< Agalatiya 3 >
1 Agalatiya opusa inu, anakulodzani ndani? Tinamuonetsa poyera pamaso panu Yesu Khristu monga wopachikidwa pa mtanda.
2 Ine ndikufuna ndiphunzire kuchokera kwa inu chinthu chimodzi ichi: Kodi munalandira Mzimu pochita ntchito za lamulo, kapena pokhulupirira zimene munamva?
3 Kani ndinu opusa chotere? Inu mutayamba ndi Mzimu, kodi mukufuna kutsiriza ndi ntchito zathupi?
4 Kodi munavutika kwambiri pachabe, ngati kunali kwachabedi?
5 Kodi Mulungu amene anakupatsani Mzimu wake ndi kuchita zodabwitsa pakati panu, amachita zimenezi chifukwa mumachita ntchito za lamulo kapena chifukwa mumakhulupirira zimene munamva?
6 Nʼchimodzimodzinso Abrahamu, “Iye anakhulupirira Mulungu, ndipo Mulungu anamutenga kukhala wolungama.”
7 Tsono zindikirani kuti amene akhulupirira, ndi ana a Abrahamu.
8 Malemba anaonetseratu kuti Mulungu adzalungamitsa anthu a mitundu ina mwachikhulupiriro, ndipo ananeneratu Uthenga Wabwino kwa Abrahamu kuti, “Mitundu yonse ya anthu idzadalitsika kudzera mwa iwe.”
9 Choncho iwo amene ali ndi chikhulupiriro ndi odalitsidwa pamodzi ndi Abrahamu, munthu wachikhulupiriro.
10 Onse amene amadalira ntchito za lamulo ndi otembereredwa, pakuti zalembedwa mʼBuku la Malamulo kuti, “Ndi wotembereredwa aliyense amene sachita zonse zimene zalembedwa mʼBuku la Malamulo.”
11 Chodziwikiratu nʼchakuti palibe amene amalungamitsidwa pamaso pa Mulungu ndi lamulo, chifukwa, “Wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.”
12 Koma chikhulupiriro si Malamulo, chifukwa Malemba akuti, “Munthu amene achita zinthu izi adzakhala ndi moyo pozichita.”
13 Khristu anatiwombola ku temberero la lamulo pokhala temberero mʼmalo mwathu, pakuti analemba kuti, “Aliyense wopachikidwa pamtengo ndi wotembereredwa.”
14 Iye anatiwombola ife ndi cholinga chakuti madalitso woperekedwa kwa Abrahamu abwere kwa anthu a mitundu ina kudzera mwa Khristu Yesu, kuti ndi chikhulupiriro tilandire lonjezo la Mzimu.
15 Abale, ndiloleni ndipereke chitsanzo cha zochitika mʼmoyo wa tsiku ndi tsiku. Pangano likakhazikitsidwa palibe amene angachotsepo kapena kuwonjezerapo, choncho ndi chimodzimodzi pa nkhani iyi.
16 Malonjezo awa anaperekedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbewu yake. Malemba sakunena kuti, “kwa mbewu zake,” kutanthauza anthu ambiri, koma, “kwa mbewu yako,” kutanthauza munthu mmodzi, amene ndi Khristu.
17 Chimene ndikutanthauza ine ndi ichi: Malamulo amene anabwera patatha zaka 430, sangathetse pangano limene linakhazikitsidwa kale ndi Mulungu ndi kuliwononga lonjezolo.
18 Ngati madalitso athu akudalira ntchito za lamulo ndiye kuti madalitsowo sakupatsidwa chifukwa cha lonjezo. Koma Mulungu mwachisomo chake anadalitsa Abrahamu kudzera mu lonjezo.
19 Nanga tsono cholinga cha lamulo chinali chiyani? Linaperekedwa chifukwa cha zolakwa mpaka itafika mbewu imene lonjezo limanena. Malamulowo anaperekedwa ndi angelo kudzera mwa mʼkhalapakati.
20 Ngakhale zili chomwecho, mʼkhalapakati sayimira mbali imodzi yokha, koma Mulungu ndi mmodzi.
21 Kodi ndiye kuti lamulo limatsutsana ndi malonjezo a Mulungu? Ayi. Nʼkosatheka! Pakuti ngati tikanapatsidwa malamulo opatsa moyo ndiye kuti mwa lamulo tikanakhala olungama.
22 Koma Malemba akunenetsa kuti dziko lonse lili mu ulamuliro wauchimo, kuti mwachikhulupiriro mwa Yesu Khristu, chimene chinalonjezedwa chiperekedwe kwa amene akhulupirira.
23 Chikhulupiriro ichi chisanabwere, ife tinali mʼndende ya lamulo, otsekeredwa mpaka pamene chikhulupiriro chikanavumbulutsidwa.
24 Choncho lamulo linayikidwa kukhala lotiyangʼanira kuti lititsogolere kwa Khristu kuti tilungamitsidwe mwachikhulupiriro.
25 Tsopano pakuti chikhulupiriro chabwera, ife sitilinso mu ulamuliro wa lamulo.
26 Nonse ndinu ana a Mulungu kudzera mʼchikhulupiriro mwa Khristu Yesu,
27 pakuti nonse amene munalumikizana ndi Khristu mu ubatizo munavala Khristu.
28 Palibe Myuda kapena Mgriki, kapolo kapena mfulu, mwamuna kapena mkazi, pakuti nonse ndinu amodzi mwa Khristu Yesu.
29 Ngati inu muli ake a Khristu, ndiye kuti ndinu mbewu ya Abrahamu, ndi olowamʼmalo molingana ndi lonjezo.