< Genesis 8 >

1 Tsono Mulungu anakumbukira Nowa ndi nyama zonse zakuthengo ndi ziweto zimene anali nazo mu chombo. Yehova anatumiza mphepo pa dziko lapansi ndipo madzi anaphwera.
Or, Dieu se souvint de Noé, et de tous les animaux et de tout le bétail qui étaient avec lui dans l'arche. Et Dieu fit passer un vent sur la terre, et les eaux s'arrêtèrent.
2 Tsono akasupe a madzi ambiri a pansi pa dziko ndi zitseko za madzi a kumwamba zinatsekedwa, ndipo mvula inaleka kugwa.
Et les sources de l'abîme et les bondes des cieux se fermèrent; et la pluie fut retenue des cieux.
3 Madzi amaphwabe pa dziko lapansi. Pakutha pa masiku 150, madzi anatsika,
Et les eaux se retirèrent de dessus la terre; elles allèrent se retirant; et les eaux diminuèrent au bout de cent cinquante jours.
4 ndipo pa tsiku la 17 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, chombo chija chinakakhazikika pa mapiri a Ararati.
Et au septième mois, au dix-septième jour du mois, l'arche s'arrêta sur les montagnes d'Ararat.
5 Madzi anapitirira kuphwa mpaka mwezi wa khumi, ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wa khumiwo msonga za mapiri zinayamba kuonekera.
Et les eaux allèrent diminuant, jusqu'au dixième mois. Au dixième mois, au premier jour du mois, ap-parurent les sommets des montagnes.
6 Patapita masiku makumi anayi, Nowa anatsekula zenera limene anapanga mʼchombomo
Et il arriva qu'au bout de quarante jours Noé ouvrit la fenêtre qu'il avait faite à l'arche.
7 natulutsa khwangwala, koma khwangwalayo ankangowuluka uku ndi uku mpaka madzi anawuma pa dziko lapansi.
Et il lâcha le corbeau, qui sortit, allant et revenant, jusqu'à ce que les eaux eussent séché de dessus la terre.
8 Kenaka anatulutsa nkhunda kuti aone ngati madzi aphwa pa dziko.
Puis il lâcha la colombe d'avec lui, pour voir si les eaux avaient fort diminué à la surface de la terre.
9 Koma nkhunda sinapeze poti nʼkutera chifukwa panali madzi ponseponse pa dziko lapansi. Choncho inabwerera kwa Nowa mʼchombo. Nowa anatulutsa dzanja lake kunja ndi kutenga nkhundayo kuyibwezera mʼchombo mmene iye anali.
Mais la colombe ne trouva pas où poser la plante de son pied, et elle retourna vers lui dans l'arche; car il y avait de l'eau à la surface de toute la terre. Et Noé avança sa main, la prit, et la ramena vers lui dans l'arche.
10 Choncho anadikirabe masiku ena asanu ndi awiri ndipo anatulutsanso nkhundayo mʼchombo muja.
Et il attendit encore sept autres jours, puis il lâcha de nouveau la colombe hors de l'arche.
11 Pamene nkhunda inabwerera madzulo ake, inali itanyamula tsamba laliwisi la mtengo wa olivi. Motero Nowa anadziwa kuti madzi aphwadi pa dziko lapansi.
Et la colombe revint à lui vers le soir; et voici, une feuille d'olivier fraîche était à son bec; et Noé comprit que les eaux avaient fort diminué sur la terre.
12 Iye anadikira masiku ena asanu ndi awiri ndipo anatumizanso nkhunda ija, koma nthawi imeneyi sinabwererenso kwa iye.
Et il attendit encore sept autres jours; puis il lâcha la colombe; mais elle ne retourna plus à lui.
13 Pofika tsiku loyamba la mwezi woyamba wa chaka chimene Nowa anakwanitsa zaka 601, madzi anawuma pa dziko lapansi. Ndipo Nowa anachotsa denga la chombo ndipo anaona kuti kunja kwawuma.
Et il arriva en l'an six cent un de la vie de Noé, au premier mois, au premier jour du mois, que les eaux avaient séché sur la terre; et Noé ôta la couverture de l'arche, et regarda; et voici, la surface du sol avait séché.
14 Pokwana tsiku la 27 la mwezi wachiwiri dziko lapansi linawumiratu.
Au second mois, au vingt-septième jour du mois, la terre fut sèche.
15 Tsono Mulungu anawuza Nowa kuti,
Alors Dieu parla à Noé, en disant:
16 “Iwe, mkazi wako, ana ako pamodzi ndi akazi awo tulukani mʼchombomo.
Sors de l'arche, toi, ta femme, tes fils, et les femmes de tes fils avec toi.
17 Tulutsa zamoyo zonse zili ndi iwe, mbalame, nyama ndi zokwawa zonse kuti ziswane ndi kuchulukana pa dziko lapansi.”
Fais sortir avec toi tous les animaux qui sont avec toi, de toute chair, tant des oiseaux que des bêtes, et de tous les reptiles qui rampent sur la terre; et qu'ils peuplent en abondance la terre, et qu'ils croissent et multiplient sur la terre.
18 Nowa anatuluka pamodzi ndi ana ake aamuna, mkazi wake ndi akazi a ana ake.
Et Noé sortit, et ses fils, sa femme, et les femmes de ses fils avec lui.
19 Nyama zonse, zokwawa zonse, mbalame zonse, chilichonse choyenda pa dziko lapansi, zinatuluka mʼchombo motsogozana monga mwa mitundu yawo.
Tous les animaux, tous les reptiles et tous les oiseaux, tout ce qui rampe sur la terre, selon leurs familles, sortirent de l'arche.
20 Pamenepo Nowa anamanga guwa lansembe la Yehova ndipo anatengako mtundu uliwonse wa nyama zoti nʼkudya ndi mbalame zoti nʼkudya naperekapo nsembe yopsereza.
Et Noé bâtit un autel à l'Éternel; et il prit de toute bête pure, et de tout oiseau pur, et il offrit des holocaustes sur l'autel.
21 Yehova atamva fungo labwino anati mu mtima mwake: “Sindidzatembereranso nthaka chifukwa cha munthu, ngakhale kuti maganizo a mu mtima mwake ndi oyipa kuyambira ubwana wake. Ndipo sindidzawononganso zolengedwa zonse zamoyo monga ndachitiramu.
Et l'Éternel respira l'agréable odeur, et l'Éternel dit en son cœur: Je ne maudirai plus la terre, à cause de l'homme; car la nature du cœur de l'homme est mauvaise dès sa jeunesse; et je ne frapperai plus tout ce qui vit, comme je l'ai fait.
22 “Nthawi zonse mmene dziko lapansi lidzakhalire, nthawi yodzala ndi nthawi yokolola yozizira ndi yotentha, dzinja ndi chilimwe, usana ndi usiku, sizidzatha.”
Tant que la terre durera, les semailles et la moisson, le froid et le chaud, l'été et l'hiver, et le jour et la nuit, ne cesseront point.

< Genesis 8 >

A Dove is Sent Forth from the Ark
A Dove is Sent Forth from the Ark