< Ezara 7 >
1 Zitatha izi, Aritasasita ali mfumu ya ku Perisiya, panali wansembe wina dzina lake Ezara. Iyeyu abambo ake anali Seraya mwana wa Azariya, mwana wa Hilikiya,
이 일 후 바사 왕 아닥사스다가 위에 있을 때에 에스라라 하는 자가 있으니라 저는 스라야의 아들이요 아사랴의 손자요 힐기야의 증손이요
2 mwana wa Salumu, mwana wa Zadoki, mwana wa Ahitubi,
살룸의 현손이요 사독의 오대손이요 아히둡의 육대손이요
3 mwana wa Amariya, mwana wa Azariya, mwana wa Merayoti,
아마랴의 칠대손이요 아사랴의 팔대손이요 므라욧의 구대손이요
4 mwana wa Zerahiya, mwana wa Uzi, mwana wa Buki,
스라히야의 십대손이요 웃시엘의 십일대손이요 북기의 십이대손이요
5 mwana wa Abisuwa, mwana wa Finehasi, mwana wa Eliezara, mwana wa Aaroni mkulu wa ansembe uja.
아비수아의 십삼대손이요 비느하스의 십사대손이요 엘르아살의 십오대손이요 대제사장 아론의 십륙대손이라
6 Ezara ameneyu anabwera kuchokera ku Babuloni. Iyeyu anali wophunzira kwambiri za malamulo a Mose, amene Yehova Mulungu wa Israeli anapereka. Mfumu inamupatsa chilichonse chimene anapempha pakuti dzanja la Yehova Mulungu wake linali pa iye.
이 에스라가 바벨론에서 올라왔으니 저는 이스라엘 하나님 여호와께서 주신 바 모세의 율법에 익숙한 학사로서 그 하나님 여호와의 도우심을 입으므로 왕에게 구하는 것은 다 받는 자더니
7 Tsono mʼchaka cha chisanu ndi chiwiri cha ufumu wa Aritasasita, Ezara pamodzi ndi Aisraeli ena, kuphatikizapo ansembe, Alevi, oyimba nyimbo, alonda, ndi anthu ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu ananyamuka kubwerera ku Yerusalemu.
아닥사스다 왕 칠년에 이스라엘 자손과 제사장들과 레위 사람들과 노래하는 자들과 문지기들과 느디님 사람들 중에 몇 사람이 예루살렘으로 올라올 때에
8 Ezara anafika ku Yerusalemu pa mwezi wachisanu wa chaka chachisanu ndi chiwiri cha mfumu.
이 에스라가 올라왔으니 왕의 칠년 오월이라
9 Iye anayamba ulendo wochoka ku Babuloni pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, ndipo anafika ku Yerusalemu pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu chifukwa dzanja labwino la Mulungu wake linali pa iye.
정월 초하루에 바벨론에서 길을 떠났고 하나님의 선한 손의 도우심을 입어 오월 초하루에 예루살렘에 이르니라
10 Popeza Ezara anadzipereka kuwerenga ndi kusunga malamulo a Yehova, iye anafunitsitsa kuphunzitsa Aisraeli malamulo ndi malangizo a Mulungu.
에스라가 여호와의 율법을 연구하여 준행하며 율례와 규례를 이스라엘에게 가르치기로 결심하였었더라
11 Iyi ndi kalata imene mfumu Aritasasita anapereka kwa wansembe Ezara, mlembi wa malamulo, munthu wophunzira kwambiri zokhudza malamulo ndi malangizo amene Yehova anapereka kwa Aisraeli.
여호와의 계명의 말씀과 이스라엘에게 주신 율례의 학사인 학사겸 제사장 에스라에게 아닥사스다 왕이 내린 조서 초본은 아래와 같으니라
12 Ndine Aritasasita, mfumu ya mafumu. Ndikulembera iwe Ezara wansembe ndi mlembi wa malamulo a Mulungu Wakumwamba. Malonje.
모든 왕의 왕 아닥사스다는 하늘의 하나님의 율법에 완전한 학사 겸 제사장 에스라에게
13 Tsopano ndikulamula kuti Mwisraeli aliyense, wansembe kapena Mlevi wokhala mʼdziko langa, amene akufuna kupita ku Yerusalemu ndi iwe, apite.
조서하노니 우리 나라에 있는 이스라엘 백성과 저희 제사장들과 레위 사람들 중에 예루살렘으로 올라갈 뜻이 있는 자는 누구든지 너와 함께 갈지어다
14 Ine mfumu pamodzi ndi alangizi anga asanu ndi awiri tikukutumani kuti mukafufuze za dziko la Yuda ndi mzinda wa Yerusalemu kuti mukaone mmene anthu akutsatira malamulo a Mulungu wanu, amene anawapereka kwa inu.
너는 네 손에 있는 네 하나님의 율법을 좇아 유다와 예루살렘의 정형을 살피기 위하여 왕과 일곱 모사의 보냄을 받았으니
15 Utenge siliva ndi golide zimene ine mfumu ndi alangizi anga tapereka mwa ufulu kwa Mulungu wa Israeli, amene amakhala ku Yerusalemu.
왕과 모사들이 예루살렘에 거하신 이스라엘 하나님께 성심으로 드리는 은금을 가져가고
16 Mutengenso siliva yense ndi golide amene mungamupeze mʼdziko lonse la Babuloni, ngakhalenso zinthu zimene anthu pamodzi ndi ansembe adzapereka mwaufulu kuperekera ku Nyumba ya Mulungu wawo ya ku Yerusalemu.
또 네가 바벨론 온 도에서 얻을 모든 은금과 및 백성과 제사장들이 예루살렘 그 하나님의 전을 위하여 즐거이 드릴 예물을 가져다가
17 Ndi ndalama zimenezi mudzaonetsetse kuti mwagula ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa aamuna pamodzi ndi zopereka zake za chakudya ndi za chakumwa. Mudzapereke zimenezi pa guwa lansembe la Nyumba ya Mulungu wanu ya ku Yerusalemu.
그 돈으로 수송아지와 수양과 어린 양과 그 소제와 그 전제의 물품을 신속히 사서 예루살렘 네 하나님의 전 단 위에 드리고
18 Ndalama zotsala mudzagwiritse ntchito zimene inuyo ndi abale anu zikakukomerani malingana nʼkufuna kwa Mulungu wanu.
그 나머지 은금은 너와 너의 형제가 선히 여기는 일에 너희 하나님의 뜻을 좇아 쓸지며
19 Ziwiya zonse zimene akupatsani kuti mukatumikire nazo mʼNyumba ya Mulungu wanu, kaziperekeni kwa Mulungu ku Yerusalemu.
네 하나님의 전에서 섬기는 일을 위하여 네게 준 기명은 예루살렘 하나님 앞에 드리고
20 Ndipo chilichonse chimene chingafunike mʼNyumba ya Mulungu wanu, chimene mudzapeze mpata wopereka, ndalama zake zogulira zidzachokere mʼthumba la chuma cha mfumu.
그 외에도 네 하나님의 전에 쓰일 것이 있어서 네가 드리고자 하거든 무엇이든지 왕의 내탕고에서 취하여 드릴지니라
21 Tsopano Ine, mfumu Aritasasita, ndikulamula asungichuma onse a dera la Patsidya pa Yufurate kuti, chilichonse chimene wansembe Ezara, mlembi wa malamulo a Mulungu Wakumwamba adzapempha kwa inu, mupatseni mwa msanga.
나 곧 나 아닥사스다 왕이 강 서편 모든 고지기에게 조서를 내려 이르기를 하늘의 하나님의 율법의 학사 겸 제사장 에스라가 무릇 너희에게 구하는 것은 신속히 시행하되
22 Ngakhale atafunika makilogalamu 3,400 asiliva, makilogalamu 10,000 a tirigu, malita 2,000 a vinyo, malita 2,000 a mafuta ndi mchere wochuluka motani, zonsezi mupereke monga zingafunikire.
은은 일백 달란트까지, 밀은 일백 고르까지, 포도주는 일백 밧까지, 기름도 일백 밧까지 하고 소금은 정수없이 하라
23 Chimene Mulungu Wakumwamba walamula, chichitike mosamalitsa ku Nyumba ya Mulungu Wakumwamba kuopa kuti mkwiyo wa Mulungu ungayakire mfumu, dziko lake ndi ana ake.
무릇 하늘의 하나님의 전을 위하여 하늘의 하나님의 명하신 것은 삼가 행하라 어찌하여 진노가 왕과 왕자의 나라에 임하게 하랴
24 Tikukudziwitsaninso kuti kudzakhala kosaloledwa kukhometsa msonkho uliwonse anthu awa: ansembe, Alevi, oyimba nyimbo, alonda kapena aliyense wogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu.
내가 너희에게 이르노니 제사장들이나 레위 사람들이나 노래하는 자들이나 문지기들이나 느디님 사람들이나 혹 하나님의 전에서 일하는 자들에게 조공과 잡세와 부세를 받는 것이 불가하니라 하였노라
25 Ndipo iwe, Ezara, monga mwa nzeru za Mulungu wako zimene uli nazo, usankhe oyendetsa zinthu ndi oweruza kuti azilamulira anthu onse okhala ku dera la Patsidya pa Yufurate, onse amene amadziwa malamulo a Mulungu wako. Ndipo uphunzitse aliyense amene sawadziwa.
에스라여 너는 네 손에 있는 네 하나님의 지혜를 따라 네 하나님의 율법을 아는 자로 유사와 재판관을 삼아 강 서편 모든 백성을 재판하게 하고 그 알지 못하는 자는 너희가 가르치라
26 Ndipo amene sadzamvera lamulo la Mulungu wako ndi lamulo la mfumu alangidwe kolimba kapena aphedwe kapena achotsedwe mʼdzikolo, kapena katundu wake alandidwe, kapena aponyedwe mʼndende.
무릇 네 하나님의 명령과 왕의 명령을 준행치 아니하는 자는 속히 그 죄를 정하여 혹 죽이거나 정배하거나 가산을 적몰하거나 옥에 가둘지니라 하였더라
27 Ezara anati atamandike Yehova, Mulungu wa makolo athu, amene wayika ichi mu mtima wa mfumu kuti alemekeze Nyumba ya Yehova ya ku Yerusalemu mʼnjira imeneyi.
우리 열조의 하나님 여호와를 송축할지로다 그가 왕의 마음에 예루살렘 여호와의 전을 아름답게 할 뜻을 두시고
28 Ameneyonso waonetsa chikondi chake chosasinthika kwa ine pamaso pa mfumu, alangizi ake ndi nduna zake zamphamvu kuti andikomere mtima. Choncho ndinalimba mtima popeza Yehova, Mulungu wanga anali nane, ndipo ndinasonkhanitsa atsogoleri ambiri a Israeli kuti apite nane pamodzi.
또 나로 왕과 그 모사들의 앞과 왕의 권세 있는 모든 방백의 앞에서 은혜를 얻게 하셨도다 나의 하나님 여호와의 손이 나의 위에 있으므로 내가 힘을 얻어 이스라엘 중에 두목을 모아 나와 함께 올라오게 하였노라