< Genesis 39 >
1 Tsopano Yosefe anatengedwa kupita ku Igupto. Potifara Mwigupto amene anali mmodzi wa akuluakulu a Farao ndiponso mkulu wa asilikali olonda ku nyumba kwa Farao, anagula Yosefe kwa Aismaeli amene anapita naye kumeneko.
若瑟被人帶到埃及,有個埃及人普提法爾,是法郎的內臣兼衛隊長,從帶若瑟來的依市瑪耳人手裏買了他。
2 Koma Yehova anali ndi Yosefe ndipo zake zonse zimayenda bwino. Iye ankakhala mʼnyumba ya mbuye wake wa ku Igupto.
上主與若瑟同在,他便事事順利,住在他埃及主人家裏。
3 Mbuye wake anaona kuti Yehova anali naye Yosefe ndi kuti pa chilichonse chimene anachita Yehova ankaonetsetsa kuti achite bwino.
他主人見上主與若瑟同在,又見上主使他手中所做的事,無不順利;
4 Potifara anakondwera ndi Yosefe chifukwa cha matumikiridwe ake. Choncho anamusandutsa woyangʼanira nyumba yake ndi zonse za mʼnyumba yake.
為此若瑟在他主人眼中得了寵,令他服事自己,託他管理自己的家務,將所有的一切,都交在他手中。
5 Kuchokera pa nthawi imene anamuyika kukhala woyangʼanira wa nyumbayo ndi zonse za mʼnyumbamo, Yehova anadalitsa nyumba ya Mwiguptoyo chifukwa cha Yosefe. Madalitso a Yehova anali pa chilichonse chimene Potifara anali nacho, za mʼnyumba komanso za ku munda.
自從主人託他管理家務和所有一切以來,上主為若瑟的原故,祝福了這埃及人的家庭,他家內和田間所有的一切,都蒙受了上主的祝福。
6 Choncho anasiyira mʼmanja mwa Yosefe chilichonse chomwe anali nacho, kotero kuti samadandaula ndi chilichonse kupatula chakudya chimene ankadya. Tsopano Yosefe anali wa thupi labwino ndi wokongola.
普提法爾將自己所有的一切,都交在若瑟的手裏;只要有他在,除自己所吃的食物外,其餘一概不管。若瑟生來體態秀雅,容貌俊美。
7 Patapita kanthawi, mkazi wa mbuye wake anayamba kusirira Yosefe nati, “Bwanji ugone nane!”
這些事以後,有一回,主人的妻子向若瑟以目傳情,並且說:「你與我同睡罷! 」
8 Koma iye anakana namuwuza kuti, “Inu mukuona kuti mbuye wanga sadandaula ndi kena kalikonse mʼnyumba muno, ndipo chawo chilichonse anachiyika mʼmanja mwanga.
他立即拒絕,對主人的妻子說:「你看,有我在,家中的事,我主人什麼都不管;凡他所有的一切,都交在我手中。
9 Motero kuti palibe wina wamkulu kuposa ine mʼnyumba muno. Ndipo palibe chilichonse chimene mbuye wanga sanachipereke kwa ine kupatula inuyo, chifukwa ndinu mkazi wake. Tsono ndingachite bwanji choyipa choterechi ndi kuchimwira Mulungu?”
在這一家內,他並不比我更有權勢,因為他沒有留下一樣不交給我;只有你除外,因為你是他的妻子。我怎能做這極惡的事,得罪天主呢﹖」
10 Ndipo ngakhale kuti iye anayankhula mawu omwewa ndi Yosefe tsiku ndi tsiku, Yosefe sanalole kugona naye ngakhale kukhala naye pafupi.
她雖然天天這樣對若瑟說,若瑟總不聽從與她同睡,與她結合。
11 Tsiku lina Yosefe analowa mʼnyumbamo kukagwira ntchito zake, ndipo munalibe wina aliyense wantchito mʼnyumbamo.
有這麼一天,若瑟走進屋內辦事,家人都沒有在屋裏,
12 Mkazi uja anamugwira mkanjo Yosefe nati, “Tiye ugone nane!” Koma Yosefe anasiya mkanjo wake mʼmanja mwa mkaziyo nathawira kunja kwa nyumba.
她便抓住若瑟的衣服說:「與我同睡罷! 」若瑟把自己的外衣,捨在她手中,就跑到外面去了。
13 Pamene mkazi uja anaona kuti Yosefe wamusiyira mkanjo wake mʼmanja mwake nathawira kunja kwa nyumba,
她一見若瑟把自己的外衣捨在她手中,跑到外面去了。
14 iye anayitana antchito ake a mʼnyumba nati, “Taonani mwamuna wanga anabwera ndi Mhebri uyu mʼnyumba muno kuti adzagone nane. Iyeyu analowa ku chipinda kwanga kuti adzagone nane ndipo ine ndinakuwa kwambiri.
就召喚她的家人來,對他們說:「你們看! 他給我們帶來的希伯來人竟敢調戲我啊! 他來到我這裏,要與我同睡,我就大聲呼喊。
15 Atandimva ndikukuwa, anandisiyira mkanjo wakewu nʼkuthawira kunja.”
他一聽見我高聲呼喊,把他的衣服捨在我身邊,就跑到外面去了。」
16 Tsono mkazi wa Potifara uja anasunga mkanjowo mpaka mbuye wake wa Yosefe atabwera ku nyumba.
她便將若瑟的衣服留在身邊,等他的主人回家,
17 Tsono anamuwuza nkhaniyi nati: “Wantchito Wachihebri amene munatibweretsera uja anabwera kuti adzagone nane.
她又用同樣的話給他講述說:「你給我們帶來的那個希伯來僕人,竟到這裏來調戲我。
18 Koma pamene ndinakuwa, iye anandisiyira mkanjo wake nathawira kunja.”
我一高聲呼喊,他就把他的衣服捨在我身邊,跑到外面去了。」
19 Mbuye wake wa Yosefe atamva nkhani imene mkazi wake anamuwuza kuti, “Ndi zimene anandichitira wantchito wanu,” anapsa mtima kwambiri.
主人一聽見他妻子對他所說:「你的僕人如此如此對待我的話,」便大發憤怒。
20 Tsono iye anatenga Yosefe namuyika mʼndende mmene ankasungiramo amʼndende a mfumu. Ndipo Yosefe anakhala mʼndendemo
若瑟的主人遂捉住若瑟放在監裏,即囚禁君王囚犯人的地方。他雖在那裏坐監,
21 koma Yehova anali naye, ndipo anamuonetsa kukoma mtima kwake, kotero kuti woyangʼanira ndende anakondwera ndi Yosefe.
上主仍與他同在,對他施恩,使他在獄長眼中得寵;
22 Choncho woyangʼanira ndende uja anamuyika Yosefe kukhala woyangʼanira onse amene anayikidwa mʼndende. Ndiponso anamupatsa udindo woyangʼanira zonse zochitika mʼndendemo.
因此獄長將監中所有的囚犯都交在若瑟手中;凡獄中應辦的事,都由他辦理。
23 Woyangʼanira ndende uja sankayangʼaniranso china chilichonse chimene chinali mu ulamuliro wa Yosefe, chifukwa Yehova anali ndi Yosefe. Ndipo Yehova anaonetsetsa kuti chilichonse chimene Yosefe ankachita chimuyendere bwino.
凡交在若瑟手中的事,獄長一概不聞不問,因為上主與他同在,凡他所做的,上主無不使之順遂。