< Genesis 10 >

1 Nayi mbiri ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti. Ana atatuwa anabereka ana awo chitatha chigumula.
ノアの子セム、ハム、ヤペテの傳は是なり洪水の後彼等に子等生れたり
2 Ana aamuna a Yafeti anali: Gomeri, Magogi, Madai, Yavani, Tubala, Mesaki ndi Tirasi.
ヤペテの子はゴメル、マゴグ、マデア、ヤワン、トバル、メセク、テラスなり
3 Ana aamuna a Gomeri anali: Asikenazi, Rifati ndi Togarima.
ゴメルの子はアシケナズ、リパテ、トガルマなり
4 Ana aamuna a Yavani anali: Elisa, Tarisisi, Kitimu ndi Rodanimu.
ヤワンの子はエリシヤ、タルシシ、キツテムおよびドダニムなり
5 (Amenewa ndiwo makolo a anthu okhala mʼmphepete mwa nyanja. Awa ndi ana a Yafeti monga mwa mafuko a mu mitundu yawo, uliwonse ndi chiyankhulo chake).
是等より諸國の洲島の民は派分れ出て各其方言と其宗族と其邦國とに循ひて其地に住り
6 Ana aamuna a Hamu anali: Kusi, Miziraimu, Puti ndi Kanaani.
ハムの子はクシ、ミツライム、フテおよびカナンなり
7 Ana aamuna a Kusi anali: Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka. Ana aamuna a Raama anali: Seba ndi Dedani.
クシの子はセバ、ハビラ、サブタ、ラアマ、サブテカなりラアマの子はシバおよびデダンなり
8 Kusi anabereka Nimurodi amene anali wankhondo wamphamvu kwambiri pa dziko lapansi.
クシ、ニムロデを生り彼始めて世の權力ある者となれり
9 Iye anali mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova; nʼchifukwa chake anthu ali ndi chisudzo, chakuti, “Ndiwe mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova monga Nimurodi.”
彼はヱホバの前にありて權力ある獵夫なりき是故にヱホバの前にある夫權力ある獵夫ニムロデの如しといふ諺あり
10 Malo oyambirira a ufumu wake anali Babeli, Ereki, Akadi ndi Kaline. Malo onsewa anali mʼdziko la Sinara.
彼の國の起初はシナルの地のバベル、エレク、アツカデ、及びカルネなりき
11 Atachoka mʼdziko limeneli anapita ku Asiriya kumene anakamanga Ninive, Rehoboti-Iri, Kala,
其地より彼アッスリヤに出でニネベ、レホポテイリ、カラ
12 ndi Reseni, mzinda waukulu umene uli pakati pa Ninive ndi Kala.
およびニネベとカラの間なるレセンを建たり是は大なる城邑なり
13 Igupto ndiye kholo la Aludi, Aanami, Alehabu, Anafutu,
ミツライム、ルデ族アナミ族レハビ族ナフト族
14 Apaturusi, Akasilu ndi Akafitori (kumene kunachokera Afilisti).
バテロス族カスル族およびカフトリ族を生りカスル族よりペリシテ族出たり
15 Kanaani anabereka mwana wake wachisamba, Sidoni, ndipo anaberekanso Ahiti;
カナン其冢子シドンおよびヘテ
16 Ayebusi, Aamori, Agirigasi;
エブス族アモリ族ギルガシ族
17 Ahivi, Aariki, Asini,
ヒビ族アルキ族セニ族
18 Aaravadi, Azemari ndi Ahamati. Pambuyo pake, mafuko a Akanaani anafalikira ponseponse,
アルワデ族ゼマリ族ハマテ族を生り後に至りてカナン人の宗族蔓延りぬ
19 mpaka ku malire a Kanaani. Malirewo anachokera ku Sidoni kulowa cha ku Gerari mpaka ku Gaza, ndi kulowa ku Sodomu, Gomora, Adima ndi Zeboimu mpaka ku Lasa.
カナン人の境はシドンよりゲラルを經てガザに至りソドム、ゴモラ、アデマ、ゼボイムに沿てレシヤにまで及べり
20 Amenewa ndiwo ana aamuna a Hamu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe amakhala ndi mitundu yawo.
是等はハムの子孫にして其宗族と其方言と其土地と其邦國に隨ひて居りぬ
21 Semu amene anali mkulu wake wa Yafeti nayenso anabereka nakhala kholo la Eberi.
セムはヱベルの全の子孫の先祖にしてヤペテの兄なり彼にも子女生れたり
22 Ana aamuna a Semu anali: Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi ndi Aramu.
セムの子はエラム、アシユル、アルパクサデルデ、アラムなり
23 Ana aamuna a Aramu anali: Uzi, Huri, Geteri ndi Mesaki.
アラムの子はウヅ、ホル、ゲテル、マシなり
24 Aripakisadi anabereka Sela, ndipo Selayo anabereka Eberi.
アルパクサデ、シラを生みシラ、エベルを生り
25 A Eberi anabereka ana aamuna awiri: Wina anamutcha Pelegi chifukwa pa nthawiyo anthu a pa dziko lapansi anagawikana. Dzina la mʼbale wake linali Yokitani.
エベルに二人の子生れたり一人の名をペレグ(分れ)といふ其は彼の代に邦國分れたればなり其弟の名をヨクタンと曰ふ
26 Yokitani anabereka Alimodadi, Selefi, Hazari-Maveti, Yera,
ヨクタン、アルモダデ、シヤレフ、ハザルマウテ、ヱラ
27 Hadoramu, Uzali, Dikila,
ハドラム、ウザル、デクラ
28 Obali, Abimaeli, Seba,
オバル、アビマエル、シバ
29 Ofiri, Havila ndi Yobabu. Onsewa anali ana aamuna a Yokitani.
オフル、ハビラおよびヨバブを生り是等は皆ヨクタンの子なり
30 Chigawo chimene ankakhala chinayambira ku Mesa mpaka ku Seferi, ku dera la mapiri chakummawa.
彼等の居住所はメシヤよりして東方の山セバルにまで至れり
31 Amenewa ndiwo ana a Semu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe ankakhala ndi mitundu yawo.
是等はセムの子孫にして其宗族と其方言と其土地と其邦國とに隨ひて居りぬ
32 Amenewa ndiwo mafuko a ana aamuna a Nowa monga mwa mibado ya mitundu yawo. Mitundu yonse ya anthu inatuluka mwa iwowa ndi kufalikira pa dziko lonse lapansi chitatha chigumula chija.
是等はノアの子の宗族にして其血統と其邦國に隨ひて居りぬ洪水の後是等より地の邦國の民は派分れ出たり

< Genesis 10 >