< Ezekieli 43 >
1 Pambuyo pake munthuyo anapita nane ku chipinda choyangʼana kummawa,
Then he brought me to the gate, even to the gate that looketh toward the east.
2 ndipo ndinaona ulemerero wa Mulungu wa Israeli ukubwera kuchokera kummawa. Liwu lake linali ngati mkokomo wamadzi, ndipo dziko linawala ndi ulemerero wake.
And behold, the glory of the God of Israel came from the east; and the sound thereof was as the sound of great waters, and the earth shone with his glory.
3 Masomphenya amene ndinawaonawa anali ngati masomphenya amene ndinawaona pamene Yehova anabwera kudzawononga mzinda ndiponso ngati masomphenya amene ndinawaona ku mtsinje wa Kebara. Ndipo ndinadzigwetsa chafufumimba.
And the appearance was like the vision which I saw, like the vision which I saw when I came to destroy the city; it was a vision like the vision which I saw at the river Chebar. And I fell upon my face.
4 Ulemerero wa Yehova unalowa mʼNyumba ya Mulungu kudzera pa chipata choyangʼana kummawa.
And the glory of Jehovah came into the house by way of the gate, whose prospect was toward the east.
5 Tsono Mzimu unandinyamula nundilowetsa mʼbwalo lamʼkati, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza Nyumba ya Mulungu.
Then the spirit took me up and brought me into the inner court; and behold, the glory of Jehovah filled the house.
6 Munthuyo ali chiyimire pambali panga, ndinamva wina akundiyankhula kuchokera mʼNyumba ya Mulungu.
And I heard one speaking to me out of the house, and a man was standing by me.
7 Iye anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, awa ndi malo a mpando wanga waufumu, ndi malo opondapo mapazi anga. Pano ndiye pamene ndidzakhala pakati pa Aisraeli mpaka muyaya. Aisraeliwa kapena mafumu awo sadzayipitsa dzina langa popembedza milungu ina kapena poyika mitembo ya mafumu awo ku zitunda zachipembedzo.
And he said to me: Son of man, this is the place of my throne, and the place of the soles of my feet, where I will dwell in the midst of the sons of Israel forever; and the house of Israel shall no more pollute my holy name, neither they nor their kings, by their fornication, and by the dead bodies of their kings in their sepulchres;
8 Ankamanga chiwundo chawo pafupi ndi chiwundo changa, ndiponso mphuthu zawo pafupi ndi mphuthu zanga, nʼkungokhala khoma chabe pakati pa iwowo ndi Ine. Motero anayipitsa dzina langa loyera ndi machitidwe awo onyansa. Choncho Ine ndinawawononga ndili wokwiya.
in that they set their threshold by my threshold, and their post near my post, so that there was only a wall between me and them, and defiled my holy name by the abominations which they committed; wherefore I have consumed them in my anger.
9 Tsopano alekeretu kupembedza milungu ina ndipo achotseretu mitembo ya mafumu awo, isakhale pafupi ndi Ine, ndipo Ine ndidzakhala pakati pawo mpaka muyaya.
Now let them remove far away from me their fornication, and the carcasses of their kings; and I will dwell in the midst of them forever.
10 “Iwe mwana wa munthu, awuze Aisraeliwa za Nyumba ya Mulunguyi, mamangidwe ake ndipo achite manyazi ndi machimo awo,
And thou, son of man, show this house to the house of Israel, that they may be ashamed of their iniquities, and that they may measure the pattern.
11 akachita manyazi ndi zoyipa zonse anachita, uwafotokozera za Nyumba ya Mulungu, mamangidwe ake, makomo ake otulukira ndi makomo olowera, ndiye kuti, mamangidwe ake onse. Uwafotokozerenso malangizo ndi malamulo ake. Uwalembe akuona kuti athe kuwasunga ndi kuwachita.
And if they be ashamed of all which they have done, let them know the form of the house and the fashion thereof, and the passages for going out and coming in, and all the forms thereof, and all the statutes thereof, and all the laws thereof, and write it in their sight, that they may keep the whole form thereof, and all the statutes thereof, and do them.
12 “Limeneli ndi lamulo la Nyumba ya Mulungu imene idzamangidwe pamwamba pa phiri. Malo ake onse ozungulira adzakhala oyera kwambiri. Limeneli ndilo lamulo la Nyumba ya Mulungu.
This is the law of the house. Upon the top of the mountain, all within its limits shall be most holy. Behold, this is the law of the house.
13 “Miyeso ya guwa lansembe ndi iyi: Pa tsinde pake padzakhala ngalande ya masentimita makumi asanu kuzama kwake ndi mulifupi mwake. Mʼphepete mwa ngalandeyo kuzungulira guwa lonse, mudzakhala mkombero wa masentimita 25.
And these are the measures of the altar by cubits; each cubit being a cubit and a hand-breadth. The bottom shall be a cubit high and a cubit broad; and the border thereof, by the edge thereof round about, shall be a span; and this shall be the outer part of the altar.
14 Kuchokera mʼngalande ya pansi padzakhala mpaka pa phaka lapansi mita imodzi, mulifupi mwake theka la mita. Kuchokera pa phaka lalingʼono mpaka pa phaka lalikulu, msinkhu wake ndi mamita awiri, mulifupi mwake ndi masentimita makumi asanu.
And from the bottom upon the ground to the lower ledge shall be two cubits, and the breadth one cubit; and from the lesser ledge to the greater ledge shall be four cubits, and the breadth a cubit.
15 Malo osonkhapo moto pa guwa, msinkhu wake udzakhala mamita awiri. Pa ngodya iliyonse ya malo osonkhapo motowo panatuluka nyanga imodzi.
And the altar shall be four cubits; and from the altar upward shall be four horns.
16 Malo osankhalapo moto pa guwa lansembe miyeso yake ndi yofanana mbali zonse. Mulitali mwake mudzakhala mamita asanu ndi limodzi ndipo mulifupi mwake mudzakhalanso mamita asanu ndi limodzi.
And the altar shall be twelve cubits long by twelve broad; square on the four sides thereof.
17 Phaka lapamwamba muyeso wake udzakhala wofanana mbali zonse. Mulitali mudzakhala mamita asanu ndi awiri ndiponso mulifupi mwake mudzakhalanso mamita asanu ndi awiri. Mkombero wake udzakhala wa masentimita 25 ndiponso ngalande yake yozungulira idzakhala ya masentimita 25. Makwerero a guwa lansembe adzayangʼana kummawa.”
And the ledge shall be fourteen cubits long by fourteen broad on the four sides thereof; and the border about it shall be half a cubit; and the bottom thereof shall be a cubit round about; and its steps shall look toward the east.
18 Kenaka munthuyo anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, Ambuye Yehova akuti: Guwalo litamangidwa, tsono malamulo awa azidzatsatidwa popereka nsembe zopsereza ndiponso powaza magazi pa guwapo.
And he said to me, Son of man, thus saith the Lord Jehovah: These are the statutes of the altar, in the day when it is made, to offer burnt-offerings thereon, and to sprinkle blood thereon.
19 Udzawapatse ansembe, omwe ndi Alevi, a banja la Zadoki, amene amabwera pafupi nane kudzanditumikira, mwana wangʼombe wamwamuna kuti aperekere nsembe yopepesera machimo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
To the priests, the sons of Levi, of the race of Zadok, that come near to me, saith the Lord Jehovah, to minister to me, thou shalt give a young bullock for a sin-offering.
20 Udzatengeko magazi ake ena ndi kuwapaka pa nyanga zinayi za pa guwa lansembe, pa ngodya zinayi za phaka ndiponso mozungulira mkombero wonse. Motero udzaliyeretsa ndi kulipatula.
And thou shalt take of the blood thereof, and put it on its four horns, and on the four corners of the ledge, and on the border round about, and thus cleanse and purge it.
21 Udzatenge ngʼombe yayimuna yomwe yaperekedwa ngati nsembe yopepesera machimo, ndipo udzayiwotche pa malo ake enieni mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu, kunja kwa malo opatulika.
And thou shalt take the bullock of the sin-offering, and it shall be burned in the appointed place of the house, without the sanctuary.
22 “Mmawa mwake udzatenge mbuzi yopanda chilema kuti nayonso iperekedwe ngati nsembe yopepesera machimo. Pambuyo pake idzayeretse guwa lansembe monga unachitira ndi ngʼombe yayimuna ija.
And on the second day thou shalt offer a he-goat without blemish for a sin-offering; and they shall cleanse the altar, as they cleansed it with the bullock.
23 Utatha kuyeretsa guwa lansembelo, udzatenge mwana wangʼombe wamwamuna wopanda chilema ndiponso nkhosa yayimuna yopanda chilema.
And when thou hast made an end of cleansing it, thou shalt offer a young bullock without blemish, and a ram out of the flock without blemish.
24 Udzapereke zonsezi pamaso pa Yehova, ndipo ansembe adzazithire mchere ndi kuzipereka kuti zikhale nsembe zopsereza kwa Yehova.
And thou shalt offer them before Jehovah, and the priests shall cast salt upon them, and offer them up for a burnt-offering to Jehovah.
25 “Kwa masiku asanu ndi awiri, uzidzapereka tsiku ndi tsiku mbuzi yayimuna, mwana wangʼombe, ndiponso nkhosa kuti zikhale nsembe zopepesera machimo. Zonsezi zidzakhale zopanda chilema.
Seven days shalt thou sacrifice daily a goat for a sin-offering; they shall also sacrifice a young bullock, and a ram out of the flock without blemish.
26 Kwa masiku asanu ndi awiriwo ansembe adzachite mwambo woyeretsa ndi kupatula guwa lansembelo.
Seven days shall they purge the altar, and purify it, and consecrate themselves.
27 Masiku amenewa atatha, kuyambira tsiku lachisanu ndi chitatu, ansembe azipereka nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pa guwa lansembe. Apo ndidzakulandirani. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”
And when they have finished these days, it shall be that on the eighth day and forward the priests shall present your burnt-offerings and your thank-offerings upon the altar, and I will accept you, saith the Lord Jehovah.