< Ezekieli 31 >

1 Pa tsiku loyamba la mwezi wachitatu, chaka cha khumi ndi chimodzi, Yehova anandiyankhula kuti:
ויהי באחת עשרה שנה בשלישי באחד לחדש היה דבר יהוה אלי לאמר
2 “Iwe mwana wa munthu, unene kwa Farao mfumu ya Igupto ndi gulu lake lankhondo. Awawuze kuti, “‘Kodi mu ukulu wanu ndani angafanane ndi inu?
בן אדם אמר אל פרעה מלך מצרים ואל המונו אל מי דמית בגדלך
3 Taonani, ndidzakufanizirani ndi mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni, wa nthambi zokongola zochititsa mthunzi mʼnkhalango. Unali wautali, msonga zake zooneka pamwamba pa nkhalango.
הנה אשור ארז בלבנון יפה ענף וחרש מצל--וגבה קומה ובין עבתים היתה צמרתו
4 Madzi ndiwo ankawukulitsa mkungudzawo, akasupe ozama ankawutalikitsa. Mitsinje yake inkayenda mozungulira malo amene unaliwo ndipo ngalande zake zinkafika ku mitengo yonse ya mʼmunda.
מים גדלוהו תהום רממתהו את נהרתיה הלך סביבות מטעה ואת תעלתיה שלחה אל כל עצי השדה
5 Choncho unatalika kwambiri kupambana mitengo yonse ya mʼmunda. Nthambi zake zinachuluka ndi kutalika kwambiri, chifukwa inkalandira madzi ambiri.
על כן גבהא קמתו מכל עצי השדה ותרבינה סרעפתיו ותארכנה פארתו ממים רבים--בשלחו
6 Mbalame zonse zamlengalenga zinkamanga zisa zake mʼnthambi za mtengowo. Nyama zakuthengo zonse zinkaswanirana mʼmunsi mwa nthambi zake. Mitundu yotchuka ya anthu inkakhala mu mthunzi wake.
בסעפתיו קננו כל עוף השמים ותחת פארתיו ילדו כל חית השדה ובצלו ישבו כל גוים רבים
7 Unali wokongola kwambiri, wa nthambi zake zotambalala, chifukwa mizu yake inazama pansi kumene kunali madzi ochuluka.
וייף בגדלו בארך דליותיו כי היה שרשו אל מים רבים
8 Mʼmunda wa Mulungu munalibe mkungudza wofanana nawo, kapena mitengo ya payini ya nthambi zofanafana ndi nthambi zake. Munalibenso mtengo wa mkuyu nthambi zofanafana ndi zake. Mʼmunda wa Mulungu munalibe mtengo wina uliwonse wofanana ndi iwo kukongola kwake.
ארזים לא עממהו בגן אלהים--ברושים לא דמו אל סעפתיו וערמנים לא היו כפראתיו כל עץ בגן אלהים--לא דמה אליו ביפיו
9 Ine ndinawupanga wokongola wa nthambi zochuluka. Mitengo yonse ya mu Edeni, mʼmunda wa Mulungu inawuchitira nsanje.
יפה עשיתיו ברב דליותיו ויקנאהו כל עצי עדן אשר בגן האלהים
10 “‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Chifukwa kuti mtengowo unatalika kwambiri, unatulutsa songa zake mpaka ku thambo, ndipo unadzikweza chifukwa cha msinkhu wake,
לכן כה אמר אדני יהוה יען אשר גבהת בקומה ויתן צמרתו אל בין עבותים ורם לבבו בגבהו
11 ndinawupereka mʼdzanja la mfumu ya mitundu ya anthu kuti awulange molingana ndi kuyipa kwake.
ואתנהו--ביד איל גוים עשו יעשה לו כרשעו גרשתהו
12 Anthu ankhanza kwambiri amitundu ya anthu achilendo adzawudula ndi kuwusiya. Nthambi zake zidzagwera pa mapiri ndi mu zigwa zonse. Nthambi zake zidzathyokera mʼmitsinje ya mʼdzikomo. Motero mitundu yonse ya anthu a dziko lapansi amene ankasangalala mu mthunzi wake idzawusiya.
ויכרתהו זרים עריצי גוים ויטשהו אל ההרים ובכל גאיות נפלו דליותיו ותשברנה פראתיו בכל אפיקי הארץ וירדו מצלו כל עמי הארץ ויטשהו
13 Mbalame zonse zamlengalenga zidzakhala pa mtengo wakugwawo, ndipo nyama zakuthengo zonse zidzakhala pa nthambi zake.
על מפלתו ישכנו כל עוף השמים ואל פראתיו היו כל חית השדה
14 Zidzakutero kuti pasakhalenso mitengo inanso ya mʼmbali mwa madzi yotalika kwambiri, imene idzatalike kwambiri ndi songa zake kufika mpaka ku mitambo. Komanso kuti pasadzakhalenso mitengo yolandira bwino madzi, imene idzatalika motero. Paja yonseyo kutha kwake ndi kufa, kupita ku dziko lapansi kukhala ndi anthu akufa amene analowa mʼmanda kale.
למען אשר לא יגבהו בקומתם כל עצי מים ולא יתנו את צמרתם אל בין עבתים ולא יעמדו אליהם בגבהם כל שתי מים כי כלם נתנו למות אל ארץ תחתית בתוך בני אדם--אל יורדי בור
15 “‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa nthawi imene mkungudzawo unatsikira ku manda, ndinawuza nyanja kuti iwulire maliro pakuwuphimba. Ndinawumitsa mitsinje ndipo madzi ambiri anaphwa. Ndinabweretsa mdima pa Lebanoni chifukwa cha mtengowo ndipo mitengo yonse ya mʼdzikomo inawuma. (Sheol h7585)
כה אמר אדני יהוה ביום רדתו שאולה האבלתי כסתי עליו את תהום ואמנע נהרותיה ויכלאו מים רבים ואקדר עליו לבנון וכל עצי השדה עליו עלפה (Sheol h7585)
16 Mitundu ya anthu inagwedezeka pakumva mkokomo wa kugwa kwake, pamene ndinawutsitsira ku manda pamodzi ndi iwo amene anafa. Pamenepo ku dziko la akufa mitengo yonse ya ku Edeni pamodzi ndi ya ku Lebanoni yosankhidwa bwino inasangalatsidwa chifukwa cha zimenezi. (Sheol h7585)
מקול מפלתו הרעשתי גוים בהורדי אתו שאולה את יורדי בור וינחמו בארץ תחתית כל עצי עדן--מבחר וטוב לבנון כל שתי מים (Sheol h7585)
17 Amene ankakhala mu mthunzi wake, amene ankayanjana nawo, iwonso anapita nawo pamodzi ku manda, kukakhala pamodzi ndi amene anaphedwa ndi lupanga pakati pa mitundu ya anthu. (Sheol h7585)
גם הם אתו ירדו שאולה--אל חללי חרב וזרעו ישבו בצלו בתוך גוים (Sheol h7585)
18 “‘Ndi mitengo iti ya mu Edeni imene ingafanane ndi kukongola kwako ndi ulemerero wako? Komabe iwenso, udzatsikira ku dziko la anthu akufa pamodzi ndi mitengo ya mu Edeni. Udzagona pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, anthu amene anaphedwa pa nkhondo. “‘Mtengowo ndi Farao ndi gulu lake lankhondo, akutero Ambuye Yehova.’”
אל מי דמית ככה בכבוד ובגדל בעצי עדן והורדת את עצי עדן אל ארץ תחתית בתוך ערלים תשכב את חללי חרב--הוא פרעה וכל המונה נאם אדני יהוה

< Ezekieli 31 >