< Ezekieli 48 >

1 “Nawa mayina a mafuko a Israeli: Dani adzakhala ndi chigawo chimodzi kuyambira kumalire akumpoto kuchokera ku nyanja kudzera ku Hetiloni mpaka ku chipata cha Hamati, kukafika ku Hazari-Enani, mzinda umene uli kumpoto kwa malire a Damasiko oyangʼanana ndi Hamati, kuchokera mʼchigawo chimodzi kummawa mpaka kumadzulo.
“Here is a list of the tribes of Israel [and the territory that each tribe is to receive]: [The tribe of] Dan will be allotted land at the northern boundary [of Israel]: It will extend east from the Mediterranean Sea east to Hethlon [city], then from there to Hamath Pass, and on to [the town of] Hazar-Enan south of Damascus, between Damascus and Hamath. The tribe of Dan will receive land on the northern border [of Israel] from the eastern end [of the country] west to the [Mediterranean] Sea.
2 “Aseri adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi dziko la Dani kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
South of their land will be the territory [for the tribe] of Asher.
3 “Nafutali adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi dziko la Aseri kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
South of their land will be the territory [for the tribe] of Naphtali.
4 “Manase adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi dziko la Nafutali kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
South of their land will be the territory [for the tribe] of Manasseh.
5 “Efereimu adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi dziko la Manase kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
South of their land will be the territory [for the tribe] of Ephraim.
6 “Rubeni adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi Efereimu kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
South of their land will be the territory [for the tribe] of Reuben.
7 “Yuda adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi Rubeni kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
South of their land will be the territory [for the tribe] of Judah.
8 “Kuchita malire ndi Yuda kuchokera kummawa mpaka kumadzulo padzakhala chigawo chimene mudzachipereke ngati mphatso yapadera. Mulifupi mwake mudzakhala makilomita khumi ndi awiri ndi theka, ndipo mulitali mwake, kuchokera kummawa mpaka kumadzulo, mudzafanana ndi zigawo zina za mafuko. Malo a Nyumba ya Mulungu adzakhala pakati pake.
South of their land will be an area set apart for special use. The temple will be in the center of that area.
9 “Chigawo chapadera chimene mudzachipereke kwa Yehova mulitali mwake mudzakhala makilomita khumi ndi awiri ndi theka ndipo mulifupi mwake makilomita asanu.
It must be (8.3 miles/13.3 km.) long and (6.7 miles/10.6 km.) wide.
10 Ichi chidzakhala chigawo chopatulika cha ansembe ndipo chidzagawidwe motere: Mbali ya kumpoto kutalika kwake kudzakhala makilomita khumi ndi awiri ndi theka, mbali ya kumadzulo kudzakhala makilomita asanu, mbali ya kummawa makilomita asanu ndiponso makilomita khumi ndi awiri ndi theka mbali yakummwera. Pakati pake padzakhala malo a Nyumba ya Mulungu.
For the priests, there must be a strip of land (8.3 miles/13.3 km.) long and (3.3 miles/5.3 km.) wide. The temple will be in the center of that area.
11 Chimenechi chidzakhala chigawo cha ansembe opatulika, ana a Zadoki, amene ndi okhulupirika ponditumikira Ine, ndipo sanasochere ngati momwe anachitira Alevi pamene Aisraeli anasochera.
That area is for the priests who are descendants of Zadok. They are ones who served me faithfully and did not turn away from me, like most of the descendants of Levi and the other Israeli people did.
12 Chigawochi, mwa zigawo zonse za mʼdzikomo, chidzakhala kwa ansembewo ngati mphatso yawo yapadera. Chidzachita malire ndi dziko la Alevi.
When the land is distributed, that area must be given to the priests; it is land that is very sacred. It will be next to the land that will be given to the other descendants of Levi.
13 “Moyandikana ndi chigawo cha ansembe, Alevi adzakhala ndi dera lawo lotalika makilomita khumi ndi awiri ndi theka, ndipo mulifupi mwake makilomita asanu. Kutalika kwake konse kudzakhala makilomita khumi ndi awiri ndi theka ndipo mulifupi mwake makilomita asanu.
The land that will be allotted to the [other] descendants of Levi will be the same size as the land allotted to the priests. So together, those two portions of land will be (8.3 miles/13.3 km.) long and (6.6 miles/10.6 km.) wide.
14 Asagulitse kapena kusinthitsa mbali iliyonse ya chigawo chimenechi. Ichi ndi chigawo chabwino kwambiri ndipo chisapatsidwe kwa anthu ena, chifukwa ndi chopatulikira Yehova.
None of this special land will ever be permitted to be sold or traded or used by other people, because it belongs to me, Yahweh. It is set apart for me.
15 “Chigawo chotsala mulifupi mwake makilomita awiri ndi theka ndipo mulitali mwake makilomita khumi ndi awiri ndi theka, chidzakhala malo a anthu wamba, chomangapo nyumba ndiponso chodyetsera ziweto zawo. Mzinda udzamangidwa pomwepo ndipo udzakhala pakati ndi pakati.
The rest [of that sacred area, a strip of land] (8.3 miles/13.3 km.) long and (1.7 miles/2.65 km.) wide will be allotted for other people to use. It will be land where they will be permitted to build homes and have pasturelands. There will be a city at the center.
16 Miyeso yake ndi iyi: kumpoto kutalika kwake kudzakhala mamita 2,250, kummwera mamita 2,250, kummawa mamita 2,250 ndipo kumadzulo mamita 2,250.
The city will be square, (1.5 miles/2.4 km.) on each side.
17 Chigawo cha mzinda chodyetsera ziweto chidzakhala motere: kumpoto kutalika kwake kudzakhala mamita 125, kummwera kutalika kwake kudzakhala mamita 125, kummawa kutalika kwake kudzakhala mamita 125, ndipo kumadzulo kutalika kwake kudzakhala mamita 125.
Around the city there will be an area for farming, that will be (150 yards/135 meters) in each direction.
18 Chigawo chotsala, choyandikana ndi chigawo chopatulika, kutalika kwake makilomita asanu mbali yakummawa ndiponso makilomita asanu mbali ya kumadzulo. Dera limeneli lidzakhale lolimamo anthu ogwira ntchito mu mzinda.
Outside the city, to the east and to the west, there will be a farming area. It will extend (3 miles/4.8 km.) to the east and (3 miles/4.8 km.) to the west. [Men who work there] will produce food for the people who work in the city.
19 Anthu ogwira ntchito mu mzinda amene adzalime mʼmundamo adzachokera ku mafuko onse a Israeli.
[Some of] those who come from the various Israeli tribes to work in the city may also work on the farmland.
20 Chigawo chopatulika chonsechi chidzakhale makilomita khumi ndi awiri ndi theka mbali zonse. Ndiye kuti, mudzapatule padera chigawo chopatulika pamodzi ndi kadziko ka mzindawo.
That entire special area, including the sacred lands and the city, will be a square that is (8.3 miles/13.3 km.) on each side.
21 “Tsono chigawo chotsala pambali zonse ziwiri za chigawo chopatulika ndi za kadziko ka mzinda, chikhale cha mfumu. Chidzayenda motere: kuyambira mʼmalire a chigawo chopatulika kukalekezera mʼmalire akummawa. Mbali ina kuyambiranso mʼmalire a chigawo chopatulika kukalekezera malire a kumadzulo, kudutsa kufupi ndi zigawo za mafuko. Dera lonselo likhale la mfumu.
The areas to the east and to the west of the sacred area and the city will belong to the king. One area will extend east to the eastern boundary of Israel and the other will extend west to the Mediterranean Sea. The sacred area in which the temple is located will be in the middle.
22 Choncho chigawo cha Alevi ndi chigawo cha mzinda zidzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzayambira mbali ya kummawa mpaka ya kumadzulo kwa dziko la Benjamini.
The area that belongs to the king will be between the land [of the tribe] of [to the north] and the land [of the tribe] of Benjamin [to the south].
23 “Za mafuko ena otsala zidzayenda motere: Benjamini adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzayambira mbali ya kummawa mpaka ya kumadzulo.
South of that special area, each of the other tribes must be allotted one portion of land that extends from the eastern [boundary of Israel] west [to the Mediterranean Sea]. [Beginning at the north] will be land for [the tribe of] Benjamin.
24 “Simeoni adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi chigawo cha Benjamini kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
South of their land will be the territory for [the tribe of] Simeon.
25 “Isakara adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi chigawo cha Simeoni kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
South of their land will be the territory for [the tribe of] Issachar.
26 “Zebuloni adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi chigawo cha Isakara kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
South of their land will be the territory for [the tribe of] Zebulun.
27 “Gadi adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi chigawo cha Zebuloni kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
South of their land will be the territory for [the tribe of] Gad.
28 “Malire a Gadi a mbali yakummwera ku Negevi adzayenda kuchokera ku Tamara mpaka ku dziwe la Meriba Kadesi komanso kuchokera ku Mtsinje wa Igupto mpaka ku Nyanja Yayikulu.
The southern boundary of [the tribe of] Gad will extend south from Tamar to the springs at Meribah-Kadesh, and from there [to the west] along the dry riverbed at the border of Egypt to the Mediterranean Sea.
29 “Ili ndilo dziko limene mudzagawire mafuko a Israeli kuti likhale cholowa. Zimenezi zidzakhala zigawo zawo, ndikutero Ine Ambuye Yehova.
That is the land that you must allot to the tribes of Israel, to belong to them permanently. [That is what I], Yahweh the Lord, declare.”
30 “Izi ndizo zidzakhale zipata zotulukira mzinda, ndipo zidzatchulidwa mayina a mafuko a Israeli. Kuyambira kumpoto kumene kudzakhala kotalika mamita 2,250,
These will be the exits from the city: On the north side, which will be (1.5 miles/2.4 km.) long,
31 kudzakhale zipata zitatu izi: cha Rubeni, cha Yuda ndi cha Levi.
there must be three gates; each one will have the name of one of the tribes of Israel. The first one will be named for Reuben, the next for Judah, the next for Levi.
32 “Mbali ya kummawa, imene kutalika kwake ndi mamita 2,250, kudzakhala zipata zitatu izi: chipata cha Yosefe, chipata cha Benjamini ndi chipata cha Dani.
On the east side, [also] (1.5 miles/2.4 km.) long, will be gates named for Joseph, Benjamin, and Dan.
33 “Mbali yakummwera, imene kutalika kwake ndi mamita 2,250, kudzakhala zipata zitatu izi: chipata cha Simeoni, chipata cha Isakara ndi chipata cha Zebuloni.
On the south side, [also] (1.5 miles/2.4 km.) long, will be gates named for Simeon, Issachar, and Zebulun.
34 “Mbali ya kumadzulo, imene kutalika kwake ndi mamita 2,250 kudzakhala zipata zitatu izi: chipata cha Gadi, chipata cha Aseri ndi chipata cha Nafutali.
On the west side, [also] (1.5 miles/2.4 km.) long, will be gates named for Gad, Asher, and Naphtali.
35 “Choncho kutalika kwa mzinda kuzungulira kwake kudzakhala mamita 9,000. “Ndipo dzina la mzindawo kuyambira nthawi imeneyo mpaka mʼtsogolo lidzakhala: Yehova Ali Pano.”
[So] the distance around the city will thus be (6 miles/9.6 km.). And from that time on, the name of the city will be ‘Yahweh Is There’.’

< Ezekieli 48 >