< Ezekieli 34 >

1 Yehova anandiyankhula kuti:
여호와의 말씀이 내게 임하여 가라사대
2 “Iwe mwana wa munthu, yankhula mawu oyimba mlandu abusa a Israeli. Lengeza ndipo uwawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti, ‘Tsoka kwa abusa a Israeli amene mumangodzisamala nokha! Kodi abusa sayenera kusamalira nkhosa?
인자야 너는 이스라엘 목자들을 쳐서 예언하라 그들 곧 목자들에게 예언하여 이르기를 주 여호와의 말씀에 자기만 먹이는 이스라엘 목자들은 화 있을진저 목자들이 양의 무리를 먹이는 것이 마땅치 아니하냐
3 Mumadya chambiko, mumadziveka zovala zaubweya, ndi kupha nyama zonenepa, koma simusamalira nkhosazo.
너희가 살진 양을 잡아 그 기름을 먹으며 그 털을 입되 양의 무리는 먹이지 아니하는도다
4 Simunalimbitse nkhosa zofowoka, kapena kuchiritsa zodwala, kapena kumanga mabala a nkhosa zopweteka. Simunabweze zosochera kapena kufunafuna zotayika. Munaziweta mozunza ndi mwankhanza.
너희가 그 연약한 자를 강하게 아니하며 병든 자를 고치지 아니하며 상한 자를 싸매어 주지 아니하며 쫓긴 자를 돌아오게 아니하며 잃어버린 자를 찾지 아니하고 다만 강포로 그것들을 다스렸도다
5 Kotero zinabalalika chifukwa zinalibe mʼbusa, ndipo pamene zinabalalika zinakhala chakudya cha zirombo zonse zakuthengo.
목자가 없으므로 그것들이 흩어지며 흩어져서 모든 들짐승의 밥이 되었도다
6 Nkhosa zanga zinayendayenda mʼmapiri onse ndi mʼzitunda zonse zazitali. Zinabalalika pa dziko lonse lapansi, ndipo palibe amene anazilondola kapena kuzifunafuna.
내 양의 무리가 모든 산과 높은 멧부리에마다 유리되었고 내 양의 무리가 온 지면에 흩어졌으되 찾고 찾는 자가 없었도다
7 “‘Choncho Inu abusa, tamvani zimene Ine Yehova ndikukuwuzani.
그러므로 목자들아 여호와의 말씀을 들을지어다
8 Pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Wamphamvuzonse, ndithu, nkhosa zanga zinajiwa ndi zirombo zakuthengo, zinasanduka chakudya cha zirombo chifukwa panalibe abusa. Abusa anga sanafunefune nkhosa zanga. Iwo ankangosamala za iwo okha mʼmalo mosamala nkhosa zanga.
주 여호와의 말씀에 내가 나의 삶을 두고 맹세하노라 내 양의 무리가 노략거리가 되고 모든 들짐승의 밥이 된 것은 목자가 없음이라 내 목자들이 양을 찾지 아니하고 자기만 먹이고 내 양의 무리를 먹이지 아니하였도다
9 Chifukwa chake, inu abusa, tamvani zimene Ine Yehova ndikukuwuzani.
그러므로 너희 목자들아 여호와의 말씀을 들을지어다
10 Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndayipidwa nanu, inu abusa. Ndidzakulandani nkhosa zanga ndipo simudzazidyetsanso. Ndidzakuchotsani pa ntchito ya ubusa kuti musamangodzidyetsa nokha. Ndidzalanditsa nkhosa zanga kukamwa kwanu ndipo simudzazidyanso.
주 여호와의 말씀에 내가 목자들을 대적하여 내 양의 무리를 그들의 손에서 찾으리니 목자들이 양을 먹이지 못할 뿐 아니라 그들이 다시는 자기를 먹이지 못할지라 내가 내 양을 그들의 입에서 건져내어서 다시는 그 식물이 되지 않게 하리라
11 “‘Tsono Ine Ambuye Yehova ndikuti, mwini wakene ndidzazifunafuna nkhosa zanga ndi kuzisamalira.
나 주 여호와가 말하노라 나 곧 내가 내 양을 찾고 찾되
12 Monga mʼbusa amanka nafunafuna nkhosa zake pamene zina zabalalikira kutali, moteronso Ine ndidzafunafuna nkhosa zanga. Ndidzazipulumutsa kuchoka kumalo onse kumene zinabalalikira pa nthawi yankhungu ndi mdima.
목자가 양 가운데 있는 날에 양이 흩어졌으면 그 떼를 찾는 것 같이 내가 내 양을 찾아서 흐리고 캄캄한 날에 그 흩어진 모든 곳에서 그것들을 건져낼지라
13 Ndidzazitulutsa pakati pa mitundu ya anthu ndi kuzisonkhanitsa kuchokera ku mayiko ena, ndipo ndidzazibwezera ku dziko lawo. Ndidzaziwetera ku mapiri a Israeli, mʼmbali mwa mitsinje ndi kumalo kumene kumakhala anthu.
내가 그것들을 만민 중에서 끌어내며 열방 중에서 모아 그 본토로 데리고 가서 이스라엘 산 위에와 시냇가에와 그 땅 모든 거주지에서 먹이되
14 Ndidzaziwetera kumalo a msipu wabwino. Mapiri okwera a Israeli adzakhala malo azidyetserako. Kumeneko zidzapumula ku abusa abwino a msipu ndipo zizidzadyadi msipu wonenepetsa pa mapiri a Israeli.
좋은 꼴로 먹이고 그 우리를 이스라엘 높은 산 위에 두리니 그것들이 거기서 좋은 우리에 누워 있으며 이스라엘 산 위에서 살진 꼴을 먹으리라
15 Ine mwini wake ndidzaziweta nkhosa zanga ndi kuzilola kuti zipumule. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
나 주 여호와가 말하노라 내가 친히 내 양의 목자가 되어 그것들로 누워 있게 할지라
16 Ndidzafunafuna zotayika ndi kubweza zosochera. Ndidzamanga mabala a zopweteka ndi kulimbikitsa zofowoka. Koma zonenepa ndi zamphamvu ndidzaziwononga. Ndidzaweta nkhosazo mwachilungamo.
그 잃어버린 자를 내가 찾으며 쫓긴 자를 내가 돌아오게 하며 상한 자를 내가 싸매어 주며 병든 자를 내가 강하게 하려니와 살진 자와 강한 자는 내가 멸하고 공의대로 그것들을 먹이리라
17 “‘Kunena za inu, nkhosa zanga, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzaweruza pakati pa nkhosa ndi nkhosa, pakati pa nkhosa zazimuna ndi mbuzi zazimuna.
나 주 여호와가 말하노라 나의 양떼 너희여 내가 양과 양의 사이와 수양과 수염소의 사이에 심판하노라
18 Kodi sikukukwanirani kudya msipu wabwino kuti muzichita kuponderezanso msipu umene simunadyewo? Kodi simukhutira ndi kumwa madzi abwino kuti muzinka mudetsanso madzi otsalawo ndi mapazi anu?
너희가 좋은 꼴 먹은 것을 작은 일로 여기느냐 어찌하여 남은 꼴을 발로 밟았느냐 너희가 맑은 물 마신 것을 작은 일로 여기느냐 어찌하여 남은 물을 발로 더럽혔느냐
19 Kodi nkhosa zanga zidye zimene mwazipondaponda ndi kumwa madzi amene mwawadetsa ndi mapazi anu?
나의 양은 너희 발로 밟은 것을 먹으며 너희 발로 더럽힌 것을 마시는도다 하셨느니라
20 “‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Taonani, Ine mwini wake ndidzaweruza pakati pa nkhosa zonenepa ndi nkhosa zowonda.
그러므로 주 여호와께서 그들에게 대하여 말씀하시기를 나 곧 내가 살진 양과 파리한 양 사이에 심판하리라
21 Popeza zofowoka mumaziwomba ndi kuzikankhira kumbali, ndipo mumazigunda ndi nyanga zanu nʼkuzimwazira kutali,
너희가 옆구리와 어깨로 밀뜨리고 모든 병든 자를 뿔로 받아 무리로 밖으로 흩어지게 하는도다
22 tsono Ine ndidzapulumutsa nkhosa zanga, ndipo sindidzalolanso kuti zijiwe. Ndidzaweruza pakati pa nkhosa ina ndi nkhosa inanso.
그러므로 내가 내 양떼를 구원하여 그들로 다시는 노략거리가 되지 않게 하고 양과 양 사이에 심판하리라
23 Ndidzaziyikira mʼbusa mmodzi, mtumiki wanga Davide. Iyeyo ndiye azidzazisamala. Adzakhala mʼbusa wawo.
내가 한 목자를 그들의 위에 세워 먹이게 하리니 그는 내 종 다윗이라 그가 그들을 먹이고 그들의 목자가 될지라
24 Ine Yehova ndidzakhala Mulungu wake ndipo mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu pakati pa nkhosazo. Ine Yehova ndayankhula.
나 여호와는 그들의 하나님이 되고 내 종 다윗은 그들 중에 왕이 되리라 나 여호와의 말이니라
25 “‘Ndidzapangana nazo pangano la mtendere. Ndidzachotsa mʼdzikomo zirombo zolusa. Choncho nkhosa zanga zidzakhala mu mtendere mu chipululu ngakhalenso mʼthengo.
내가 또 그들과 화평의 언약을 세우고 악한 짐승을 그 땅에서 그치게 하리니 그들이 빈 들에 평안히 거하며 수풀 가운데서 잘지라
26 Ndidzakhazika anthu anga pafupi ndi phiri langa loyera ndipo ndidzawadalitsa. Ndidzawagwetsera mvula pa nthawi yake ndipo idzakhala mvula ya madalitso.
내가 그들에게 복을 내리며 내 산 사면 모든 곳도 복되게 하여 때를 따라 비를 내리되 복된 장마비를 내리리라
27 Mitengo ya mʼminda idzabereka zipatso zake, ndipo nthaka idzakhala ndi zokolola zake. Anthu adzakhala mwamtendere mʼdziko lawo. Iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pamene ndidzathyola magoli awo ndi kuwapulumutsa kuchoka mʼmanja mwa amene anawagwira ukapolo.
그리한즉 밭에 나무가 열매를 맺으며 땅이 그 소산을 내리니 그들이 그 땅에서 평안할지라 내가 그들의 멍엣목을 꺾고 그들로 종을 삼은 자의 손에서 그들을 건져낸 후에 그들이 나를 여호와인 줄 알겠고
28 Anthu amitundu ina sadzawafunkhanso ndipo sadzadyedwa ndi zirombo zakuthengo. Adzakhala mwamtendere ndipo palibe amene adzawaopseze.
그들이 다시는 이방의 노략거리가 되지 아니하며 땅의 짐승의 삼킨바 되지 아니하고 평안히 거하리니 놀랠 사람이 없으리라
29 Ndidzawapatsa zokolola zochuluka motero kuti sadzavutikanso ndi njala. Anthu a mitundu ina sadzawanyozanso.
내가 그들을 위하여 유명한 종식할 땅을 일으키리니 그들이 다시는 그 땅에서 기근으로 멸망하지 아니할지며 다시는 열국의 수치를 받지 아니할지라
30 Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine Yehova Mulungu wawo ndili nawo pamodzi, ndipo kuti iwo, Aisraeli, ndi anthu anga. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
그들이 나 여호와 그들의 하나님이 그들과 함께 있는 줄을 알며 그들 곧 이스라엘 족속이 내 백성인 줄 알리라 나 주 여호와의 말이라
31 Inu ndinu nkhosa zanga, nkhosa zimene ndimazidyetsa. Ine ndine Mulungu wanu. Ndikutero Ine Ambuye Wamphamvuzonse.’”
내 양 곧 내 초장의 양 너희는 사람이요 나는 너희 하나님이라 나 주 여호와의 말이니라

< Ezekieli 34 >