< Ezekieli 3 >
1 Tsono Mulungu anandiwuza kuti, “Mwana wa munthu, idya chimene ndikukupatsachi. Idya kenaka upite ukayankhule ndi Aisraeli.”
2 Choncho ndinayasama ndipo anandipatsa mpukutuwo kuti ndidye.
3 Kenaka Iye anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, idya mpukutu umene ndikukupatsa kuti ukhute.” Choncho ndinadya, ndipo unkatsekemera ngati uchi mʼkamwa mwanga.
4 Pamenepo Iye anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, pita tsopano kwa Aisraeli ndipo ukawawuze mawu anga.
5 Sindikukutuma kwa anthu oyankhula chiyankhulo chachilendo ndi chovuta, koma kwa Aisraeli.
6 Sindikukutuma kwa mitundu yambiri ya anthu oyankhula chiyankhulo chachilendo ndi chovuta, amene mawu ake sungawamvetse. Ndithu ndikanakutuma kwa iwowa, bwenzi iwo atakumvera.
7 Koma Aisraeli sadzakumvera chifukwa iwo sakufuna kumvera Ine. Paja Aisraeli onse ndi okanika ndiponso a mtima wowuma.
8 Tsono ine ndakhwimitsa nkhope yako mofanana ndi nkhope zawo. Ndalimbitsanso mutu wako mofanana ndi mitu yawo.
9 Ine ndidzakusandutsa wolimba ngati mwala wa dayimondi umene uposa thanthwe lina lililonse kulimba kwake. Usachite nawo mantha kapena kuopsedwa nawo. Paja anthuwa ndi awupandu.”
10 Anatinso, “Iwe mwana wa munthu, umvetsetse bwino zimene ndikukuwuzazi ndipo mawu angawa uwasunge bwino mu mtima mwako.
11 Tsopano upite kwa Aisraeli anzako amene ali ku ukapolo ndipo ukayankhule nawo. ‘Kaya akamvera kaya sakamvera,’ koma uzikawawuza kuti, Ambuye Wamphamvuzonse akuti zakutizakuti.”
12 Pamenepo Mzimu unandinyamula ndipo kumbuyo kwanga ndinamva liwu lamphamvu ngati chivomerezi chachikulu, lonena kuti, “Utamandike ulemerero wa Yehova kumene Iye amakhala!”
13 Phokoso ndinkalimvalo linali la kugundana kwa mapiko a zamoyo ndiponso phokoso la mikombero ya pambali pake ija, limene linkamveka ngati chivomerezi chachikulu.
14 Mzimu wa Yehova unandikweza ndi kundinyamula ndipo ndinachokapo ndili wowawidwa ndi wonyuka mu mtima. Ndipo dzanja la Yehova linali pa ine mwa mphamvu.
15 Choncho ndinafika kwa amene anali mu ukapolo ku Telabibu pafupi ndi mtsinje wa Kebara. Ndinakhala pansi pakati pawo masiku asanu ndi awiri, ndili wothedwa nzeru kwambiri.
16 Atatha masiku asanu ndi awiriwo, Yehova anandiwuza kuti,
17 “Iwe mwana wa munthu, Ine ndakuyika kuti ukhale mlonda wa Aisraeli. Uziti ukamva mawu anga, ndiye uzikawachenjeza.
18 Ndikawuza munthu woyipa kuti, ‘Iwe udzafa ndithu,’ koma iwe osamuchenjeza kapena kumuyankhula kuti aleke njira zake zoyipa ndi kuti akhale ndi moyo, munthu woyipayo adzafa mu uchimo wake, koma Ine ndidzakuyimba mlandu chifukwa cha imfa yake.
19 Koma ukamuchenjeza munthu woyipa koma iye osatembenuka mtima kuleka zoyipa zake kapena kusiya njira zake zoyipa, munthuyo adzafa chifukwa cha uchimo wake koma iwe udzapulumutsa moyo wako.
20 “Ngati munthu wolungama asiya chilungamo chake ndi kuchita uchimo ndipo Ine nʼkumuyika mʼzoopsa, munthuyo adzafa ndithu. Popeza iwe sunamuchenjeze, adzafadi chifukwa cha tchimo ndipo chilungamo chake sichidzakumbukiridwa, koma ndidzakuyimba mlandu chifukwa cha imfa yake.
21 Koma ngati umuchenjeza munthu wolungama kuti asachimwe ndipo iye nʼkuleka kuchimwa adzakhala ndi moyo ndithu chifukwa anamvera chenjezo, ndipo iwe udzapulumutsa moyo wako.”
22 Nthawi ina dzanja la Yehova linali pa ine ndipo anandiwuza kuti, “Nyamuka upite ku chigwa, kumeneko ndikayankhula nawe.”
23 Choncho ndinanyamuka kupita ku chigwa. Ndipo ndinaona ulemerero wa Yehova kumeneko, ngati ulemerero umene ndinaona mʼmbali mwa mtsinje wa Kebara ndipo ndinagwa pansi chafufumimba.
24 Koma Mzimu wa Mulungu unalowa mwa ine ndipo unandiyimiritsa. Tsono Yehova anandiyankhula nati: “Pita, kadzitsekere mʼnyumba mwako.
25 Ndipo iwe mwana wa munthu, adzakumanga ndi zingwe motero kuti sudzatha kuyendanso pakati pa anthu.
26 Ndidzamatirira lilime lako kukhosi, kotero kuti udzakhala chete wosatha kuwadzudzula, chifukwa iwo ndi anthu aupandu.
27 Koma pamene ndidzayankhula kwa iwe, ndidzatsekula pakamwa pako ndipo udzawawuza kuti, ‘Ambuye Yehova akuti zakutizakuti.’ Aliyense wofuna kumva amve ndipo wokana kumva, muleke akane; pakuti iwo ndi anthu opanduka.”