< Ezara 8 >
1 Nawa mayina a atsogoleri a mabanja amene anabwera nane kuchokera ku Babuloni nthawi ya ulamuliro wa mfumu Aritasasita:
2 Geresomu wa fuko la Finehasi; Danieli wa fuko la Itamara; Hatusi
3 mwana wa Sekaniya wa fuko la Davide; Zekariya wa fuko la Parosi. Pamodzi ndi iyeyu panalembedwa anthu ena 150;
4 Elihunai mwana wa Zerahiya, wa fuko la Pahati-Mowabu. Pamodzi ndi iyeyu panalinso anthu ena 400.
5 Sekaniya, mwana wa Yahazieli wa fuko la Zatu. Pamodzi ndi iyeyu panalembedwanso anthu 300.
6 Ebedi, mwana wa Yonatani wa fuko la Adini. Pamodzi naye analembedwanso anthu ena makumi asanu.
7 Yesaiya, mwana wa Ataliya wa fuko la Elamu. Pamodzi naye panali anthu ena 70.
8 Zebadiya, mwana wa Mikayeli wa fuko la Sefatiya. Pamodzi naye panalinso anthu 80.
9 Obadiya, mwana wa Yehieli wa fuko la Yowabu. Pamodzi naye panalinso anthu 218.
10 Selomiti mwana wa Yosifiya wa fuko la Bani. Pamodzi ndi iyeyu panalinso anthu 160.
11 Zekariya, mwana wa Bebai wa fuko la Babai. Pamodzi naye analembedwanso anthu 28.
12 Yohanani, mwana wa Hakatani wa fuko la Azigadi. Pamodzi naye panalinso anthu 110.
13 Atsogoleri a fuko la Adonikamu, anthu amene anabwera pambuyo pake mayina awo anali Elifeleti, Yeiyeli ndi Semaya. Pamodzi ndi iwowa panalinso anthu 60.
14 Atsogoleri a fuko la Bigivai anali Utai ndi Zakuri. Pamodzi ndi iwowa panali anthu 70.
15 Anthu onse ndinawasonkhanitsa ku mtsinje umene umapita mpaka ku Ahava, ndipo kumeneko tinagona mʼmisasa masiku atatu. Nditayangʼana pakati pa anthu ndi ansembe, ndinapeza kuti panalibe Alevi.
16 Choncho ndinayitana atsogoleri awa: Eliezara, Arieli, Semaiya, Elinatani, Yaribu, Elinatani, Natani, Zekariya ndi Mesulamu, pamodzi ndi aphunzitsi awiri, Yoyaribu ndi Elinatani,
17 ndipo ndinawatuma kwa Ido, mtsogoleri wa malo otchedwa Kasifiya. Ine ndinawawuza zoti akanene kwa Ido ndi kwa abale ake, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu ku Kasifiyako, kuti atitumizire anthu odzatumikira ku Nyumba ya Mulungu.
18 Chifukwa cha kutikomera mtima kwa Mulungu wathu, Ido anatitumizira munthu wanzeru, Serabiya, wa fuko la Mahili, mwana wa Levi, mwana wa Israeli, pamodzi ndi ana ake aamuna ndi abale ake, anthu 18.
19 Anatitumiziranso Hasabiya ndi Yesaiya wa fuko la Merari pamodzi ndi abale ake ndi adzukulu ake, anthu makumi awiri.
20 Panalinso anthu ena 220 mwa anthu ogwira ntchito mʼNyumba ya Mulungu amene Davide ndi nduna zake anawasankha kuti azitumikira Alevi. Anthu onsewa analembedwa potsata mayina awo.
21 Ku mtsinje wa Ahava, ndinalengeza kuti anthu onse asale zakudya, adzichepetse pamaso pa Mulungu wathu ndi kupempha kuti atiyendetse bwino ife ndi ana athu, ndi kuteteza katundu wathu yense.
22 Ine ndinali ndi manyazi kupempha mfumu kuti atipatse asilikali oyenda pansi ndi ena okwera pa akavalo kuti atiteteze kwa adani athu pa ulendo wathuwu popeza tinali titawuza kale mfumu kuti “Yehova amateteza aliyense amene amamudalira, koma amakwiyira onse amene amamukana.”
23 Choncho tinasala zakudya ndi kupemphera kwa Mulungu wathu kuti atiteteze ndipo Iye anamva pemphero lathu.
24 Tsono ndinasankha atsogoleri a ansembe khumi ndi awiri awa, Serebiya, Hasabiya ndi abale awo khumi
25 ndipo ndinawayezera siliva ndi golide, ndiponso ziwiya ndi zopereka za ku Nyumba ya Mulungu wathu zimene mfumu ndi alangizi ake, nduna zake ndi Aisraeli onse amene anali kumeneko anazipereka.
26 Nditayeza zonse, ndinapereka mʼmanja mwawo, matani 22 asiliva, ziwiya zasiliva zolemera makilogalamu 70, ndiponso makilogalamu 3,400 a golide,
27 mbale zagolide makumi awiri zolemera makilogalamu asanu ndi atatu ndi theka ndiponso ziwiya ziwiri zamkuwa wosalala, wonyezimira bwino ngati golide wamtengowapatali.
28 Kenaka ndinawawuza kuti, “Inu ndi opatulika a Yehova, ndiponso mphatso zonsezi ndi zopatulika. Siliva ndi golideyu ndi zopereka zaufulu kwa Yehova, Mulungu wa makolo anu.
29 Muzisamale bwino mpaka mutaziyeza pamaso pa atsogoleri a ansembe ndi Alevi ndi akulu a mabanja a Israeli mʼzipinda za mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu.”
30 Choncho ansembe ndi Alevi analandira zonse zoyezedwa zija, siliva, golide pamodzi ndi ziwiya kuti apite nazo ku Nyumba ya Yehova ku Yerusalemu.
31 Pa tsiku la khumi ndi chiwiri la mwezi woyamba, tinachoka ku mtsinje wa Ahava kupita ku Yerusalemu. Ndipo Mulungu wathu anali nafe, ndipo anatiteteza kwa adani athu makamaka otibisalira pa njira.
32 Tinafika ku Yerusalemu, komwe tinapumula masiku atatu.
33 Pa tsiku la chinayi lake, mʼNyumba ya Mulungu wathu, tinayeza siliva ndi golide ndi ziwiya zija nʼkuzipereka mʼmanja mwa Meremoti mwana wa wansembe Uriya. Pamodzi ndi iyeyo panali Eliezara mwana wa Finehasi ndiponso Alevi awa: Yozabadi mwana wa Yesuwa ndi Nowadiya mwana wa Binuyi.
34 Zonsezi anaziwerenga ndi kuziyeza ndipo analemba kulemera kwa chinthu chilichonse.
35 Pamenepo anthu amene anatengedwa ukapolo aja anabwerera, anapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu wa Israeli: ngʼombe zazimuna khumi ndi ziwiri, kuperekera Aisraeli onse, nkhosa zazimuna 96, ana ankhosa 77, ndiponso mbuzi zazimuna khumi ndi ziwiri ngati nsembe yopepesera machimo. Zonsezi zinali nsembe yopsereza zopereka kwa Yehova.
36 Iwo anaperekanso chidziwitso cha mfumu chija kwa akuluakulu a mfumu ndi kwa akazembe a mʼdera la Patsidya pa Yufurate. Pamenepo iwo anathandiza Ayuda ndiponso ntchito za pa Nyumba ya Mulungu.