< Ezekieli 5 >
1 Tsiku lina Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, tsopano tenga lupanga lakuthwa ndipo uligwiritse ntchito ngati lumo lometera. Umete tsitsi ndi ndevu zako. Kenaka utenge sikelo ndipo ugawe tsitsilo patatu.
2 Kuzinga mzinda kuja kukatha, chimodzi cha zigawo zitatu za tsitsilo uchitenthe pakati pa mzinda. Chigawo chachiwiri uchiduledule ndi lupanga, poyenda muzungulire mzinda wonsewo. Chigawo chachitatu uchimwazire ku mphepo, ndidzachitsata nditasolola lupanga.
3 Koma utengeko tsitsi pangʼono, ulimange mu mpindiro wa mkanjo wako.
4 Pa tsitsi limeneli utapepo lina, uliponye pa moto ndi kulitentha. Moto udzayambira pamenepo mpaka ku nyumba yonse ya Israeli.”
5 Ambuye Yehova akunena kuti, “Uyu ndi Yerusalemu amene ndamuyika pakati pa mitundu ya anthu, ndipo mayiko onse amuzungulira.
6 Koma anthu a Yerusalemu aphwanya malamulo anga pochita zoyipa kuposa anthu a mitundu ina. Iwo anandipandukira kupambana anthu ena amene awazungulira. Iwo anakana malamulo anga ndipo sanasunge malangizo anga.
7 “Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti: Popeza mwakhala osamvera kupambana anthu a mitundu ina amene akuzungulirani, popeza simunatsate malamulo anga kapena kusunga malangizo anga, mʼmalo mwake mwakhala mukutsata makhalidwe a anthu a mitundu ina amene akuzungulirani.
8 “Tsono Ambuye Yehova akuti: Ine mwini ndikutsutsana nawe, Yerusalemu, choncho Ine ndidzakulangani. Ine ndidzakulangani anthu a mitundu ina akuona.
9 Chifukwa cha ntchito zanu zonyansa ndidzakulangani ndi chilango chimene sindinakulangeni nacho nʼkale lomwe ndipo sindidzakulangani ndi chofanana nacho mʼtsogolomo.
10 Tsono pakati panu makolo adzadya ana awo, ndipo ana adzadya makolo awo. Ndidzakulanga ndipo otsala onse ndidzawabalalitsa ku mphepo zonse zinayi.
11 Ndithu, pali Ine, akutero Ambuye Yehova Wamoyo, pakuti mwayipitsa Nyumba yanga ndi mafano ano oyipa ndi miyambo yanu yonyansa, Inenso ndidzakulangani. Sindidzakulekererani kapena kukumverani chisoni.
12 Chimodzi mwa zigawo zitatu za anthu ako chidzafa ndi mliri, kapena chidzawonongeka ndi njala; chigawo china chidzaphedwa ndi lupanga kunja kwa mzinda, ndipo chigawo china ndidzachibalalitsira ku mphepo zonse zinayi pochita kuchithamangitsa.
13 “Ndi mmene udzachitire mkwiyo wanga. Ndikadzatsiriza kuwalanga, pamenepo mtima wanga udzakhala pansi. Adzadziwa kuti Ine Yehova ndinawayankhula mwa nsanje ndikadzawalanga.
14 “Ndidzakusandutsa iwe bwinja ndi chinthu chonyozeka pakati pa anthu a mitundu ina amene akuzungulira, ndi kwa onse odutsapo
15 Udzakhala chinthu chonyozeka ndi chonyogodoledwa. Udzakhala chenjezo ndi chinthu choopsa kwa anthu a mitundu ina amene akuzungulira ndikadzakulanga mokwiya ndi mwaukali ndi kugamula mlandu wako mokwiya. Ine Yehova ndayankhula.
16 Pamene ndidzakulasa ndi njala yolasa ngati mivi yoopsa ndi yosakaza ndidzatero nʼcholinga choti ndikuwonongeni. Ndidzagwetsa njalayo pa iwe mowirikiza pochepetsa chakudya chako cha tsiku ndi tsiku.
17 Ndidzatumiza njala ndi zirombo za kuthengo, ndipo zidzakulanda ana ako. Mliri ndi kuphana zidzakhala pakati pako, ndipo ndidzakubweretsera nkhondo. Ine Yehova ndayankhula.”