< Ezekieli 9 >

1 Pambuyo pake Yehova anandiyankhula mofuwula kuti, “Bwerani pafupi, inu odzalanga mzindawu, aliyense ali ndi chida chake mʼmanja.”
Et clamavit in auribus meis voce magna, dicens: Appropinquaverunt visitationes urbis, et unusquisque vas interfectionis habet in manu sua.
2 Ndipo ndinaona anthu asanu ndi mmodzi akubwera kuchokera ku chipata chakumtunda chimene chimaloza kumpoto, aliyense ali ndi chida choopsa cha nkhondo mʼdzanja lake. Pagulu pawopa panali munthu wovala chovala chabafuta, atatenga zolembera pambali pake. Iwo analowa ndi kuyima pambali pa guwa lamkuwa.
Et ecce sex viri veniebant de via portæ superioris, quæ respicit ad aquilonem, et uniuscujusque vas interitus in manu ejus: vir quoque unus in medio eorum vestitus erat lineis, et atramentarium scriptoris ad renes ejus: et ingressi sunt, et steterunt juxta altare æreum.
3 Tsono ulemerero wa Mulungu wa Israeli unakwera kuchokera pamwamba pa akerubi, pamene unali, ndipo unafika pa chiwundo cha Nyumba ya Mulungu. Pamenepo Yehova anayitana munthu amene anavala chovala chabafuta uja amene anatenga zolembera pambali pake
Et gloria Domini Israël assumpta est de cherub, quæ erat super eum ad limen domus: et vocavit virum qui indutus erat lineis, et atramentarium scriptoris habebat in lumbis suis:
4 ndipo anamuwuza kuti, “Pita mu mzinda wonse wa Yerusalemu ndi kuyika chizindikiro pamphumi pa anthu amene akumva chisoni ndi kulira chifukwa cha zinthu zonse zonyansa zimene zikuchitika mu mzindamo.”
et dixit Dominus ad eum: Transi per mediam civitatem, in medio Jerusalem, et signa thau super frontes virorum gementium et dolentium super cunctis abominationibus quæ fiunt in medio ejus.
5 Kenaka ndinamva Yehova akuwuza anthu ena aja kuti, “Mutsateni mu mzinda wonse ndipo mukakanthe aliyense mopanda kumvera chisoni kapena chifundo.
Et illis dixit, audiente me: Transite per civitatem sequentes eum, et percutite: non parcat oculus vester, neque misereamini:
6 Mukaphe kotheratu anthu okalamba, anyamata ndi atsikana, makanda ndi akazi koma musakakhudze wina aliyense amene ali ndi chizindikiro. Muyambire ku Nyumba yanga yopatulika.” Motero iwo anayamba ndi akuluakulu amene anali kutsogolo kwa Nyumba ya Mulungu.
senem, adolescentulum et virginem, parvulum et mulieres interficite usque ad internecionem: omnem autem super quem videritis thau, ne occidatis: et a sanctuario meo incipite. Cœperunt ergo a viris senioribus, qui erant ante faciem domus.
7 Ndipo Yehova anawawuza kuti, “Ipitsani Nyumba ya Mulungu ndipo mudzaze mabwalo ake ndi anthu akufa. Pitani.” Choncho iwo anapita nayamba kupha anthu mu mzinda monse.
Et dixit ad eos: Contaminate domum, et implete atria interfectis; egredimini. Et egressi sunt, et percutiebant eos qui erant in civitate.
8 Pamene iwo ankapha anthu, ine ndinatsala ndekha. Tsono ndinadzigwetsa chafufumimba ndi kufuwula kuti, “Aa, Ambuye Yehova! Kodi mwawakwiyiratu anthu a ku Yerusalemu motero kuti mudzawononga kotheratu anthu onse otsala ku Israeli?”
Et cæde completa, remansi ego, ruique super faciem meam, et clamans aio: Heu! heu! heu! Domine Deus: ergone disperdes omnes reliquias Israël, effundens furorem tuum super Jerusalem?
9 Iye anandiyankha kuti, “Tchimo la Aisraeli ndi Yuda ndi lalikulu kwambiri; dziko ladzaza ndi zophana ndipo mu mzinda mwadzaza ndi zosalungama. Iwo akunena kuti, ‘Yehova walisiya dziko lake; Yehova sakuona.’
Et dixit ad me: Iniquitas domus Israël et Juda magna est nimis valde, et repleta est terra sanguinibus, et civitas repleta est aversione: dixerunt enim: Dereliquit Dominus terram, et Dominus non videt.
10 Choncho sindidzawamvera chisoni kapena kuwaleka, koma Ine ndidzawalanga potsata zochita zawo.”
Igitur et meus non parcet oculus, neque miserebor: viam eorum super caput eorum reddam.
11 Ndipo munthu wovala chovala chabafuta uja atatenga zolembera pambali pake anadzafotokozera Yehova kuti, “Ndachita monga munandilamulira.”
Et ecce vir qui erat indutus lineis, qui habebat atramentarium in dorso suo, respondit verbum, dicens: Feci sicut præcepisti mihi.

< Ezekieli 9 >