< Ezekieli 41 >

1 Ndipo munthuyo anapita nane mʼchipinda chopatulika cha Nyumba ya Mulungu ndipo anayeza khonde lake; mulifupi mwa khondelo munali mamita atatu mbali iliyonse kutalika kwake.
ויביאני אל ההיכל וימד את האילים שש אמות רחב מפו ושש אמות רחב מפו רחב האהל׃
2 Mulifupi mwa khomo munali motalika mamita asanu. Makoma a mbali zonse anali a mamita awiri ndi theka mulifupi mwake. Anayezanso kutalika kwa chipinda chopatulika chija ndipo mulitali mwake munali motalika mamita makumi awiri ndi mulifupi mwake munali mamita khumi.
ורחב הפתח עשר אמות וכתפות הפתח חמש אמות מפו וחמש אמות מפו וימד ארכו ארבעים אמה ורחב עשרים אמה׃
3 Kenaka munthuyo anakalowa mʼkati ndipo anayeza khonde la pa khomo; khondelo linali mita imodzi mulifupi mwake. Mulifupi mwa khondelo munali mamita atatu.
ובא לפנימה וימד איל הפתח שתים אמות והפתח שש אמות ורחב הפתח שבע אמות׃
4 Ndiponso anayeza kutalika kwa chipinda chopatulika chenichenicho. Mulitali mwake munali mamita khumi, ndipo mulifupi mwake munali mamita khumi. Munthuyo anandiwuza kuti, “Ichi ndicho chipinda chopatulika kwambiri.”
וימד את ארכו עשרים אמה ורחב עשרים אמה אל פני ההיכל ויאמר אלי זה קדש הקדשים׃
5 Tsono munthuyo anayeza khoma la Nyumba ya Mulungu; kuchindikira kwake kunali mamita atatu. Panalinso zipinda zina kuzungulira Nyumba ya Mulungu ndipo chilichonse chinali cha mamita awiri mulifupi wake.
וימד קיר הבית שש אמות ורחב הצלע ארבע אמות סביב סביב לבית סביב׃
6 Zipindazo zinali zitatu zosanjikizana. Chigawo chilichonse chinali ndi zipinda makumi atatu. Pa makoma a Nyumba ya Mulungu panali zochirikiza zipindazo kuti zisatsamire khoma la Nyumba ya Mulungu.
והצלעות צלע אל צלע שלוש ושלשים פעמים ובאות בקיר אשר לבית לצלעות סביב סביב להיות אחוזים ולא יהיו אחוזים בקיר הבית׃
7 Zipinda za mʼmbalizo zinkapita zikulirakulira pomakwera chipinda ndi chipinda potsata kukulirakulira kwa zochirikiza za zipinda zija. Pambali pa Nyumba ya Mulungu panali makwerero okwerera pamwamba, kuchokera chigawo chapansi kudzera chapakati, mpaka kukafika pamwamba.
ורחבה ונסבה למעלה למעלה לצלעות כי מוסב הבית למעלה למעלה סביב סביב לבית על כן רחב לבית למעלה וכן התחתונה יעלה על העליונה לתיכונה׃
8 Ndinaona chiwundo kuzungulira Nyumba ya Mulungu. Chinapanga maziko a zipindazo ndipo chinali cha mamita atatu.
וראיתי לבית גבה סביב סביב מיסדות הצלעות מלו הקנה שש אמות אצילה׃
9 Khoma lakunja la zipindazo linali la mamita awiri ndi theka kuchindikira kwake. Pakati pa chiwundocho
רחב הקיר אשר לצלע אל החוץ חמש אמות ואשר מנח בית צלעות אשר לבית׃
10 ndi zipinda za Nyumba ya Mulungu panali bwalo limeneli la mamita khumi kupingasa kwake kuzungulira Nyumba yonse ya Mulungu.
ובין הלשכות רחב עשרים אמה סביב לבית סביב סביב׃
11 Zitseko za zipinda zamʼmbalizo zinali zotsekulira ku chiwundo. Chitseko chimodzi chinkayangʼana kumpoto ndipo china chinkayangʼana kummwera. Chiwundo chosamangapo kanthu chinali mamita awiri ndi theka kukula kwake kuzungulira ponseponse.
ופתח הצלע למנח פתח אחד דרך הצפון ופתח אחד לדרום ורחב מקום המנח חמש אמות סביב סביב׃
12 Nyumba imene inali chakummwera moyangʼanana ndi bwalo la Nyumba ya Mulungu inali mamita 35 mulifupi mwake. Khoma la nyumbayo linali mamita awiri ndi theka kuchindikira kwake kuzungulira ponseponse, ndipo mulitali mwake linali mamita 45.
והבנין אשר אל פני הגזרה פאת דרך הים רחב שבעים אמה וקיר הבנין חמש אמות רחב סביב סביב וארכו תשעים אמה׃
13 Ndipo munthuyo anayeza Nyumba ya Mulungu ndipo mulitali mwake inali mamita makumi asanu. Nyumbayo ndi makoma ake, zonse zinali za mamita makumi asanu.
ומדד את הבית ארך מאה אמה והגזרה והבניה וקירותיה ארך מאה אמה׃
14 Kumaso kwa Nyumba ya Mulungu chakummawa kwa bwalolo mulifupi mwake munali mamita makumi asanu.
ורחב פני הבית והגזרה לקדים מאה אמה׃
15 Kenaka anayeza kutalika kwa nyumba yoyangʼanana ndi bwalo chakumadzulo kwa Nyumba ya Mulungu, kuphatikizapo njira zamʼkati ku mbali iliyonse. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu. Chipinda chachikulu cha Nyumba ya Mulungu, chimene chili chamʼkati, khonde lamʼkati loyangʼanana ndi bwalo,
ומדד ארך הבנין אל פני הגזרה אשר על אחריה ואתוקיהא מפו ומפו מאה אמה וההיכל הפנימי ואלמי החצר׃
16 mazenera ndi maferemu ake, zonsezi zinali zokutidwa ndi matabwa. Pamwamba moyangʼanana ndi chiwundo, Nyumba ya Mulungu inakutidwa ndi matabwa kuyambira pansi mpaka ku mazenera, (mazenerawo anali okutidwa),
הספים והחלונים האטמות והאתיקים סביב לשלשתם נגד הסף שחיף עץ סביב סביב והארץ עד החלנות והחלנות מכסות׃
17 pamwamba pa khomo lolowera ku malo opatulika amʼkati komanso kuzungulira makoma onse kunja ndi mʼkati,
על מעל הפתח ועד הבית הפנימי ולחוץ ואל כל הקיר סביב סביב בפנימי ובחיצון מדות׃
18 anajambulapo zithunzi za kerubi mmodzi atakhala pakati pa kanjedza muwiri. Kerubi aliyense anali ndi nkhope ziwiri:
ועשוי כרובים ותמרים ותמרה בין כרוב לכרוב ושנים פנים לכרוב׃
19 imodzi inali nkhope ya munthu yoyangʼana kanjedza mbali imodzi, ndi ina inali nkhope ya mkango yoyangʼana kanjedza mbali ina. Zinajambulidwa kuzungulira Nyumba ya Mulungu yonse.
ופני אדם אל התמרה מפו ופני כפיר אל התמרה מפו עשוי אל כל הבית סביב סביב׃
20 Motero kuyambira pansi mpaka pamwamba pa khomo komanso pa makoma onse a chipinda chachikulu cha Nyumba ya Mulungu, anajambula zithunzi za akerubi ndi kanjedza pa makoma onse a malo opatulika.
מהארץ עד מעל הפתח הכרובים והתמרים עשוים וקיר ההיכל׃
21 Mphuthu za chipinda chachikulu cha Nyumba ya Mulungu kutalika kwake mbali zonse kunali kofanana. Ndipo kumaso kwa malo opatulika kunali chinthu china chooneka ngati
ההיכל מזוזת רבעה ופני הקדש המראה כמראה׃
22 guwa lansembe la matabwa. Msinkhu wake unali mita imodzi ndi theka, mulitali mwake munali mita imodzi, mulifupi mwake munalinso mita imodzi. Mphuthu zake, tsinde lake ndi mbali zonse zinali za matabwa. Munthuyo anandiwuza kuti, “Tebulo limeneli ndilo limakhala pamaso pa Yehova.”
המזבח עץ שלוש אמות גבה וארכו שתים אמות ומקצעותיו לו וארכו וקירתיו עץ וידבר אלי זה השלחן אשר לפני יהוה׃
23 Chipinda chachikulu chija chinali ndi zitseko ziwiri. Malo opatulika aja analinso ndi zitseko ziwiri.
ושתים דלתות להיכל ולקדש׃
24 Chitseko chilichonse chinali ndi zigawo ziwiri zopatukana.
ושתים דלתות לדלתות שתים מוסבות דלתות שתים לדלת אחת ושתי דלתות לאחרת׃
25 Ndipo pa zitsekopo anajambulipo zithunzi za akerubi ndi kanjedza monga zomwe anajambulapo pa makoma. Kunja kwake kunali ngati denga lamatabwa pamwamba pa khonde lamʼkati.
ועשויה אליהן אל דלתות ההיכל כרובים ותמרים כאשר עשוים לקירות ועב עץ אל פני האולם מהחוץ׃
26 Pa mbali zonse za khonde lamʼkatilo panali mazenera, ndipo pa makoma ake onse anajambulapo zithunzi za kanjedza.
וחלונים אטמות ותמרים מפו ומפו אל כתפות האולם וצלעות הבית והעבים׃

< Ezekieli 41 >