< Habakuku 2 >

1 Ndidzakhala pa malo anga aulonda, ndi kuyima pa mitumbira ya nkhondo; ndidzadikira kuti ndimve zimene Iye adzandiwuze, ndi yankho limene ndidzapatsidwe pa madandawulo anga.
על משמרתי אעמדה ואתיצבה על מצור ואצפה לראות מה ידבר בי ומה אשיב על תוכחתי
2 Tsono Yehova anandiyankha, nati: “Lemba masomphenyawa ndipo uwalembe mooneka bwino pa mapale kuti wowerenga awawerenge mosavuta.
ויענני יהוה ויאמר כתב חזון ובאר על הלחות--למען ירוץ קורא בו
3 Pakuti masomphenyawa akudikira nthawi yake; masomphenyawa akunena zamʼtsogolo ndipo sizidzalephera kuchitika. Ngakhale achedwe kukwaniritsidwa, uwayembekezere; zidzachitika ndithu ndipo sadzachedwa.
כי עוד חזון למועד ויפח לקץ ולא יכזב אם יתמהמה חכה לו--כי בא יבא לא יאחר
4 “Taona, mdani wadzitukumula; zokhumba zake sizowongoka, koma wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.
הנה עפלה לא ישרה נפשו בו וצדיק באמונתו יחיה
5 Ndithu, wasokonezeka ndi vinyo; ndi wodzitama ndiponso wosakhazikika. Pakuti ngodzikonda ngati manda, ngosakhutitsidwa ngati imfa, wadzisonkhanitsira mitundu yonse ya anthu ndipo wagwira ukapolo anthu a mitundu yonse. (Sheol h7585)
ואף כי היין בגד גבר יהיר ולא ינוה אשר הרחיב כשאול נפשו והוא כמות ולא ישבע ויאסף אליו כל הגוים ויקבץ אליו כל העמים (Sheol h7585)
6 “Kodi onse ogwidwawo sadzamunyoza ndi kumunyogodola ponena kuti, “Tsoka kwa amene amadzikundikira katundu amene si wake ndipo amadzilemeretsa ndi chuma cholanda! Kodi izi zidzachitika mpaka liti?
הלוא אלה כלם עליו משל ישאו ומליצה חידות לו ויאמר הוי המרבה לא לו--עד מתי ומכביד עליו עבטיט
7 Kodi angongole ako sadzakuwukira mwadzidzidzi? Kodi sadzadzuka ndi kukuchititsa mantha? Pamenepo iwe udzalandidwa kalikonse.
הלוא פתע יקומו נשכיך ויקצו מזעזעיך והיית למשסות למו
8 Pakuti unafunkha mitundu yambiri ya anthu, mitundu ina imene inatsala idzakufunkha iweyo. Pakuti wakhetsa magazi a anthu; wawononga mayiko ndi mizinda ndi aliyense wokhala mʼmenemo.
כי אתה שלות גוים רבים ישלוך כל יתר עמים מדמי אדם וחמס ארץ קריה וכל ישבי בה
9 “Tsoka kwa amene amalemera ndi chuma chochipeza mwachinyengo, kukweza malo ake okhalapo, kuthawa mavuto!
הוי בצע בצע רע--לביתו לשום במרום קנו להנצל מכף רע
10 Wakonzekera kuwononga mitundu yambiri ya anthu, kuchititsa manyazi nyumba yako yomwe ndi kuwononga moyo wako.
יעצת בשת לביתך קצות עמים רבים וחוטא נפשך
11 Mwala pa khoma udzafuwula, ndipo mitanda ya matabwa idzavomereza zimenezi.
כי אבן מקיר תזעק וכפיס מעץ יעננה
12 “Tsoka kwa amene amanga mzinda pokhetsa magazi ndi kukhazikitsa mzinda pochita zoyipa!
הוי בנה עיר בדמים וכונן קריה בעולה
13 Kodi Yehova Wamphamvuzonse sanatsimikize kuti ntchito za anthu zili ngati nkhuni pa moto, ndi kuti mitundu ya anthu imadzitopetsa popanda phindu?
הלוא הנה מאת יהוה צבאות וייגעו עמים בדי אש ולאמים בדי ריק יעפו
14 Pakuti dziko lapansi lidzadzaza ndi chidziwitso cha ulemerero wa Yehova, monga momwe madzi amadzazira nyanja.
כי תמלא הארץ לדעת את כבוד יהוה כמים יכסו על ים
15 “Tsoka kwa amene amamwetsa anzake zakumwa zoledzeretsa, kutsanula mʼbotolo mpaka ataledzera, kuti aone umaliseche wawo.
הוי משקה רעהו מספח חמתך ואף שכר--למען הביט על מעוריהם
16 Udzachita manyazi mʼmalo mokhala ndi ulemerero. Tsopano ino ndi nthawi yako! Imwa mpaka umaliseche wako uwonekere! Chikho chochokera mʼdzanja lamanja la Yehova chikubwera kwa iwe, ndipo manyazi adzaphimba ulemerero wako.
שבעת קלון מכבוד שתה גם אתה והערל תסוב עליך כוס ימין יהוה וקיקלון על כבודך
17 Udzathedwa nzeru ndi chiwawa chimene unachita ku Lebanoni, ndiponso udzachita mantha ndi nyama zimene unaziwononga. Pakuti wakhetsa magazi a anthu; wawononga mayiko ndi mizinda ndi aliyense wokhala mʼmenemo.
כי חמס לבנון יכסך ושד בהמות יחיתן מדמי אדם וחמס ארץ קריה וכל ישבי בה
18 “Kodi fano lili ndi phindu lanji, poti analisema ndi munthu, kapena chifanizo chimene chimaphunzitsa mabodza? Pakuti munthu amene walipanga amakhulupirira ntchito ya manja ake; amapanga mafano amene samatha kuyankhula.
מה הועיל פסל כי פסלו יצרו--מסכה ומורה שקר כי בטח יצר יצרו עליו לעשות אלילים אלמים
19 Tsoka kwa amene amawuza mtengo kuti, ‘Khala wamoyo!’ Kapena mwala wopanda moyo kuti, ‘Dzuka!’ Kodi zimenezi zingathe kulangiza? Ndi zokutidwa ndi golide ndi siliva; mʼkati mwake mulibe mpweya.
הוי אמר לעץ הקיצה עורי לאבן דומם הוא יורה--הנה הוא תפוש זהב וכסף וכל רוח אין בקרבו
20 Koma Yehova ali mʼNyumba yake yopatulika; dziko lonse lapansi likhale chete pamaso pake.”
ויהוה בהיכל קדשו הס מפניו כל הארץ

< Habakuku 2 >