< Ezara 2 >

1 Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerako ku ukapolo, amene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anawagwira ukapolo ndi kupita nawo ku Babuloni (iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wake.
These are the people in the province who went up from the captivity of King Nebuchadnezzar, who had exiled them in Babylon, the people who returned to each of their cities of Jerusalem and in Judea.
2 Iwo anabwerera pamodzi ndi Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Seruya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu ndi Baana). Chiwerengero cha anthu aamuna a Israeli chinali chotere:
They came with Zerubbabel, Joshua, Nehemiah, Seraiah, Reelaiah, Mordecai, Bilshan, Mispar, Bigvai, Rehum, and Baanah. This is the record of the men of the people of Israel.
3 Zidzukulu za Parosi 2,172
The descendants of Parosh: 2,172.
4 zidzukulu za Sefatiya 372
The descendants of Shephatiah: 372.
5 zidzukulu za Ara 775
The descendants of Arah: 775.
6 zidzukulu za Pahati-Mowabu (zochokera kwa Yesuwa ndi Yowabu) 2,812
The descendants of Pahath-Moab, through Jeshua and Joab: 2,812.
7 zidzukulu za Elamu 1,254
The descendants of Elam: 1,254.
8 zidzukulu za Zatu 945
The descendants of Zattu: 945.
9 zidzukulu za Zakai 760
The descendants of Zakkai: 760.
10 zidzukulu za Bani 642
The descendants of Bani: 642.
11 zidzukulu za Bebai 623
The descendants of Bebai: 623.
12 zidzukulu za Azigadi 1,222
The descendants of Azgad: 1,222.
13 zidzukulu za Adonikamu 666
The descendants of Adonikam: 666.
14 zidzukulu za Bigivai 2,056
The descendants of Bigvai: 2,056.
15 zidzukulu za Adini 454
The descendants of Adin: 454.
16 zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya) 98
The men of Ater, through Hezekiah: ninety-eight.
17 zidzukulu za Bezayi 323
The descendants of Bezai: 323.
18 zidzukulu za Yora 112
The descendants of Jorah: 112.
19 zidzukulu za Hasumu 223
The men of Hashum: 223.
20 zidzukulu za Gibari 95.
The men of Gibbar: ninety-five.
21 Anthu a ku Betelehemu 123
The men of Bethlehem: 123.
22 Anthu aamuna a ku Netofa 56
The men of Netophah: fifty-six.
23 Anthu aamuna a ku Anatoti 128
The men of Anathoth: 128.
24 Anthu aamuna a ku Azimaveti 42
The men of Azmaveth: forty-two.
25 Anthu aamuna a ku Kiriati Yearimu, Kefira ndi Beeroti 743
The men of Kiriath Arim, Kephirah, and Beeroth: 743.
26 Anthu aamuna a ku Rama ndi Geba 621
The men of Ramah and Geba: 621.
27 Anthu aamuna a ku Mikimasi 122
The men of Michmas: 122.
28 Anthu aamuna a ku Beteli ndi Ai 223
The men of Bethel and Ai: 223.
29 Anthu aamuna a ku Nebo 52
The men of Nebo: fifty-two.
30 Anthu aamuna a ku Magaibisi 156
The men of Magbish: 156.
31 Anthu aamuna a ku Elamu wina 1,254
The men of the other Elam: 1,254.
32 Anthu aamuna a ku Harimu 320
The men of Harim: 320.
33 Anthu aamuna a ku Lodi, Hadidi ndi Ono 725
The men of Lod, Hadid, and Ono: 725.
34 Anthu aamuna a ku Yeriko 345
The men of Jericho: 345.
35 Anthu aamuna a ku Sena 3,630.
The men of Senaah: 3,630.
36 Ansembe anali awa: Zidzukulu za Yedaya (kudzera mu banja la Yesuwa) 973
The priests: descendants of Jedaiah of the house of Jeshua: 973.
37 Zidzukulu za Imeri 1,052
Immer's descendants: 1,052.
38 Zidzukulu za Pasuri 1,247
Pashhur's descendants: 1,247.
39 Zidzukulu za Harimu 1,017.
Harim's descendants: 1,017.
40 Alevi anali awa: Zidzukulu za Yesuwa ndi Kadimieli (kudzera mwa ana a Hodaviya) 74.
The Levites: descendants of Jeshua and Kadmiel, descendants of Hodaviah: seventy-four.
41 Anthu oyimba nyimbo anali awa: Zidzukulu za Asafu 128.
The temple singers, descendants of Asaph: 128.
42 Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa: Zidzukulu za Salumu, zidzukulu za Ateri, zidzukulu za Talimoni, zidzukulu za Akubu, zidzukulu za Hatita ndi zidzukulu za Sobai 139.
The descendants of the gatekeepers: descendants of Shallum, Ater, Talmon, Akkub, Hatita, and Shobai: 139 total.
43 Otumikira ku Nyumba ya Mulungu anali awa: Zidzukulu za Ziha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti,
Those who were assigned to serve in the temple: descendants of Ziha, Hasupha, Tabbaoth,
44 zidzukulu za Kerosi, zidzukulu za Siyaha, Padoni,
Keros, Siaha, Padon,
45 zidzukulu za Lebana, zidzukulu za Hagaba, zidzukulu za Akubu,
Lebanah, Hagabah, Akkub,
46 zidzukulu za Hagabu, zidzukulu za Salimayi, zidzukulu za Hanani,
Hagab, Shalmai, and Hanan.
47 zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari, zidzukulu za Reaya,
The descendants of Giddel: Gahar, Reaiah,
48 zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nekoda, zidzukulu za Gazamu,
Rezin, Nekoda, Gazzam,
49 zidzukulu za Uza, zidzukulu za Peseya, zidzukulu za Besai,
Uzza, Paseah, Besai,
50 zidzukulu za Asina, zidzukulu za Meunimu, Nefusimu,
Asnah, Meunim, and Nephusim.
51 zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri,
The descendants of Bakbuk: Hakupha, Harhur,
52 zidzukulu za Baziruti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa,
Bazluth, Mehida, Harsha,
53 zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema,
Barkos, Sisera, Temah,
54 zidzukulu za Neziya ndi zidzukulu za Hatifa.
Neziah, and Hatipha.
55 Zidzukulu za antchito a Solomoni zinali izi: Zidzukulu za Sotai, zidzukulu za Hasofereti, zidzukulu za Peruda,
The descendants of Solomon's servants: descendants of Sotai, Hassophereth, Peruda,
56 zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli,
Jaalah, Darkon, Giddel,
57 zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu, zidzukulu za Pokereti, Hazebayimu ndi Ami.
Shephatiah, Hattil, Pochereth Hazzebaim, and Ami.
58 Chiwerengero cha onse otumikira ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za Solomoni chinali 392.
There were 392 total descendants of those assigned to serve in the temple and descendants of Solomon's servants.
59 Anthu ali mʼmunsiwa anabwera kuchokera ku mizinda ya Teli-Mela, Teli-Harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri, ngakhale samatha kutsimikiza kuti mafuko awo analidi Aisraeli enieni kapena ayi:
Those who left Tel Melah, Tel Harsha, Kerub, Addon, and Immer—but were not able to prove their ancestry from Israel
60 Zidzukulu za Delaya, zidzukulu za Tobiya, ndi zidzukulu za Nekoda. Onse pamodzi anali 652.
—included 652 descendants of Delaiah, Tobiah, and Nekoda.
61 Ndi ena pakati pa ansembe anali awa: Zidzukulu za Hobiya, Hakozi, ndi Barizilai (Zidzukulu za Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai. Barizilai ameneyu ndi uja anakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi ndipo ankadziwika ndi dzina la bambo wawoyo.)
Also, from the priest's descendants: the descendants of Habaiah, Hakkoz, and Barzillai (who took his wife from the daughters of Barzillai of Gilead and was called by their name).
62 Amenewa anafufuza mayina awo mʼbuku lofotokoza mbiri ya mafuko awo, koma mayinawo sanawapezemo, choncho anawachotsa pa unsembe ngati anthu odetsedwa pa zachipembedzo.
They searched for their genealogical records, but could not find them, so they were excluded from the priesthood as unclean.
63 Bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo mpaka atapezeka wansembe wodziwa kuwombeza ndi Urimu ndi Tumimu.
So the governor told them they must not eat any of the holy sacrifices until a priest with Urim and Thummim approved.
64 Chiwerengero cha anthu onse pamodzi chinali 42,360,
The whole group totaled 42,360,
65 kuwonjezera pamenepo, panalinso antchito awo aamuna ndi aakazi okwanira 7,337. Analinso ndi amuna ndi akazi oyimba nyimbo okwanira 200.
not including their servants and their maidservants (these were 7,337) and their male and female temple singers (two hundred).
66 Anali ndi akavalo 736, nyulu 245,
Their horses: 736. Their mules: 245.
67 ngamira 435 ndi abulu 6,720.
Their camels: 435. Their donkeys: 6,720.
68 Atafika ku Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu, ena mwa atsogoleri a mabanja anapereka zopereka zaufulu zothandizira kumanganso Nyumba ya Mulungu pamalo pake pakale.
When they went to Yahweh's house in Jerusalem, the chief patriarchs offered freewill gifts to build the house.
69 Anapereka kwa msungichuma wa ntchitoyo molingana ndi mmene aliyense chuma chake chinalili: golide wa makilogalamu 500, siliva makilogalamu 2,800 ndi zovala za ansembe zokwanira 100.
They gave according to their ability to the work fund: sixty-one thousand gold darics, five thousand silver minas, and one hundred priestly tunics.
70 Ansembe, Alevi, oyimba nyimbo, alonda ndi antchito a ku Nyumba ya Yehova pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmidzi ya makolo awo.
So the priests and Levites, the people, the temple singers and gatekeepers, and those assigned to serve in the temple inhabited their cities. All the people in Israel were in their cities.

< Ezara 2 >