< Ezara 1 >
1 Mʼchaka choyamba cha ufumu wa Koresi mfumu ya Perisiya, pofuna kukwaniritsa zimene anayankhula kudzera mwa Yeremiya, Yehova anayika maganizo mu mtima mwa Koresi mfumu ya Perisiya kuti alengeze mʼdziko lake lonse ndi mawu apakamwa ngakhalenso ochita kulemba.
In the first year of Cyrus king of the Persians, that the word of the Lord by the mouth of Jeremias might be fulfilled, the Lord stirred up the spirit of Cyrus king of the Persians: and he made a proclamation throughout all his kingdom, and in writing also, saying:
2 Iye anati, “Koresi mfumu ya Perisiya ikunena kuti, “‘Yehova, Mulungu wakumwamba wandipatsa maufumu onse a dziko lapansi, ndipo wandipatsa udindo woti ndimumangire Nyumba ku Yerusalemu mʼdziko la Yuda.
Thus saith Cyrus king of the Persians: The Lord the God of heaven hath given to me all the kingdoms of the earth, and he hath charged me to build him a house in Jerusalem, which is in Judea.
3 Aliyense wa inu amene ali wa Yehova, Mulungu wakeyo akhale naye. Tsono aliyense wa inu apite ku Yerusalemu, mʼdziko la Yuda kuti akamange Nyumba ya Yehova, Mulungu wa Israeli. Iyeyu ndi Mulungu amene ali mu Yerusalemu.
Who is there among you of all his people? His God be with him. Let him go up to Jerusalem, which is in Judea, and build the house of the Lord the God of Israel: he is the God that is in Jerusalem.
4 Ndipo kumalo kulikonse kumene otsalawo akukhala, athandizidwe ndi eni dzikolo powapatsa siliva, golide, katundu ndi ziweto ndi zopereka za ufulu zoti akapereke ku Nyumba ya Yehova imene ili ku Yerusalemu.’”
And let all the rest in all places wheresoever they dwell, help him every man from his place. with silver and gold, and goods, and cattle, besides that which they offer freely to the temple of God, which is in Jerusalem.
5 Choncho atsogoleri a mabanja afuko la Yuda ndi la Benjamini komanso ansembe ndi Alevi, aliyense amene Mulungu anawutsa mtima wake, anayamba kukonzeka kupita kukamanga Nyumba ya Yehova imene ili ku Yerusalemu.
Then rose up the chief of the fathers of Juda and Benjamin, and the priests, and Levites, and every one whose spirit God had raised up, to go up to build the temple of the Lord, which was in Jerusalem.
6 Onse oyandikana nawo anawathandiza powapatsa ziwiya za siliva ndi zagolide, kuphatikizaponso katundu ndi ziweto, ndiponso mphatso zamtengo wapatali, kuwonjezera pa zopereka zaufulu zija.
And all they that were round about, helped their hands with vessels of silver, and gold, with goods, and with beasts, and with furniture, besides what they had offered on their own accord.
7 Nayenso mfumu Koresi anatulutsa ziwiya za mʼNyumba ya Yehova zimene Nebukadinezara anazitenga kuzichotsa ku Yerusalemu ndi kuziyika mʼnyumba ya milungu yake.
And king Cyrus brought forth the vessels of the temple of the Lord, which Nabuchodonosor had taken from Jerusalem, and had put them in the temple of his god.
8 Koresi, mfumu ya ku Perisiya inatulutsa ziwiyazi ndi kuzipereka kwa Miteridati, msungichuma amene anaziwerenga pamaso pa Sesibazara nduna yayikulu ya dziko la Yuda.
Now Cyrus king of Persia brought them forth by the hand of Mithridates the son of Gazabar, and numbered them to Sassabasar the prince of Juda.
9 Chiwerengerochi chinali motere: Mabeseni agolide 30 mabeseni asiliva 1,000 a zopereka 29
And this is the number of them: thirty bowls of gold, a thousand bowls of silver, nine and twenty knives, thirty cups of gold,
10 timiphika tagolide 230 timiphika tasiliva 410 ziwiya zina 1,000.
Silver cups of a second sort, four hundred and ten: other vessels a thousand.
11 Ziwiya zonse zagolide ndi siliva pamodzi zinalipo 5,400. Zonsezi ndi zimene Sezi-Bazara anabwera nazo pamene otengedwa ukapolo aja ankabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku Babuloni.
All the vessels of gold and silver, five thousand four hundred: all these Sassabasar brought with them that came up from the captivity of Babylon to Jerusalem.