< Ezekieli 38 >

1 Yehova anandiyankhula kuti:
Et factus est sermo Domini ad me, dicens:
2 “Iwe mwana wa munthu, tembenukira kwa Gogi, wa ku dziko la Magogi, amene ali kalonga wamkulu wa mzinda wa Mesaki ndi Tubala. Umuyimbe mlandu.
Fili hominis pone faciem tuam contra Gog, et terram Magog, principem capitis Mosoch, et Thubal: et vaticinare de eo,
3 Umuwuze mawu a Ine Ambuye Yehova akuti, ‘Ine ndikudana nawe, iwe Gogi, kalonga wamkulu wa ku Mesaki ndi Tubala.
et dices ad eum: Haec dicit Dominus Deus: Ecce ego ad te Gog principem capitis Mosoch et Thubal,
4 Ndidzakuzunguza, ndidzakukola ndi mbedza mʼkamwa mwako. Ndidzakutulutsa iweyo pamodzi ndi gulu lako lonse la nkhondo, akavalo ako ndi okwerapo ake. Onse adzakhala atanyamula zida za nkhondo, zishango ndi malihawo ndipo malupanga awo adzakhala osolola.
et circumagam te, et ponam frenum in maxillis tuis: et educam te, et omnem exercitum tuum, equos et equites vestitos loricis universos, multitudinem magnam, hastam et clypeum arripientium et gladium.
5 Pamodzi ndi iwowo, padzakhalanso ankhondo a ku Perisiya, ku Kusi, ndi ku Puti. Onsewa adzakhala atanyamula zishango ndi kuvala zipewa zankhondo.
Persae, Aethiopes, et Libyes cum eis, omnes scutati et galeati.
6 Padzakhalanso Gomeri pamodzi ndi ankhondo ake onse ndiponso banja la Togarima ndi gulu lake lonse lankhondo lochokera kutali kumpoto. Padzakhaladi mitundu yambiri ya anthu pamodzi ndi iwe.
Gomer, et universa agmina eius, domus Thogorma, latera Aquilonis, et totum robur eius, populique multi tecum.
7 “‘Konzekani! Mukhaledi okonzeka, iweyo pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo limene lakusonkhanira. Iweyo udzawatsogolera pokamenya nkhondo.
Praepara, et instrue te, et omnem multitudinem tuam, quae coacervata est ad te: et esto eis in praeceptum.
8 Pakapita masiku ambiri ndidzakuyitana. Zaka zikubwerazi ndidzakulowetsa mʼdziko limene lapulumuka ku nkhondo. Anthu ake anasonkhanitsidwa kuchokera ku mitundu ya anthu ambiri nʼkukakhazikika pa mapiri a Israeli amene kwa nthawi yayitali anali ngati chipululu. Anthu onsewa tsopano akukhala mwa mtendere.
Post dies multos visitaberis: in novissimo annorum venies ad terram, quae reversa est a gladio, et congregata est de populis multis ad montes Israel, qui fuerunt deserti iugiter: haec de populis educta est, et habitabunt in ea confidenter universi.
9 Tsono iwe pamodzi ndi ankhondo ako onse ndiponso mitundu yambiri ya anthu imene ili nawe mudzabwera ngati mphepo yamkuntho. Mudzaphimba dziko lonse ngati mitambo.
Ascendens autem quasi tempestas venies, et quasi nubes, ut operias terram tu, et omnia agmina tua, et populi multi tecum.
10 “Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa tsiku limenelo mu mtima mwako mudzabwera maganizo ofuna kukonzekera kuchita zoyipa.
Haec dicit Dominus Deus: In die illa ascendent sermones super cor tuum, et cogitabis cogitationem pessimam:
11 Iwe udzanena kuti, ‘Ndikukathira nkhondo dziko la midzi yopanda mipanda; ndikathira nkhondo anthu okhala mwamtendere, anthu amene satchinjirizidwa ndi mipanda, zipata kapena mipiringidzo.
et dices: Ascendam ad terram absque muro: veniam ad quiescentes, habitantesque secure: hi omnes habitant sine muro, vectes, et portae non sunt eis:
12 Ndipita kukalanda chuma chawo ndi kukafunkha zinthu zawo. Ndidzalimbana ndi midzi imene kale inali mabwinja. Ndikathira nkhondo anthu amene anasonkhanitsidwa kuchokera kwa anthu a mitundu ina. Iwowa ali ndi ziweto zambiri, katundu wochuluka ndiponso amakhala pakatikati pa dziko lapansi.’
Ut diripias spolia, et invadas praedam, ut inferas manum tuam super eos, qui deserti fuerant, et postea restituti, et super populum, qui est congregatus ex Gentibus, qui possidere coepit, et esse habitator umbilici terrae.
13 Anthu a ku Seba, a ku Dedani ndiponso amalonda a ku Tarisisi pamodzi ndi midzi yake yonse adzakufunsa kuti, ‘Kodi wabwera kudzafunkha? Kodi wasonkhanitsa gulu lako la nkhondo kudzalanda chuma, kudzatenga siliva ndi golide, ziweto ndi katundu kuti zikhale zofunkha zochuluka?’”
Saba, et Dedan, et negotiatores Tharsis, et omnes leones eius dicent tibi: Numquid ad sumenda spolia tu venis? ecce ad diripiendam praedam congregasti multitudinem tuam, ut tollas argentum, et aurum, et auferas supellectilem, atque substantiam, et diripias manubias infinitas.
14 “Nʼchifukwa chake, iwe mwana wa munthu, nenera ndipo uwuze Gogi kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa nthawi imene anthu anga adzakhala pa mtendere, iwe udzanyamuka.
Propterea vaticinare fili hominis, et dices ad Gog: Haec dicit Dominus Deus: Numquid non in die illo, cum habitaverit populus meus Israel confidenter, scies?
15 Udzabwera kuchokera ku dziko lako kutali kumpoto, iwe pamodzi ndi mitundu yambiri ya anthu imene ili nawe, onse okwera akavalo, gulu lankhondo lalikulu ndi lamphamvu.
Et venies de loco tuo a lateribus Aquilonis tu et populi multi tecum ascensores equorum universi, coetus magnus, et exercitus vehemens.
16 Udzabwera kudzalimbana ndi anthu anga Aisraeli ngati mtambo wophimba dziko. Masiku amenewo, iwe Gogi, ndidzabwera nawe kuti ulimbane ndi dziko langa, kuti anthu a mitundu ina andidziwe Ine, pamene ndidzaonetsa kuyera kwanga pa zimene ndidzakuchite iweyo.
Et ascendes super populum meum Israel quasi nubes, ut operias terram. In novissimis diebus eris, et adducam te super terram meam: ut sciant Gentes me, cum sanctificatus fuero in te in oculis eorum, o Gog.
17 “‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Kodi iwe si amene ndinayankhula za iwe masiku amakedzana kudzera mwa atumiki anga aneneri a Israeli? Pa zaka zambiri iwo ankalengeza kuti ndidzawutsa iwe kuti udzalimbane ndi Israeli.
Haec dicit Dominus Deus: Tu ergo ille es, de quo locutus sum in diebus antiquis in manu servorum meorum prophetarum Israel, qui prophetaverunt in diebus illorum temporum, ut adducerem te super eos.
18 Zimene chidzachitika pa tsiku limenelo ndi izi: Gogi akadzathira nkhondo dziko la Israeli, mkwiyo wanga woopsa udzayaka. Ndikutero Ine Ambuye Wamphamvuzonse.
Et erit in die illa, in die adventus Gog super terram Israel, ait Dominus Deus, ascendet indignatio mea in furore meo.
19 Chifukwa cha mkwiyo ndi ukali wanga woyakawo Ine ndikunenetsa kuti pa nthawi imeneyo padzakhala chivomerezi chachikulu mʼdziko la Israeli.
Et in zelo meo, in igne irae meae locutus sum. Quia in die illa erit commotio magna super terram Israel:
20 Nsomba za mʼnyanja, mbalame zamumlengalenga, zirombo zakuthengo, cholengedwa chilichonse chimene chimakwawa pansi, ndiponso anthu onse okhala pa dziko lapansi, adzanjenjemera pamaso panga. Mapiri adzangʼambika, malo okwera kwambiri adzagumuka ndipo khoma lililonse lidzagwa pansi.
et commovebuntur a facie mea pisces maris, et volucres caeli, et bestiae agri, et omne reptile, quod movetur super humum, cunctique homines, qui sunt super faciem terrae: et subvertentur montes, et cadent sepes, et omnis murus corruet in terram.
21 Ndidzawutsira Gogi nkhondo kuchokera ku mapiri anga. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. Anthu a Gogiyo adzaphana okhaokha ndi malupanga.
Et convocabo adversus eum in cunctis montibus meis gladium, ait Dominus Deus: gladius uniuscuiusque in fratrem suum dirigetur.
22 Ine ndidzamulanga ndi mliri ndi imfa. Ndidzagwetsa mvula yoopsa ya matalala, ndiponso sulufule ndi miyala ya moto pa iye ndi pa asilikali ake ndiponso pa mitundu yambiri ya anthu imene ili naye.
Et iudicabo eum peste, et sanguine, et imbre vehementi et lapidibus immensis: ignem, et sulphur pluam super eum, et super exercitum eius, et super populos multos, qui sunt cum eo.
23 Motero ndidzadzionetsa kuti ndine wamphamvu ndi woyera. Ndiponso ndidzadziwika pamaso pa anthu a mitundu ina yambiri. Momwemo adzadziwadi kuti Ine ndine Yehova.’”
Et magnificabor, et sanctificabor: et notus ero in oculis multarum gentium, et scient quia ego Dominus.

< Ezekieli 38 >