< Genesis 24 >

1 Tsopano Abrahamu anali atakalamba kwambiri, ndipo Yehova anamudalitsa mu zonse anachita.
亚伯拉罕年纪老迈,向来在一切事上耶和华都赐福给他。
2 Tsiku lina Abrahamu anawuza wantchito wake wamkulu amene ankayangʼanira zonse anali nazo, kuti “Ika dzanja lako pansi pa ntchafu yanga.
亚伯拉罕对管理他全业最老的仆人说:“请你把手放在我大腿底下。
3 Ndikufuna kuti ulumbire pamaso pa Yehova, Mulungu wakumwamba ndi dziko lapansi, kuti sudzamupezera mwana wanga mkazi pakati pa atsikana Achikanaani a kuno kumene ndikukhala,
我要叫你指着耶和华—天地的主起誓,不要为我儿子娶这迦南地中的女子为妻。
4 koma kuti udzapita ku dziko la kwathu ndi kukamupezera mkazi mwana wanga Isake pakati pa abale anga.”
你要往我本地本族去,为我的儿子以撒娶一个妻子。”
5 Wantchito uja anafunsa kuti, “Nanga atakhala kuti mkaziyo sakufuna kubwera nane kuno? Kodi ine ndingadzatenge mwana wanu ndi kubwerera naye ku dziko kumene munachokera?”
仆人对他说:“倘若女子不肯跟我到这地方来,我必须将你的儿子带回你原出之地吗?”
6 Abrahamu anati, “Uwonetsetse kuti usadzabwerere naye mwana wanga kumeneko.
亚伯拉罕对他说:“你要谨慎,不要带我的儿子回那里去。
7 Yehova Mulungu wakumwamba amene ananditenga kwa makolo anga nanditulutsa mʼdziko lobadwira, ameneyo anayankhula nane molumbira kuti, ‘Kwa zidzukulu zako ndidzapereka dziko ili.’ Iyeyu adzatumiza mngelo wake kuti akutsogolere kumeneko kukapezera mwana wanga mkazi.
耶和华—天上的主曾带领我离开父家和本族的地,对我说话,向我起誓说:‘我要将这地赐给你的后裔。’他必差遣使者在你面前,你就可以从那里为我儿子娶一个妻子。
8 Ngati mkaziyo adzakana kubwerera nawe ndiye kuti udzakhala womasuka ku lumbiro langa. Koma usadzamutenge mwana wanga ndi kubwerera naye kumeneko.”
倘若女子不肯跟你来,我使你起的誓就与你无干了,只是不可带我的儿子回那里去。”
9 Choncho wantchitoyo anayika dzanja lake pansi pa ntchafu ya mbuye wake Abrahamu nalumbira kwa iye kuti adzachitadi monga mwa mawu a Abrahamu.
仆人就把手放在他主人亚伯拉罕的大腿底下,为这事向他起誓。
10 Tsono wantchito uja anatengapo ngamira khumi mwa ngamira za mbuye wake pamodzi ndi zinthu zabwino za mitundumitundu. Ndipo ananyamuka kupita ku mzinda wa Nahori, mʼdziko la Mesopotamiya.
那仆人从他主人的骆驼里取了十匹骆驼,并带些他主人各样的财物,起身往美索不达米亚去,到了拿鹤的城。
11 Atafika, anagwaditsa pansi ngamira zija pafupi ndi chitsime chimene chinali kunja kwa mzinda uja. Awa anali madzulo ndithu, nthawi imene amayi amapita kukatunga madzi.
天将晚,众女子出来打水的时候,他便叫骆驼跪在城外的水井那里。
12 Ndipo wantchito uja anapemphera nati, “Haa, Yehova, Mulungu wa mbuye wanga Abrahamu, mulole kuti zinthu zindiyendere ine lero, ndipo muonetseni mbuye wanga Abrahamu kukoma mtima kwanu kosasinthika.
他说:“耶和华—我主人亚伯拉罕的 神啊,求你施恩给我主人亚伯拉罕,使我今日遇见好机会。
13 Taonani ndayima pambali pa chitsimechi, ndipo atsikana a mu mzindawu akubwera kudzatunga madzi.
我现今站在井旁,城内居民的女子们正出来打水。
14 Ine ndipempha mtsikana wina kuti, ‘Chonde tula mtsuko wako kuti ndimweko madzi.’ Tsono iye akayankha kuti ‘Imwani,’ ndipo ndidzapatsanso ngamira zanu madziwo, ameneyo akhale mkazi amene mwasankhira mtumiki wanu Isake.” Zimenezi zikachitika, ndidzadziwa kuti mwaonetsadi kukoma mtima kwanu kosasinthika kwa mbuye wanga.
我向那一个女子说:‘请你拿下水瓶来,给我水喝’,她若说:‘请喝!我也给你的骆驼喝。’愿那女子就作你所预定给你仆人以撒的妻。这样,我便知道你施恩给我主人了。”
15 Asanatsirize kupemphera, anangoona Rebeka watulukira atasenza mtsuko wake pa phewa. Iyeyu anali mwana wa Betueli mwana wa Milika, mkazi wa Nahori mʼbale wake wa Abrahamu.
话还没有说完,不料,利百加肩头上扛着水瓶出来。利百加是彼土利所生的;彼土利是亚伯拉罕兄弟拿鹤妻子密迦的儿子。
16 Mtsikanayo anali wokongola kwambiri, namwali amene sanadziwe mwamuna. Iye anatsikira ku chitsime nadzaza mtsuko nakweranso ku mtunda.
那女子容貌极其俊美,还是处女,也未曾有人亲近她。她下到井旁,打满了瓶,又上来。
17 Wantchito uja anathamanga kukakumana naye nati, “Chonde patseko madzi pangʼono a mu mtsuko wakowo kuti ndimwe.”
仆人跑上前去迎着她,说:“求你将瓶里的水给我一点喝。”
18 Mtsikanayo anati, “Imwani mbuye wanga.” Ndipo mofulumira anatsitsa mtsuko uja nawuyika mʼmanja ndi kumupatsa kuti amwe.
女子说:“我主请喝!”就急忙拿下瓶来,托在手上给他喝。
19 Atatha kupereka madzi akumwa kwa mlendo uja, mtsikanayo anati, “Ndikatungiranso ngamira madzi kuti zimwe mpaka zitakwana.”
女子给他喝了,就说:“我再为你的骆驼打水,叫骆驼也喝足。”
20 Choncho anafulumira kukhuthula madzi a mu mtsuko aja momwera ziweto, nathamanga kubwerera ku chitsime kukatunga madzi ena, ndipo anatunga okwanira ngamira zake zonse.
她就急忙把瓶里的水倒在槽里,又跑到井旁打水,就为所有的骆驼打上水来。
21 Modekha, munthu uja anayangʼanitsitsa kwambiri mtsikana uja kuti adziwedi ngati Yehova anamutsogolera pa ulendo wake uja kapena ayi.
那人定睛看她,一句话也不说,要晓得耶和华赐他通达的道路没有。
22 Ngamira zija zitatha kumwa, mlendo uja anatulutsa chipini chagolide cholemera theka la sekeli ndi zibangiri zagolide ziwiri zolemera masekeli 100.
骆驼喝足了,那人就拿一个金环,重半舍客勒,两个金镯,重十舍客勒,给了那女子,
23 Kenaka anafunsa namwaliyo kuti, “Chonde tandiwuza, kodi ndiwe mwana wa yani? Ndipo kodi malo alipo kwanu woti ife nʼkugona?”
说:“请告诉我,你是谁的女儿?你父亲家里有我们住宿的地方没有?”
24 Anamuyankha kuti, “Ine ndine mwana wa Betueli, mwana amene Milika anaberekera Nahori.”
女子说:“我是密迦与拿鹤之子彼土利的女儿”;
25 Ndipo anapitiriza kunena kuti, “Chakudya chodyetsa nyamazi chilipo kwathu ndipo malo woti mugone aliponso.”
又说:“我们家里足有粮草,也有住宿的地方。”
26 Kenaka munthuyo anawerama pansi napembedza Yehova,
那人就低头向耶和华下拜,
27 nati, “Alemekezeke Yehova, Mulungu wa mbuye wanga Abrahamu, amene waonetsa kukoma mtima kwake kosasintha ndi kukhulupirika kwake kwa mbuye wanga. Yehova wanditsogolera pa ulendo wanga mpaka ndafika ku nyumba kwa abale ake a mbuye wanga.”
说:“耶和华—我主人亚伯拉罕的 神是应当称颂的,因他不断地以慈爱诚实待我主人。至于我,耶和华在路上引领我,直走到我主人的兄弟家里。”
28 Mtsikana uja anathamanga nakafotokozera zimenezi anthu a kwa amayi ake.
女子跑回去,照着这些话告诉她母亲和她家里的人。
29 Tsono Rebeka anali ndi mlongo wake dzina lake Labani.
利百加有一个哥哥,名叫拉班,看见金环,又看见金镯在他妹子的手上,并听见他妹子利百加的话,说那人对我如此如此说。拉班就跑出来往井旁去,到那人跟前,见他仍站在骆驼旁边的井旁那里,
30 Iyeyu atangoona chipini pa mphuno ndi zibangiri pa mikono ya mlongo wake komanso kumva zimene mlendo uja ananena kwa Rebekayo, anathamangira kwa mlendo uja, ndipo anamupeza atangoyima ndi ngamira zake pafupi ndi chitsime.
31 Iye anati, “Tiyeni kwathu, ndinu munthu amene Yehova wamudalitsa. Bwanji mwangoyimirira panja pano? Ine ndakukonzerani malo ogona inu ndi ngamira zanu.”
便对他说:“你这蒙耶和华赐福的,请进来,为什么站在外边?我已经收拾了房屋,也为骆驼预备了地方。”
32 Choncho munthu uja analowa mʼnyumba. Labani anatsitsa katundu anali pa ngamira uja. Kenaka anazipatsa ngamira zija chakudya, ndiponso anapereka madzi wosamba mapazi kwa mlendo uja ndi anthu ena onse.
那人就进了拉班的家。拉班卸了骆驼,用草料喂上,拿水给那人和跟随的人洗脚;
33 Chakudya chitabwera mlendo uja anati, “Sindidya mpaka nditakuwuzani zimene ndadzera kuno.” Labani anati, “Yankhulani.”
把饭摆在他面前,叫他吃,他却说:“我不吃,等我说明白我的事情再吃。”拉班说:“请说。”
34 Motero iye anati, “Ine ndine wantchito wa Abrahamu.
他说:“我是亚伯拉罕的仆人。
35 Yehova wadalitsa mbuye wanga kwambiri, ndiponso walemera. Wamupatsa nkhosa ndi ngʼombe, siliva ndi golide, antchito aamuna ndi antchito aakazi, komanso ngamira ndi abulu.
耶和华大大地赐福给我主人,使他昌大,又赐给他羊群、牛群、金银、仆婢、骆驼,和驴。
36 Sara, mkazi wa mbuye wanga anamubalira iye mwana wamwamuna ngakhale kuti Sarayo anali wokalamba. Tsono mbuye wanga wamupatsa mwanayo chuma chonse.
我主人的妻子撒拉年老的时候给我主人生了一个儿子;我主人也将一切所有的都给了这个儿子。
37 Tsono mbuye wanga anandilumbiritsa kuti ndisunge mawu ake akuti, ‘Usadzamupezere mwana wanga mkazi kuchokera mwa atsikana a dziko lino la Kanaani,
我主人叫我起誓说:‘你不要为我儿子娶迦南地的女子为妻。
38 koma upite ku banja la abambo anga ndi kwa abale anga kuti ukamupezere mkazi mwana wanga.’”
你要往我父家、我本族那里去,为我的儿子娶一个妻子。’
39 “Ndipo ine ndinati kwa mbuye wanga, ‘Nanga mkaziyo akakapanda kubwera nane pamodzi?’
我对我主人说:‘恐怕女子不肯跟我来。’
40 “Iye anayankha, ‘Yehova amene ndakhala ndikumumvera nthawi zonse, adzatumiza mngelo wake kuti akuperekeze ndipo adzakuthandiza mpaka ukamupezere mwana wanga mkazi kuchokera ku mtundu wanga, wa fuko langa.
他就说:‘我所事奉的耶和华必要差遣他的使者与你同去,叫你的道路通达,你就得以在我父家、我本族那里,给我的儿子娶一个妻子。
41 Ukadzachita zimenezi udzakhala mfulu wosamangidwa ndi lumbiro langali. Koma tsono ukadzafika kwa fuko langa, ndipo ngati sadzalola kukupatsa mbeta ya mwana wanga, aponso udzamasuka ku lumbiro langali.’”
只要你到了我本族那里,我使你起的誓就与你无干。他们若不把女子交给你,我使你起的誓也与你无干。’
42 “Tsono lero lino pamene ndafika pa chitsime, ndinapempha kuti, ‘Yehova, Mulungu wa mbuye wanga, Abrahamu, ngati Inu mwandidalitsadi pa ulendowu,
“我今日到了井旁,便说:‘耶和华—我主人亚伯拉罕的 神啊,愿你叫我所行的道路通达。
43 taonani ndayima pambali pa chitsime ichi; ndipo ndidzati kwa namwali amene atabwere kudzatunga kuti, chonde nditamwako madzi a mu mtsuko wakowu,’
我如今站在井旁,对哪一个出来打水的女子说:请你把你瓶里的水给我一点喝;
44 ndipo ngati adzandiyankha kuti, ‘Imwani ndipo ndizimwetsanso madzi ngamira zanuzi,’ ameneyo akhale yemwe Yehova wamusankhira mwana wa mbuye wanga.”
她若说:你只管喝,我也为你的骆驼打水;愿那女子就作耶和华给我主人儿子所预定的妻。’
45 “Ndisanatsirize kupemphera, ndinangoona Rebeka akutulukira mtsuko wake uli pa phewa. Anatsetserekera ku chitsime kukatunga madzi ndipo ndinati kwa iye, ‘Chonde patseko madzi akumwa.’
我心里的话还没有说完,利百加就出来,肩头上扛着水瓶,下到井旁打水。我便对她说:‘请你给我水喝。’
46 “Mofulumira, anatsitsa mtsuko wake pa phewa pake nati, ‘Imwani ndiponso ndizimwetsa madzi ngamira zanuzi.’ Kotero ine ndinamwa ndipo anamwetsanso ngamirazo.
她就急忙从肩头上拿下瓶来,说:‘请喝!我也给你的骆驼喝。’我便喝了;她又给我的骆驼喝了。
47 “Ndinamufunsa kuti, ‘Ndiwe mwana wa yani?’ “Iye anati, ‘Ndine mwana wa Betueli mwana wa Nahori, amene Milika anamuberekera.’ “Tsono ndinayika chipini pa mphuno yake ndi kumveka zibangiri mʼmikono yake,
我问她说:‘你是谁的女儿?’她说:‘我是密迦与拿鹤之子彼土利的女儿。’我就把环子戴在她鼻子上,把镯子戴在她两手上。
48 kenaka ndinawerama pansi ndi kupembedza Yehova. Ndipo ndinatamanda Yehova, Mulungu wa mbuye wanga Abrahamu, amene anandilondolera mokhulupirika njira yanga. Iye wandifikitsa kwa mʼbale wake kumene ndapezera mbeta mwana wa mbuye wanga.
随后我低头向耶和华下拜,称颂耶和华—我主人亚伯拉罕的 神;因为他引导我走合式的道路,使我得着我主人兄弟的孙女,给我主人的儿子为妻。
49 Tsono ngati mukufuna kuonetsa kukoma mtima kwanu kwa mbuye wanga, ndikuonetsa kukhulupirika kwanu, ndiwuzeni; ndipo ngati si choncho ndiwuzeninso kuti ndidziwe chochita.”
现在你们若愿以慈爱诚实待我主人,就告诉我;若不然,也告诉我,使我可以或向左,或向右。”
50 Labani ndi Betueli anayankha nati, “Izi ndi zochokera kwa Yehova, ndipo ife sitinganenepo kanthu.
拉班和彼土利回答说:“这事乃出于耶和华,我们不能向你说好说歹。
51 Nayu Rebeka, mutengeni muzipita naye kuti akakhale mkazi wa mwana wa mbuye wanu, monga Yehova wanenera.”
看哪,利百加在你面前,可以将她带去,照着耶和华所说的,给你主人的儿子为妻。”
52 Wantchito wa Abrahamu uja atamva zimene anawerama pansi pamaso pa Yehova.
亚伯拉罕的仆人听见他们这话,就向耶和华俯伏在地。
53 Kenaka wantchitoyo anatulutsa ziwiya zagolide ndi zasiliva ndi zovala nazipereka kwa Rebeka. Anaperekanso mphatso zina za mtengowapatali kwa mlongo wake ndi amayi ake a Rebeka.
当下仆人拿出金器、银器,和衣服送给利百加,又将宝物送给她哥哥和她母亲。
54 Tsono wantchito uja ndi anthu amene anali naye anadya, kumwa nagona komweko. Kutacha mmawa wake, wantchito uja anati, “Mundilole ndibwerere kwa mbuye wanga.”
仆人和跟从他的人吃了喝了,住了一夜。早晨起来,仆人就说:“请打发我回我主人那里去吧。”
55 Koma mlongo wake ndi amayi ake a Rebeka anayankha kuti, “Muloleni mtsikanayu abakhala nafe masiku khumi kapena kupyolerapo, kenaka mukhoza kupita.”
利百加的哥哥和她母亲说:“让女子同我们再住几天,至少十天,然后她可以去。”
56 Koma iye anawawuza kuti, “Chonde musandichedwetse. Yehova wandithandiza kale pa ulendo wanga. Mundilole ndibwerere kwa mbuye wanga.”
仆人说:“耶和华既赐给我通达的道路,你们不要耽误我,请打发我走,回我主人那里去吧。”
57 Koma iwo anati, “Bwanji timuyitane mtsikanayo ndipo timufunse ngati afuna kupita nanu panopa.”
他们说:“我们把女子叫来问问她”,
58 Choncho iwo anamuyitana Rebeka uja namufunsa kuti, “Kodi ukufuna kupita ndi munthuyu panopa?” Iye anayankha kuti, “Ndipita.”
就叫了利百加来,问她说:“你和这人同去吗?”利百加说:“我去。”
59 Kotero anamulola Rebeka pamodzi ndi mlezi wake kuti apite ndi wantchito wa Abrahamu pamodzi ndi anthu amene anali naye.
于是他们打发妹子利百加和她的乳母,同亚伯拉罕的仆人,并跟从仆人的,都走了。
60 Ndipo iwo anadalitsa Rebeka ndi kumuwuza kuti, “Iwe ndiwe mlongo wathu, Mulungu akudalitse iwe, ukhale mayi wa anthu miyandamiyanda; ndi kuti zidzukulu zako zidzalanda mizinda ya adani awo.”
他们就给利百加祝福说: 我们的妹子啊,愿你作千万人的母! 愿你的后裔得着仇敌的城门!
61 Kenaka Rebeka ndi antchito ake ananyamuka kukakwera ngamira zawo ndipo anapita naye pamodzi munthu uja. Choncho wantchito uja anatenga Rebeka nʼkumapita.
利百加和她的使女们起来,骑上骆驼,跟着那仆人,仆人就带着利百加走了。
62 Pa nthawiyi nʼkuti Isake atafika kuchokera ku chitsime cha Wamoyo Wondipenya (Beeri-lahai-roi), popeza tsopano ankakhala ku Negevi.
那时,以撒住在南地,刚从庇耳·拉海·莱回来。
63 Tsiku lina chakumadzulo, Isake anatuluka kukayendayenda ku munda, ndipo atakweza maso anaona ngamira zikubwera.
天将晚,以撒出来在田间默想,举目一看,见来了些骆驼。
64 Rebeka nayenso anatukula maso naona Isake. Ndipo anatsika pa ngamira yake
利百加举目看见以撒,就急忙下了骆驼,
65 nafunsa wantchito uja kuti, “Kodi munthu uyo ndi ndani akuyenda mʼmundamo kubwera kudzakumana nafe?” Wantchitoyo anayankha, “Ndiye mbuye wanga.” Choncho Rebeka anatenga nsalu ndi kufunda kumaso.
问那仆人说:“这田间走来迎接我们的是谁?”仆人说:“是我的主人。”利百加就拿帕子蒙上脸。
66 Tsono wantchito uja anawuza Isake zonse zimene anazichita.
仆人就将所办的一切事都告诉以撒。
67 Isake analowa naye Rebeka mu tenti ya amayi ake Sara, ndipo anakhala mkazi wake. Isake anamukonda kwambiri Rebeka mkazi wake motero kuti zimenezi zinamutonthoza imfa ya amayi ake.
以撒便领利百加进了他母亲撒拉的帐棚,娶了她为妻,并且爱她。以撒自从他母亲不在了,这才得了安慰。

< Genesis 24 >