< Ezekieli 39 >

1 “Iwe mwana wa munthu, nenera modzudzula Gogi ndi kumuwuza kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: ‘Ine ndikudana nawe, iwe Gogi, kalonga wamkulu wa Mesaki ndi Tubala.
人の子よゴグにむかひ預言して言へ主ヱホバかく言たまふロシ、メセク、トバルの君ゴグよ視よ我汝を罰せん
2 Ine ndidzakuzunguza ndi kukupirikitsira kutsogolo. Ndidzakutenga kuchokera kutali kumpoto ndi kukutumiza kuti ukalimbane ndi anthu a ku mapiri a Israeli.
我汝をひきもどし汝をみちびき汝をして北の極より上りてイスラエルの山々にいたらしめ
3 Kenaka Ine ndidzathyola uta wa mʼdzanja lako lamanzere ndipo ndidzagwetsa mivi ya mʼdzanja lako lamanja.
汝の左の手より弓をうち落し右の手より矢を落しむべし
4 Udzagwa ku mapiri a ku Israeli, iwe ndi magulu ako onse ankhondo ndiponso mitundu ya anthu imene ili nawe. Ndidzakusandutsa chakudya cha mitundu yonse ya mbalame zodya nyama, ndiponso cha zirombo zakuthengo.
汝と汝の諸の軍勢および汝とともなる民はイスラエルの山々に仆れん我汝を諸の類の鷙鳥と野の獣にあたへて食しむべし
5 Udzafera pa mtetete kuthengo, pakuti Ine ndayankhula. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
汝は野の表面に仆れん我これを言ばなりと主ヱホバ言たまふ
6 Ndidzatumiza moto pa Magogi ndi pa onse amene amakhala mwamtendere mʼmbali mwa nyanja. Choncho adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’
我マゴグと島々に安然に住る者とに火をおくり彼らをして我のヱホバなるを知しめん
7 “Ndidzachititsa kuti dzina langa loyera lidziwike pakati pa anthu anga Israeli. Sindidzalola kuti dzina langa liyipitsidwenso, ndipo mitundu ya anthu idzadziwa kuti Ine Yehova ndine Woyera mu Israeli.
我わが聖き名をわが民イスラエルの中に知しめ重てわが聖き名を汚さしめじ國々の民すなはち我がヱホバにしてイスラエルにありて聖者なることを知るにいたらん
8 Zikubwera! Ndipo zidzachitikadi, ndikutero Ine Ambuye Yehova. Ndiye tsiku limene ndinanena lija.
主ヱホバいひたまふ視よ是は來れり成れり是わが言る日なり
9 “Pamenepo okhala mʼmizinda ya Israeli adzatuluka ndipo adzasonkhanitsa zida zankhondo kuti zikhale nkhuni ndipo adzazitentha; zishango ndi lihawo, mauta ndi mivi, zibonga za nkhondo ndi mikondo. Adzazisonkhera moto kwa zaka zisanu ndi ziwiri.
茲にイスラエルの邑々に住る者出きたり甲冑 大楯 小楯 弓 矢 手鎗 手矛および槍を燃し焚き之をもて七年のあひだ火を燃さん
10 Iwo sadzatolera nkhuni kuthengo kapena kukadula ku nkhalango, chifukwa adzasonkhera moto zidazo. Ndipo iwo adzafunkha amene anawafunkhawo, ndi kulanda chuma cha amene anawalanda, ndikutero Ine Ambuye Yehova.
彼ら野より木をとりきたること無く林より木をきりとらずして甲冑をもて火を燃しまた己を掠めし者をかすめ己の物を奪ひし者の物を奪はん主ヱホバこれを言ふ
11 “Pa tsiku limenelo ndidzamupatsa Gogi manda mu Israeli, mʼchigwa cha apaulendo, kummawa kwa Nyanja Yakufa. Mandawo adzatseka njira ya apaulendo, chifukwa Gogi ndi gulu lake lankhondo adzayikidwa kumeneko. Ndipo chigwacho chidzatchedwa chigwa cha gulu lankhondo la Gogi.
其日に我イスラエルにおいて墓地をゴグに與へん是往來の人の谷にして海の東にあり是往來の人を礙げん其處に人ゴグとその群衆を埋めこれをゴグの群衆の谷となづけん
12 “Nyumba ya Israeli idzakhala ikukwirira mitembo kwa miyezi isanu ndi iwiri ndi cholinga choyeretsa dziko.
イスラエルの家之を埋めて地を淸むるに七月を費さん
13 Anthu onse a mʼdzikomo adzakwirira nawo mitembo. Ntchito imeneyo adzatchuka nayo pa tsiku limene ndidzaonetsa ulemerero wanga. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
國の民みなこれを埋め之によりて名をえん是我が榮光をあらはす日なり
14 “Patapita miyezi isanu ndi iwiri adzalemba ntchito anthu ena odzayenda mʼdziko lonse kufunafuna mitembo imene inatsalira nʼkumayikwirira. Choncho adzayeretseratu dzikolo.
彼等定れる人を選む其人國の中をゆきめぐりて往來の人とともにかの地の面に遺れる者を埋めてこれを淸む七月の終れる後かれら尋ぬることをなさん
15 Poyenda mʼdzikomo azidzati akaona fupa la munthu azidzayikapo chizindikiro pambali pake mpaka okumba manda atakalikwirira fupalo ku chigwa cha gulu lankhondo la Gogi.
國を行巡る者往來し人の骨あるを見るときはその傍に標をたつれば死人を埋むる者これをゴグの群衆の谷に埋む
16 (Komwekonso kudzakhala mzinda wotchedwa Gulu la nkhondo). Ndipo potero adzayeretsa dziko.
邑の名もまた群衆ととなへられん斯かれら國を淸めん
17 “Tsono iwe mwana wa munthu, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Itana mbalame za mitundu yonse ndi zirombo zonse zakuthengo ndipo uziwuze kuti, ‘Sonkhanani ndipo bwerani kuchokera ku mbali zonse ku nsembe imene ndikukonzerani inu, nsembe yayikulu pa mapiri a Israeli. Kumeneko inu mudzadya mnofu ndi kumwa magazi.
人の子よ主ヱホバかく言ふ汝諸の類の鳥と野の諸の獸に言べし汝等集ひ來り我が汝らのために殺せるところの犧牲に四方より聚れ即ちイスラエルの山々の上なる大なる犠牲に臨み肉を食ひ血を飮め
18 Mudzadya mnofu wa anthu ankhondo amphamvu ndi kumwa magazi a akalonga a dziko lapansi. Onsewo anaphedwa ngati nkhosa zazimuna, ana ankhosa onenepa, mbuzi ndiponso ngati ngʼombe zazimuna zonenepa za ku Basani.
汝ら勇士の肉を食ひ地の君等の血を飮め 牡羊 羔羊 牡山羊 牡牛など凡てバシヤンの肥たる畜を食ヘ
19 Ku phwando lansembe limene ndikukonzera inulo, mudzadya zonona mpaka kukhuta ndi kumwa magazi mpaka kuledzera.
汝らわが汝らのために殺せるところの犠牲につきて飽まで脂を食ひ醉まで血を飮べし
20 Pa tebulo langa mudzakhuta pakudya akavalo ndi okwerapo ake, anthu amphamvu ndi asilikali amitundumitundu,’ ndikutero Ine Ambuye Yehova.
汝らわが席につきて馬と騎者と勇士と諸の軍人に黶べしと主ヱホバいひたまふ
21 “Ine ndidzaonetsa ulemerero wanga pakati pa anthu a mitundu ina, ndipo adzaona mmene ndidzawalangire ndikadzayika dzanja langa pa iwo.
我わが榮光を國々の民にしめさん國々の民みな我がおこなふ審判を見我がかれらの上に加ふる手を見るべし
22 Kuyambira tsiku limenelo mpaka mʼtsogolo Aisraeli adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo.
是日より後イスラエルの家我ヱホバの己の神なることを知ん
23 Ndipo anthu a mitundu ina adzadziwa kuti anthu a Israeli anatengedwa ukapolo chifukwa cha tchimo lawo, chifukwa anali osakhulupirika kwa Ine. Choncho Ine ndinawabisira nkhope yanga ndi kuwapereka kwa adani awo. Motero anaphedwa pa nkhondo.
又國々の民イスラエルの家の擄へうつされしは其惡によりしなるを知べし彼等われに背きたるに因て我わが面を彼らに隱し彼らをその敵の手に付したれば皆劍に仆れたり
24 Ndinawachita zimenezi chifukwa cha kunyansa kwawo ndi zolakwa zawo, ndipo ndinawabisira nkhope yanga.
我かれらの汚穢と愆惡とにしたがひて彼らを待ひわが面を彼等に隱せり
25 “Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Tsopano ndidzakhazikanso pa bwino banja la Yakobo. Ndidzachitira chifundo Aisraeli onse, ndipo ndidzateteza dzina langa loyera.
然ば主ヱホバかく言たまふ我今ヤコブの俘擄人を歸しイスラエルの全家を憐れみ吾聖き名のために熱中せん
26 Anthuwo akadzakhala mwamtendere mʼdziko lawo popanda wina wowaopseza, pamenepo adzayiwala zamanyazi zawo zimene zinawachitikira chifukwa chosandikhulupirira Ine.
彼らその地に安然に住ひて誰も之を怖れしむる者なきに至る時はその我にむかひて爲たるところの諸の悖れる行爲のために愧べし
27 Ndidzawabwezeranso kwawo kuchokera pakati pa anthu a mitundu ina ndipo ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku mayiko a adani awo. Poteropo ndidzaonetsa pamaso pa anthu a mitundu yambiri kuti ndine Woyera.
我かれらを國々より導きかへりその敵の國々より集め彼らをもて我の聖き事を衆多の國民にしめす時
28 Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo, ngakhale kuti ndinawapereka ku ukapolo pakati pa anthu a mitundu ina. Ine ndidzawasonkhanitsanso ku dziko lawo osasiyako wina mʼmbuyo.
彼等すなはち我ヱホバの己の神なるを知ん是は我かれらを國々に移し又その地にひき歸りて一人をも其處にのこさざればなり
29 Ine sindidzawabisiranso nkhope yanga, pakuti ndidzathira Mzimu wanga pa Aisraeli. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”
我わが靈をイスラエルの家にそそぎたれば重て吾面を彼らに隱さじ主ヱホバこれを言ふ

< Ezekieli 39 >