< Genesis 11 >

1 Nthawi imeneyo anthu onse a pa dziko lapansi ankayankhula chiyankhulo chimodzi ndipo mawu amene ankayankhula anali amodzi.
Byla pak všecka země jazyku jednoho a řeči jedné.
2 Pamene anthu amapita chakummawa anapeza chigwa ku dziko la Sinara nakhazikikako.
I stalo se, když se brali od východu, nalezli pole v zemi Sinear, a bydlili tam.
3 Tsono anawuzana kuti, “Tiyeni tiwumbe njerwa ndi kuziwotcha bwinobwino.” Tsono mʼmalo mwa miyala anagwiritsa ntchito njerwa zowotcha, ndipo mʼmalo mwa matope anagwiritsa ntchito phula.
A řekli jeden druhému: Nuže, nadělejme cihel, a vypalme je ohněm. I měli cihly místo kamení, a zemi lepkou místo vápna.
4 Kenaka anati, “Tiyeni tidzimangire mzinda wokhala ndi nsanja yoti ikafike kumwamba kuti titchuke. Kupanda kutero tibalalikana pa dziko lonse lapansi.”
Nebo řekli: Nuže, vystavějme sobě město a věži, jejíž by vrch dosahal k nebi; a tak učiňme sobě jméno, abychom nebyli rozptýleni po vší zemi.
5 Koma Yehova anatsika kudzaona mzindawo ndi nsanja imene anthu aja ankayimanga.
Sstoupil pak Hospodin, aby viděl to město a věži, kterouž stavěli synové lidští.
6 Yehova anati, “Anthuwa ndi amodzi, ndipo ali ndi chiyankhulo chimodzi. Izi akuchitazi nʼchiyambi chabe cha zomwe akufuna kukwaniritsa kuchita.
A řekl Hospodin: Aj, lid jeden a jazyk jeden všechněch těchto, a toť jest začátek díla jejich; nyní pak nedadí sobě v tom překaziti, což umínili dělati.
7 Tiyeni titsikireko tikasokoneze chiyankhulo chawo kuti asamamvetsetsane.”
Protož sstupme a změťme tam jazyk jejich, aby jeden druhého jazyku nerozuměl.
8 Choncho Yehova anabalalitsa anthu aja pa dziko lonse lapansi ndipo analeka kumanga mzindawo.
A tak rozptýlil je Hospodin odtud po vší zemi; i přestali stavěti města toho.
9 Nʼchifukwa chake mzindawo unatchedwa Babeli, popeza Yehova anasokoneza chiyankhulo cha anthu onse. Powachotsa kumeneko, Yehova anawabalalitsira pa dziko lonse lapansi.
Protož nazváno jest jméno jeho Bábel; nebo tu zmátl Hospodin jazyk vší země; a odtud rozptýlil je Hospodin po vší zemi.
10 Nayi mibado yochokera kwa Semu. Patapita zaka ziwiri chitatha chigumula, Semu ali ndi zaka 100, anabereka Aripakisadi.
Titoť jsou rodové Semovi: Sem, když byl ve stu letech, zplodil Arfaxada ve dvou letech po potopě.
11 Atabereka Aripakisadi, Semu anakhala ndi moyo zaka 500 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
A byl živ Sem po zplození Arfaxada pět set let; a plodil syny a dcery.
12 Pamene Aripakisadi anali ndi zaka 35, anabereka Sela.
Arfaxad pak živ byl pět a třidceti let, a zplodil Sále.
13 Atabereka Sela, Aripakisadi anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
A po zplození Sále živ byl Arfaxad čtyři sta a tři léta; a plodil syny a dcery.
14 Pamene Sela anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Eberi.
Sále také živ byl třidceti let, a zplodil Hebera.
15 Atabereka Eberi, Sela anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
A živ byl Sále po zplození Hebera čtyři sta a tři léta; a plodil syny a dcery.
16 Pamene Eberi anali ndi zaka 34 anabereka Pelegi.
Živ pak byl Heber čtyři a třidceti let, a zplodil Pelega.
17 Atabereka Pelegi, Eberi anakhala ndi moyo zaka zina 430 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
A živ byl Heber po zplození Pelega čtyři sta a třidceti let; a plodil syny a dcery.
18 Pamene Pelegi anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Reu.
Peleg pak živ byl třidceti let, a zplodil Réhu.
19 Atabereka Reu, Pelegi anakhala zaka zina 209 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
A živ byl Peleg po zplození Réhu dvě stě a devět let; a plodil syny a dcery.
20 Pamene Reu anali ndi zaka 32, anabereka Serugi.
Réhu také živ byl třidceti a dvě létě, a zplodil Sáruga.
21 Atabereka Serugi, Reu anakhala ndi moyo zaka zina 207 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
A po zplození Sáruga živ byl Réhu dvě stě a sedm let; a plodil syny a dcery.
22 Pamene Serugi anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Nahori.
Živ pak byl Sárug třidceti let, a zplodil Náchora.
23 Atabereka Nahori, Serugi anakhala ndi moyo zaka zina 200 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
A byl živ Sárug po zplození Náchora dvě stě let; a plodil syny a dcery.
24 Pamene Nahori anali ndi zaka 29, anabereka Tera.
Náchor pak živ byl dvadceti a devět let, a zplodil Táre.
25 Atabereka Tera, Nahori anakhala ndi moyo zaka zina 119 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
A živ byl Náchor po zplození Táre sto a devatenácte let; a plodil syny a dcery.
26 Pamene Tera anali ndi zaka 70, anabereka Abramu, Nahori ndi Harani.
Živ pak byl Táre sedmdesáte let, a zplodil Abrama, Náchora a Hárana.
27 Nayi mibado yochokera mwa Tera. Tera anabereka Abramu, Nahori ndi Harani. Ndipo Harani anabereka Loti.
Tito jsou pak rodové Táre: Táre zplodil Abrama, Náchora a Hárana; Háran pak zplodil Lota.
28 Abambo ake a Tera akanali ndi moyo, Harani anamwalira ku Uri wa ku Akaldeya kumene anabadwira.
Umřel pak Háran prvé než Táre otec jeho v zemi narození svého, totiž v Ur Kaldejských.
29 Abramu ndi Nahori onse anakwatira. Dzina la mkazi wa Abramu linali Sarai, ndipo la mkazi wa Nahori linali Milika. Iyeyu ndi Isika abambo awo anali Harani.
I zpojímali sobě ženy Abram a Náchor; jméno ženy Abramovy Sarai, a jméno ženy Náchorovy Melcha, dcera Háranova, kterýž byl otec Melchy a Jeschy.
30 Sarai analibe ana chifukwa anali wosabereka.
Byla pak Sarai neplodná, a neměla dětí.
31 Tera anatenga mwana wake Abramu, mdzukulu wake Loti, ndi mpongozi wake Sarai, mkazi wa Abramu natuluka mzinda wa Uri wa ku Akaldeya kupita ku Kanaani. Pamene anafika ku Harani, anakhazikika kumeneko.
I vzal Táre Abrama syna svého, a Lota syna Háranova, vnuka svého, a Sarai nevěstu svou, ženu Abrama syna svého, a vyšli spolu z Ur Kaldejských, aby se brali do země Kananejské, a přišli až do Cháran, a bydlili tam.
32 Tera anamwalira ku Harani ali ndi zaka 205.
A byli dnové Táre dvě stě a pět let; i umřel Táre v Cháran.

< Genesis 11 >