< Genesis 12 >

1 Tsiku lina Yehova anamuwuza Abramu kuti, “Tuluka mʼdziko lako. Siya abale ako ndi banja la abambo ako ndipo pita ku dziko limene ndidzakusonyeza.
耶和華對亞伯蘭說:「你要離開本地、本族、父家,往我所要指示你的地去。
2 “Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu wa anthu ndipo ndidzakudalitsa; ndi kukusandutsa wotchuka kotero kuti udzakhala dalitso kwa anthu ambiri.
我必叫你成為大國。我必賜福給你,叫你的名為大;你也要叫別人得福。
3 Ndidzadalitsa amene adzadalitsa iwe, ndi kutemberera amene adzatemberera iwe; ndipo mafuko onse a pa dziko lapansi adzadalitsika kudzera mwa iwe.”
為你祝福的,我必賜福與他;那咒詛你的,我必咒詛他。地上的萬族都要因你得福。」
4 Choncho Abramu ananyamuka monga momwe Yehova anamuwuzira, napita pamodzi ndi Loti. Pamene Abramu amachoka ku Harani nʼkuti ali ndi zaka 75.
亞伯蘭就照着耶和華的吩咐去了;羅得也和他同去。亞伯蘭出哈蘭的時候年七十五歲。
5 Abramu anatenga mkazi wake Sarai, Loti, mwana wamngʼono wake, pamodzi ndi chuma chawo chimene anapeza ndi antchito amene anali nawo ku Harani. Iwo ananyamuka ulendo mpaka kukafika ku dziko la Kanaani.
亞伯蘭將他妻子撒萊和姪兒羅得,連他們在哈蘭所積蓄的財物、所得的人口,都帶往迦南地去。他們就到了迦南地。
6 Abramu anadutsa mʼdzikomo mpaka kukafika ku Sekemu pa mtengo wa thundu wa ku More. Nthawi imeneyo Akanaani analipobe mʼdzikomo.
亞伯蘭經過那地,到了示劍地方、摩利橡樹那裏。那時迦南人住在那地。
7 Yehova anadza kwa Abramu nati, “Kwa zidzukulu zako ndidzapereka dziko limeneli.” Choncho Abramu anamangira Yehova amene anadza kwa iye, guwa lansembe.
耶和華向亞伯蘭顯現,說:「我要把這地賜給你的後裔。」亞伯蘭就在那裏為向他顯現的耶和華築了一座壇。
8 Atachoka pamenepo analowera cha ku mapiri a kummawa kwa Beteli namangako tenti yake pakati pa Beteli chakumadzulo ndi Ai chakummawa. Kumeneko anamangira Yehova guwa lansembe napemphera mʼdzina la Yehovayo.
從那裏他又遷到伯特利東邊的山,支搭帳棚;西邊是伯特利,東邊是艾。他在那裏又為耶和華築了一座壇,求告耶和華的名。
9 Kenaka Abramu ananyamuka kumalowera cha ku Negevi.
後來亞伯蘭又漸漸遷往南地去。
10 Kunagwa njala yayikulu mʼdzikomo, ndipo Abramu anapita ku Igupto kukakhala ngati mlendo kwa kanthawi kochepa popeza njalayo inakula kwambiri.
那地遭遇饑荒。因饑荒甚大,亞伯蘭就下埃及去,要在那裏暫居。
11 Atatsala pangʼono kulowa mu Igupto, Abramu anamuwuza mkazi wake Sarai kuti, “Ndimadziwa kuti ndiwe mkazi wokongola kwambiri.
將近埃及,就對他妻子撒萊說:「我知道你是容貌俊美的婦人。
12 Tsono Aigupto akakuona adzanena kuti ‘Ameneyu ndi mkazi wake.’ Tsono adzandipha ine nakusiya iwe ndi moyo.
埃及人看見你必說:『這是他的妻子』,他們就要殺我,卻叫你存活。
13 Tsono udzikawawuza kuti iwe ndiwe mlongo wanga. Ukatero zidzandiyendera bwino ndipo ndidzapulumuka chifukwa cha iwe.”
求你說,你是我的妹子,使我因你得平安,我的命也因你存活。」
14 Pamene Abramu anafika ku Igupto, Aigupto aja anaona kuti Sarai anali mkazi wokongoladi.
及至亞伯蘭到了埃及,埃及人看見那婦人極其美貌。
15 Pamene akuluakulu a ku nyumba ya Farao anamuona, anakamuyamikira pamaso pa Farao ndipo ananka naye ku nyumba ya Farao.
法老的臣宰看見了她,就在法老面前誇獎她。那婦人就被帶進法老的宮去。
16 Abramu naye zinthu zinkamuyendera bwino chifukwa cha Sarai. Farao anamupatsa nkhosa, ngʼombe, abulu aamuna ndi abulu aakazi, antchito aakazi pamodzi ndi ngamira.
法老因這婦人就厚待亞伯蘭,亞伯蘭得了許多牛、羊、駱駝、公驢、母驢、僕婢。
17 Koma Yehova anabweretsa matenda owopsa pa Farao pamodzi ndi banja lake lonse chifukwa cha Sarai mkazi wa Abramu.
耶和華因亞伯蘭妻子撒萊的緣故,降大災與法老和他的全家。
18 Choncho Farao anayitanitsa Abramu namufunsa kuti, “Nʼchiyani wandichitirachi? Nʼchifukwa chiyani sunandiwuze kuti ameneyu ndi mkazi wako?
法老就召了亞伯蘭來,說:「你這向我做的是甚麼事呢?為甚麼沒有告訴我她是你的妻子?
19 Nʼchifukwa chiyani unati ndi mlongo wako, mpaka ine ndinamutenga kukhala mkazi wanga? Eko mkazi wako. Mutenge uzipita!”
為甚麼說她是你的妹子,以致我把她取來要作我的妻子?現在你的妻子在這裏,可以帶她走吧。」
20 Farao analamula asilikali ake ndipo iwo anamutulutsa Abramu pamodzi ndi mkazi wake ndi zonse anali nazo.
於是法老吩咐人將亞伯蘭和他妻子,並他所有的都送走了。

< Genesis 12 >