< Ezekieli 29 >

1 Pa tsiku lakhumi ndi chiwiri la mwezi wakhumi, chaka chakhumi, Yehova anandiyankhula kuti:
In the tenthe yeer, in the tweluethe monethe, in the firste dai of the monethe, the word of the Lord was maad to me, and he seide,
2 “Iwe mwana wa munthu, tembenukira kwa Farao, mfumu ya Igupto, ndipo unenere modzudzula mfumuyo pamodzi ndi dziko lake.
Thou, sone of man, sette thi face ayens Farao, king of Egipt; and thou schalt profesie of hym, and of al Egipt.
3 Uyiwuze mfumuyo kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti, “‘Ndine mdani wako, iwe Farao mfumu ya Igupto, iwe ngʼona yayikulu yogona pakati pa mitsinje yako. Umanena kuti, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga; ndinadzipangira ndekha.’
Speke thou, and thou schalt seie, The Lord God seith these thingis, Lo! Y to thee, thou Farao, kyng of Egipt, thou grete dragoun, that liggist in the myddis of thi floodis, and seist, The flood is myn, and Y made mysilf.
4 Koma ndidzakukola ndi mbedza mʼkamwa mwako ndipo nsomba za mʼmitsinje yako zidzakangamira ku mamba ako. Tsono ndidzakutulutsa mu mtsinje mwakomo pamodzi ndi nsomba zimene zakangamira ku mamba ako.
And Y schal sette a bridil in thi chekis, and Y schal glue the fischis of thi floodis to thi scalis; and Y schal drawe thee out of the myddis of thi floodis, and alle thi fischis schulen cleue to thi scalis.
5 Ndidzakutaya ku chipululu, iwe pamodzi ndi nsomba zonse za mʼmitsinje yako. Udzagwera pamtetete kuthengo popanda munthu woti akutole kuti akayike maliro ako. Ndidzakusandutsa chakudya cha zirombo za pa dziko lapansi ndi mbalame za mlengalenga.
And Y schal caste thee forth in to desert, and alle the fischis of thi flood; on the face of erthe thou schalt falle doun, thou schalt not be gaderid, nethir schalt be gaderid togidere; to the beestis of erthe, and to the volatilis of the eir Y yaf thee to be deuourid.
6 Motero aliyense amene amakhala mu Igupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova. “‘Iwe unakhala ngati ndodo yabango ku Aisraeli.
And alle the dwelleris of Egipt schulen knowe, that Y am the Lord. For that that thou were a staf of rehed to the hous of Israel, whanne thei token thee with hond,
7 Pamene anakugwira unathethekera mʼmanja mwawo ndi kucheka mapewa awo. Pamene anakutsamira, unathyoka ndipo misana yawo inagwedezeka.
and thou were brokun, and to-rentist ech schuldre of hem, and whanne thei restiden on thee, thou were maad lesse, and thou hast discoumfortid alle the reynes of hem;
8 “‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, ndikubweretsera lupanga kuti lidzaphe anthu pamodzi ndi nyama zomwe.
therfor the Lord God seith these thingis, Lo! Y schal bringe a swerd on thee, and Y schal sle of thee man and beeste;
9 Dziko la Igupto lidzasanduka lopanda anthu. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova. “‘Popeza iwe unati, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga; ndinawupanga ndine,’
and the lond of Egipt schal be in to desert, and in to wildirnesse, and thei schulen wite, that Y am the Lord. For that that thou seidist, The flood is myn, and Y made it, therfor lo!
10 nʼchifukwa chake Ine ndikudana nawe pamodzi ndi mitsinje yakoyo, ndipo ndidzasandutsa dziko la Igupto bwinja kuyambira chipululu cha Migidoli mpaka ku mzinda wa Asiwani, kukafika ku malire a Kusi.
Y to thee, and to thi floodis. And Y schal yyue `in to wildirnesses the lond of Egipt distried bi swerd, fro the tour of Sienes til to the termes of Ethiopie.
11 Palibe phazi la munthu kapena la nyama limene lidzapondepo. Kudzakhala kopanda anthu kwa zaka makumi anayi.
The foot of man schal not passe bi it, nether the foot of beeste schal go in it, and it schal not be enhabitid in fourti yeer.
12 Ndidzasandutsa dziko la Igupto kukhala chipululu ngati zipululu za mayiko ena. Kwa zaka makumi anayi mizinda yakenso idzakhala yopasuka pakati pa mizinda yopasuka. Ndipo ndidzathamangitsira Aigupto pakati pa mitundu ya anthu ndi kuwabalalitsira mʼmayiko.
And Y schal yyue the lond of Egipt forsakun, in the myddis of londis forsakun, and the citees therof in the myddis of a citee distried, and tho schulen be desolat bi fourti yeer. And Y schal scatere Egipcians in to naciouns, and Y schal wyndewe hem in to londis.
13 “‘Komabe Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pakutha pa zaka makumi anayi ndidzasonkhanitsa Aigupto onse kuchokera ku mayiko amene ndinawabalalitsirako.
For the Lord God seith these thingis, After the ende of fourti yeer Y schal gadere togidere Egipt fro puplis, among whiche thei weren scaterid;
14 Ndidzachotsa Aiguptowo ku ukapolo ndipo ndidzawabwezera ku Patirosi kumene anachokera. Kumeneko iwo adzakhala ufumu wotsika.
and Y schal bringe ayen the caitifte of Egipte. And Y schal sette hem in the lond of Phatures, in the lond of her birthe; and thei schulen be there in to a meke rewme,
15 Udzakhala ufumu wotsika kwambiri kupambana maufumu ena onse ndipo sudzadzitukumula pakati pa mitundu ina. Ndidzawufowoketsa kwambiri kotero kuti sudzathanso kulamulira mitundu ya anthu.
and among othere rewmes it schal be most low, and it schal no more be reisid ouer naciouns. And Y schal make hem lesse, that thei regne not on hethene men;
16 Aisraeli sadzadaliranso Aigupto. Koma kuti chilango chawo chidzawakumbutsa tchimo lawo lija lofunafuna thandizo kuchokera ku Igupto. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.’”
and thei schulen no more be to the hous of Israel in trist, techinge wickidnesse, that thei fle, and sue hem; and thei schulen knowe, that Y am the Lord God.
17 Pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, chaka cha 27, Yehova anandiyankhula kuti:
And it was don in the seuene and twentithe yeer, in the firste monethe, in the firste dai of the monethe, the word of the Lord was maad to me,
18 “Iwe mwana wa munthu, kale Nebukadinezara mfumu ya Babuloni inagwiritsa ntchito ankhondo ake kukathira nkhondo mzinda wa Turo, mpaka munthu aliyense anachita dazi chifukwa chosenza katundu, ndipo ananyuka pa phewa. Komabe ngakhale iyeyo, kapena gulu lake lankhondo sanaphulepo kanthu pa ntchito yonse imene anayigwira polimbana ndi mzindawo.
and he seide, Thou, sone of man, Nabugodonosor, kyng of Babiloyne, made his oost to serue bi greet seruyce ayens Tire; ech heed was maad ballid, and ech schuldir was maad bare of heer, and meede was not yoldun of Tire to hym, nether to his oost, for the seruyce bi which he seruede to me ayens it.
19 Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, Ine ndidzapereka Igupto kwa Nebukadinezara mfumu ya Babuloni, ndipo iyo idzatenga chuma chake ndi kuchifunkha ngati malipiro a gulu lake lankhondo.
Therfor the Lord God seith these thingis, Lo! Y schal yyue Nabugodonosor, kyng of Babiloyne, in the lond of Egipt, and he schal take the multitude therof; and he schal take in preye the clothis therof, and he schal rauysche the spuylis therof, and meede schal be to his oost,
20 Ndamupatsa Nebukadinezara Igupto ngati mphotho ya kulimbika kwake chifukwa iyo ndi gulu lake lankhondo anandigwirira ntchito, akutero Ambuye Yehova.
and to the werk for which he seruyde to me ayens it; and Y yaf the lond of Egipt to hym, for that that he trauelide to me, seith the Lord God.
21 “Pa nthawi imeneyo ndidzapereka mphamvu yatsopano pa Aisraeli, ndipo ndidzatsekula pakamwa pako, iwe, Ezekieli kuti uthe kuyankhula pakati pawo. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
In that dai an horn of the hous of Israel schal come forth, and Y schal yyue to thee an open mouth in the myddis of hem; and thei schulen wite, that Y am the Lord.

< Ezekieli 29 >