< Ezekieli 28 >

1 Yehova anandiyankhula nati:
ויהי דבר יהוה אלי לאמר׃
2 “Iwe mwana wa munthu, iwuze mfumu ya ku Turo mawu a Ine Ambuye Yehova akuti, “‘Iwe ndi mtima wako wodzikuza umanena kuti, ‘Ine ndine mulungu; ndimakhala pa mpando wa mulungu pakati pa nyanja.’ Koma ndiwe munthu chabe osati mulungu, ngakhale ukuganiza kuti ndiwe wanzeru ngati mulungu.
בן אדם אמר לנגיד צר כה אמר אדני יהוה יען גבה לבך ותאמר אל אני מושב אלהים ישבתי בלב ימים ואתה אדם ולא אל ותתן לבך כלב אלהים׃
3 Taona, ndiwedi wanzeru kupambana Danieli. Ndipo palibe chinsinsi chobisika kwa iwe.
הנה חכם אתה מדנאל כל סתום לא עממוך׃
4 Mwa nzeru zako ndi kumvetsa kwako unadzipezera chuma ndipo unasonkhanitsa golide ndi siliva mʼnyumba zosungira chuma chako.
בחכמתך ובתבונתך עשית לך חיל ותעש זהב וכסף באוצרותיך׃
5 Ndi nzeru zako zochitira malonda unachulukitsa chuma chako ndipo wayamba kunyada chifukwa cha chuma chakocho.
ברב חכמתך ברכלתך הרבית חילך ויגבה לבבך בחילך׃
6 “‘Choncho Ine Ambuye Yehova ndikuti, “‘Popeza umadziganizira kuti ndiwe mulungu,
לכן כה אמר אדני יהוה יען תתך את לבבך כלב אלהים׃
7 Ine ndidzabwera ndi anthu achilendo, anthu ankhanza, kuti adzalimbane nawe. Adzakuthira nkhondo kuti awononge zonse zimene unazipeza ndi nzeru zako, ndipo adzawononga kunyada kwakoko.
לכן הנני מביא עליך זרים עריצי גוים והריקו חרבותם על יפי חכמתך וחללו יפעתך׃
8 Iwo adzakuponyera ku dzenje ndipo udzafa imfa yoopsa mʼnyanja yozama.
לשחת יורדוך ומתה ממותי חלל בלב ימים׃
9 Kodi udzanenabe kuti, ‘Ine ndine mulungu,’ pamaso pa iwo amene akukupha? Iwe udzaoneka kuti ndiwe munthu chabe, osati mulungu, mʼmanja mwa iwo amene akukuphawo.
האמר תאמר אלהים אני לפני הרגך ואתה אדם ולא אל ביד מחלליך׃
10 Udzafa imfa ya anthu osachita mdulidwe mʼmanja mwa anthu achilendo. Ine ndayankhula zimenezi, akutero Ambuye Yehova.’”
מותי ערלים תמות ביד זרים כי אני דברתי נאם אדני יהוה׃
11 Yehova anandiyankhula kuti:
ויהי דבר יהוה אלי לאמר׃
12 “Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yodandaulira mfumu ya Turo ndipo uyiwuze mawu a Ine Ambuye Yehova akuti, “‘Iwe unali chitsanzo cha ungwiro weniweni, wodzaza ndi nzeru ndi wokongola kwambiri.
בן אדם שא קינה על מלך צור ואמרת לו כה אמר אדני יהוה אתה חותם תכנית מלא חכמה וכליל יפי׃
13 Iwe unkakhala ngati mu Edeni, munda wa Mulungu. Miyala yokongola ya mitundu yonse: rubi, topazi ndi dayimondi, kirisoliti, onikisi, yasipa, safiro, kalineliyoni ndi berili ndiwo inali zofunda zako. Ndipo zoyikamo miyalayo zinali zagolide. Anakupangira zonsezi pa tsiku limene unalengedwa.
בעדן גן אלהים היית כל אבן יקרה מסכתך אדם פטדה ויהלם תרשיש שהם וישפה ספיר נפך וברקת וזהב מלאכת תפיך ונקביך בך ביום הבראך כוננו׃
14 Ndinayika kerubi kuti azikulondera. Unkakhala pa phiri langa lopatulika, ndipo unkayendayenda pakati pa miyala ya moto.
את כרוב ממשח הסוכך ונתתיך בהר קדש אלהים היית בתוך אבני אש התהלכת׃
15 Makhalidwe ako anali abwino kuyambira pamene unalengedwa mpaka nthawi imene unayamba kuchita zoyipa.
תמים אתה בדרכיך מיום הבראך עד נמצא עולתה בך׃
16 Unatanganidwa ndi zamalonda. Zotsatira zake zinali zoti unachulukitsa zandewu ndi kumachimwa. Choncho ndinakuchotsa ku phiri langa lopatulika. Mkerubi amene ankakulondera uja anakupirikitsa kukuchotsa ku miyala yamoto.
ברב רכלתך מלו תוכך חמס ותחטא ואחללך מהר אלהים ואבדך כרוב הסכך מתוך אבני אש׃
17 Unkadzikuza mu mtima mwako chifukwa cha kukongola kwako, ndipo unayipitsa nzeru zako chifukwa chofuna kutchuka. Kotero Ine ndinakugwetsa pansi kuti ukhala chenjezo pamaso pa mafumu.
גבה לבך ביפיך שחת חכמתך על יפעתך על ארץ השלכתיך לפני מלכים נתתיך לראוה בך׃
18 Ndi malonda ako achinyengo unachulukitsa machimo ako. Motero unayipitsa malo ako achipembedzo. Choncho ndinabutsa moto pakati pako, ndipo unakupsereza, ndipo unasanduka phulusa pa dziko lapansi pamaso pa anthu onse amene amakuona.
מרב עוניך בעול רכלתך חללת מקדשיך ואוצא אש מתוכך היא אכלתך ואתנך לאפר על הארץ לעיני כל ראיך׃
19 Anthu onse amitundu amene ankakudziwa akuchita mantha chifukwa cha iwe. Watheratu mochititsa mantha ndipo sudzakhalaponso mpaka muyaya.’”
כל יודעיך בעמים שממו עליך בלהות היית ואינך עד עולם׃
20 Yehova anandiyankhula nati:
ויהי דבר יהוה אלי לאמר׃
21 “Iwe mwana wa munthu, utembenukire ku mzinda wa Sidoni ndipo unenere mowudzudzula kuti,
בן אדם שים פניך אל צידון והנבא עליה׃
22 ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti, “‘Ndine mdani wako, iwe Sidoni, ndipo ndidzalemekezedwa chifukwa cha iwe. Anthu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova ndikadzakulanga ndi kudzionetsa kuti ndine woyera pakati pako.
ואמרת כה אמר אדני יהוה הנני עליך צידון ונכבדתי בתוכך וידעו כי אני יהוה בעשותי בה שפטים ונקדשתי בה׃
23 Ndidzatumiza mliri pa iwe ndi kuchititsa magazi kuti ayende mʼmisewu yako. Anthu ophedwa ndi lupanga adzagwa mbali zonse. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
ושלחתי בה דבר ודם בחוצותיה ונפלל חלל בתוכה בחרב עליה מסביב וידעו כי אני יהוה׃
24 “‘Nthawi imeneyo Aisraeli sadzakhalanso ndi anthu pafupi achipongwe amene ali ngati nthula zowawa ndi ngati minga zopweteka. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.
ולא יהיה עוד לבית ישראל סלון ממאיר וקוץ מכאב מכל סביבתם השאטים אותם וידעו כי אני אדני יהוה׃
25 “‘Ine Ambuye Yehova mawu anga ndi awa: Nditasonkhanitsa Aisraeli kuchoka ku mayiko kumene anamwazikira, ndidzadzionetsa kuti ndine woyera pakati pawo pamaso pa anthu a mitundu ina. Adzakhala mʼdziko lawo, limene ndinalipereka kwa mtumiki wanga Yakobo.
כה אמר אדני יהוה בקבצי את בית ישראל מן העמים אשר נפצו בם ונקדשתי בם לעיני הגוים וישבו על אדמתם אשר נתתי לעבדי ליעקב׃
26 Adzakhala kumeneko mwamtendere ndipo adzamanga nyumba ndi kulima minda ya mpesa. Adzakhala kumeneko mwamtendere pamene ndidzalange anthu oyandikana nawo, amene ankawanyoza. Motero iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo.’”
וישבו עליה לבטח ובנו בתים ונטעו כרמים וישבו לבטח בעשותי שפטים בכל השאטים אתם מסביבותם וידעו כי אני יהוה אלהיהם׃

< Ezekieli 28 >