< Ezekieli 44 >
1 Munthu uja anabwerera nane ku chipata chakunja kwa malo opatulika, chomwe chimayangʼana kummawa. Chipatacho chinali chotseka.
Et convertit me ad viam portae sanctuarii exterioris, quae respiciebat ad Orientem: et erat clausa.
2 Yehova anandiwuza kuti, “Chipata ichi chikhale chotseka, chisatsekulidwe. Wina asalowerepo chifukwa Yehova, Mulungu wa Israeli walowera pomwepa.
Et dixit Dominus ad me: Porta haec clausa erit: non aperietur, et vir non transibit per eam: quoniam Dominus Deus Israel ingressus est per eam, eritque clausa
3 Kalonga yekha angathe kukhala mʼmenemo ndi kumadya chakudya pamaso pa Yehova. Iye adzalowere pa njira ya ku khonde lamʼkati ndi kutulukiranso njira yomweyo.”
principi. Princeps ipse sedebit in ea, ut comedat panem coram Domino: per viam portae vestibuli ingredietur, et per viam eius egredietur.
4 Kenaka munthuyo anandidzeretsa pa chipata chakumpoto ndipo tinafika kumaso kwa Nyumba ya Mulungu. Nditapenyetsetsa ndinangoona ulemerero wa Yehova utadzaza mʼNyumba ya Mulungu, ndipo ndinadzigwetsa pansi chafufumimba.
Et adduxit me per viam portae Aquilonis in conspectu domus: et vidi, et ecce implevit gloria Domini domum Domini: et cecidi in faciem meam.
5 Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, samala bwino ndipo uyangʼanitsitse ndi kumvetsa bwino zonse zimene ndikuwuze zokhudza malamulo ndi malangizo a Nyumbayi. Usamalitse za amene angalowe ndi kutuluka mʼNyumbayi.
Et dixit ad me Dominus: Fili hominis pone cor tuum, et vide oculis tuis, et auribus tuis audi omnia, quae ego loquor ad te de universis ceremoniis domus Domini, et de cunctis legibus eius: et pones cor tuum in viis templi per omnes exitus sanctuarii.
6 Uwuze mtundu wopanduka wa Israeli kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: Inu Aisraeli, andikwana machitidwe anu onyansawo!
Et dices ad exasperantem me domum Israel: Haec dicit Dominus Deus: Sufficiant vobis omnia scelera vestra domus Israel:
7 Munalowetsa alendo osachita mdulidwe mu mtima ndi mʼthupi momwe mʼNyumba yanga ndipotu anayipitsa Nyumba yanga. Pamene inu munkandipatsa chakudya changa ndi magazi omwe kuwonjezera pa zonyansa zanu zonse ndiye kuti munaphwanya pangano langa.
eo quod inducitis filios alienos incircumcisos corde, et incircumcisos carne, ut sint in sanctuario meo, et polluant domum meam: et offertis panes meos, adipem, et sanguinem: et dissolvitis pactum meum in omnibus sceleribus vestris.
8 Mʼmalo moti muzisamalira zinthu zanga zopatulika, mwayika alendo kuti aziyangʼanira malo anga opatulika.
Et non servastis praecepta sanctuarii mei: et posuistis custodes observationum mearum in sanctuario meo vobismetipsis.
9 Ambuye Wamphamvuzonse akuti: Palibe mlendo wosachita mdulidwe mu mtima ndi mʼthupi ngakhalenso mlendo amene amakhala pakati pa Aisraeli amene adzalowe mʼmalo anga opatulika.
Haec dicit Dominus Deus: Omnis alienigena incircumcisus corde, et incircumcisus carne, non ingredietur sanctuarium meum, omnis filius alienus qui est in medio filiorum Israel.
10 “Ndiponso Alevi amene anandisiya kutali pa nthawi imene Israeli anasochera potsata mafano, adzalangidwa chifukwa cha tchimo lawo.
Sed et Levitae, qui longe recesserunt a me in errore filiorum Israel, et erraverunt a me post idola sua, et portaverunt iniquitatem suam:
11 Adzangokhala atumiki chabe mʼmalo anga opatulika. Azidzayangʼanira zipata za Nyumba ya Mulungu ndi kugwira ntchito kumeneko. Azidzapha nyama za nsembe zopsereza ndi za nsembe zina za anthu. Choncho azidzayimirira pamaso pa anthu nʼkumawatumikira.
erunt in sanctuario meo aeditui, et ianitores portarum domus, et ministri domus: ipsi mactabunt holocausta, et victimas populi: et ipsi stabunt in conspectu eorum, ut ministrent eis.
12 Iwowa ankatumikira anthu popembedza mafano awo, ndipo anachititsa Aisraeli kugwa mu uchimo. Nʼchifukwa chake Ine ndikulumbira kuti iwowa ayenera kulangidwa chifukwa cha machimo awo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
Pro eo quod ministraverunt illis in conspectu idolorum suorum, et facti sunt domui Israel in offendiculum iniquitatis: idcirco levavi manum meam super eos, ait Dominus Deus, et portabunt iniquitatem suam:
13 Iwo sayenera kufika pafupi ndi Ine ndi kunditumikira ngati ansembe, kapena kuyandikira chilichonse cha zinthu zanga zopatulika, kapenanso zopereka zanga zopatulika kwambiri. Iwo adzachititsidwa manyazi chifukwa cha machitidwe awo onyansa.
et non appropinquabunt ad me ut sacerdotio fungantur mihi, neque accedent ad omne sanctuarium meum iuxta sancta sanctorum: sed portabunt confusionem suam, et scelera sua quae fecerunt.
14 Komabe ndidzawayika kuti aziyangʼanira Nyumba yanga ndi kutumikira pa ntchito zake zonse zoyenera kuti zigwiridwe mʼmenemo.
Et dabo eos ianitores domus in omni ministerio eius, et in universis, quae fient in ea.
15 “Koma ansembe, a fuko la Levi, a banja la Zadoki amene ankatumikira mokhulupirika ku malo anga opatulika pa nthawi imene Aisraeli anasochera ndi kundisiya Ine; iwowa adzasendera kwa Ine kudzanditumikira. Adzafika pamaso panga kuti apereke nsembe za mafuta ndi magazi. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
Sacerdotes autem et Levitae filii Sadoc, qui custodierunt ceremonias sanctuarii mei, cum errarent filii Israel a me, ipsi accedent ad me ut ministrent mihi: et stabunt in conspectu meo ut offerant mihi adipem, et sanguinem, ait Dominus Deus.
16 Okhawa ndiwo adzalowe ku malo anga opatulika ndi kudzayandikira tebulo langa kuti adzanditumikire. Amenewa okha ndiwo adzasamalire zinthu zanga.
Ipsi ingredientur sanctuarium meum, et ipsi accedent ad mensam meam ut ministrent mihi, et custodiant ceremonias meas.
17 “Pamene alowa ku zipata za bwalo lamʼkati azivala zovala zabafuta. Asamavale chovala china chilichonse cha ubweya wankhosa pamene akutumikira pa zipata za bwalo la mʼkati kapena kunja kwa Nyumba ya Mulungu.
Cumque ingredientur portas atrii interioris, vestibus lineis induentur: nec ascendet super eos quidquam laneum, quando ministrant in portis atrii interioris et intrinsecus.
18 Azivala nduwira za bafuta ndi kabudula wabafuta mʼkati. Asavale chilichonse chowachititsa thukuta.
Vittae lineae erunt in capitibus eorum, et feminalia linea erunt in lumbis eorum, et non accingentur in sudore.
19 Pamene atuluka ndi kupita ku bwalo lakunja kumene kuli anthu, azivula zovala zimene amatumikira nazo, ndipo azisiye zovalazo mu zipinda zopatulika. Pambuyo pake avale zovala zina, kuopa kuti angapatsireko kuyera anthu enawo ndi zovala zawozo.
Cumque egredientur atrium exterius ad populum, exuent se vestimentis suis, in quibus ministraverant, et reponent ea in gazophylacio sanctuarii, et vestient se vestimentis aliis: et non sanctificabunt populum in vestibus suis.
20 “‘Ansembe asamamete mpala kapena kusunga tsitsi lalitali kwambiri, koma azingoliyepula.
Caput autem suum non radent, neque comam nutrient: sed tondentes attondent capita sua.
21 Wansembe asamwe vinyo pamene ali pafupi kulowa mʼbwalo la mʼkati.
Et vinum non bibet omnis sacerdos quando ingressurus est atrium interius.
22 Iwo asakwatire akazi amasiye kapena osudzulidwa; koma azikwatira anamwali osadziwa mwamuna a fuko la Israeli kapena akazi amasiye a ansembe anzawo.
Et viduam, et repudiatam non accipient uxores, sed virgines de semine domus Israel: sed et viduam, quae fuerit vidua a sacerdote, accipient.
23 Ansembe aziphunzitsa anthu anga kusiyanitsa pakati pa zinthu zopatulika ndi zinthu wamba, ndiponso pakati pa zinthu zoyenera ndi zosayenera kuperekedwa nsembe.
Et populum meum docebunt quid sit inter sanctum et pollutum, et inter mundum et immundum ostendent eis.
24 “‘Pakakhala milandu, ansembe azikhala oweruza ndipo agamule milanduyo potsata malamulo anga. Atsate malamulo anga ndi malangizo anga pa za masiku anga onse a chikondwerero. Asamalirenso kuti masiku anga a Sabata akhale oyera.
Et cum fuerit controversia, stabunt in iudiciis meis, et iudicabunt: leges meas, et praecepta mea in omnibus sollemnitatibus meis custodient, et Sabbata mea sanctificabunt.
25 “‘Wansembe asadziyipitse pokhudza munthu wakufa, pokhapokha ngati wakufayo ndi abambo ake kapena amayi ake, mwana wake wamwamuna kapena wamkazi, mʼbale wake kapena mlongo wake wosakwatiwa.
Et ad mortuum hominem non ingredientur, ne polluantur, nisi ad patrem et matrem, et filium et filiam, et fratrem et sororem, quae alterum virum non habuerit: in quibus contaminabuntur.
26 Atatha kuyeretsedwa adikirebe masiku asanu ndi awiri kuti ayere ndithu.
Et postquam fuerit emundatus, septem dies numerabuntur ei.
27 Pa tsiku lomwe akukalowa mʼbwalo la mʼkati la malo opatulika kuti akatumikire, apereke nsembe yopepesera machimo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
Et in die introitus sui in sanctuarium ad atrium interius ut ministret mihi in sanctuario, offeret pro peccato suo, ait Dominus Deus.
28 “‘Ansembe asadzakhale ndi cholowa chilichonse ayi. Cholowa chawo ndi Ine. Musadzawapatse chuma mu Israeli; Ine ndidzakhala chuma chawo.
Non erit autem eis hereditas, ego hereditas eorum: et possessionem non dabitis eis in Israel, ego enim possessio eorum.
29 Iwo azidzadya nsembe ya chakudya, nsembe yopereka chifukwa cha tchimo ndi nsembe yopepesera machimo. Zinthu zonse zoperekedwa kwa Yehova mu Israeli zidzakhala zawo.
Victimam et pro peccato et pro delicto ipsi comedent: et omne votum in Israel ipsorum erit.
30 Zabwino za zipatso zanu zoyambirira kucha ndiponso mphatso zanu zonse zapadera zidzakhala za ansembe. Inu muziwapatsa chigawo choyamba cha ufa wanu kuti pa nyumba panu pakhale madalitso.
Et primitiva omnium primogenitorum, et omnia libamenta ex omnibus, quae offeruntur, sacerdotum erunt: et primitiva ciborum vestrorum dabitis sacerdoti, ut reponat benedictionem domui suae.
31 Ansembe sayenera kudya kalikonse kofa kokha, kaya mbalame, kapena nyama. Kapena yochita kujiwa.’”
Omne morticinum, et captum a bestia de avibus et de pecoribus non comedent Sacerdotes.