< Ezara 4 >
1 Adani a Yuda ndi Benjamini anamva kuti anthu obwera ku ukapolo aja akumangira Nyumba Yehova, Mulungu wa Israeli.
audierunt autem hostes Iudae et Beniamin quia filii captivitatis aedificarent templum Domino Deo Israhel
2 Tsono anapita kwa Zerubabeli ndi kwa atsogoleri a mabanja awo ndi kunena kuti, “Mutilole kuti tikuthandizeni kumangaku chifukwa ife timapembedza Mulungu wanu monga momwe mumachitira inu, ndipo takhala tikupereka nsembe kwa Iye kuyambira nthawi ya Esrahadoni, mfumu ya ku Asiriya, amene anabwera nafe kuno.”
et accedentes ad Zorobabel et ad principes patrum dixerunt eis aedificemus vobiscum quia ita ut vos quaerimus Deum vestrum ecce nos immolamus victimas ex diebus Asoraddan regis Assur qui adduxit nos huc
3 Koma Zerubabeli, Yesuwa ndi atsogoleri ena otsala a mabanja a Aisraeli anayankha kuti, “Inu simungatithandize kumangira Nyumba Yehova, Mulungu wathu. Tokha tidzamumangira Nyumba Yehova, Mulungu wa Aisraeli, monga mfumu Koresi, mfumu ya Perisiya inatilamulira.”
et dixit eis Zorobabel et Iosue et reliqui principes patrum Israhel non est vobis et nobis ut aedificemus domum Deo nostro sed nos ipsi soli aedificabimus Domino Deo nostro sicut praecepit nobis rex Cyrus rex Persarum
4 Tsono anthu a mʼdzikomo anayamba kuchititsa ulesi anthu a ku Yuda, ndi kuwachititsa mantha kuti aleke ntchito yomangayo.
factum est igitur ut populus terrae inpediret manus populi Iudae et turbaret eos in aedificando
5 Analemba alangizi ena kuti alepheretse cholinga chawo pa ntchitoyo pa nthawi yonse ya Koresi, mfumu ya ku Perisiya, ndiponso mpaka pamene Dariyo mfumu ya ku Perisiya ankalamulira dzikolo.
conduxerunt quoque adversum eos consiliatores ut destruerent consilium eorum omnibus diebus Cyri regis Persarum et usque ad regnum Darii regis Persarum
6 Mfumu Ahasiwero atangoyamba kulamulira dzikolo, adani aja analemba kalata yoneneza anthu a Yuda ndi Yerusalemu.
in regno autem Asueri principio regni eius scripserunt accusationem adversum habitatores Iudae et Hierusalem
7 Ndiponso mʼnthawi ya Aritasasita mfumu ya Perisiya, Bisilamu, Mitiredati, Tabeeli ndi anzawo ena analemba kalata inanso kwa Aritasasita. Kalatayo inalembedwa mʼChiaramu ndipo ankatanthauzira poyiwerenga.
et in diebus Artarxersis scripsit Beselam Mitridatis et Tabel et reliqui qui erant in consilio eorum ad Artarxersen regem Persarum epistula autem accusationis scripta erat syriace et legebatur sermone syro
8 Rehumu mkulu wankhondo ndi Simisai mlembi, nawonso analemba kalata yawo yoneneza anthu a ku Yerusalemu kwa mfumu Aritasasita. Anayilemba motere:
Reum Beelteem et Samsai scriba scripserunt epistulam unam de Hierusalem Artarxersi regi huiuscemodi
9 Kalata yochokera kwa Rehumu, mkulu wa gulu lankhondo, mlembi Simisai ndi anzawo awa: oweruza, nduna, akuluakulu ena, anthu a ku Peresiya, Ereki, Babuloni, Susa mʼdziko la Elamu,
Reum Beelteem et Samsai scriba et reliqui consiliatores eorum Dinei et Apharsathei Terphalei Apharsei Erchuei Babylonii Susannechei Deaei Aelamitae
10 ndi mitundu ina imene mkulu wolemekezeka, Osanipara anayisamutsa ndi kuyikhazika mʼmizinda ya Samariya ndi mʼmadera ena apatsidya la Yufurate.
et ceteri de gentibus quas transtulit Asennaphar magnus et gloriosus et habitare eas fecit in civitatibus Samariae et in reliquis regionibus trans Flumen in pace
11 Mawu a mʼkalata ya kwa Aritasasita anali awa: Kwa mfumu Aritasasita: Kuchokera kwa atumiki anu, anthu a kutsidya kwa Yufurate:
hoc est exemplar epistulae quam miserunt ad eum Artarxersi regi servi tui viri qui sunt trans Fluvium salutem dicunt
12 Amfumu tati mudziwe kuti Ayuda amene anabwera kuno kuchokera kwanuko apita ku Yerusalemu ndipo akumanganso mzinda wa anthu owukira ndi oyipa uja. Akumaliza makoma ake ndipo akukonzanso maziko.
notum sit regi quia Iudaei qui ascenderunt a te ad nos venerunt in Hierusalem civitatem rebellem et pessimam quam aedificant extruentes muros eius et parietes conponentes
13 Kuwonjeza apo amfumu mudziwe kuti ngati amalize kumanganso mzindawu ndi kukonzanso makoma ake, adzaleka kukhoma msonkho, kulipira ndalama zakatundu olowa mʼdziko kapena msonkho wina uliwonse, ndipo chuma cha thumba la ufumu chidzachepa.
nunc igitur notum sit regi quia si civitas illa aedificata fuerit et muri eius instaurati tributum et vectigal et annuos reditus non dabunt et usque ad reges haec noxa perveniet
14 Popeza tsono ife timadya nawo kwa mfumu sitiyenera tizingoonerera zinthu zochititsa mfumu manyazi. Nʼchifukwa chake tikutumiza uthenga kwa inu a mfumu kuti mudziwe zonse.
nos ergo memores salis quod in palatio comedimus et quia laesiones regis videre nefas ducimus idcirco misimus et nuntiavimus regi
15 Choncho pachitike kafukufuku mʼbuku la mbiri yakale ya makolo anu. Mʼbuku la mbiri zakale mudzapezamo ndi kuwerenga kuti mzinda umenewu ndi waupandu, wosautsa mafumu ndi nduna zamʼmadera zomwe. Kuyambira kale wakhala ukuwukira ulamuliro uliwonse. Nʼchifukwa chake mzinda umenewu anawuwononga.
ut recenseas in libris historiarum patrum tuorum et invenies scriptum in commentariis et scies quoniam urbs illa urbs rebellis est et nocens regibus et provinciis et bella concitant in ea ex diebus antiquis quam ob rem et civitas ipsa destructa est
16 Tsono tikukudziwitsani amfumu kuti ngati mzinda umenewu umangidwanso ndi makoma ake nʼkutsirizidwanso ndiye kuti inu simudzalamuliranso chigawo cha patsidya pa Yufurate.
nuntiamus nos regi quoniam si civitas illa aedificata fuerit et muri ipsius instaurati possessionem trans Fluvium non habebis
17 Mfumu inatumiza yankho ili: Mkulu wa gulu lankhondo Rehumu, mlembi Simisai ndi anzanu onse amene akukhala ku Samariya ndi mʼzigawo zina zonse za Patsidya pa Yufurate. Landirani moni.
verbum misit rex ad Reum Beelteem et Samsai scribam et ad reliquos qui erant in consilio eorum habitatores Samariae et ceteris trans Fluvium salutem dicens et pacem
18 Kalata imene munatumiza ija yawerengedwa bwino lomwe pamaso panga.
accusationem quam misistis ad nos manifeste lecta est coram me
19 Ine nditalamula kuti afufuze nkhaniyi kwapezekadi kuti mzinda umenewu uli ndi mbiri yowukira mafumu ndi kuti zaupandu ndi zowukira zinkachitikadi mʼmenemo.
et a me praeceptum est et recensuerunt inveneruntque quoniam civitas illa a diebus antiquis adversum reges rebellat et seditiones et proelia concitantur in ea
20 Mafumu amphamvu akhala akulamulira Yerusalemu ndi chigawo chonse cha Patsidya pa Yufurate. Iwo ankalandira msonkho ndi kulipira ndalama zakatundu olowa mʼdziko pa kanthu kena kalikonse.
nam et reges fortissimi fuerunt in Hierusalem qui et dominati sunt omni regioni quae trans Fluvium est tributum quoque et vectigal et reditus accipiebant
21 Tsopano inu khazikitsani lamulo kuti anthu amenewo asiye ntchitoyo, asamangenso mzindawo mpaka ine nditalamula
nunc ergo audite sententiam ut prohibeatis viros illos et urbs illa non aedificetur donec si forte a me iussum fuerit
22 Musachedwe kuchita zimenezi. Kodi ine ndingalole bwanji kuti zowononga zotere zikule ndi kupweteka ine mfumu?
videte ne neglegenter hoc impleatis et paulatim crescat malum contra reges
23 Kalata ya mfumu Aritasasitayi itangowerengedwa pamaso pa Rehumu ndi Simisai mlembi uja, ndi anzawo onse, iwo anapita msangamsanga ku Yerusalemu kukawaletsa Ayuda aja mwamphamvu kuti asapitirire ntchito yawo.
itaque exemplum edicti Artarxersis regis lectum est coram Reum et Samsai scriba et consiliariis eorum et abierunt festini in Hierusalem ad Iudaeos et prohibuerunt eos in brachio et robore
24 Motero ntchito yomanga Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu inayimitsidwa mpaka chaka cha chiwiri cha ulamuliro wa Dariyo mfumu ya ku Perisiya.
tunc intermissum est opus domus Dei in Hierusalem et non fiebat usque ad annum secundum regni Darii regis Persarum