< Ezekieli 7 >

1 Yehova anandipatsa uthenga uwu kuti,
ויהי דבר יהוה אלי לאמר׃
2 “Iwe mwana wa munthu, Ine Ambuye Yehova ndikuwuza dziko la Israeli kuti: “Chimaliziro! Chimaliziro chafika ku ngodya zinayi za dziko.
ואתה בן אדם כה אמר אדני יהוה לאדמת ישראל קץ בא הקץ על ארבעת כנפות הארץ׃
3 Chimaliziro chili pa iwe tsopano. Mkwiyo wanga ndidzawuthira pa iwe. Ndidzakuweruza molingana ndi machitidwe ako ndi kukulanga chifukwa cha zonyansa zako.
עתה הקץ עליך ושלחתי אפי בך ושפטתיך כדרכיך ונתתי עליך את כל תועבתיך׃
4 Ine sindidzakumvera chisoni kapena kukuleka. Ndidzakulanga ndithu chifukwa cha ntchito zako zoyipa komanso chifukwa cha miyambo yako yonyansa imene ili pakati pako. Pamenepo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
ולא תחוס עיני עליך ולא אחמול כי דרכיך עליך אתן ותועבותיך בתוכך תהיין וידעתם כי אני יהוה׃
5 “Zimene ndikunena Ine Ambuye Yehova ndi izi: “Chiwonongeko! Chiwonongeko chimene sichinamvekepo! Taona chikubwera!
כה אמר אדני יהוה רעה אחת רעה הנה באה׃
6 Chimaliziro chafika! Chimaliziro chafika! Chiwonongeko chakugwera. Taona chafika!
קץ בא בא הקץ הקיץ אליך הנה באה׃
7 Inu anthu okhala mʼdziko, chiwonongeko chakugwerani. Nthawi yafika, tsiku layandikira; tsiku la chisokonezo osati la chimwemwe pa mapiri.
באה הצפירה אליך יושב הארץ בא העת קרוב היום מהומה ולא הד הרים׃
8 Ine ndili pafupi kukukwiyirani, ndipo ukali wanga udzathera pa iwe; Ine ndidzakuweruza molingana ndi machitidwe ako ndiponso ndidzakulanga chifukwa cha miyambo yako yonyansa.
עתה מקרוב אשפוך חמתי עליך וכליתי אפי בך ושפטתיך כדרכיך ונתתי עליך את כל תועבותיך׃
9 Ine sindidzakumvera chisoni kapena kukuleka. Ndidzakulanga malingana ndi ntchito zako ndiponso chifukwa cha miyambo yako yonyansa pakati pako.
ולא תחוס עיני ולא אחמול כדרכיך עליך אתן ותועבותיך בתוכך תהיין וידעתם כי אני יהוה מכה׃
10 “Taona, tsikulo! Taona, lafika! Chiwonongeko chako chabwera. Ndodo yaphuka mphundu za maluwa. Kudzitama kwaphuka.
הנה היום הנה באה יצאה הצפרה צץ המטה פרח הזדון׃
11 Chiwawa chasanduka ndodo yowakwapulira chifukwa cha kuyipa kwawo. Palibe mwa anthu amenewo amene adzatsale. Palibe ndi mmodzi yemwe mwa unyinji wawo. Palibiretu ndipo sipadzapezeka munthu wowalira maliro.
החמס קם למטה רשע לא מהם ולא מהמונם ולא מהמהם ולא נה בהם׃
12 Nthawi yafika! Tsiku layandikira! Munthu wogula asakondwere ndipo wogulitsa asamve chisoni, popeza ukali wanga uli pa gulu lonse.
בא העת הגיע היום הקונה אל ישמח והמוכר אל יתאבל כי חרון אל כל המונה׃
13 Wogulitsa sadzazipezanso zinthu zimene anagulitsa kwa wina chinkana onse awiri akanali ndi moyo, pakuti chilango chidzagwera onsewo ndipo sichingasinthike. Chifukwa cha machimo awo, palibe aliyense amene adzapulumutsa moyo wake.
כי המוכר אל הממכר לא ישוב ועוד בחיים חיתם כי חזון אל כל המונה לא ישוב ואיש בעונו חיתו לא יתחזקו׃
14 “Lipenga lalira, ndipo zonse zakonzeka. Koma palibe ndi mmodzi yemwe amene akupita ku nkhondo, pakuti mkwiyo wanga uli pa gulu lonse.
תקעו בתקוע והכין הכל ואין הלך למלחמה כי חרוני אל כל המונה׃
15 Ku bwalo kuli kumenyana ndipo mʼkati muli mliri ndi njala. Anthu okhala ku midzi adzafa ndi nkhondo. Iwo okhala ku mizinda adzafa ndi mliri ndi njala.
החרב בחוץ והדבר והרעב מבית אשר בשדה בחרב ימות ואשר בעיר רעב ודבר יאכלנו׃
16 Onse amene adzapulumuka ndi kumakakhala ku mapiri, azidzalira ngati nkhunda za ku zigwa. Aliyense azidzabuwula chifukwa cha machimo ake.
ופלטו פליטיהם והיו אל ההרים כיוני הגאיות כלם המות איש בעונו׃
17 Dzanja lililonse lidzalefuka, ndipo bondo lililonse lidzalobodoka ngati madzi.
כל הידים תרפינה וכל ברכים תלכנה מים׃
18 Iwo adzavala ziguduli ndipo adzagwidwa ndi mantha. Adzakhala ndi nkhope zamanyazi ndipo mitu yawo adzameta mpala.
וחגרו שקים וכסתה אותם פלצות ואל כל פנים בושה ובכל ראשיהם קרחה׃
19 “Iwo adzataya siliva wawo mʼmisewu ndipo golide wawo adzakhala chinthu chonyansa. Siliva ndi golide wawo sizidzatha kuwapulumutsa pa tsiku la ukali wa Yehova. Chuma chawochi sichidzawathandiza kuthetsa njala, kapena kukhala okhuta, pakuti ndicho chinawagwetsa mʼmachimo.
כספם בחוצות ישליכו וזהבם לנדה יהיה כספם וזהבם לא יוכל להצילם ביום עברת יהוה נפשם לא ישבעו ומעיהם לא ימלאו כי מכשול עונם היה׃
20 Iwo ankanyadira zodzikongoletsera zawo zamakaka ndipo ankazigwiritsa ntchito kupanga mafano awo onyansa ndi zonyansa zawo zina. Nʼchifukwa chake Ine ndidzazisandutsa kukhala zowanyansa.
וצבי עדיו לגאון שמהו וצלמי תועבתם שקוציהם עשו בו על כן נתתיו להם לנדה׃
21 Ndidzazipereka kwa alendo kuti azifunkhe. Anthu oyipa a dziko lapansi adzazilanda ndi kudziyipitsa.
ונתתיו ביד הזרים לבז ולרשעי הארץ לשלל וחללה׃
22 Ine ndidzawalekerera anthuwo ndipo adzayipitsa malo anga apamtima. Adzalowamo ngati mbala ndi kuyipitsamo.
והסבותי פני מהם וחללו את צפוני ובאו בה פריצים וחללוה׃
23 “Konzani maunyolo, chifukwa dziko ladzaza ndi anthu opha anzawo ndipo mzinda wadzaza ndi chiwawa.
עשה הרתוק כי הארץ מלאה משפט דמים והעיר מלאה חמס׃
24 Ndidzabweretsa mitundu ya anthu oyipitsitsa kuti idzalande nyumba zawo. Ndidzathetsa kunyada kwa anthu amphamvu pamene anthu akunja adzalowa mʼmalo awo achipembedzo ndi kuyipitsamo.
והבאתי רעי גוים וירשו את בתיהם והשבתי גאון עזים ונחלו מקדשיהם׃
25 Nkhawa ikadzawafikira adzafunafuna mtendere koma osawupeza.
קפדה בא ובקשו שלום ואין׃
26 Tsoka lidzatsatana ndi tsoka linzake, ndipo mphekesera idzatsatana ndi mphekesera inzake. Iwo adzayesa kufuna masomphenya kuchokera kwa mneneri. Adzasowa ansembe owaphunzitsa malamulo, ndipo anthu akuluakulu sadzakhalanso ndi uphungu.
הוה על הוה תבוא ושמעה אל שמועה תהיה ובקשו חזון מנביא ותורה תאבד מכהן ועצה מזקנים׃
27 Mfumu idzalira, kalonga adzagwidwa ndi mantha. Manja a anthu a mʼdzikomo azidzangonjenjemera ndi mantha. Ine ndidzawalanga molingana ndi machitidwe awo, ndipo ndidzawaweruza molingana ndi momwe anaweruzira anzawo.
המלך יתאבל ונשיא ילבש שממה וידי עם הארץ תבהלנה מדרכם אעשה אותם ובמשפטיהם אשפטם וידעו כי אני יהוה׃

< Ezekieli 7 >