< Ezekieli 32 >

1 Pa tsiku loyamba la mwezi wa khumi ndi chiwiri, chaka chakhumi ndi chiwiri, Yehova anandiyankhula kuti:
ויהי בשתי עשרה שנה בשני עשר חדש באחד לחדש היה דבר יהוה אלי לאמר
2 “Iwe mwana wa munthu imba nyimbo ya maliro a Farao mfumu ya Igupto ndipo uyiwuze kuti, “Iwe umadziyesa ngati mkango pakati pa mitundu ya anthu. Koma iwe uli ngati ngʼona mʼnyanja. Umakhuvula mʼmitsinje yako, kuvundula madzi ndi mapazi ako ndi kudetsa madzi mʼmitsinje.
בן אדם שא קינה על פרעה מלך מצרים ואמרת אליו כפיר גוים נדמית ואתה כתנים בימים ותגח בנהרותיך ותדלח מים ברגליך ותרפס נהרותם
3 “Tsono Ine Ambuye Yehova ndikuti, “‘Pogwiritsa ntchito gulu la anthu a mitundu yambiri, ndidzakuponyera khoka langa ndi kukugwira mu ukonde wanga.
כה אמר אדני יהוה ופרשתי עליך את רשתי בקהל עמים רבים והעלוך בחרמי
4 Ndidzakuponya ku mtunda ndi kukutayira pansi. Ndidzabweretsa mbalame zamumlengalenga kuti zidzatere pa iwe, ndipo zirombo zonse za dziko lapansi zidzakudya.
ונטשתיך בארץ על פני השדה אטילך והשכנתי עליך כל עוף השמים והשבעתי ממך חית כל הארץ
5 Ndidzayanika mnofu wako pa mapiri ndipo zigwa zidzadzaza ndi zotsalira zako.
ונתתי את בשרך על ההרים ומלאתי הגאיות רמותך
6 Ndidzanyowetsa dziko ndi magazi ako, mpaka kumapiri komwe, ndipo mitsinje idzadzaza ndi mnofu wako.
והשקיתי ארץ צפתך מדמך אל ההרים ואפקים ימלאון ממך
7 Ndikadzakuwononga, ndidzaphimba miyamba ndikudetsa nyenyezi zake. Ndidzaphimba dzuwa ndi mtambo, ndipo mwezi sudzawala.
וכסיתי בכבותך שמים והקדרתי את ככביהם שמש בענן אכסנו וירח לא יאיר אורו
8 Zowala zonse zamumlengalenga ndidzazizimitsa; ndidzachititsa mdima pa dziko lako, akutero Ambuye Yehova.
כל מאורי אור בשמים אקדירם עליך ונתתי חשך על ארצך נאם אדני יהוה
9 Ndidzasautsa mitima ya anthu a mitundu yambiri pamene ndidzakupititsa ku ukapolo pakati pa mitundu ya anthu, ku mayiko amene iwe sunawadziwe.
והכעסתי--לב עמים רבים בהביאי שברך בגוים על ארצות אשר לא ידעתם
10 Ine ndidzachititsa kuti anthu a mitundu yambiri adabwe nawe, ndipo mafumu awo adzanjenjemera ndi mantha aakulu chifukwa cha iwe pamene ndidzaonetsa lupanga langa pamaso pawo. Pa nthawi ya kugwa kwako, aliyense wa iwo adzanjenjemera moyo wake wonse.
והשמותי עליך עמים רבים ומלכיהם ישערו עליך שער בעופפי חרבי על פניהם וחרדו לרגעים איש לנפשו ביום מפלתך
11 “‘Pakuti ndikunena Ine Ambuye Yehova kuti, “‘Lupanga la mfumu ya ku Babuloni lidzabwera kudzalimbana nawe.
כי כה אמר אדני יהוה חרב מלך בבל תבואך
12 Ndidzachititsa gulu lako lankhondo kuti ligwe ndi lupanga la anthu amphamvu, anthu ankhanza kwambiri pakati pa mitundu yonse ya anthu. Adzathetsa kunyada kwa Igupto, ndipo gulu lake lonse la nkhondo lidzagonjetsedwa.
בחרבות גבורים אפיל המונך עריצי גוים כלם ושדדו את גאון מצרים ונשמד כל המונה
13 Ndidzawononga ziweto zake zonse zokhala mʼmbali mwa madzi ambiri. Ku madziko sikudzaonekanso phazi la munthu kapena kudetsedwa ndi phazi la ziweto.
והאבדתי את כל בהמתה מעל מים רבים ולא תדלחם רגל אדם עוד ופרסות בהמה לא תדלחם
14 Pambuyo pake ndidzayeretsa madzi ake ndipo mitsinje yake idzayenda mokometsera ngati mafuta, akutero Ambuye Yehova.
אז אשקיע מימיהם ונהרותם כשמן אוליך--נאם אדני יהוה
15 Ndikadzasandutsa dziko la Igupto kukhala bwinja; ndikadzawononga dziko lonse ndi kukantha onse okhala kumeneko, adzadziwa kuti ndine Yehova.’
בתתי את ארץ מצרים שממה ונשמה ארץ ממלאה--בהכותי את כל יושבי בה וידעו כי אני יהוה
16 “Mawu angawa adzakhala nyimbo ya maliro. Ana a akazi amitundu ya anthu adzayimba, kuyimbira Igupto ndi gulu lake lonse la nkhondo, akutero Ambuye Yehova.”
קינה היא וקוננוה בנות הגוים תקוננה אותה על מצרים ועל כל המונה תקוננה אותה נאם אדני יהוה
17 Pa tsiku la 15 la mwezi woyamba, chaka cha khumi ndi chiwiri, Yehova anayankhula kuti:
ויהי בשתי עשרה שנה בחמשה עשר לחדש היה דבר יהוה אלי לאמר
18 “Iwe mwana wa munthu, lirira gulu lankhondo la Igupto ndipo uwalowetse pamodzi ndi anthu ena amphamvu a mayiko ena ku dziko la anthu akufa.
בן אדם--נהה על המון מצרים והורדהו אותה ובנות גוים אדרם אל ארץ תחתיות--את יורדי בור
19 Ufunse kuti, ‘Ndani amene akukuposa kukongola? Tsikirani ku manda ndi kukhala pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe.’
ממי נעמת רדה והשכבה את ערלים
20 Aigupto adzagwa pakati pa amene akuphedwa ndi lupanga. Lupanga ndi losololedwa kale. Iye adzaphedwa pamodzi ndi gulu lake lankhondo.
בתוך חללי חרב יפלו חרב נתנה משכו אותה וכל המוניה
21 Mʼkati mwa manda atsogoleri amphamvu pamodzi ndi ogwirizana nawo azidzakambirana za Igupto nʼkumati, ‘Afika kuno anthu osachita mdulidwe aja! Ndi awa agona apawa, ophedwa pa nkhondo.’ (Sheol h7585)
ידברו לו אלי גבורים מתוך שאול--את עזריו ירדו שכבו הערלים חללי חרב (Sheol h7585)
22 “Asiriya ali komweko ndipo ankhondo ake onse ali mʼmanda omuzungulira. Onsewo anaphedwa pa nkhondo.
שם אשור וכל קהלה סביבותיו קברתיו כלם חללים הנפלים בחרב
23 Manda awo ali kumalo ozama a dzenje, ndipo ankhondo ake azungulira manda ake. Onse amene anaopseza dziko la anthu amoyo aphedwa, agwa ndi lupanga.
אשר נתנו קברתיה בירכתי בור ויהי קהלה סביבות קברתה כלם חללים נפלים בחרב אשר נתנו חתית בארץ חיים
24 “Elamu ali komweko ndipo ankhondo ake ali mʼmanda omuzungulira. Onsewa anaphedwa pa nkhondo, natsikira ku manda ali osachita mdulidwe. Iwowa kale ankaopseza anthu pa dziko lapansi. Tsopano akuchita manyazi pamodzi ndi amene ali mʼmanda.
שם עילם וכל המונה סביבות קברתה כלם חללים הנפלים בחרב אשר ירדו ערלים אל ארץ תחתיות אשר נתנו חתיתם בארץ חיים וישאו כלמתם את יורדי בור
25 Amukonzera pogona pakati pa anthu ophedwa, pamodzi ndi gulu lake lonse la nkhondo litazungulira manda ake. Onsewo ndi anthu osachita mdulidwe ophedwa ndi lupanga. Paja anthuwa ankaopsa mʼdziko la anthu a moyo. Koma tsopano akuchita manyazi pamodzi ndi amene ali mʼmanda. Iwo ayikidwa pakati pa anthu ophedwa.
בתוך חללים נתנו משכב לה בכל המונה--סביבותיו קברתה כלם ערלים חללי חרב כי נתן חתיתם בארץ חיים וישאו כלמתם את יורדי בור בתוך חללים נתן
26 “Mesaki ndi Tubala ali komweko, pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo litazungulira manda awo. Onsewo ndi anthu osachita mdulidwe, ophedwa ndi lupanga. Paja ankaopsa mʼdziko la anthu amoyo.
שם משך תבל וכל המונה סביבותיו קברותיה כלם ערלים מחללי חרב כי נתנו חתיתם בארץ חיים
27 Iwo sanayikidwe mwaulemu ngati ankhondo amphamvu amakedzana, amene anatsikira ku dziko la anthu akufa ndi zida zawo zomwe za nkhondo. Malupanga awo anawayika ku mitu yawo, ndipo zishango zawo anaphimba mafupa awo. Kale anthu amphamvu amenewa ankaopsa dziko la anthu amoyo. (Sheol h7585)
ולא ישכבו את גבורים נפלים מערלים אשר ירדו שאול בכלי מלחמתם ויתנו את חרבותם תחת ראשיהם ותהי עונתם על עצמותם--כי חתית גבורים בארץ חיים (Sheol h7585)
28 “Iwenso Farao, udzaphwanyidwa ndi kuyikidwa pakati pa anthu osachita mdulidwe, amene anaphedwa ndi lupanga.
ואתה בתוך ערלים תשבר ותשכב--את חללי חרב
29 “Edomu ali kumeneko pamodzi ndi mafumu ake ndi akalonga ake onse. Ngakhale anali amphamvu, koma anayikidwa. Ayikidwa pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, pamodzi ndi iwo amene akutsikira ku dzenje.
שמה אדום מלכיה וכל נשיאיה אשר נתנו בגבורתם את חללי חרב המה את ערלים ישכבו ואת ירדי בור
30 “Akalonga onse akumpoto pamodzi ndi anthu onse a ku Sidoni ali kumeneko. Anatsikira ku dziko la anthu akufa mwamanyazi ngakhale anali owopsa ndi mphamvu zawo. Iwo akugona osachita mdulidwe pamodzi ndi amene anaphedwa ndi lupanga ndipo akuchita manyazi pamodzi ndi iwo amene anatsikira kale ku manda.
שמה נסיכי צפון כלם וכל צדני אשר ירדו את חללים בחתיתם מגבורתם בושים וישכבו ערלים את חללי חרב וישאו כלמתם את יורדי בור
31 “Farao ndi gulu lake lankhondo akadzawaona iwowa adzathunza mtima pokumbukira kuchuluka kwa gulu lake lankhondo limene linaphedwa pa nkhondo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
אותם יראה פרעה ונחם על כל המונה--חללי חרב פרעה וכל חילו נאם אדני יהוה
32 Paja ankaopsa mʼdziko la anthu amoyo. Koma Faraoyo pamodzi ndi ankhondo ake onse adzayikidwa pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, pamodzi ndi amene anaphedwa pa nkhondo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”
כי נתתי את חתיתו (חתיתי) בארץ חיים והשכב בתוך ערלים את חללי חרב פרעה וכל המונה--נאם אדני יהוה

< Ezekieli 32 >