< Ezara 6 >

1 Atalandira mawuwo mfumu Dariyo anapereka lamulo ndipo kafukufuku anachitikadi ku Babuloni mʼnyumba yosungira chuma ndi mabuku ambiri yakale.
באדין דריוש מלכא שם טעם ובקרו בבית ספריא די גנזיא מהחתין תמה--בבבל
2 Ndipo ku Ekibatana, likulu la dera la Mediya, kunapezeka mpukutu mmene munalembedwa kuti, Chikumbutso:
והשתכח באחמתא בבירתא די במדי מדינתא--מגלה חדה וכן כתיב בגוה דכרונה
3 Mʼchaka choyamba cha ufumu wa Koresi, mfumuyo inapereka lamulo lokhudza Nyumba ya Mulungu mu Yerusalemu. Analamula kuti Nyumba ya Mulungu imangidwenso kukhala malo woperekerako nsembe. Maziko ake amangidwe kolimba pa malo pomwe paja pali maziko ake akale ndipo mulitali mwake mukhale mamita 27, mulifupi mwake mukhale mamita 27.
בשנת חדה לכורש מלכא כורש מלכא שם טעם--בית אלהא בירושלם ביתא יתבנא אתר די דבחין דבחין ואשוהי מסובלין רומה אמין שתין פתיה אמין שתין
4 Mumange mizere itatu ya miyala yayikulu ndi mzere umodzi wa matabwa, ndalama zake zolipirira ntchitoyo zichokere mʼthumba la ufumu.
נדבכין די אבן גלל תלתא ונדבך די אע חדת ונפקתא--מן בית מלכא תתיהב
5 Ndipo ziwiya zagolide ndi zasiliva za ku Nyumba ya Mulungu zimene Nebukadinezara anatenga mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu kupita nazo ku Babuloni, zonsezi zibwezedwe ndipo zipite ku Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Chilichonse chikabwezedwe pamalo pake mʼNyumbayo.
ואף מאני בית אלהא די דהבה וכספא די נבוכדנצר הנפק מן היכלא די בירושלם והיבל לבבל--יהתיבון ויהך להיכלא די בירושלם לאתרה ותחת בבית אלהא
6 Tsopano Tatenai, bwanamkubwa wa dera la Patsidya pa Yufurate ndiponso Setari-Bozenai pamodzi ndi anzanu muchokeko kumeneko.
כען תתני פחת עבר נהרה שתר בוזני וכנותהון אפרסכיא די בעבר נהרה--רחיקין הוו מן תמה
7 Ntchito yomanga Nyumba ya Mulunguyi muyileke. Mulekeni bwanamkubwa wa Ayuda ndiponso akuluakulu a Ayuda kuti amangenso Nyumba ya Mulunguyo pamalo pake.
שבקו לעבידת בית אלהא דך פחת יהודיא ולשבי יהודיא בית אלהא דך יבנון על אתרה
8 Kuwonjezera pamenepo, ndikukhazikitsa lamulo lonena za mmene mudzachitire ndi akuluakulu a Ayuda powathandiza kumanganso Nyumba ya Mulunguyo: Anthuwa muwalipire msanga kuchokera mʼthumba la ufumu, kuchotsa pa msonkho wa dera la Patsidya pa Yufurate.
ומני שים טעם--למא די תעבדון עם שבי יהודיא אלך למבנא בית אלהא דך ומנכסי מלכא די מדת עבר נהרה אספרנא נפקתא תהוא מתיהבא לגבריא אלך די לא לבטלא
9 Ndipo zonse zofunikira monga, ana angʼombe, nkhosa zazimuna, ana ankhosa aamuna zoperekera nsembe yopsereza kwa Mulungu wakumwamba, ndi tirigu, mchere, vinyo ndi mafuta monga mmene ansembe a ku Yerusalemu angafunire, muziwapatsa zimenezo tsiku ndi tsiku ndipo musamalephere kutero.
ומה חשחן ובני תורין ודכרין ואמרין לעלון לאלה שמיא חנטין מלח חמר ומשח כמאמר כהניא די בירושלם להוא מתיהב להם יום ביום--די לא שלו
10 Zikatero ndiye kuti azipereka nsembe za fungo lokomera Mulungu wakumwamba ndi kupempherera moyo wa mfumu ndi ana ake.
די להון מהקרבין ניחוחין לאלה שמיא ומצלין לחיי מלכא ובנוהי
11 Ndikulamulanso kuti ngati wina asintha zimene ndalamulazi, mtanda umodzi wa nyumba yake udzasololedwa ndi kumunkhomera pamenepo ndipo nyumba yake adzayisandutse dzala.
ומני שים טעם--די כל אנש די יהשנא פתגמא דנה יתנסח אע מן ביתה וזקיף יתמחא עלהי וביתה נולו יתעבד על דנה
12 Mulungu amene anasankha kuti anthu azimupembedza pa malo amenewa, achotse mfumu iliyonse kapena munthu aliyense amene adzasinthe zimenezi kapena kuwononga Nyumba ya Mulungu ya ku Yerusalemuko. Ine Dariyo ndikuyika lamuloli, aliyense alitsate mosamala kwambiri.
ואלהא די שכן שמה תמה ימגר כל מלך ועם די ישלח ידה להשניה לחבלה בית אלהא דך--די בירושלם אנה דריוש שמת טעם אספרנא יתעבד
13 Tsono potsata zomwe analamula mfumu Dariyo, Tatenai bwanamkubwa wa dera la Patsidya pa Yufurate, Setari-Bozenai ndi anzawo anatsatira mosamala kwambiri zimene mfumu Dariyo analamula.
אדין תתני פחת עבר נהרה שתר בוזני--וכנותהון לקבל די שלח דריוש מלכא כנמא--אספרנא עבדו
14 Ndipo akuluakulu a Ayuda anapitiriza ntchito yomanga ija molimbikitsidwa ndi aneneri Hagai ndi Zekariya mwana wa Ido. Anamaliza ntchito yomanga Nyumbayo, monga momwe Mulungu wa Israeli analamulira ndiponso potsata lamulo la Koresi, Dariyo ndi Aritasasita, mafumu a ku Perisiya.
ושבי יהודיא בנין ומצלחין בנבואת חגי נביאה וזכריה בר עדוא ובנו ושכללו מן טעם אלה ישראל ומטעם כורש ודריוש וארתחששתא מלך פרס
15 Anatsiriza kumanga Nyumbayo pa tsiku lachitatu la mwezi wa Adara mʼchaka chachisanu ndi chimodzi cha ulamuliro wa mfumu Dariyo.
ושיציא ביתה דנה עד יום תלתה לירח אדר--די היא שנת שת למלכות דריוש מלכא
16 Choncho Aisraeli, ansembe, Alevi ndi anthu ena onse amene anali atabwerako ku ukapolo, anachita chikondwerero chopereka Nyumba ya Mulungu mwachimwemwe.
ועבדו בני ישראל כהניא ולויא ושאר בני גלותא חנכת בית אלהא דנה--בחדוה
17 Poporeka Nyumba ya Mulunguyi, anthu anapereka nsembe za ngʼombe zazimuna 100, nkhosa zazimuna 200, ana ankhosa aamuna 400. Anaperekanso mbuzi zazimuna 12 ngati nsembe yopepesera machimo a anthu onse, potsata chiwerengero cha mafuko a Israeli.
והקרבו לחנכת בית אלהא דנה תורין מאה דכרין מאתין אמרין ארבע מאה וצפירי עזין לחטיא (לחטאה) על כל ישראל תרי עשר--למנין שבטי ישראל
18 Ndipo anakhazikitsa ansembe ndi Alevi pa ntchito zawo zotumikira Mulungu mu Yerusalemu monga zinalembedwera mʼbuku la Mose.
והקימו כהניא בפלגתהון ולויא במחלקתהון על עבידת אלהא די בירושלם ככתב ספר משה
19 Pa tsiku la khumi ndi chinayi la mwezi woyamba, obwera ku ukapolo aja anachita chikondwerero cha Paska.
ויעשו בני הגולה את הפסח--בארבעה עשר לחדש הראשון
20 Ansembe ndi Alevi anali atadziyeretsa ndipo onsewo anali oyeretsedwa. Alevi anapha mwana wankhosa wa Paska kuphera onse amene anatuluka ku ukapolo, ansembe anzawo ndi iwo eni.
כי הטהרו הכהנים והלוים כאחד--כלם טהורים וישחטו הפסח לכל בני הגולה ולאחיהם הכהנים ולהם
21 Nkhosa ya Paskayo anayidya ndi Aisraeli onse amene anatuluka ku ukapolo, wina aliyense amene anaphatikana nawo atadziyeretsa ku zonyansa za mitundu ina ya anthu akunja a mʼdzikomo kuti apembedze Yehova Mulungu wa Israeli.
ויאכלו בני ישראל השבים מהגולה וכל הנבדל מטמאת גוי הארץ אלהם--לדרש ליהוה אלהי ישראל
22 Choncho pa masiku asanu ndi awiri anasangalala pa chikondwerero cha buledi wopanda yisiti, chifukwa Yehova anawadzaza ndi chimwemwe. Iye anatembenuza mtima wa mfumu ya ku Asiriya motero kuti iyo inakomera mtima Aisraeli ndi kuwathandiza ntchito yomanga Nyumba ya Mulungu, Mulungu wa Israeli.
ויעשו חג מצות שבעת ימים בשמחה כי שמחם יהוה והסב לב מלך אשור עליהם--לחזק ידיהם במלאכת בית האלהים אלהי ישראל

< Ezara 6 >