< Genesis 47 >
1 Yosefe anapita kukamuwuza Farao kuti, “Abambo anga, abale anga pamodzi ndi nkhosa, ngʼombe zawo, ndi antchito awo abwera kuchokera ku dziko la Kanaani ndipo tsopano ali ku Goseni.”
Da kam Joseph und sagte es Pharao an und sprach: Mein Vater und meine Brüder, ihr kleines und großes Vieh und alles, was sie haben, sind gekommen aus dem Lande Kanaan; und siehe sie sind im Lande Gosen.
2 Iye anapita kwa Farao kuja ndi abale ake asanu, kukawaonetsa.
Und er nahm aus allen seinen Brüdern fünf und stellte sie vor Pharao.
3 Farao anafunsa abale akewo kuti, “Mumagwira ntchito yanji?” Iwo anamuyankha kuti, “Ife, bwana ndife oweta ziweto, monga ankachitira makolo athu.
Da sprach Pharao zu seinen Brüdern: Was ist eure Nahrung? Sie antworteten: Deine Knechte sind Viehhirten, wir und unsere Väter;
4 Ife tabwera kudzakhala kuno kwa kanthawi chifukwa njala yafika poopsa ku Kanaani motero kuti kulibe msipu wodyetsera ziweto. Ndiye bwana tiloleni kuti tikhale ku Goseni.”
und sagten weiter zu Pharao: Wir sind gekommen, bei euch zu wohnen im Lande; denn deine Knechte haben nicht Weide für ihr Vieh, so hart drückt die Teuerung das Land Kanaan; so laß doch nun deine Knechte im Lande Gosen wohnen.
5 Farao anati kwa Yosefe, “Abambo ako ndi abale ako abwera kwa iwe.
Pharao sprach zu Joseph: Es ist dein Vater und sind deine Brüder, die sind zu dir gekommen;
6 Dziko lonse la Igupto lili mʼdzanja lako. Uwakhazike abambo ako ndi abale ako mʼmalo achonde kwambiri. Akhale ku Goseni. Ndipo ngati ukudziwapo ena mwa iwo amene ali akatswiri pa kuweta ziweto, uwapatse udindo woyangʼanira ziweto zanga.”
das Land Ägypten steht dir offen, laß sie am besten Ort des Landes wohnen, laß sie im Lande Gosen wohnen; und so du weißt, daß Leute unter ihnen sind, die tüchtig sind, so setze sie über mein Vieh.
7 Kenaka Yosefe anapita ndi abambo ake kwa Farao kukawaonetsa, ndipo Yakobo anadalitsa Faraoyo.
Joseph brachte auch seinen Vater Jakob hinein und stellte ihn vor Pharao. Und Jakob segnete den Pharao.
8 Atatero, Farao anafunsa Yakobo kuti, “Muli ndi zaka zingati?”
Pharao aber fragte Jakob: Wie alt bist du?
9 Yakobo anayankha kuti, “Zaka za maulendo anga zakwana 130. Zaka za moyo wanga ndi zowerengeka, komanso zakhala zaka za masautso. Zaka za moyo wanga sizingafanane ndi zaka za moyo wa makolo anga.”
Jakob sprach: Die Zeit meiner Wallfahrt ist hundertdreißig Jahre; wenig und böse ist die Zeit meines Lebens und langt nicht an die Zeit meiner Väter in ihrer Wallfahrt.
10 Atatha kumudalitsa Farao uja, Yakobo anatsanzika nʼkunyamuka.
Und Jakob segnete den Pharao und ging heraus von ihm.
11 Choncho Yosefe anakhazika abambo ake aja ndi abale ake mʼdziko la Igupto. Iye anawapatsa dera la Ramesesi limene linali dziko lachonde kwambiri monga analamulira Farao.
Aber Joseph schaffte seinem Vater und seinen Brüdern Wohnung und gab ihnen Besitz in Ägyptenland, am besten Ort des Landes, im Lande Raemses, wie Pharao geboten hatte.
12 Yosefe anaperekanso chakudya kwa abambo ake, kwa abale ake ndi kwa onse a mʼnyumba ya abambo ake monga mwa chiwerengero cha ana awo.
Und er versorgte seinen Vater und seine Brüder und das ganze Haus seines Vaters mit Brot, einen jeglichen, nachdem er Kinder hatte.
13 Njala inakula kwambiri motero kuti chakudya chinasowa mʼdziko lonse. Anthu a ku Igupto ndi ku Kanaani analefuka nayo njalayo.
Es war aber kein Brot in allen Landen; denn die Teuerung war sehr schwer, daß das Land Ägypten und Kanaan verschmachteten vor der Teuerung.
14 Yosefe anasonkhanitsa ndalama zonse zimene anthu a mu Igupto ndi Kanaani ankapereka pogula tirigu, ndipo anabwera nazo ku nyumba kwa Farao.
Und Joseph brachte alles Geld zusammen, das in Ägypten und Kanaan gefunden ward, um das Getreide, das sie kauften; und Joseph tat alles Geld in das Haus Pharaos.
15 Anthu a ku Igupto ndi Kanaani ndalama zitawathera, Aigupto onse anabwera kwa Yosefe nati, “Tipatseni chakudya. Nanga tiferenji pamaso panu? Ndalama zathu zatha.”
Da nun Geld gebrach im Lande Ägypten und Kanaan, kamen alle Ägypter zu Joseph und sprachen: Schaffe uns Brot! Warum läßt du uns vor dir sterben, darum daß wir ohne Geld sind?
16 Ndipo Yosefe anawayankha kuti, “Bwerani ndi ziweto zanu ndipo tidzasinthana ndi chakudya poti mukuti ndalama zanu zatha.”
Joseph sprach: Schafft euer Vieh her, so will ich euch um das Vieh geben, weil ihr ohne Geld seid.
17 Choncho anthu anabwera ndi ziweto zawo monga akavalo, nkhosa, mbuzi, ngʼombe ndi abulu ndipo Yosefe anawapatsa zakudya.
Da brachten sie Joseph ihr Vieh; und er gab ihnen Brot um ihre Pferde, Schafe, Rinder und Esel. Also ernährte er sie mit Brot das Jahr um all ihr Vieh.
18 Chitatha chaka chimenecho, anthu anapitanso kwa Yosefe chaka chinacho nati, “Ife sitingakubisireni mbuye wathu kuti ndalama zathu zatithera ndipo ziweto zathu zili ndi inu, palibenso choti nʼkukupatsani mbuye wathu kupatula matupi athu ndi dziko lathu.
Da das Jahr um war, kamen sie zu ihm im zweiten Jahr und sprachen zu ihm: Wir wollen unserm Herrn nicht verbergen, daß nicht allein das Geld sondern auch alles Vieh dahin ist zu unserm Herrn; und ist nichts mehr übrig vor unserm Herrn denn unsre Leiber und unser Feld.
19 Tiferenji ife ndi dziko lathu inu mukuona? Mutipatse chakudya ndipo tidzigulitsa ife ndi minda yathu yomwe. Ife tidzakhala akapolo a Farao. Tipatseni mbewuzo kuti tikhale ndi moyo tisafe ndipo dziko lisachite bwinja.”
Warum läßt du uns vor dir sterben und unser Feld? Kaufe uns und unser Land ums Brot, daß wir und unser Land leibeigen seien dem Pharao; gib uns Samen, daß wir leben und nicht sterben und das Feld nicht wüst werde.
20 Choncho Yosefe anamugulira Farao dziko lonse la Igupto. Aliyense mu Igupto anagulitsa munda wake chifukwa njala inakula kwambiri. Dziko lonse linasanduka la Farao,
Also kaufte Joseph dem Pharao das ganze Ägypten. Denn die Ägypter verkauften ein jeglicher seinen Acker, denn die Teuerung war zu stark über sie. Und ward also das Land Pharao eigen.
21 ndipo Yosefe anawasandutsa anthu onse kukhala akapolo a Farao, kuchokera ku malire a mbali ina ya Igupto kukafika ku malire a mbali ina ya dzikolo.
Und er teilte das Volk aus in die Städte, von einem Ende Ägyptens bis ans andere.
22 Komabe, sanagule minda ya ansembe chifukwa Farao ankawapatsa thandizo lokwanira. Nʼchifukwa chake sanagulitse minda yawo.
Ausgenommen der Priester Feld. Das kaufte er nicht; denn es war von Pharao für die Priester verordnet, daß sie sich nähren sollten von dem Verordneten, das er ihnen gegeben hatte; darum brauchten sie ihr Feld nicht zu verkaufen.
23 Yosefe anati kwa anthuwo, “Tsono poti ndakugulani inu ndi minda yanu, kugulira Farao. Nayi mbewu kuti mudzale mʼminda yanu.
Da sprach Joseph zu dem Volk: Siehe, ich habe heute gekauft euch und euer Feld dem Pharao; siehe, da habt ihr Samen und besäet das Feld.
24 Koma podzakolola, mudzapereka gawo limodzi la magawo asanu aliwonse kwa Farao. Magawo anayi enawo adzakhala anu. Zina mudzasunge mbewu ndi zina mudzadye inuyo, mabanja anu ndi ana anu.”
Und von dem Getreide sollt ihr den Fünften geben; vier Teile sollen euer sein, zu besäen das Feld und zu eurer Speise und für euer Haus und eure Kinder.
25 Iwo anati, “Mwatipulumutsa potichitira zabwinozi, mbuye wathu, tsono tidzakhala akapolo a Farao.”
Sie sprachen: Du hast uns am Leben erhalten; laß uns nur Gnade finden vor dir, unserm Herrn, so wollen wir gerne Pharao leibeigen sein.
26 Choncho Yosefe anakhazikitsa lamulo limene lilipobe mpaka lero mʼdziko lonse la Igupto kuti limodzi la magawo asanu a zokolola ndi la Farao. Ndi minda ya ansembe yokha imene sinatengedwe kukhala ya Farao.
Also machte Joseph ihnen ein Gesetz bis auf diesen Tag über der Ägypter Feld, den Fünften Pharao zu geben; ausgenommen der Priester Feld, das ward dem Pharao nicht eigen.
27 Tsono Aisraeli anakhazikika mʼdziko la Igupto ku chigawo cha Goseni. Kumeneko anapeza chuma ndipo anaberekana nachuluka kwambiri.
Also wohnte Israel in Ägypten im Lande Gosen, und hatten's inne und wuchsen und mehrten sich sehr.
28 Yakobo anakhala ku Igupto zaka 17 ndipo zaka za moyo wake zinali 147.
Und Jakob lebte siebzehn Jahre in Ägyptenland, daß sein ganzes Alter ward hundertsiebenundvierzig Jahre.
29 Nthawi itayandikira yoti Israeli amwalire, anayitanitsa mwana wake Yosefe nati kwa iye, “Ngati ukundikondadi monga abambo ako, ika dzanja lako pansi pa ntchafu yanga ndipo ulonjeze kuti udzaonetsa kukoma mtima ndi kukhulupirika kwako kwa ine kuti sudzayika mtembo wanga kuno ku Igupto.
Da nun die Zeit herbeikam, daß Israel sterben sollte, rief er seinen Sohn Joseph und sprach zu ihm: Habe ich Gnade vor dir gefunden, so lege deine Hand unter meine Hüfte, daß du mir die Liebe und Treue an mir tust und begrabest mich nicht in Ägypten;
30 Ine ndikagona pamodzi ndi makolo anga. Choncho ndikadzamwalira udzanditulutse mu Igupto muno ndipo ukayike mtembo wanga kumene anayikidwa makolo anga.” Yosefe anati, “Ndidzachita monga mwanenera.”
sondern ich will liegen bei meinen Vätern, und du sollst mich aus Ägypten führen und in ihrem Begräbnis begraben. Er sprach: Ich will tun, wie du gesagt hast.
31 Yakobo anati, “Lumbira kwa ine.” Yosefe analumbira kwa iye, ndipo Israeli anapembedza Mulungu atatsamira ndodo yake.
Er aber sprach: So schwöre mir. Und er schwur ihm. Da neigte sich Israel zu Häupten des Bettes.