< Genesis 38 >

1 Pa nthawi imeneyi, Yuda anasiyana ndi abale ake napita kukakhala ndi munthu wina wa ku Adulamu wotchedwa Hira.
ἐγένετο δὲ ἐν τῷ καιρῷ ἐκείνῳ κατέβη Ιουδας ἀπὸ τῶν ἀδελφῶν αὐτοῦ καὶ ἀφίκετο ἕως πρὸς ἄνθρωπόν τινα Οδολλαμίτην ᾧ ὄνομα Ιρας
2 Kumeneko, Yuda anaona mwana wamkazi wa munthu wina wa Chikanaani wotchedwa Suwa. Anamukwatira nagona naye malo amodzi.
καὶ εἶδεν ἐκεῖ Ιουδας θυγατέρα ἀνθρώπου Χαναναίου ᾗ ὄνομα Σαυα καὶ ἔλαβεν αὐτὴν καὶ εἰσῆλθεν πρὸς αὐτήν
3 Iye anatenga pathupi, nabala mwana wamwamuna amene anamutcha Eri.
καὶ συλλαβοῦσα ἔτεκεν υἱὸν καὶ ἐκάλεσεν τὸ ὄνομα αὐτοῦ Ηρ
4 Anatenganso pathupi nabala mwana wa mwamuna ndipo anamutcha Onani.
καὶ συλλαβοῦσα ἔτι ἔτεκεν υἱὸν καὶ ἐκάλεσεν τὸ ὄνομα αὐτοῦ Αυναν
5 Anaberekanso mwana wina wamwamuna ndipo anamutcha Sela. Ameneyu anabadwa Yuda ali ku Kezibi.
καὶ προσθεῖσα ἔτι ἔτεκεν υἱὸν καὶ ἐκάλεσεν τὸ ὄνομα αὐτοῦ Σηλωμ αὐτὴ δὲ ἦν ἐν Χασβι ἡνίκα ἔτεκεν αὐτούς
6 Yuda anamupezera mkazi mwana wake woyamba uja Eri, ndipo dzina la mkaziyo linali Tamara.
καὶ ἔλαβεν Ιουδας γυναῖκα Ηρ τῷ πρωτοτόκῳ αὐτοῦ ᾗ ὄνομα Θαμαρ
7 Koma ntchito zoyipa za Eri, mwana wachisamba wa Yuda zinayipira Yehova. Choncho Mulungu anamulanga ndi imfa.
ἐγένετο δὲ Ηρ πρωτότοκος Ιουδα πονηρὸς ἐναντίον κυρίου καὶ ἀπέκτεινεν αὐτὸν ὁ θεός
8 Pamenepo Yuda anati kwa Onani, “Kwatira mkazi wamasiye wa mʼbale wako. Ulowe chokolo kuti mʼbale wako akhale ndi mwana.”
εἶπεν δὲ Ιουδας τῷ Αυναν εἴσελθε πρὸς τὴν γυναῖκα τοῦ ἀδελφοῦ σου καὶ γάμβρευσαι αὐτὴν καὶ ἀνάστησον σπέρμα τῷ ἀδελφῷ σου
9 Koma Onani anadziwa kuti mwanayo sadzakhala wake. Choncho nthawi zonse pamene amagona naye mkaziyo, ankatayira umuna pansi kuti asamuberekere mwana mʼbale wake.
γνοὺς δὲ Αυναν ὅτι οὐκ αὐτῷ ἔσται τὸ σπέρμα ἐγίνετο ὅταν εἰσήρχετο πρὸς τὴν γυναῖκα τοῦ ἀδελφοῦ αὐτοῦ ἐξέχεεν ἐπὶ τὴν γῆν τοῦ μὴ δοῦναι σπέρμα τῷ ἀδελφῷ αὐτοῦ
10 Zimene ankachitazi zinayipira Yehova. Choncho anamulanganso ndi imfa.
πονηρὸν δὲ ἐφάνη ἐναντίον τοῦ θεοῦ ὅτι ἐποίησεν τοῦτο καὶ ἐθανάτωσεν καὶ τοῦτον
11 Kenaka Yuda anati kwa mpongozi wake Tamara, “Bwererani ku nyumba ya abambo anu ndi kukhala kumeneko ngati wamasiye mpaka mwana wanga Sela atakula.” Ananena izi chifukwa ankaopa kuti Sela angafenso ngati abale ake aja. Choncho Tamara anapita kukakhala ku nyumba ya abambo ake.
εἶπεν δὲ Ιουδας Θαμαρ τῇ νύμφῃ αὐτοῦ κάθου χήρα ἐν τῷ οἴκῳ τοῦ πατρός σου ἕως μέγας γένηται Σηλωμ ὁ υἱός μου εἶπεν γάρ μήποτε ἀποθάνῃ καὶ οὗτος ὥσπερ οἱ ἀδελφοὶ αὐτοῦ ἀπελθοῦσα δὲ Θαμαρ ἐκάθητο ἐν τῷ οἴκῳ τοῦ πατρὸς αὐτῆς
12 Patapita nthawi yayitali, Batishua, mkazi wa Yuda anamwalira. Yuda atatha kulira maliro a mkazi wake, anapita, iyeyu pamodzi ndi bwenzi lake Hira, Mwadulamu uja, ku Timna kumene ankameta nkhosa zawo.
ἐπληθύνθησαν δὲ αἱ ἡμέραι καὶ ἀπέθανεν Σαυα ἡ γυνὴ Ιουδα καὶ παρακληθεὶς Ιουδας ἀνέβη ἐπὶ τοὺς κείροντας τὰ πρόβατα αὐτοῦ αὐτὸς καὶ Ιρας ὁ ποιμὴν αὐτοῦ ὁ Οδολλαμίτης εἰς Θαμνα
13 Tamara atamva kuti apongozi ake akupita ku Timna kukameta nkhosa,
καὶ ἀπηγγέλη Θαμαρ τῇ νύμφῃ αὐτοῦ λέγοντες ἰδοὺ ὁ πενθερός σου ἀναβαίνει εἰς Θαμνα κεῖραι τὰ πρόβατα αὐτοῦ
14 iye anavula zovala zake za umasiye, nadziphimba nkhope ndi nsalu kuti asadziwike, ndipo anakhala pansi pa chipata cha ku Enaimu popita ku Timna. Tamara anachita izi chifukwa anaona kuti ngakhale Selayo anali atakula tsopano, iye sanaperekedwe kuti amulowe chokolo.
καὶ περιελομένη τὰ ἱμάτια τῆς χηρεύσεως ἀφ’ ἑαυτῆς περιεβάλετο θέριστρον καὶ ἐκαλλωπίσατο καὶ ἐκάθισεν πρὸς ταῖς πύλαις Αιναν ἥ ἐστιν ἐν παρόδῳ Θαμνα εἶδεν γὰρ ὅτι μέγας γέγονεν Σηλωμ αὐτὸς δὲ οὐκ ἔδωκεν αὐτὴν αὐτῷ γυναῖκα
15 Yuda atamuona anangomuyesa mkazi wadama chabe, chifukwa anadziphimba nkhope.
καὶ ἰδὼν αὐτὴν Ιουδας ἔδοξεν αὐτὴν πόρνην εἶναι κατεκαλύψατο γὰρ τὸ πρόσωπον αὐτῆς καὶ οὐκ ἐπέγνω αὐτήν
16 Tsono anapita kwa mkaziyo pamphepete pa msewu paja nati, “Tabwera ndigone nawe.” Apa Yuda sankadziwa kuti mkazi uja anali mpongozi wake. Ndiye mkazi uja anamufunsa Yuda nati, “Mudzandipatsa chiyani kuti ndigone nanu?”
ἐξέκλινεν δὲ πρὸς αὐτὴν τὴν ὁδὸν καὶ εἶπεν αὐτῇ ἔασόν με εἰσελθεῖν πρὸς σέ οὐ γὰρ ἔγνω ὅτι ἡ νύμφη αὐτοῦ ἐστιν ἡ δὲ εἶπεν τί μοι δώσεις ἐὰν εἰσέλθῃς πρός με
17 Iye anati, “Ndidzakutumizira kamwana kambuzi ka mʼkhola mwanga.” Mkaziyo anayankha kuti, “Chabwino, ndavomera, koma mungandipatse chikole mpaka mutanditumizira mbuziyo?”
ὁ δὲ εἶπεν ἐγώ σοι ἀποστελῶ ἔριφον αἰγῶν ἐκ τῶν προβάτων ἡ δὲ εἶπεν ἐὰν δῷς ἀρραβῶνα ἕως τοῦ ἀποστεῖλαί σε
18 Iye anati, “Ndikupatse chikole chanji?” Mkaziyo anayankha, “Mundipatse mphete yanuyo, chingwe chanucho pamodzi ndi ndodo imene ili mʼdzanja lanulo.” Choncho anazipereka kwa iye nagona naye ndipo anatenga pathupi.
ὁ δὲ εἶπεν τίνα τὸν ἀρραβῶνά σοι δώσω ἡ δὲ εἶπεν τὸν δακτύλιόν σου καὶ τὸν ὁρμίσκον καὶ τὴν ῥάβδον τὴν ἐν τῇ χειρί σου καὶ ἔδωκεν αὐτῇ καὶ εἰσῆλθεν πρὸς αὐτήν καὶ ἐν γαστρὶ ἔλαβεν ἐξ αὐτοῦ
19 Kenaka Tamara anachoka, navula nsalu anadziphimba nayo ija, navalanso zovala zake za umasiye zija.
καὶ ἀναστᾶσα ἀπῆλθεν καὶ περιείλατο τὸ θέριστρον ἀφ’ ἑαυτῆς καὶ ἐνεδύσατο τὰ ἱμάτια τῆς χηρεύσεως αὐτῆς
20 Tsono Yuda anatuma bwenzi lake Mwadulamu uja ndi kamwana kambuzi kaja kuti akapereke kwa mkazi wadama uja, ndi kuti akatero amubwezere chikole chake chija. Koma atafika sanamupezepo.
ἀπέστειλεν δὲ Ιουδας τὸν ἔριφον ἐξ αἰγῶν ἐν χειρὶ τοῦ ποιμένος αὐτοῦ τοῦ Οδολλαμίτου κομίσασθαι τὸν ἀρραβῶνα παρὰ τῆς γυναικός καὶ οὐχ εὗρεν αὐτήν
21 Anawafunsa anthu a komweko, “Kodi mkazi wadama uja amene ankakhala pambali pa msewu wa ku Enaimu, ali kuti?” Iwo anayankha, “Sipanakhalepo mkazi wa dama aliyense pano.”
ἐπηρώτησεν δὲ τοὺς ἄνδρας τοὺς ἐκ τοῦ τόπου ποῦ ἐστιν ἡ πόρνη ἡ γενομένη ἐν Αιναν ἐπὶ τῆς ὁδοῦ καὶ εἶπαν οὐκ ἦν ἐνταῦθα πόρνη
22 Choncho anabwerera kwa Yuda nati, “Sindinamupeze mkazi uja. Kuwonjeza apo, anthu a kumeneko amati, ‘Sipanakhalepo mkazi wadama pano.’”
καὶ ἀπεστράφη πρὸς Ιουδαν καὶ εἶπεν οὐχ εὗρον καὶ οἱ ἄνθρωποι οἱ ἐκ τοῦ τόπου λέγουσιν μὴ εἶναι ὧδε πόρνην
23 Pamenepo Yuda anati, “Mulekeni atenge zinthuzo zikhale zake, kuopa kuti anthu angatiseke. Ine sindinalakwe, ndinamutumizira kamwana kambuzika, koma simunamupeze.”
εἶπεν δὲ Ιουδας ἐχέτω αὐτά ἀλλὰ μήποτε καταγελασθῶμεν ἐγὼ μὲν ἀπέσταλκα τὸν ἔριφον τοῦτον σὺ δὲ οὐχ εὕρηκας
24 Patapita miyezi itatu, Yuda anawuzidwa kuti, “Mpongozi wanu Tamara anachita zadama, ndipo zotsatira zake nʼzakuti ali ndi pathupi.” Yuda anati, “Kamutulutseni ndipo mukamutenthe kuti afe!”
ἐγένετο δὲ μετὰ τρίμηνον ἀπηγγέλη τῷ Ιουδα λέγοντες ἐκπεπόρνευκεν Θαμαρ ἡ νύμφη σου καὶ ἰδοὺ ἐν γαστρὶ ἔχει ἐκ πορνείας εἶπεν δὲ Ιουδας ἐξαγάγετε αὐτήν καὶ κατακαυθήτω
25 Akumutulutsa, iye anatuma mawu kwa apongozi ake. Anati, “Ndili ndi pathupi pa munthu amene ndi mwini wake wa zinthu izi. Taziyangʼanitsitsani, kodi mwini wa khoza, chingwe ndi ndodo yoyenderayi ndi yani?”
αὐτὴ δὲ ἀγομένη ἀπέστειλεν πρὸς τὸν πενθερὸν αὐτῆς λέγουσα ἐκ τοῦ ἀνθρώπου τίνος ταῦτά ἐστιν ἐγὼ ἐν γαστρὶ ἔχω καὶ εἶπεν ἐπίγνωθι τίνος ὁ δακτύλιος καὶ ὁ ὁρμίσκος καὶ ἡ ῥάβδος αὕτη
26 Yuda anazizindikira zinthuzo ndipo anati, “Uyu ndi wolungama kuposa ine, chifukwa sindinamupereke kwa mwana wanga Sela.” Ndipo Yuda sanagone nayenso.
ἐπέγνω δὲ Ιουδας καὶ εἶπεν δεδικαίωται Θαμαρ ἢ ἐγώ οὗ εἵνεκεν οὐκ ἔδωκα αὐτὴν Σηλωμ τῷ υἱῷ μου καὶ οὐ προσέθετο ἔτι τοῦ γνῶναι αὐτήν
27 Pamene Tamara nthawi inamukwanira yoti abeleke, mʼmimbamo munali mapasa.
ἐγένετο δὲ ἡνίκα ἔτικτεν καὶ τῇδε ἦν δίδυμα ἐν τῇ γαστρὶ αὐτῆς
28 Pamene ankabereka, mmodzi wa iwo anatulutsa dzanja lake. Choncho mzamba anatenga kawulusi kofiira nakamangirira pa mkono pa mwanayo nati, “Uyu ndiye anayamba kubadwa.”
ἐγένετο δὲ ἐν τῷ τίκτειν αὐτὴν ὁ εἷς προεξήνεγκεν τὴν χεῖρα λαβοῦσα δὲ ἡ μαῖα ἔδησεν ἐπὶ τὴν χεῖρα αὐτοῦ κόκκινον λέγουσα οὗτος ἐξελεύσεται πρότερος
29 Koma pamene anabweza mkonowo, mʼbale wake anabadwa ndipo mzamba anati, “Wachita kudziphotcholera wekha njira chonchi!” Ndipo anamutcha Perezi.
ὡς δὲ ἐπισυνήγαγεν τὴν χεῖρα καὶ εὐθὺς ἐξῆλθεν ὁ ἀδελφὸς αὐτοῦ ἡ δὲ εἶπεν τί διεκόπη διὰ σὲ φραγμός καὶ ἐκάλεσεν τὸ ὄνομα αὐτοῦ Φαρες
30 Pambuyo pake mʼbale wake amene anali ndi ulusi wofiira pa mkono wake uja anabadwa ndipo anapatsidwa dzina lakuti Zera.
καὶ μετὰ τοῦτο ἐξῆλθεν ὁ ἀδελφὸς αὐτοῦ ἐφ’ ᾧ ἦν ἐπὶ τῇ χειρὶ αὐτοῦ τὸ κόκκινον καὶ ἐκάλεσεν τὸ ὄνομα αὐτοῦ Ζαρα

< Genesis 38 >