< Ezara 3 >

1 Utafika mwezi wa chisanu ndi chiwiri Aisraeli atakhala kale mʼmidzi yawo, anthu anasonkhana ku Yerusalemu ndi cholinga chimodzi.
こうしてイスラエルの人々はその町々に住んでいたが、七月になって、民はひとりのようにエルサレムに集まった。
2 Kenaka Yesuwa mwana wa Yozadaki ndi ansembe anzake pamodzi ndi Zerubabeli mwana wa Sealatieli ndi abale ake anayamba kumanga guwa lansembe la Mulungu wa Israeli. Anatero pofuna kuti aziperekapo nsembe zopsereza monga analembera mʼbuku la Mose, munthu wa Mulungu uja.
そこでヨザダクの子エシュアとその仲間の祭司たち、およびシャルテルの子ゼルバベルとその兄弟たちは立って、イスラエルの神の祭壇を築いた。これは神の人モーセの律法にしるされたところに従って、その上に燔祭をささげるためであった。
3 Ndi mantha ndi mantha chifukwa cha anthu a mʼmayikomo, iwo anamanga guwalo pa maziko ake akale, ndipo anapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu pa guwapo mmawa ndi madzulo.
彼らは国々の民を恐れていたので、祭壇をもとの所に設けた。そしてその上で燔祭を主にささげ、朝夕それをささげた。
4 Ankasunga tsiku la chikondwerero cha misasa monga momwe zinalembedwera. Ankaperekanso nsembe za tsiku ndi tsiku monga mwa chiwerengero chake potsata mwambo wake wa tsiku ndi tsiku monga zinalembedwa.
また、しるされたところに従って仮庵の祭を行い、おきてに従って、毎日ささぐべき数のとおりに、日々の燔祭をささげた。
5 Pambuyo pake, ankapereka nsembe zopsereza, nsembe zopereka pa nthawi ya mwezi watsopano ndi za pa masiku onse a chikondwerero oyikidwa kutamandira Yehova, kudzanso nsembe zaufulu zopereka kwa Yehova.
そしてその後は常燔祭、新月と主のすべて定められた祭とにささげる供え物および各自が主にささげる真心よりの供え物をささげた。
6 Kuyambira pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri, iwo anayambanso kupereka nsembe zopsereza kwa Yehova, ngakhale kuti maziko a Nyumba ya Yehova anali asanamangidwe.
すなわち七月一日から燔祭を主にささげることを始めたが、主の宮の基礎はまだすえられてなかった。
7 Ndipo anapereka ndalama kwa amisiri a miyala ndi kwa amisiri a matabwa, ndi chakudya, chakumwa ndi mafuta kwa anthu a ku Sidoni ndi a ku Turo, kuti abweretse mitengo ya mkungudza pa nyanja kuchokera ku Lebanoni mpaka ku Yopa. Zonsezi anachita malinga ndi chilolezo chimene analandira kuchokera kwa Koresi, mfumu ya Peresiya.
そこで石工と木工に金を渡し、またシドンとツロの人々に食い物、飲み物および油を与えて、ペルシャ王クロスから得た許可に従って、レバノンからヨッパの海に香柏を運ばせた。
8 Tsono mu chaka chachiwiri atabwera ku Yerusalemu, ku malo akale a Nyumba ya Yehova, mwezi wachiwiri Zerubabeli mwana wa Sealatieli, Yesuwa mwana wa Yozadaki pamodzi ndi abale awo onse, ansembe, Alevi ndi onse amene anabwera ku Yerusalemu kuchokera ku ukapolo, anayamba kugwira ntchito. Iwo anasankha Alevi a zaka zoyambira makumi awiri kuti aziyangʼanira ntchito ya kumanga Nyumba ya Yehova.
さてエルサレムの神の宮に帰った次の年の二月に、シャルテルの子ゼルバベルとヨザダクの子エシュアはその兄弟である他の祭司、レビびとおよび捕囚からエルサレムに帰って来たすべての人々と共に工事を始め、二十歳以上のレビびとを立てて、主の宮の工事を監督させた。
9 Yesuwa ndi ana ake aamuna kudzanso abale ake, Kadimieli ndi ana ake (ana a Yuda) onse pamodzi anasenza udindo woyangʼanira antchito ku Nyumba ya Mulungu, kuphatikizanso ana a Henadadi komanso Alevi, ana awo ndi abale awo.
そこでユダの子孫であるエシュアとその子らおよびその兄弟、カデミエルとその子らは共に立って、神の宮で工事をなす者を監督した。ヘナダデの子らおよびレビびとの子らと、その兄弟たちもまた一緒であった。
10 Amisiri omanga nyumba atamanga maziko a Nyumba ya Yehova, ansembe anabwera akuyimba malipenga, atavala zovala zaunsembe. Ndipo Alevi, zidzukulu za Asafu, anadza akuyimba matambolini ndi kutenga udindo wawo wotamanda Yehova, potsata malangizo a Davide mfumu ya Aisraeli.
こうして建築者が主の宮の基礎をすえた時、祭司たちは礼服をつけてラッパをとり、アサフの子らであるレビびとはシンバルをとり、イスラエルの王ダビデの指令に従って主をさんびした。
11 Iwo ankayimba motamanda ndi mothokoza Yehova nyimbo iyi: “Yehova ndi wabwino; chikondi chake pa Israeli ndi chamuyaya.” Ndipo anthu onse ankafuwula kwambiri kumutamanda Yehova, chifukwa maziko a Nyumba ya Yehova anali kumangidwa.
彼らは互に歌いあって主をほめ、かつ感謝し、「主はめぐみ深く、そのいつくしみはとこしえにイスラエルに絶えることがない」と言った。そして民はみな主をさんびするとき、大声をあげて叫んだ。主の宮の基礎がすえられたからである。
12 Koma ambiri mwa ansembe, Alevi ndiponso atsogoleri amabanja, akuluakulu amene anaona Nyumba ya Yehova yakale, analira mokweza pamene anaona maziko a nyumbayi akumangidwa. Komanso ena ambiri ankafuwula mosangalala.
しかし祭司、レビびと、氏族の長である多くの人々のうちに、もとの宮を見た老人たちがあったが、今この宮の基礎のすえられるのを見た時、大声をあげて泣いた。また喜びのために声をあげて叫ぶ者も多かった。
13 Choncho panalibe amene ankatha kusiyanitsa liwu lofuwula mokondwerera ndi liwu la anthu olira, chifukwa anthuwo ankafuwula kwambiri. Ndipo liwu lofuwulalo limamveka kutali.
それで、人々は民の喜び叫ぶ声と、民の泣く声とを聞きわけることができなかった。民が大声に叫んだので、その声が遠くまで聞えたからである。

< Ezara 3 >