< Genesis 19 >

1 Angelo awiri aja anafika ku Sodomu madzulo ndipo Loti anali atakhala pansi pa chipata cha mzindawo. Loti atawaona, anayimirira ndi kukakumana nawo ndipo anaweramitsa mutu wake pansi mwaulemu.
ויבאו שני המלאכים סדמה בערב ולוט ישב בשער סדם וירא לוט ויקם לקראתם וישתחו אפים ארצה׃
2 Iye anati, “Ambuye wanga, chonde patukirani ku nyumba kwa mtumiki wanu. Mukhoza kusambitsa mapazi anu ndi kugona usiku uno kenaka nʼkumapitirira ndi ulendo wanu mmamawa.” Iwo anati, “Ayi, tigona panja.”
ויאמר הנה נא אדני סורו נא אל בית עבדכם ולינו ורחצו רגליכם והשכמתם והלכתם לדרככם ויאמרו לא כי ברחוב נלין׃
3 Koma iye anawawumiriza kwambiri kotero kuti anapita naye pamodzi ku nyumba kwake. Anawakonzera chakudya buledi wopanda yisiti ndipo anadya.
ויפצר בם מאד ויסרו אליו ויבאו אל ביתו ויעש להם משתה ומצות אפה ויאכלו׃
4 Alendo aja asanapite kogona, amuna onse achinyamata ndi achikulire ochokera mbali zonse za mzinda wa Sodomu anazinga nyumba ya Loti.
טרם ישכבו ואנשי העיר אנשי סדם נסבו על הבית מנער ועד זקן כל העם מקצה׃
5 Iwo anayitana Loti namufunsa kuti, “Ali kuti amuna aja amene afika kuno usiku womwe uno? Atulutse, utipatse kuti tigone nawo malo amodzi.”
ויקראו אל לוט ויאמרו לו איה האנשים אשר באו אליך הלילה הוציאם אלינו ונדעה אתם׃
6 Loti anatuluka panja kukakumana nawo natseka chitseko
ויצא אלהם לוט הפתחה והדלת סגר אחריו׃
7 ndipo anati, “Ayi anzanga, musachite zinthu zoyipa zotere.
ויאמר אל נא אחי תרעו׃
8 Taonani, ine ndili ndi ana anga akazi awiri amene sanagonepo ndi mwamuna. Mundilole ndikutulutsireni amenewo ndipo muchite nawo zimene mungafune. Koma musachite chilichonse ndi anthuwa, pakuti iwowa ndi alendo anga ndipo ndiyenera kuwatchinjiriza.”
הנה נא לי שתי בנות אשר לא ידעו איש אוציאה נא אתהן אליכם ועשו להן כטוב בעיניכם רק לאנשים האל אל תעשו דבר כי על כן באו בצל קרתי׃
9 Iwo anayankha kuti, “Tachoka apa tidutse.” Ndipo anati, “Munthu uyu anabwera kuno ngati mlendo chabe, tsono lero akufuna kuti akhale wotiweruza! Tikukhawulitsa kuposa iwowa.” Anapitiriza kumuwumiriza Loti uja nʼkumasunthira kutsogolo kuti athyole chitseko.
ויאמרו גש הלאה ויאמרו האחד בא לגור וישפט שפוט עתה נרע לך מהם ויפצרו באיש בלוט מאד ויגשו לשבר הדלת׃
10 Koma anthu aja anali mʼkatiwa anasuzumira namukokera Loti uja mʼkati mwa nyumba nʼkutseka chitseko.
וישלחו האנשים את ידם ויביאו את לוט אליהם הביתה ואת הדלת סגרו׃
11 Kenaka anawachititsa khungu anthu amene anali panja pa nyumba aja, aangʼono ndi aakulu omwe, kuti asaone pa khomo.
ואת האנשים אשר פתח הבית הכו בסנורים מקטן ועד גדול וילאו למצא הפתח׃
12 Anthu awiri aja anati kwa Loti, “Kodi uli ndi wina aliyense pano, kaya ndi akamwini ako, kaya ndi ana ako aamuna kapena aakazi, kapena aliyense mu mzindamu amene ndi anzako? Atulutse onse muno,
ויאמרו האנשים אל לוט עד מי לך פה חתן ובניך ובנתיך וכל אשר לך בעיר הוצא מן המקום׃
13 chifukwa tiwononga malo ano. Yehova waona kuti kuyipa kwa anthu a mu mzindawu kwakulitsa. Choncho watituma kuti tiwuwononge.”
כי משחתים אנחנו את המקום הזה כי גדלה צעקתם את פני יהוה וישלחנו יהוה לשחתה׃
14 Choncho Loti anatuluka nayankhula ndi akamwini ake amene anali kuyembekezera kukwatira ana ake akazi nati, “Fulumirani, tiyeni tichoke pa malo ano chifukwa Yehova watsala pangʼono kuwononga mzindawu.” Koma akamwini akewo ankayesa kuti akungoselewula.
ויצא לוט וידבר אל חתניו לקחי בנתיו ויאמר קומו צאו מן המקום הזה כי משחית יהוה את העיר ויהי כמצחק בעיני חתניו׃
15 Mmene kumacha, angelo aja anamufulumizitsa Loti nati, “Nyamuka, tenga mkazi wako ndi ana ako aakazi awiriwo, ndipo mutuluke mu mzindawo kuopa kuti mungaphedwe pamodzi nawo.”
וכמו השחר עלה ויאיצו המלאכים בלוט לאמר קום קח את אשתך ואת שתי בנתיך הנמצאת פן תספה בעון העיר׃
16 Koma Loti ankakayikabe. Koma Yehova anawachitira chifundo motero kuti anthu aja anagwira mkazi wake ndi ana ake aakazi aja nawatsogolera bwinobwino kuwatulutsa mu mzindawo.
ויתמהמה ויחזקו האנשים בידו וביד אשתו וביד שתי בנתיו בחמלת יהוה עליו ויצאהו וינחהו מחוץ לעיר׃
17 Atangowatulutsa, mmodzi wa angelowo anati, “Thawani kuti mudzipulumutse, musachewuke, musayime pena paliponse mʼchigwamo! Thawirani ku mapiri kuopa kuti mungawonongeke!”
ויהי כהוציאם אתם החוצה ויאמר המלט על נפשך אל תביט אחריך ואל תעמד בכל הככר ההרה המלט פן תספה׃
18 Koma Loti anawawuza kuti, “Ayi, ambuye anga chonde musatero!
ויאמר לוט אלהם אל נא אדני׃
19 Taonani, Inu mwachitira mtumiki wanu chifundo, ndipo mwaonetsa kukoma mtima kwanu pondipulumutsa. Sindingathawire ku mapiri chifukwa chiwonongekochi chikhoza kundipeza ndisanafike ku mapiriko ndipo ndingafe.
הנה נא מצא עבדך חן בעיניך ותגדל חסדך אשר עשית עמדי להחיות את נפשי ואנכי לא אוכל להמלט ההרה פן תדבקני הרעה ומתי׃
20 Koma, chapafupi pomwepa pali mudzi woti ndikhoza kuthamanga nʼkukafikako. Mundilole ndithawireko, ndi waungʼono kwambiri, si choncho? Mukatero, moyo wanga upulumuka.”
הנה נא העיר הזאת קרבה לנוס שמה והיא מצער אמלטה נא שמה הלא מצער הוא ותחי נפשי׃
21 Mngeloyo anati kwa iye, “Chabwino, ndavomeranso pempho lako, sindiwononga mudzi ukunenawo.
ויאמר אליו הנה נשאתי פניך גם לדבר הזה לבלתי הפכי את העיר אשר דברת׃
22 Koma uthawireko mofulumira chifukwa sindichita kena kalikonse mpaka utafikako.” (Nʼchifukwa chake mudziwo unatchedwa Zowari).
מהר המלט שמה כי לא אוכל לעשות דבר עד באך שמה על כן קרא שם העיר צוער׃
23 Pamene Loti amafika ku Zowari, nʼkuti dzuwa litatuluka.
השמש יצא על הארץ ולוט בא צערה׃
24 Ndiye Yehova anathira sulufule wamoto wochokera kumwamba kwa Yehova pa Sodomu ndi Gomora.
ויהוה המטיר על סדם ועל עמרה גפרית ואש מאת יהוה מן השמים׃
25 Kotero, anawononga mizindayo, chigwa chonse pamodzi ndi onse okhala mʼmizindayo. Anawononganso zomera zonse za mʼdzikolo.
ויהפך את הערים האל ואת כל הככר ואת כל ישבי הערים וצמח האדמה׃
26 Koma mkazi wa Loti anachewuka ndipo anasanduka mwala wa mchere.
ותבט אשתו מאחריו ותהי נציב מלח׃
27 Mmawa mwake, Abrahamu ananyamuka nabwerera kumalo kumene anakumana ndi Yehova kuja.
וישכם אברהם בבקר אל המקום אשר עמד שם את פני יהוה׃
28 Anayangʼana kumunsi ku Sodomu, Gomora ndi ku dziko lonse la ku chigwa, ndipo anaona chiwutsi chikufuka mʼdzikolo ngati chikuchokera mʼngʼanjo.
וישקף על פני סדם ועמרה ועל כל פני ארץ הככר וירא והנה עלה קיטר הארץ כקיטר הכבשן׃
29 Choncho Mulungu anawononga mizinda ya ku chigwa, koma anakumbukira pemphero la Abrahamu natulutsa Loti ku sulufule ndi moto zimene zinawononga mizinda ya kumene Loti amakhalako.
ויהי בשחת אלהים את ערי הככר ויזכר אלהים את אברהם וישלח את לוט מתוך ההפכה בהפך את הערים אשר ישב בהן לוט׃
30 Loti ndi ana ake awiri aakazi anachoka ku Zowari nakakhala ku mapiri, chifukwa amachita mantha kukhala ku Zowari. Iye ndi ana ake awiri ankakhala mʼphanga.
ויעל לוט מצוער וישב בהר ושתי בנתיו עמו כי ירא לשבת בצוער וישב במערה הוא ושתי בנתיו׃
31 Tsiku lina mwana wake wamkazi wamkulu anawuza mngʼono wake kuti, “Abambo athu ndi wokalamba ndipo palibe mwamuna aliyense pano woti atikwatire ndi kubereka ana monga mwa chikhalidwe cha pa dziko lonse lapansi.
ותאמר הבכירה אל הצעירה אבינו זקן ואיש אין בארץ לבוא עלינו כדרך כל הארץ׃
32 Tiye tiwamwetse vinyo ndipo tigone nawo. Tikatero mtundu wathu udzakhalapobe.”
לכה נשקה את אבינו יין ונשכבה עמו ונחיה מאבינו זרע׃
33 Usiku umenewo analedzeretsa vinyo abambo awo, ndipo wamkuluyo analowa nagona naye. Abambo awo samadziwa kanthu pamene mwanayo anagona naye kapena pamene anadzuka.
ותשקין את אביהן יין בלילה הוא ותבא הבכירה ותשכב את אביה ולא ידע בשכבה ובקומה׃
34 Tsiku linali mwana wamkazi wamkulu uja anati kwa mngʼono wake, “Usiku wathawu ine ndinagona ndi abambo anga. Tiye tiwaledzeretsenso vinyo usiku uno ndipo iwe upite ndi kugona nawo ndipo mtundu wathu udzakhalapobe.”
ויהי ממחרת ותאמר הבכירה אל הצעירה הן שכבתי אמש את אבי נשקנו יין גם הלילה ובאי שכבי עמו ונחיה מאבינו זרע׃
35 Choncho analedzeranso vinyo abambo awo usiku umenewonso, ndipo mwana wamkazi wamngʼono anapita nagona nawo. Abambo awo sanadziwenso kanthu pamene mwanayo anagona naye kapena pamene anadzuka.
ותשקין גם בלילה ההוא את אביהן יין ותקם הצעירה ותשכב עמו ולא ידע בשכבה ובקמה׃
36 Choncho ana onse awiri a Loti aja anatenga pathupi pa abambo awo.
ותהרין שתי בנות לוט מאביהן׃
37 Mwana wamkazi wamkulu uja anabereka mwana wa mwamuna ndipo anamutcha Mowabu. Iyeyo ndiye kholo la Amowabu onse.
ותלד הבכירה בן ותקרא שמו מואב הוא אבי מואב עד היום׃
38 Mwana wamkazi wamngʼono naye anabereka mwana wamwamuna, ndipo anamutcha iye Beni-Ammi. Iyeyu ndiye kholo la Aamoni onse.
והצעירה גם הוא ילדה בן ותקרא שמו בן עמי הוא אבי בני עמון עד היום׃

< Genesis 19 >