< Genesis 41 >
1 Patapita zaka ziwiri zathunthu, Farao analota atayimirira mʼmbali mwa mtsinje wa Nailo,
2 ndipo anangoona ngʼombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zooneka bwino ndi zonenepa zikutuluka mu mtsinje muja ndi kuyamba kudya msipu wa mu mawango.
3 Kenaka ngʼombe zina zazikazi zisanu ndi ziwiri zosaoneka bwino ndi zowonda zinatulukanso mu mtsinje wa Nailo ndipo zinayimirira pambali pa zina zija zimene zinali mʼmphepete mwa mtsinje uja.
4 Ndipo ngʼombe zosaoneka bwino ndi zowonda zija zinadya ngʼombe zonenepa zija. Kenaka Farao anadzidzimuka.
5 Posakhalitsa anagonanso ndipo analota kachiwiri: Analota ngala zisanu ndi ziwiri za tirigu zathanzi labwino zitabala pa phata limodzi.
6 Kenaka ngala zina zisanu ndi ziwiri zinaphuka. Izi zinali zowonda ndi zowauka ndi mphepo ya kummawa.
7 Ngala zowonda zija zinameza ngala zathanzi ndi zonenepa zija. Farao anadzidzimuka ndipo anaona kuti anali maloto chabe.
8 Mmawa, Farao anavutika mu mtima kotero anayitanitsa amatsenga ndi anzeru onse a mu Igupto. Iwo atabwera, iye anawawuza maloto ake, koma panalibe ndi mmodzi yemwe amene anatha kutanthauzira malotowo kwa Farao.
9 Ndipo mkulu wa operekera zakumwa anati kwa Farao, “Lero ndakumbukira kulephera kwanga.
10 Paja nthawi ina Farao anapsera mtima antchito akefe, ndipo anatitsekera (ine ndi mkulu wa ophika buledi) mʼndende, mʼnyumba ya mkulu wa alonda.
11 Tsiku lina tonse awiri tinalota maloto, ndipo loto lililonse linali ndi tanthauzo lake.
12 Tsono momwemo munali mnyamata wina Wachihebri, wantchito wa mkulu wa alonda. Ife tinamufotokozera maloto athu, ndipo anatitanthauzira malotowo. Munthu aliyense anamupatsa tanthauzo la loto lake.
13 Ndipo zinthu zinachitikadi monga mmene anatitanthauzira. Ine anandibwezera pa ntchito yanga ndipo winayo anapachikidwa.”
14 Choncho Farao anamuyitanitsa Yosefe, ndipo mofulumira anabwera naye kuchokera mʼdzenje muja. Ndipo atameta, ndi kusintha zovala, anapita kwa Farao.
15 Farao anati kwa Yosefe, “Ndinalota maloto ndipo palibe amene watha kunditanthauzira. Tsono ndawuzidwa kuti iwe ukamva loto umadziwanso kulimasulira.”
16 Yosefe anamuyankha Farao kuti, “Sindingathe koma Mulungu apereka yankho limene Farao akufuna.”
17 Ndipo Farao anati kwa Yosefe, “Ndinalota nditayimirira mʼmphepete mwa mtsinje wa Nailo,
18 ndipo ngʼombe zisanu ndi ziwiri zonenepa ndi zooneka bwino zinatuluka mu mtsinje muja ndi kumadya msipu wa mu mawango.
19 Kenaka, ngʼombe zina zisanu ndi ziwiri zinatuluka. Izi zinali zosaoneka bwino ndiponso zowonda ndipo sindinaonepo ngʼombe zosaoneka bwino chonchi mʼdziko lonse la Igupto.
20 Ngʼombe zosaoneka bwino ndi zowonda zija zinadya zisanu ndi ziwiri zonenepa zimene zinatuluka poyamba zija.
21 Koma ngakhale ngʼombezi zinadya zinazo, palibe amene akanatha kuzindikira kuti zinatero popeza zinali zosaonekabe bwino monga poyamba. Ndipo ndinadzidzimuka.
22 “Nditagonanso kachiwiri, ndinalota ngala zisanu ndi ziwiri za tirigu zathanzi ndi zonenepa zitabala pa phata limodzi.
23 Kenaka panaphukanso ngala zina zisanu ndi ziwiri zofota, zowonda ndi zowauka ndi mphepo ya kummawa.
24 Ngala zowondazo zinameza ngala zisanu ndi ziwiri zabwino zija. Ndinawawuza amatsenga koma palibe ndi mmodzi yemwe anatha kundimasulira.”
25 Ndipo Yosefe anati kwa Farao, “Maloto awiriwa ndi ofanana ndipo ali ndi tanthauzo limodzi. Mulungu waululira Farao chimene atachite.
26 Ngʼombe zisanu ndi ziwiri zabwinozo ndi zaka zisanu ndi ziwiri. Ndipo ngala zisanu ndi ziwiri zabwinozo ndi zaka zisanu ndi ziwiri. Kutanthauza kwa maloto nʼkumodzi.
27 Ngʼombe zisanu ndi ziwiri zowonda ndi zosaoneka bwino zimene zinatuluka pambuyozo ndiponso ngala zisanu ndi ziwiri zachabechabe, zowauka ndi mphepo ya kummawa zija ndi zaka zisanu ndi ziwiri za njala.
28 “Tsono ndi monga ndafotokozeramu kuti Mulungu wakuwuziranitu zimene adzachite.
29 Zaka zisanu ndi ziwiri za zokolola zochuluka zikubwera mu dziko lonse la Igupto,
30 koma zidzatsatana ndi zaka zina zisanu ndi ziwiri za njala. Chakudya chochuluka cha mu Igupto chija chidzayiwalika ndipo njalayo idzawononga dziko.
31 Zakudya zochuluka za mʼdzikomo zija sizidzakumbukirikanso chifukwa njala imene iti idzabwereyo idzakhala yoopsa.
32 Popeza kuti malotowa aperekedwa kwa inu Mfumu kawiri, ndiye kuti Mulungu watsimikiza kuti adzachitadi zimenezi posachedwapa.
33 “Tsopano Farao apezeretu munthu wozindikira ndi wanzeru ndipo amuyike kukhala woyangʼanira dziko lonse la Igupto.
34 Asankhenso akuluakulu a mʼdziko lino. Iwowa azitenga ndi kuyika padera limodzi la magawo asanu aliwonse a zokolola za mʼdziko muno mu zaka zonse zisanu ndi ziwiri za chakudya chochuluka.
35 Iwo asonkhanitse zakudya zonse za mʼzaka zabwino zikubwerazi. Pansi pa ulamuliro wa Farao, akuluakuluwo asonkhanitse ndi kusunga bwino tirigu mʼmizinda yonse.
36 Chakudya chimenechi chisungidwe kuti chidzagwiritsidwe ntchito mʼzaka zisanu ndi ziwiri za njala imene ikubwerayo mu Igupto, kuti anthu a mʼdzikoli asadzafe ndi njalayo.”
37 Farao ndi nduna zake anagwirizana nawo malangizo a Yosefe.
38 Choncho Farao anafunsa nduna zake nati, “Kodi tingathe kumupeza munthu wina ngati uyu, amene ali ndi mzimu wa Mulungu?”
39 Farao anati kwa Yosefe, “Pakuti Mulungu wakudziwitsa iwe zonsezi, palibe wina wodziwa zinthu ndi wanzeru ngati iwe.
40 Iwe ukhala nduna yayikulu mu dziko langa ndipo anthu onse adzamvera zimene walamula. Ine ndekha ndiye amene ndidzakuposa mphamvu chifukwa ndimakhala pa mpando waufumu.”
41 Choncho Farao anati kwa Yosefe, “Ine ndikukuyika iwe kukhala nduna yoyangʼanira dziko lonse la Igupto.”
42 Ndipo Farao anavula mphete ku chala chake nayiveka ku chala cha Yosefe. Anamuvekanso mkanjo wonyezimira ndi nkufu wagolide mʼkhosi mwake.
43 Anamukweza Yosefe pa galeta ngati wachiwiri pa ulamuliro. Ndipo anthu anafuwula pamaso pake nati, “Mʼgwadireni!” Motero anakhala nduna yayikulu ya dziko lonse la Igupto.
44 Kenaka Farao anati kwa Yosefe, “Ine ndine Farao; tsono iwe ukapanda kulamula, palibe amene akhoza kuchita chilichonse ngakhale kuyenda kumene mʼdziko lonse la Igupto.”
45 Farao anamupatsa Yosefe dzina lakuti Zafenati-Panea ndipo anamupatsanso Asenati mwana wa mkazi wa Potifara, wansembe wa Oni, kuti akhale mkazi wake. Choncho Yosefe anayendera dziko lonse la Igupto.
46 Yosefe anali ndi zaka 30 pamene amayamba ntchito kwa Farao, mfumu ya ku Igupto. Ndipo Yosefe anachoka pa maso pa Farao nayendera dziko lonse la Igupto.
47 Mʼzaka zisanu ndi ziwiri za zokolola zambiri zija, anthu mʼdzikomo anakolola zochuluka.
48 Yosefe anasonkhanitsa zakudya zonse zokololedwa mʼzaka zisanu ndi ziwiri zija ndipo anazisunga mʼmizinda. Mu mzinda uliwonse anayikamo chakudya chimene chinalimidwa mʼminda yozungulira komweko.
49 Yosefe anasunga tirigu wochuluka kwambiri ngati mchenga wa ku nyanja. Kunali tirigu wochuluka kwambiri motero kuti analeka nʼkulembera komwe.
50 Zisanafike zaka zanjala, Yosefe anabereka ana aamuna awiri mwa Asenati mwana wa mkazi wa Potifara, wansembe wa Oni.
51 Yosefe anamutcha mwana wake woyamba, Manase popeza anati, “Mulungu wandiyiwalitsa zovuta zanga zija ndiponso banja la abambo anga.”
52 Mwana wachiwiri wa mwamuna anamutcha Efereimu popeza anati, “Mulungu wandipatsa ana mʼdziko la masautso anga.”
53 Zaka zisanu ndi ziwiri za zokolola zochuluka zija zinatha,
54 ndipo zaka zisanu ndi ziwiri za njala zija zinayamba monga ananenera Yosefe. Njalayi inafika ku mayiko ena onse koma ku dziko lonse la Igupto kunali chakudya.
55 Pamene njala ija inakwanira dziko lonse la Igupto anthu analilira Farao kuti awapatse chakudya. Koma Farao anawawuza kuti, “Pitani kwa Yosefe ndipo mukachite zimene akakuwuzeni.”
56 Pamene njala inafalikira dziko lonse, Yosefe anatsekula nkhokwe za zakudya namagulitsa tirigu kwa anthu a ku Igupto aja, pakuti njala inafika poyipa kwambiri mu Igupto monse.
57 Anthu ankabwera ku Igupto kuchokera ku mayiko ena onse kudzagula tirigu kwa Yosefe, chifukwa njala inafika poyipa kwambiri pa dziko lonse lapansi.