< Habakuku 1 >

1 Uthenga umene mneneri Habakuku analandira mʼmasomphenya.
哈巴谷先知在神視中所得的神諭。
2 Kodi inu Yehova, ndidzakhala ndikukupemphani thandizo kwa nthawi yayitali motani, koma wosayankha? Kapena kufuwulira kwa inu kuti, “Chiwawa kuno!” koma wosatipulumutsa?
上主,我呼救而你不予垂聽,要到何時﹖向你呼喊「殘暴」,而你仍不施救﹖
3 Chifukwa chiyani mukundionetsa zinthu zoyipa? Chifukwa chiyani mukundionetsa mavutowa? Ndikuona chiwonongeko ndi chiwawa; pali ndewu ndi kukangana kwambiri.
為什麼你仗我見到邪惡,人受壓迫,而你竟坐視﹖在我面前,只有壓害和殘暴,爭吵不休,辯論迭起。
4 Kotero malamulo anu atha mphamvu, ndipo chilungamo sichikugwira ntchito. Anthu oyipa aposa olungama, kotero apotoza chilungamo.
為此法律鬆馳,正義不彰,惡人包圍了義人,因而產生歪曲的審判。
5 “Yangʼanani pakati pa mitundu ya anthu, ndipo penyetsetsani, ndipo muthedwe nazo nzeru. Pakuti ndidzachitadi zinthu pa nthawi yanu zimene inu simudzazikhulupirira, ngakhale wina atakufotokozerani.
你們應觀察列邦,且應注意視,你們必要詑異驚奇,因在你們的日子內,我要做一件事,縱然有人述說,你們也不相信。
6 Pakuti taonani, Ine ndikuwutsa Ababuloni, anthu ankhanza ndiponso amphamvu, amene amapita pa dziko lonse lapansi kukalanda malo amene si awo.
看,我要激起加色丁人──那殘暴凶猛的民族,向廣大的地區進發,侵佔別人的居所。
7 Iwowa ndi anthu ochititsa mantha, ndipo ndi owopsa; amadzipangira okha malamulo ndi kudzipezera okha ulemu.
這民族獨斷獨行,目中無人,實令人恐怖。
8 Akavalo awo ndi aliwiro kwambiri kupambana akambuku ndi owopsa kupambana mimbulu yolusa nthawi ya madzulo. Okwerapo awo akuthamanga molunjika; a pa akavalo awo ndi ochokera kutali, akuwuluka ngati chiwombankhanga chofuna kugwira nyama;
他們的馬捷於虎豹,猛於夜狼;他們的馬隊由遠方飛奔而來,像撲食的老鷹;
9 onse akubwera atakonzekera zachiwawa. Gulu la ankhondo likubwera ngati mphepo ya mʼchipululu ndi kugwira akapolo ochuluka ngati mchenga.
大事摧殘,而面目焦燥,有如烈風;聚集的俘虜,多似塵沙。
10 Akunyoza mafumu ndiponso kuchitira chipongwe olamulira. Akupeputsa mizinda yonse yotetezedwa; akumanga mitumbira ndi kulanda mizindayo.
他們嘲笑列王,譏諷諸侯,嗤笑任何堡壘只堆一堆土,即可攻下;
11 Kenaka amasesa mofulumira ngati mphepo nʼkumangopitirirabe, anthu ochimwa, amene mphamvu zawo ndiye mulungu wawo.”
然後鼓起勇氣向前猛進,以自己的力量為神。
12 Inu Yehova, kodi sindinu wachikhalire? Mulungu wanga, Woyera wanga, ife sitidzafa. Inu Yehova, munawasankha anthuwo kuti abweretse chiweruzo; Inu Thanthwe, munawayika iwowo kuti atilange.
吾主,你自古不就是我的天主,我的聖者﹖你決不會死亡! 上主,你派他們來是為審判;磐石,你立定他們是為懲罰。
13 Maso anu ndi oyera kwambiri safuna kuona choyipa; Inu simulekerera cholakwa. Chifukwa chiyani nanga mukulekerera anthu ochita zachinyengowa? Chifukwa chiyani muli chete pamene anthu oyipa akuwononga anthu olungama kupambana iwowo?
你的眼睛這樣純潔,以致見不得邪惡,見不得折磨! 你為什麼垂顧背信的人﹖當惡人吞噬較他們更義的人,你又為什麼緘默﹖
14 Mwasandutsa anthu kukhala ngati nsomba zamʼnyanja, ngati zolengedwa zamʼnyanja zimene zilibe wolamulira.
你竟把人當作海裏的魚,當作沒有主宰的爬蟲!
15 Mdani wawo woyipa amakoka anthu onse ndi mbedza, amawakola mu ukonde wake, amawasonkhanitsa mu khoka lake; kotero iyeyo amakondwa ndi kusangalala.
他們把所有的一切用鉤子鉤上來,用網拉上來,用罟收集起來,為此歡欣踴躍,
16 Choncho iye amaperekera nsembe ukonde wake ndiponso kufukizira lubani khoka lake, popeza ukonde wakewo ndiye umamubweretsera moyo wapamwamba ndipo amadya chakudya chabwino kwambiri.
向網祭獻,向罟焚香,因為給他們帶來了富裕的財物,豐美的飲食。
17 Kodi iye azipitirabe kugwiritsa ntchito makoka akewo, kuwononga mitundu ya anthu mopanda chifundo?
難道因此他們就應時常倒空自己的羅,無情地屠殺萬民﹖

< Habakuku 1 >