uyu anapereka kamodzi kokha nsembe imodzi yokha chifukwa cha machimo, Iye anakhala pansi ku dzanja lamanja la Mulungu.
hic autem unam pro peccatis offerens hostiam, in sempiternum sedet in dextera Dei,
13 Kumeneko akudikira tsono kuti Mulungu asandutse adani ake kukhala chopondapo mapazi ake.
de cetero expectans donec ponantur inimici eius scabellum pedum eius.
14 Chifukwa cha nsembe imodzi Iye anasandutsa angwiro kwamuyaya iwo amene akuwayeretsa.
Una enim oblatione, consummavit in sempiternum sanctificatos.
15 Mzimu Woyera nayenso akuchitira umboni za zimenezi kwa ife. Poyamba Iye anati,
Contestatur autem nos et Spiritus sanctus. Postquam enim dixit:
16 “Ili ndi pangano limene ndidzachita nawo atapita masiku amenewo,” akutero Yehova. “Ndidzayika malamulo anga mʼmitima mwawo, ndipo ndidzawalemba mʼmaganizo mwawo.”
Hoc autem testamentum, quod testabor ad illos post dies illos, dicit Dominus: Dabo leges meas in cordibus eorum, et in mentibus eorum superscribam eas:
17 Ndipo akutinso: “Sindidzakumbukiranso konse machimo awo ndi zolakwa zawo.”
et peccatorum, et iniquitatum eorum iam non recordabor amplius.
18 Ndipo pamene machimo akhululukidwa, sipafunikanso nsembe yoperekedwa chifukwa cha machimowo.
Ubi autem horum remissio: iam non est oblatio pro peccato.
19 Ndipo tsono abale, molimba mtima timalowa mʼMalo Opatulika kwambiri chifukwa cha magazi a Yesu.
Habentes itaque fratres fiduciam in introitu sanctorum in sanguine Christi,
20 Iye anatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo kudutsa chinsalu chotchinga, chimene ndi thupi lake.
quam initiavit nobis viam novam, et viventem per velamen, id est, carnem suam,
21 Ndiponso tili ndi wansembe wamkulu woyangʼanira nyumba ya Mulungu.
et sacerdotem magnum super domum Dei:
22 Tsono tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona ndi wodzaza ndi chikhulupiriro. Popeza mitima yathu yayeretsedwa, ndi yopanda chikumbumtima chotitsutsa, ndiponso matupi athu asambitsidwa ndi madzi woyera.
accedamus cum vero corde in plenitudine fidei, aspersi corda a conscientia mala, et abluti corpus aqua munda,
23 Tiyeni tigwiritsitse mosagwedezeka zimene timaziyembekezera ndi kuzivomereza, pakuti amene anatilonjezayo ndi wokhulupirika.
teneamus spei nostrae confessionem indeclinabilem, (fidelis enim est qui repromisit),
24 Tiziganizira mmene tingalimbikitsirane wina ndi mnzake pokondana ndi kuchita ntchito zabwino.
et consideremus invicem in provocationem charitatis, et bonorum operum:
25 Tiyeni tisaleke kusonkhana kwathu pamodzi monga mmene ena amachitira, koma tizilimbikitsana makamaka poona kuti tsiku la Ambuye layandikira.
non deserentes collectionem nostram, sicut consuetudinis est quibusdam, sed consolantes, et tanto magis quanto videritis appropinquantem diem.
26 Ngati ife tipitirira kuchimwa mwadala pamene tikudziwa choona, palibenso nsembe ina imene ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo.
Voluntarie enim peccantibus nobis post acceptam notitiam veritatis, iam non relinquitur pro peccatis hostia,
27 Koma kumangodikira kokha ndi mantha chiweruzo ndiponso moto woopsa umene udzawononga adani a Mulungu
terribilis autem quaedam expectatio iudicii, et ignis aemulatio, quae consumptura est adversarios.
28 Aliyense amene amakana malamulo a Mose amaphedwa popanda nʼchifundo chomwe, malingana pali mboni ziwiri kapena zitatu.
Irritam quis faciens legem Moysi, sine ulla miseratione duobus vel tribus testibus moritur:
29 Koposa kotani nanga ululu wachilango chimene adzalandire munthu amene amapeputsa Mwana wa Mulungu, amene amayesa magazi a pangano, amene anamuyeretsa, kukhala chinthu chodetsedwa, ndi kunyoza Mzimu wachisomo?
quanto magis putatis deteriora mereri supplicia qui filium Dei conculcaverit, et sanguinem testamenti pollutum duxerit, in quo sanctificatus est, et spiritui gratiae contumeliam fecerit?
30 Pakuti timadziwa amene anati, “Kubwezera chilango nʼkwanga; ndidzawalanga ndine.” Iye anatinso, “Ambuye adzaweruza anthu ake.”
Scimus enim qui dixit: Mihi vindictam, et ego retribuam. Et iterum: Quia iudicabit Dominus populum suum.
31 Nʼchinthu choopsa kugwa mʼmanja a Mulungu wamoyo.
Horrendum est incidere in manus Dei viventis.
32 Kumbukirani masiku akale aja mutangowunikiridwa chatsopano, pa nthawi imeneyi munapirira zowawa zambiri.
Rememoramini autem pristinos dies, in quibus illuminati, magnum certamen sustinuistis passionum:
33 Nthawi zina ankakunyozani pagulu ndi kukuzunzani. Nthawi zina munkamva zowawa pamodzi ndi amene ankasautsidwa chotere.
et in altero quidem opprobriis, et tribulationibus spectaculum facti: in altero autem socii taliter conversantium effecti.
34 Munkawamvera chisoni amene anali mʼndende ndiponso munkalola mokondwera kuti akulandeni katundu wanu chifukwa munkadziwa kuti muli nacho chuma choposa ndi chosatha.
Nam et vinctis compassi estis, et rapinam bonorum vestrorum cum gaudio suscepistis, cognoscentes vos habere meliorem, et manentem substantiam.
35 Tsono musataye kulimbika mtima kwanuko pakuti mudzalandira nako mphotho yayikulu.
Nolite itaque amittere confidentiam vestram, quae magnam habet remunerationem.
36 Nʼkofunika kuti mupirire kuti pamene muchita chifuniro cha Mulungu mudzalandire zimene Iye analonjeza.
Patientia enim vobis necessaria est: ut voluntatem Dei facientes, reportetis promissionem.
37 Pakuti nʼkanthawi kochepa chabe, Iye amene akubwera adzabwera ndipo sadzachedwa ayi.
Adhuc enim modicum aliquantulumque, qui venturus est, veniet, et non tardabit.
38 Koma wolungama wangayo adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro. Ndipo ngati iye abwerera mʼmbuyo chifukwa cha mantha, Ine sindidzakondwera naye.
iustus autem meus ex fide vivit. quod si subtraxerit se, non placebit animae meae.
39 Koma ife sindife amodzi a iwo obwerera mʼmbuyo mwa mantha ndi owonongedwa, koma ndife amodzi a amene akukhulupirira ndi wopulumutsidwa.
Nos autem non sumus subtractionis filii in perditionem, sed fidei in acquisitionem animae.