< Agalatiya 1 >

1 Paulo mtumwi, osati wosankhidwa ndi anthu kapena kutumidwa ndi munthu ayi, koma Yesu Khristu, ndi Mulungu Atate amene anamuukitsa Yesuyo kwa akufa,
παυλοσ αποστολοσ ουκ απ ανθρωπων ουδε δι ανθρωπου αλλα δια ιησου χριστου και θεου πατροσ του εγειραντοσ αυτον εκ νεκρων
2 pamodzi ndi abale onse amene ali nane, Kulembera mipingo ya ku Galatiya:
και οι συν εμοι παντεσ αδελφοι ταισ εκκλησιαισ τησ γαλατιασ
3 Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu zikhale nanu.
χαρισ υμιν και ειρηνη απο θεου πατροσ και κυριου ημων ιησου χριστου
4 Yesuyo anadzipereka yekha chifukwa cha machimo athu kuti atipulumutse ku njira za moyo woyipa uno, molingana ndi chifuniro cha Mulungu ndi Atate athu. (aiōn g165)
του δοντοσ εαυτον περι των αμαρτιων ημων οπωσ εξεληται ημασ εκ του ενεστωτοσ αιωνοσ πονηρου κατα το θελημα του θεου και πατροσ ημων (aiōn g165)
5 Ulemerero ukhale kwa Mulunguyo mpaka muyaya. Ameni. (aiōn g165)
ω η δοξα εισ τουσ αιωνασ των αιωνων αμην (aiōn g165)
6 Ine ndikudabwa kuti mukusiya mwamsangamsanga chotere Mulungu amene anakuyitanani mwachisomo cha Khristu ndipo mwatembenuka ndi kutsatira uthenga wina wosiyana,
θαυμαζω οτι ουτωσ ταχεωσ μετατιθεσθε απο του καλεσαντοσ υμασ εν χαριτι χριστου εισ ετερον ευαγγελιον
7 umene si Uthenga Wabwino konse. Pali anthu ena amene akukusokonezani komanso akufuna kupotoza Uthenga Wabwino wa Khristu.
ο ουκ εστιν αλλο ει μη τινεσ εισιν οι ταρασσοντεσ υμασ και θελοντεσ μεταστρεψαι το ευαγγελιον του χριστου
8 Ngakhale ife kapena mngelo wochokera kumwamba, akalalikira Uthenga Wabwino wosiyana ndi umene tinakulalikirani uja, iyeyo akhale wotembereredwa!
αλλα και εαν ημεισ η αγγελοσ εξ ουρανου ευαγγελιζηται υμιν παρ ο ευηγγελισαμεθα υμιν αναθεμα εστω
9 Monga tanena kale, tsopano ndikubwereza kunenanso kuti, “Ngati wina aliyense akulalikirani Uthenga Wabwino wosiyana ndi umene munawulandira, iyeyo akhale wotembereredwa.”
ωσ προειρηκαμεν και αρτι παλιν λεγω ει τισ υμασ ευαγγελιζεται παρ ο παρελαβετε αναθεμα εστω
10 Kodi tsopano ndikufuna kukopa anthu kuti andivomereze, kapena Mulungu? Kapena ndikufuna kukondweretsa anthu? Ngati ine ndikanakhala kuti ndikufunabe kukondweretsa anthu, sindikanakhala mtumiki wa Khristu.
αρτι γαρ ανθρωπουσ πειθω η τον θεον η ζητω ανθρωποισ αρεσκειν ει γαρ ετι ανθρωποισ ηρεσκον χριστου δουλοσ ουκ αν ημην
11 Abale, ine ndikufuna kuti mudziwe, kuti Uthenga Wabwino umene ndinalalikira si ochokera kwa munthu ayi.
γνωριζω δε υμιν αδελφοι το ευαγγελιον το ευαγγελισθεν υπ εμου οτι ουκ εστιν κατα ανθρωπον
12 Ine sindinawulandire kuchokera kwa munthu aliyense, kapena kuphunzitsidwa; koma ndinawulandira mwa vumbulutso lochokera kwa Khristu.
ουδε γαρ εγω παρα ανθρωπου παρελαβον αυτο ουτε εδιδαχθην αλλα δι αποκαλυψεωσ ιησου χριστου
13 Pakuti inu munamva za moyo wanga wakale mʼChiyuda, mmene ndinkazunzira mpingo wa Mulungu koopsa ndi kuyesetsa kuwuwononga.
ηκουσατε γαρ την εμην αναστροφην ποτε εν τω ιουδαισμω οτι καθ υπερβολην εδιωκον την εκκλησιαν του θεου και επορθουν αυτην
14 Ine ndinkapambana Ayuda ambiri a msinkhu wanga pochita za Chiyuda, ndipo ndinali wachangu koposa pa miyambo ya makolo athu.
και προεκοπτον εν τω ιουδαισμω υπερ πολλουσ συνηλικιωτασ εν τω γενει μου περισσοτερωσ ζηλωτησ υπαρχων των πατρικων μου παραδοσεων
15 Koma Mulungu, amene anandipatula ine ndisanabadwe, ndi kundiyitana mwachisomo chake, atakondweretsedwa
οτε δε ευδοκησεν ο θεοσ ο αφορισασ με εκ κοιλιασ μητροσ μου και καλεσασ δια τησ χαριτοσ αυτου
16 kuvumbulutsa Mwana wake mwa ine, kuti ndikalalikire Khristuyo pakati pa anthu a mitundu ina, ine sindinapemphe nzeru kwa munthu aliyense.
αποκαλυψαι τον υιον αυτου εν εμοι ινα ευαγγελιζωμαι αυτον εν τοισ εθνεσιν ευθεωσ ου προσανεθεμην σαρκι και αιματι
17 Ine sindinapite ku Yerusalemu kukaonana ndi amene anali atumwi ine ndisanakhale mtumwi. Mʼmalo mwake nthawi yomweyo ndinapita ku Arabiya ndi kubwereranso ku Damasiko.
ουδε ανηλθον εισ ιεροσολυμα προσ τουσ προ εμου αποστολουσ αλλα απηλθον εισ αραβιαν και παλιν υπεστρεψα εισ δαμασκον
18 Pambuyo pake, patatha zaka zitatu, ndinapita ku Yerusalemu kukaonana ndi Petro ndikukhala naye masiku khumi ndi asanu.
επειτα μετα ετη τρια ανηλθον εισ ιεροσολυμα ιστορησαι πετρον και επεμεινα προσ αυτον ημερασ δεκαπεντε
19 Ine sindinaonane ndi atumwi enawo koma Yakobo yekha, mʼbale wa Ambuye.
ετερον δε των αποστολων ουκ ειδον ει μη ιακωβον τον αδελφον του κυριου
20 Ine ndikutsimikizira inu pamaso pa Mulungu kuti zimene ndikukulemberani si zonama ayi.
α δε γραφω υμιν ιδου ενωπιον του θεου οτι ου ψευδομαι
21 Pambuyo pake ndinapita ku Siriya ndi ku Kilikiya.
επειτα ηλθον εισ τα κλιματα τησ συριασ και τησ κιλικιασ
22 Koma sindimadziwika ndi nkhope ku mipingo ya ku Yudeya imene ili mwa Khristu.
ημην δε αγνοουμενοσ τω προσωπω ταισ εκκλησιαισ τησ ιουδαιασ ταισ εν χριστω
23 Iwo anangomva mbiri yokha yakuti, “Munthu amene poyamba anatizunza ife, tsopano akulalikira chikhulupiriro chimene iyeyo nthawi ina anafuna kuchiwononga.”
μονον δε ακουοντεσ ησαν οτι ο διωκων ημασ ποτε νυν ευαγγελιζεται την πιστιν ην ποτε επορθει
24 Ndipo iwo anayamika Mulungu chifukwa cha ine.
και εδοξαζον εν εμοι τον θεον

< Agalatiya 1 >