< Ezekieli 45 >

1 “‘Mukamadzagawa dziko kuti fuko lililonse lilandire cholowa chake, mudzapatuleko chigawo chimodzi kuti chikhale cha Yehova. Mulitali mwake mudzakhale makilomita khumi ndi awiri ndi theka ndipo mulifupi mwake makilomita khumi. Malo onsewo adzakhale opatulika.
ובהפילכם את הארץ בנחלה תרימו תרומה ליהוה קדש מן הארץ ארך חמשה ועשרים אלף ארך ורחב עשרה אלף קדש הוא בכל גבולה סביב׃
2 Mʼkati mwa chigawo chimenechi, malo a mamita 250 mbali iliyonse adzakhala malo a Nyumba ya Mulungu. Pozungulira pake ponse padzakhala malo a mamita 25.
יהיה מזה אל הקדש חמש מאות בחמש מאות מרבע סביב וחמשים אמה מגרש לו סביב׃
3 Mʼchigawo chopatulikacho muyeze malo a makilomita 12 ndi theka mulitali mwake, makilomita asanu mulifupi mwake. Pamenepo padzakhala malo opatulika kwambiri.
ומן המדה הזאת תמוד ארך חמש ועשרים אלף ורחב עשרת אלפים ובו יהיה המקדש קדש קדשים׃
4 Malo opatulika amenewa adzakhalanso a ansembe amene amatumikira ku malo opatulika, amene amayandikira Yehova kuti amutumikire. Pamenepo padzakhala malo omangapo nyumba zawo ndi malo omangapo Nyumba ya Mulungu.
קדש מן הארץ הוא לכהנים משרתי המקדש יהיה הקרבים לשרת את יהוה והיה להם מקום לבתים ומקדש למקדש׃
5 Alevi otumikira ku Nyumba ya Mulungu adzakhala ndi malo a makilomita khumi ndi awiri ndi theka mulitali mwake ndi makilomita asanu mulifupi mwake. Kumeneko ndiko kudzakhale midzi yawo.
וחמשה ועשרים אלף ארך ועשרת אלפים רחב יהיה ללוים משרתי הבית להם לאחזה עשרים לשכת׃
6 “‘Moyandikana ndi malo opatulika, padzakhale malo a makilomita awiri ndi theka mulifupi mwake ndi makilomita khumi ndi awiri ndi theka mulitali mwake; kuti akhale malo a mzinda. Malo amenewa adzakhala a Aisraeli onse.
ואחזת העיר תתנו חמשת אלפים רחב וארך חמשה ועשרים אלף לעמת תרומת הקדש לכל בית ישראל יהיה׃
7 “‘Mfumu idzakhale ndi malo okhudzana ndi chigawo cha malo opatulika ndi cha mzinda. Malowo ayandikane ndi zigawozo chakummawa ndi chakumadzulo. Malowo atalike ngati chigawo chimodzi cha fuko la Israeli kuyambira ku malire akummawa mpaka ku malire akumadzulo.
ולנשיא מזה ומזה לתרומת הקדש ולאחזת העיר אל פני תרומת הקדש ואל פני אחזת העיר מפאת ים ימה ומפאת קדמה קדימה וארך לעמות אחד החלקים מגבול ים אל גבול קדימה׃
8 Malowa adzakhala chigawo cha mfumu mu Israeli. Choncho mafumu anga sadzazunzanso anthu anga, koma adzidzalola Aisraeli kuti akhale ndi zigawo zawozawo.
לארץ יהיה לו לאחזה בישראל ולא יונו עוד נשיאי את עמי והארץ יתנו לבית ישראל לשבטיהם׃
9 “‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Tsono pakwana, inu akalonga a Israeli. Lekani nkhanza zanu ndi kupondereza anthu anga. Muzitsata chilungamo ndi kuchita zokomera anthu. Musapirikitse anthu anga mʼdzikomo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
כה אמר אדני יהוה רב לכם נשיאי ישראל חמס ושד הסירו ומשפט וצדקה עשו הרימו גרשתיכם מעל עמי נאם אדני יהוה׃
10 Miyeso yanu yoyezera zinthu monga efa ndi bati zizikhala zokhulupirika.
מאזני צדק ואיפת צדק ובת צדק יהי לכם׃
11 Efa ndi bati ikhale miyeso yolingana kukula kwake. Muyeso wa homeri ukhale wokwanira mabati khumi, ukhalenso wokwanira maefa khumi. Ndiye kuti kukula kwa miyeso iwiriyo kuzidzatsata kukula kwa homeriyo.
האיפה והבת תכן אחד יהיה לשאת מעשר החמר הבת ועשירת החמר האיפה אל החמר יהיה מתכנתו׃
12 Muyeso wa sekeli ukhale wokwanira magera makumi awiri. Muyeso wa mina ukhale wolemera masekeli 60.
והשקל עשרים גרה עשרים שקלים חמשה ועשרים שקלים עשרה וחמשה שקל המנה יהיה לכם׃
13 “‘Zopereka zomwe mudzidzapereka ndi izi: chimodzi mwa zigawo 60 za tirigu, barelenso chimodzimodzi ndiponso gawo limodzi la magawo asanu ndi limodzi la efa, kulitapa pa barele wa homeri.
זאת התרומה אשר תרימו ששית האיפה מחמר החטים וששיתם האיפה מחמר השערים׃
14 Gawo loyenera la mafuta, loyezedwa ndi bati, ndiponso chigawo mwa zigawo 100 za mafuta. Miyeso yake ili motere: mabati khumi afanana ndi homeri imodzi kapena kori imodzi.
וחק השמן הבת השמן מעשר הבת מן הכר עשרת הבתים חמר כי עשרת הבתים חמר׃
15 Muperekenso nkhosa imodzi pa gulu lankhosa 200 za pa msipu wabwino wa mu Israeli. Izi zidzagwiritsidwa ntchito monga nsembe za chakudya, nsembe zopsereza, ndi nsembe zachiyanjano ndi nsembe zopepesera milandu ya anthu. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
ושה אחת מן הצאן מן המאתים ממשקה ישראל למנחה ולעולה ולשלמים לכפר עליהם נאם אדני יהוה׃
16 Anthu onse a mʼdzikomo azidzapereka zimenezi kwa mfumu ya Israeli.
כל העם הארץ יהיו אל התרומה הזאת לנשיא בישראל׃
17 Udzakhala udindo wa mfumu kupereka zofunikira ku nsembe zopsereza, nsembe za chakudya, ndi nsembe za zakumwa pa nthawi ya zikondwerero, chikondwerero cha mwezi watsopano ndi cha masabata, nthawi yonse ya zikondwerero zoyikika za Aisraeli. Mfumuyo idzapereka nsembe zopepesera machimo, nsembe za chakudya, nsembe zopsereza, ndi nsembe zachiyanjano kuti zikhale nsembe zopepesera machimo a Aisraeli.
ועל הנשיא יהיה העולות והמנחה והנסך בחגים ובחדשים ובשבתות בכל מועדי בית ישראל הוא יעשה את החטאת ואת המנחה ואת העולה ואת השלמים לכפר בעד בית ישראל׃
18 “‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa tsiku loyamba la mwezi woyamba muzitenga mwana wangʼombe wamwamuna wopanda chilema ndi kuchita mwambo woyeretsa malo opatulika.
כה אמר אדני יהוה בראשון באחד לחדש תקח פר בן בקר תמים וחטאת את המקדש׃
19 Wansembe atengeko magazi a nsembe yopepesera machimoyo ndipo awapake pa mphuthu za Nyumba ya Mulungu, pa ngodya zinayi za pamwamba pa guwa lansembe ndi pa mphuthu za pa chipata cha bwalo la mʼkati.
ולקח הכהן מדם החטאת ונתן אל מזוזת הבית ואל ארבע פנות העזרה למזבח ועל מזוזת שער החצר הפנימית׃
20 Muzichita chimodzimodzi pa tsiku la chisanu ndi chiwiri la mwezi, kuchitira aliyense amene wachimwa mosafuna kapena mosadziwa. Motero Nyumba ya Mulungu idzakhala yoyera.
וכן תעשה בשבעה בחדש מאיש שגה ומפתי וכפרתם את הבית׃
21 “‘Pa tsiku la 14 la mwezi woyamba muzichita chikondwerero cha Paska, chikondwerero chake cha masiku asanu ndi awiri. Pa masiku amenewo muzidzadya buledi wopanda yisiti.
בראשון בארבעה עשר יום לחדש יהיה לכם הפסח חג שבעות ימים מצות יאכל׃
22 Pa tsiku loyamba la chikondwererocho, mfumu ipereke nsembe ya ngʼombe yayimuna monga nsembe yopepesera machimo ake ndi machimo a anthu onse a mʼdziko.
ועשה הנשיא ביום ההוא בעדו ובעד כל עם הארץ פר חטאת׃
23 Pa masiku asanu ndi awiri a chikondwererocho, mfumu ipereke kwa Yehova nsembe zopsereza izi: ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri, zonsezi zopanda chilema. Pa masikuwa mfumu iziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ngati nsembe yopepesera machimo.
ושבעת ימי החג יעשה עולה ליהוה שבעת פרים ושבעת אילים תמימם ליום שבעת הימים וחטאת שעיר עזים ליום׃
24 Pamodzi ndi ngʼombe iliyonse yayimuna ndi nkhosa iliyonse yayimuna, mfumu ipereke chopereka cha chakudya chokwanira efa imodzi ndiponso mafuta okwanira hini imodzi pa efa iliyonse.
ומנחה איפה לפר ואיפה לאיל יעשה ושמן הין לאיפה׃
25 “‘Pa nthawi ya chikondwerero cha masiku asanu ndi awiri, chimene chimayamba pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, mfumuyo iziperekanso nsembe za mtundu womwewo: nsembe zopepesera machimo, nsembe zopsereza, nsembe za chakudya ndi za mafuta.’”
בשביעי בחמשה עשר יום לחדש בחג יעשה כאלה שבעת הימים כחטאת כעלה וכמנחה וכשמן׃

< Ezekieli 45 >