< Ezekieli 30 >
1 Yehova anandiyankhula kuti:
The LORD’s word came again to me, saying,
2 “Iwe mwana wa munthu, nenera ndipo ulengeze zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena. “‘Ufuwule mawu awa akuti, ‘Kalanga, tsiku lafika!’
“Son of man, prophesy, and say, ‘The Lord GOD says: “Wail, ‘Alas for the day!’
3 Pakuti tsiku layandikira, tsiku la Yehova lili pafupi, tsiku la mitambo yakuda, tsiku lachiwonongeko cha mitundu ya anthu.
For the day is near, even the LORD’s day is near. It will be a day of clouds, a time of the nations.
4 Lupanga lidzabwera kudzalimbana ndi Igupto ndipo mavuto adzafika pa Kusi. Pamene anthu ambiri adzaphedwa mu Igupto, chuma chake chidzatengedwa ndipo maziko ake adzagumuka.
A sword will come on Egypt, and anguish will be in Ethiopia, when the slain fall in Egypt. They take away her multitude, and her foundations are broken down.
5 Kusi, Puti, Ludi ndi Arabiya yense, Libiya ndiponso anthu a mʼdziko logwirizana naye adzaphedwa ndi lupanga pamodzi ndi Igupto.
“‘“Ethiopia, Put, Lud, all the mixed people, Cub, and the children of the land that is allied with them, will fall with them by the sword.”
6 “‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: “‘Onse othandiza Igupto adzaphedwa ndipo kunyadira mphamvu zake kudzatheratu. Adzaphedwa ndi lupanga kuyambira ku Migidoli mpaka ku mzinda wa Asiwani,’” ndikutero Ine Ambuye Yehova.
“‘The LORD says: “They also who uphold Egypt will fall. The pride of her power will come down. They will fall by the sword in it from the tower of Seveneh,” says the Lord GOD.
7 “‘Dziko la Igupto lidzasanduka bwinja kupambana mabwinja ena onse opasuka, ndipo mizinda yake idzakhala yopasuka kupambana mizinda ina yonse.
“They will be desolate in the middle of the countries that are desolate. Her cities will be among the cities that are wasted.
8 Nditatha kutentha Igupto ndi kupha onse omuthandiza, pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
They will know that I am the LORD when I have set a fire in Egypt, and all her helpers are destroyed.
9 “‘Nthawi imeneyo ikadzafika, amithenga adzapita mofulumira kuchokera kwa Ine kukaopseza Kusi, iwowo osadziwako kanthu. Ndipo adzada nkhawa pa tsiku limene Igupto adzawonongedwa, chifukwa tsikulo lidzafika ndithu.
“‘“In that day messengers will go out from before me in ships to make the careless Ethiopians afraid. There will be anguish on them, as in the day of Egypt; for, behold, it comes.”
10 “‘Ine Ambuye Yehova ndikuti, “‘Ndidzagwiritsa ntchito Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni kuti ndithetse gulu lankhondo la Igupto.
“‘The Lord GOD says: “I will also make the multitude of Egypt to cease, by the hand of Nebuchadnezzar king of Babylon.
11 Iye ndi gulu lake lankhondo, mtundu wa anthu ankhanza kwambiri aja adzabwera kudzawononga dzikolo. Adzasolola malupanga awo kulimbana ndi Igupto ndipo dziko lidzadzaza ndi mitembo.
He and his people with him, the terrible of the nations, will be brought in to destroy the land. They will draw their swords against Egypt, and fill the land with the slain.
12 Ndidzawumitsa mtsinje wa Nailo ndi kugulitsa dziko la Igupto kwa anthu oyipa. Ndidzagwiritsa ntchito anthu achilendo kuti ndiwononge dzikolo pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo. Ine Yehova ndayankhula.
I will make the rivers dry, and will sell the land into the hand of evil men. I will make the land desolate, and all that is therein, by the hand of foreigners. I, the LORD, have spoken it.”
13 “‘Ine Ambuye Yehova ndikuti, “‘Ndidzawononga mafano ndi kuthetsa milungu yosema ya ku Mefisi. Simudzakhalanso mfumu mu Igupto, ndipo ndidzaopseza dziko lonse.
“‘The Lord GOD says: “I will also destroy the idols, and I will cause the images to cease from Memphis. There will be no more a prince from the land of Egypt. I will put a fear in the land of Egypt.
14 Ndidzasandutsa chipululu mzinda wa Patirosi, ndi kutentha mzinda wa Zowani. Ndidzalanga mzinda wa Thebesi.
I will make Pathros desolate, and will set a fire in Zoan, and will execute judgments on No.
15 Ndidzakhuthulira ukali wanga pa mzinda wa Peluziumu, linga lolimba la Igupto, ndi kuwononga gulu lankhondo la Thebesi.
I will pour my wrath on Sin, the stronghold of Egypt. I will cut off the multitude of No.
16 Ndidzatentha ndi moto dziko la Igupto; Peluziumu adzazunzika ndi ululu. Malinga a Thebesi adzagumuka, ndipo mzindawo udzasefukira ndi madzi.
I will set a fire in Egypt Sin will be in great anguish. No will be broken up. Memphis will have adversaries in the daytime.
17 Anyamata a ku Oni ndi ku Pibeseti adzaphedwa ndi lupanga ndipo okhala mʼmizinda yake adzatengedwa ukapolo.
The young men of Aven and of Pibeseth will fall by the sword. They will go into captivity.
18 Ku Tehafinehezi kudzakhala mdima pamene ndidzathyola goli la Igupto; motero kunyada kwake kudzatha. Iye adzaphimbidwa ndi mitambo yakuda, ndipo okhala mʼmizinda yake adzapita ku ukapolo.
At Tehaphnehes also the day will withdraw itself, when I break the yokes of Egypt there. The pride of her power will cease in her. As for her, a cloud will cover her, and her daughters will go into captivity.
19 Kotero ndidzalanga dziko la Igupto, ndipo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’”
Thus I will execute judgments on Egypt. Then they will know that I am the LORD.”’”
20 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri la mwezi woyamba wa chaka chakhumi ndi chimodzi, Yehova anandiyankhula kuti:
In the eleventh year, in the first month, in the seventh day of the month, the LORD’s word came to me, saying,
21 “Iwe mwana wa munthu, ndathyola dzanja la Farao mfumu ya Igupto. Taona, silinamangidwe kuti lipole, ngakhale kulilimbitsa ndi nsalu kuti lithe kugwiranso lupanga.
“Son of man, I have broken the arm of Pharaoh king of Egypt. Behold, it has not been bound up, to apply medicines, to put a bandage to bind it, that it may become strong to hold the sword.
22 Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, Ine ndikudana ndi Farao mfumu ya Igupto. Ndidzathyola manja ake onse; dzanja labwino pamodzi ndi lothyokalo, ndipo lupanga lidzagwa mʼmanja mwake.
Therefore the Lord GOD says: ‘Behold, I am against Pharaoh king of Egypt, and will break his arms, the strong arm, and that which was broken. I will cause the sword to fall out of his hand.
23 Ndidzamwaza Aigupto pakati pa mitundu ya anthu ndikuwabalalitsira ku mayiko ambiri.
I will scatter the Egyptians among the nations, and will disperse them through the countries.
24 Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babuloni, ndipo mʼmanja mwake ndidzayikamo lupanga langa. Koma ndidzathyola manja a Farao, ndipo adzabuwula ngati wolasidwa koopsa pamaso pa mfumu ya ku Babuloniyo.
I will strengthen the arms of the king of Babylon, and put my sword in his hand; but I will break the arms of Pharaoh, and he will groan before the king of Babylon with the groaning of a mortally wounded man.
25 Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babuloni, koma manja a Farao adzafowoka. Motero anthu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzayika lupanga langa mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni. Ndipo adzaligwiritsa ntchito pothira nkhondo dziko la Igupto.
I will hold up the arms of the king of Babylon, but the arms of Pharaoh will fall down. Then they will know that I am the LORD when I put my sword into the hand of the king of Babylon, and he stretches it out on the land of Egypt.
26 Ndidzamwaza Aigupto pakati pa mitundu ya anthu, ndikuwabalalitsira ku mayiko ambiri. Motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
I will scatter the Egyptians among the nations and disperse them through the countries. Then they will know that I am the LORD.’”