< Genesis 36 >

1 Nazi zidzukulu za Esau amene ankatchedwanso Edomu:
以扫就是以东,他的后代记在下面。
2 Esau anakwatira akazi atatu a ku Kanaani. Iwowa ndiwo Ada mwana wa Eloni Mhiti; Oholibama mwana wa Ana amene anali mwana wa Zibeoni Mhivi
以扫娶迦南的女子为妻,就是赫人以伦的女儿亚大和希未人祭便的孙女、亚拿的女儿阿何利巴玛,
3 ndi Basemati mwana wa Ismaeli, amenenso anali mlongo wa Nabayoti.
又娶了以实玛利的女儿、尼拜约的妹子巴实抹。
4 Ada anaberekera Esau, Elifazi; Basemati anabereka Reueli;
亚大给以扫生了以利法;巴实抹生了流珥;
5 ndipo Oholibama anabereka Yeusi, Yolamu ndi Kora. Amenewa anali ana a Esau amene anabadwira ku Kanaani.
阿何利巴玛生了耶乌施、雅兰、可拉。这都是以扫的儿子,是在迦南地生的。
6 Esau anatenga akazi ake, ana ake aamuna ndi aakazi ndi ena onse a pa banja pake. Anatenganso ziweto zake ndi ziweto zake zonse pamodzi ndi katundu wake yense amene anamupata ku Kanaani, ndipo anachoka ku dziko la Kanaani kupatukana ndi mʼbale wake Yakobo.
以扫带着他的妻子、儿女,与家中一切的人口,并他的牛羊、牲畜,和一切货财,就是他在迦南地所得的,往别处去,离了他兄弟雅各。
7 Iwo anatero chifukwa dziko limene ankakhalamo silikanakwanira awiriwo. Iwowa anali ndi ziweto zochuluka motero kuti sakanatha kukhala pamodzi.
因为二人的财物群畜甚多,寄居的地方容不下他们,所以不能同居。
8 Choncho Esau (amene ndi Edomu) anakakhazikika ku dziko la mapiri ku Seiri.
于是以扫住在西珥山里;以扫就是以东。
9 Nazi zidzukulu za Esau, kholo la Aedomu amene ankakhala ku Seiri.
以扫是西珥山里以东人的始祖,他的后代记在下面。
10 Awa ndi mayina a ana aamuna a Esau: Elifazi, mwana wa Ada, mkazi wa Esau, ndi Reueli, mwana wamwamuna wa Basemati, mkazi wa Esau.
以扫众子的名字如下。以扫的妻子亚大生以利法;以扫的妻子巴实抹生流珥。
11 Awa ndi mayina a ana a Elifazi: Temani, Omari, Zefo, Gatamu ndi Kenazi.
以利法的儿子是提幔、阿抹、洗玻、迦坦、基纳斯。
12 Timna anali mzikazi wa Elifazi, mwana wa Esau. Iyeyo anaberekera Elifazi mwana dzina lake Amaleki. Amenewa ndiwo zidzukulu za Ada, mkazi wa Esau.
亭纳是以扫儿子以利法的妾;她给以利法生了亚玛力。这是以扫的妻子亚大的子孙。
13 Awa ndi ana a Reueli: Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Amenewa ndi ana a Basemati, mkazi wa Esau.
流珥的儿子是拿哈、谢拉、沙玛、米撒。这是以扫妻子巴实抹的子孙。
14 Ana aamuna a Oholibama, mkazi wa Esau, mwana wa Ana ndi mdzukulu wa Zebeoni ndi awa: Yeusi, Yolamu ndi Kora.
以扫的妻子阿何利巴玛是祭便的孙女,亚拿的女儿;她给以扫生了耶乌施、雅兰、可拉。
15 Nawa mafumu a zidzukulu za Esau: Mwa ana a Elifazi, mwana woyamba wa Esau panali mafumu awa: Temani, Omari, Zefo, ndi Kenazi,
以扫子孙中作族长的记在下面。以扫的长子以利法的子孙中,有提幔族长、阿抹族长、洗玻族长、基纳斯族长、
16 Kora, Gatamu, ndi Amaleki. Awa anali mafumu mwa ana a Elifazi ku Edomu ndipo onsewa anali zidzukulu za Ada.
可拉族长、迦坦族长、亚玛力族长。这是在以东地从以利法所出的族长,都是亚大的子孙。
17 Mwa ana a Reueli, mwana wa Esau munali mafumu awa: Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Awa anali mafumu mwa ana a Reueli ku Edomu. Iwowa anali zidzukulu za Basemati mkazi wa Esau.
以扫的儿子流珥的子孙中,有拿哈族长、谢拉族长、沙玛族长、米撒族长。这是在以东地从流珥所出的族长,都是以扫妻子巴实抹的子孙。
18 Mwa ana a Oholibama, mkazi wa Esau munali mafumu awa: Yeusi, Yolamu, ndi Kora. Amenewa anali mafumu mwa ana a mkazi wa Esau, Oholibama, mwana wa Ana.
以扫的妻子阿何利巴玛的子孙中,有耶乌施族长、雅兰族长、可拉族长。这是从以扫妻子,亚拿的女儿,阿何利巴玛子孙中所出的族长。
19 Amenewa ndiwo zidzukulu za Esau (amene ndi Edomu) ndiponso mafumu awo.
以上的族长都是以扫的子孙;以扫就是以东。
20 Awa ndi ana a Seiri Mhori, amene ankakhala mʼdzikomo: Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana,
那地原有的居民—何利人西珥的子孙记在下面:就是罗坍、朔巴、祭便、亚拿、
21 Disoni, Ezeri ndi Disani. Amenewa ndiwo ana a Seiri a ku Edomu ndipo analinso mafumu a Ahori.
底顺、以察、底珊。这是从以东地的何利人西珥子孙中所出的族长。
22 Ana aamuna a Lotani anali awa: Hori ndi Homamu. Timna anali mlongo wake wa Lotani.
罗坍的儿子是何利、希幔;罗坍的妹子是亭纳。
23 Ana aamuna a Sobala anali awa: Alivani, Manahati, Ebala, Sefo ndi Onamu.
朔巴的儿子是亚勒文、玛拿辖、以巴录、示玻、阿南。
24 Ana aamuna a Zibeoni anali awa: Ayiwa ndi Ana. Uyu ndi Ana amene anapeza akasupe a madzi amoto mʼchipululu pamene ankadyetsa abulu abambo wake Zibeoni.
祭便的儿子是亚雅、亚拿(当时在旷野放他父亲祭便的驴,遇着温泉的,就是这亚拿)。
25 Ana a Ana anali: Disoni ndi Oholibama mwana wake wamkazi.
亚拿的儿子是底顺;亚拿的女儿是阿何利巴玛。
26 Ana aamuna a Disoni anali awa: Hemudani, Esibani, Itirani ndi Kerani.
底顺的儿子是欣但、伊是班、益兰、基兰。
27 Ana aamuna a Ezeri anali awa: Bilihani, Zaavani ndi Akani.
以察的儿子是辟罕、撒番、亚干。
28 Ana aamuna a Disani anali awa: Uzi ndi Arani.
底珊的儿子是乌斯、亚兰。
29 Mafumu a Ahori anali awa: Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana,
从何利人所出的族长记在下面:就是罗坍族长、朔巴族长、祭便族长、亚拿族长、
30 Disoni, Ezeri ndi Disani. Amenewa ndiwo mafumu a Ahori, monga mwa mafuko awo, mʼdziko la Seiri.
底顺族长、以察族长、底珊族长。这是从何利人所出的族长,都在西珥地,按着宗族作族长。
31 Awa ndi mafumu amene ankalamulira dziko la Edomu, mfumu iliyonse ya Israeli isanayambe kulamulira kumeneko:
以色列人未有君王治理以先,在以东地作王的记在下面。
32 Bela mwana wa Beori anakhala mfumu ya ku Edomu. Mzinda wake ankawutcha Dinihaba.
比珥的儿子比拉在以东作王,他的京城名叫亭哈巴。
33 Bela atamwalira, Yobabu mwana wa Zera wochokera ku Bozira analowa ufumu mʼmalo mwake.
比拉死了,波斯拉人谢拉的儿子约巴接续他作王。
34 Atafa Yobabu, Husamu wochokera ku dziko la Atemani, analowa mʼmalo mwake ngati mfumu.
约巴死了,提幔地的人户珊接续他作王。
35 Husamu atamwalira, Hadadi mwana wa Bedadi, amene anagonjetsa Amidiyani mʼdziko la Mowabu, analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Aviti.
户珊死了,比达的儿子哈达接续他作王;这哈达就是在摩押地杀败米甸人的,他的京城名叫亚未得。
36 Hadadi atamwalira, Samila wochokera ku Masireka, analowa ufumu mʼmalo mwake.
哈达死了,玛士利加人桑拉接续他作王。
37 Samila atamwalira, Sauli wochokera ku Rehoboti wa ku Mtsinje, analowa ufumu mʼmalo mwake.
桑拉死了,大河边的利河伯人扫罗接续他作王。
38 Sauli atamwalira, Baala-Hanani, mwana wa Akibori analowa ufumu mʼmalo mwake.
扫罗死了,亚革波的儿子巴勒·哈南接续他作王。
39 Pamene Baala-Hanani mwana wa Akibori anamwalira, Hadari analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Pau, ndipo dzina la mkazi wake linali Mehatabeli, mwana wamkazi wa Matiredi, mwana wamkazi wa Me-Zahabu.
亚革波的儿子巴勒·哈南死了,哈达接续他作王,他的京城名叫巴乌;他的妻子名叫米希她别,是米·萨合的孙女,玛特列的女儿。
40 Mayina a mafumu ochokera mwa zidzukulu za Esau malingana ndi mafuko awo ndi malo a fuko lililonse anali awa: Timna, Aliva, Yeteti,
从以扫所出的族长,按着他们的宗族、住处、名字记在下面:就是亭纳族长、亚勒瓦族长、耶帖族长、
41 Oholibama, Ela, Pinoni,
阿何利巴玛族长、以拉族长、比嫩族长、
42 Kenazi, Temani, Mibezari,
基纳斯族长、提幔族长、米比萨族长、
43 Magidieli ndi Iramu. Awa anali mafumu a ku Edomu molingana ndi malo awo okhala mʼdzikomo. Umenewu ndi mndandanda wa mʼbado wa Esau, kholo la Aedomu.
玛基叠族长、以兰族长。这是以东人在所得为业的地上,按着他们的住处。(所有的族长都是以东人的始祖以扫的后代。)

< Genesis 36 >