< Ezekieli 37 >

1 Dzanja la Yehova linali pa ine, ndipo Mzimu wa Yehova unandinyamula nʼkukandikhazika pakati pa chigwa. Chigwacho chinali chodzaza ndi mafupa.
היתה עלי יד יהוה ויוצאני ברוח יהוה ויניחני בתוך הבקעה והיא מלאה עצמות׃
2 Yehova anandiyendetsa uku ndi uku pakati pa mafupawo. Mafupawo anali ochuluka kwambiri mʼchigwa monsemo ndipo anali owuma kwambiri.
והעבירני עליהם סביב סביב והנה רבות מאד על פני הבקעה והנה יבשות מאד׃
3 Tsono Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi mafupa amenewa angakhalenso ndi moyo?” Ndinayankha kuti, “Inu Ambuye Yehova, Inuyo nokha ndiye mukudziwa.”
ויאמר אלי בן אדם התחיינה העצמות האלה ואמר אדני יהוה אתה ידעת׃
4 Pamenepo anandiwuza kuti, “Lengeza kwa mafupa amenewa ndi kuwawuza kuti amve mawu a Ine Yehova!
ויאמר אלי הנבא על העצמות האלה ואמרת אליהם העצמות היבשות שמעו דבר יהוה׃
5 Uwawuze kuti zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena kwa mafupa ndi izi: Ndidzawuzira mpweya mwa inu, ndipo mudzakhalanso ndi moyo.
כה אמר אדני יהוה לעצמות האלה הנה אני מביא בכם רוח וחייתם׃
6 Ndidzakupatsani mitsempha ndi mnofu. Ndiponso ndidzakukutani ndi khungu. Pambuyo pake ndidzawuzira mpweya mwa inu ndipo mudzakhalanso ndi moyo. Pamenepo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
ונתתי עליכם גדים והעלתי עליכם בשר וקרמתי עליכם עור ונתתי בכם רוח וחייתם וידעתם כי אני יהוה׃
7 Ndipo ndinanenera monga anandilamulira. Ndipo pamene ndinkanenera, ndinamva gobedegobede, ndipo mafupa aja anayamba kulumikizana, fupa ku fupa linzake.
ונבאתי כאשר צויתי ויהי קול כהנבאי והנה רעש ותקרבו עצמות עצם אל עצמו׃
8 Ine ndinayangʼana, ndipo mitsempha ndi mnofu zinabwera pa mafupawo ndipo khungu linaphimba pamwamba pake, koma munalibe mpweya mwa iwo.
וראיתי והנה עליהם גדים ובשר עלה ויקרם עליהם עור מלמעלה ורוח אין בהם׃
9 Tsono Yehova anandiwuza kuti, “Nenera kwa mpweya, nenera iwe mwana wa munthu ndi kuwuza mpweya mawu a Ine Ambuye Yehova kuti, ‘Bwera kuno iwe mpweya. Bwera kuchokera ku mbali zonse zinayi ndi kudzawuzira anthu ophedwawa kuti akhalenso ndi moyo.’
ויאמר אלי הנבא אל הרוח הנבא בן אדם ואמרת אל הרוח כה אמר אדני יהוה מארבע רוחות באי הרוח ופחי בהרוגים האלה ויחיו׃
10 Choncho ndinanenera monga anandilamulira ndipo mpweya unalowa mwa iwo; apo anthu akufawo anakhala ndi moyo, nayimirira ndipo linali gulu lalikulu lankhondo.”
והנבאתי כאשר צוני ותבוא בהם הרוח ויחיו ויעמדו על רגליהם חיל גדול מאד מאד׃
11 Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, mafupa awa ndi nyumba yonse ya Israeli. Iwo amanena kuti, ‘Mafupa athu awuma ndipo chiyembekezo chathu chatayika, ife tawonongeka!’
ויאמר אלי בן אדם העצמות האלה כל בית ישראל המה הנה אמרים יבשו עצמותינו ואבדה תקותנו נגזרנו לנו׃
12 Nʼchifukwa chake nenera ndi kuwawuza kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Inu anthu anga, ndidzafukula manda anu, ndipo ndidzakutulutsanimo ndi kukubwezerani ku dziko la Israeli.
לכן הנבא ואמרת אליהם כה אמר אדני יהוה הנה אני פתח את קברותיכם והעליתי אתכם מקברותיכם עמי והבאתי אתכם אל אדמת ישראל׃
13 Ndipo inu, anthu anga, mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pamene ndidzafukula manda anu ndikukutulutsanimo.
וידעתם כי אני יהוה בפתחי את קברותיכם ובהעלותי אתכם מקברותיכם עמי׃
14 Ine ndidzayika Mzimu wanga mwa inu ndipo mudzakhalanso ndi moyo. Pambuyo pake ndidzakulowetsani mʼdziko lanulanu. Choncho mudzadziwa kuti Ambuye Yehova ndayankhula zimenezi, ndipo ndidzazichitadi. Ndikutero Ine Yehova!’”
ונתתי רוחי בכם וחייתם והנחתי אתכם על אדמתכם וידעתם כי אני יהוה דברתי ועשיתי נאם יהוה׃
15 Yehova anandiyankhula kuti:
ויהי דבר יהוה אלי לאמר׃
16 “Iwe mwana wa munthu, tenga ndodo ndipo ulembepo kuti, ‘Ndodo ya Yuda ndi Aisraeli oyanjana nawo.’ Utengenso ndodo ina ndipo ulembepo kuti, ‘Ndodo ya Efereimu, ndiye kuti fuko la Yosefe ndi Aisraeli onse oyanjana nawo.’
ואתה בן אדם קח לך עץ אחד וכתב עליו ליהודה ולבני ישראל חברו ולקח עץ אחד וכתוב עליו ליוסף עץ אפרים וכל בית ישראל חברו׃
17 Ulumikize ndodo ziwirizi kuti zikhale ndodo imodzi mʼdzanja lako.
וקרב אתם אחד אל אחד לך לעץ אחד והיו לאחדים בידך׃
18 “Anthu a mtundu wako akadzakufunsa tanthauzo la zimenezi
וכאשר יאמרו אליך בני עמך לאמר הלוא תגיד לנו מה אלה לך׃
19 iwe udzawawuze mawu awa a Ine Ambuye Yehova akuti, ‘Ine ndidzatenga ndodo ya Yosefe imene ili mʼdzanja la Efereimu, ndi ya mafuko a Aisraeli oyanjana naye, ndi kuyilumikiza ku ndodo ya Yuda, kuti zikhale ndodo imodzi, ndipo zidzakhaladi ndodo imodzi mʼdzanja langa!’
דבר אלהם כה אמר אדני יהוה הנה אני לקח את עץ יוסף אשר ביד אפרים ושבטי ישראל חברו ונתתי אותם עליו את עץ יהודה ועשיתם לעץ אחד והיו אחד בידי׃
20 Ndodo ziwiri zimene udzalembepozo zikadzakhala mʼmanja mwako pamaso pa anthu onse,
והיו העצים אשר תכתב עליהם בידך לעיניהם׃
21 udzawawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzawachotsa Aisraeli pakati pa anthu a mitundu ina kumene anapita ku ukapolo. Ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku mbali zonse ndi kubwera nawo ku dziko lawolawo.
ודבר אליהם כה אמר אדני יהוה הנה אני לקח את בני ישראל מבין הגוים אשר הלכו שם וקבצתי אתם מסביב והבאתי אותם אל אדמתם׃
22 Ndidzawasandutsa mtundu umodzi mʼdzikomo, pa mapiri a Israeli. Padzakhala mfumu imodzi yowalamulira, ndipo sadzakhalanso mitundu iwiri kapena kugawikana maufumu awiri.
ועשיתי אתם לגוי אחד בארץ בהרי ישראל ומלך אחד יהיה לכלם למלך ולא יהיה עוד לשני גוים ולא יחצו עוד לשתי ממלכות עוד׃
23 Sadzadziyipitsanso ndi mafano awo, kapena ndi zinthu zawo zonyansa, kapenanso ndi ntchito zawo zoyipa zilizonse. Ndidzawapulumutsa ku machimo awo onse ndi kuwayeretsa. Choncho adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo.
ולא יטמאו עוד בגלוליהם ובשקוציהם ובכל פשעיהם והושעתי אתם מכל מושבתיהם אשר חטאו בהם וטהרתי אותם והיו לי לעם ואני אהיה להם לאלהים׃
24 “‘Mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yawo, motero onsewa adzakhala ndi mʼbusa mmodzi. Iwo adzatsatira malamulo anga ndipo adzasamalira kusunga malangizo anga.
ועבדי דוד מלך עליהם ורועה אחד יהיה לכלם ובמשפטי ילכו וחקתי ישמרו ועשו אותם׃
25 Iwo adzakhala mʼdziko limene ndinalipereka kwa mtumiki wanga Yakobo, dziko limene makolo anu ankakhalamo. Iwo ndi ana awo pamodzi ndi zidzukulu zawo adzakhala kumeneko ndipo Davide adzakhala mfumu yawo kwa muyaya.
וישבו על הארץ אשר נתתי לעבדי ליעקב אשר ישבו בה אבותיכם וישבו עליה המה ובניהם ובני בניהם עד עולם ודוד עבדי נשיא להם לעולם׃
26 Ndidzachita nawo pangano lamtendere; lidzakhala pangano lamuyaya. Ndidzawakhazikitsa ndi kuwachulukitsa, ndipo ndidzayika malo anga opatulika pakati pawo kwamuyaya.
וכרתי להם ברית שלום ברית עולם יהיה אותם ונתתים והרביתי אותם ונתתי את מקדשי בתוכם לעולם׃
27 Nyumba yanga yokhalamo idzakhala pakati pawo; Ine ndidzakhala Mulungu wawo, ndipo iwo adzakhala anthu anga.
והיה משכני עליהם והייתי להם לאלהים והמה יהיו לי לעם׃
28 Pamenepo anthu a mitundu ina adzadziwa kuti Ine Yehova ndiye amene ndimasandutsa Israeli kukhala woyera, pamene malo anga opatulika adzakhala pakati pawo kwamuyaya!’”
וידעו הגוים כי אני יהוה מקדש את ישראל בהיות מקדשי בתוכם לעולם׃

< Ezekieli 37 >