< Genesis 5 >
1 Ndondomeko ya mibado ya Adamu ndi iyi: Pamene Mulungu analenga munthu, anamulenga mʼchifaniziro cha Mulungu.
亚当的后代记在下面。(当 神造人的日子,是照着自己的样式造的,
2 Iye analenga mwamuna ndi mkazi. Anawadalitsa ndipo anawatcha “Munthu.”
并且造男造女。在他们被造的日子, 神赐福给他们,称他们为“人”。)
3 Pamene Adamu anali ndi zaka 130, anabereka mwana wamwamuna wofanana naye ndipo anamutcha Seti.
亚当活到一百三十岁,生了一个儿子,形象样式和自己相似,就给他起名叫塞特。
4 Atabadwa Seti, Adamu anakhala ndi moyo zaka zina 800 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
亚当生塞特之后,又在世八百年,并且生儿养女。
5 Zaka zonse za Adamu zinali 930 ndipo anamwalira.
亚当共活了九百三十岁就死了。
6 Pamene Seti anali ndi zaka 105, anabereka Enosi.
塞特活到一百零五岁,生了以挪士。
7 Atabadwa Enosi, Seti anakhala ndi moyo zaka zina 807 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
塞特生以挪士之后,又活了八百零七年,并且生儿养女。
8 Zaka zonse za Seti zinali 912 ndipo anamwalira.
塞特共活了九百一十二岁就死了。
9 Pamene Enosi anali ndi zaka 90, anabereka Kenani.
以挪士活到九十岁,生了该南。
10 Atabadwa Kenani, Enosi anakhala ndi moyo zaka zina 815 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
以挪士生该南之后,又活了八百一十五年,并且生儿养女。
11 Zaka zonse za Enosi pamodzi zinali 905 ndipo anamwalira.
以挪士共活了九百零五岁就死了。
12 Pamene Kenani anali ndi zaka 70, anabereka Mahalaleli.
该南活到七十岁,生了玛勒列。
13 Atabadwa Mahalaleli, Kenani anakhala ndi moyo zaka zina 840 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
该南生玛勒列之后,又活了八百四十年,并且生儿养女。
14 Zaka zonse za Kenani zinali 910, ndipo anamwalira.
该南共活了九百一十岁就死了。
15 Pamene Mahalaleli anali ndi zaka 65, anabereka Yaredi.
玛勒列活到六十五岁,生了雅列。
16 Atabadwa Yaredi, Mahalaleli anakhala ndi moyo zaka zina 830 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
玛勒列生雅列之后,又活了八百三十年,并且生儿养女。
17 Zaka zonse za Mahalaleli zinali 895 ndipo anamwalira.
玛勒列共活了八百九十五岁就死了。
18 Pamene Yaredi anali ndi zaka 162, anabereka Enoki.
雅列活到一百六十二岁,生了以诺。
19 Atabadwa Enoki, Yaredi anakhala ndi moyo zaka zina 800 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
雅列生以诺之后,又活了八百年,并且生儿养女。
20 Zaka zonse za Yaredi zinali 962 ndipo anamwalira.
雅列共活了九百六十二岁就死了。
21 Pamene Enoki anali ndi zaka 65, anabereka Metusela.
以诺活到六十五岁,生了玛土撒拉。
22 Atabadwa Metusela, Enoki anayenda ndi Mulungu zaka 300 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
以诺生玛土撒拉之后,与 神同行三百年,并且生儿养女。
23 Zaka zonse za Enoki zinali 365.
以诺共活了三百六十五岁。
24 Enoki anayenda ndi Mulungu; ndipo iye sanaonekenso chifukwa Mulungu anamutenga.
以诺与 神同行, 神将他取去,他就不在世了。
25 Pamene Metusela anali ndi zaka 187, anabereka Lameki.
玛土撒拉活到一百八十七岁,生了拉麦。
26 Ndipo atabadwa Lameki, Metusela anakhala ndi moyo zaka zina 782 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
玛土撒拉生拉麦之后,又活了七百八十二年,并且生儿养女。
27 Zaka zonse za Metusela zinali 969, ndipo anamwalira.
玛土撒拉共活了九百六十九岁就死了。
28 Pamene Lameki anali ndi zaka 182, anabereka mwana wamwamuna.
拉麦活到一百八十二岁,生了一个儿子,
29 Ndipo anamutcha Nowa ndipo anati, “Iyeyu adzatipumulitsa ku ntchito zathu zolemetsazi, zolima nthaka imene Yehova anayitemberera.”
给他起名叫挪亚,说:“这个儿子必为我们的操作和手中的劳苦安慰我们;这操作劳苦是因为耶和华咒诅地。”
30 Atabadwa Nowa, Lameki anakhala zaka zina 595 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
拉麦生挪亚之后,又活了五百九十五年,并且生儿养女。
31 Zaka zonse za Lameki zinali 777, ndipo kenaka anamwalira.
拉麦共活了七百七十七岁就死了。
32 Pamene Nowa anali ndi zaka 500, anabereka Semu, Hamu ndi Yafeti.
挪亚五百岁生了闪、含、雅弗。