< Ezekieli 27 >
1 Yehova anandiyankhula kuti:
2 “Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yodandaulira Turo.
3 Uza Turo, mzinda wokhala pa dooko la nyanja, wochita malonda ndi anthu ambiri a mʼmbali mwa nyanja kuti: Ambuye Yehova akuti, “Iwe Turo, umanena kuti, ‘Ndine wokongola kwambiri.’
4 Malire ako anali mʼkati mwenimweni mwa nyanja; amisiri ako anakukongoletsa kwambiri.
5 Anakupanga ndi matabwa a payini ochokera ku Seniri; anatenga mikungudza ya ku Lebanoni kupangira mlongoti wako.
6 Ndi mitengo ya thundu ya ku Basani anapanga zopalasira zako; ndi matabwa a mitengo ya payini yochokera ku zilumba za Kitimu. Pakuti anapanga thandala lako pakati pa matabwawo panali minyanga ya njovu.
7 Nsalu yabafuta yopeta yochokera ku Igupto inali thanga yako, ndipo inakhala ngati mbendera. Nsalu zophimba matenti ako zinali za mtundu wamtambo ndi pepo zochokera ku zilumba za Elisa.
8 Anthu a ku Sidoni ndi Arivadi ndi amene anali opalasa ako. Anthu aluso ako, iwe Turo, anali mwa iwe ndiwo amene ankakuyendetsa.
9 Akuluakulu ndi eni luso a ku Gebala anali mʼkati mwako, ngati okonza zibowo zako. Sitima za pa nyanja zonse, ndi oyendetsa ake ankabwera pamodzi ndi katundu kudzachita nawe malonda.
10 “Anthu a ku Perisiya, a ku Ludi ndi Puti anali asilikali mʼgulu lako la nkhondo. Iwo ankapachika zishango ndi zipewa zawo zankhondo pa makoma ako, kubweretsa kwa iwe ulemerero.
11 Anthu a ku Arivadi ndi Heleki ankalondera mbali zonse za mpanda wako; anthu a ku Gamadi anali mu nsanja zako, Iwo ankapachika zishango zawo pa makoma ako onse. Amenewo ndiwo anakukongoletsa kwambiri.
12 “Dziko la Tarisisi linachita nawe malonda chifukwa cha kuchuluka kwa katundu wako wamtundumtundu. Iwo ankapereka siliva, chitsulo, chitini ndi mtovu mosinthanitsa ndi katundu wako.
13 “Yavani, Tubala ndi Mesaki ankachita nawe malonda; iwo ankapereka akapolo ndi ziwiya za mtovu mosinthanitsa ndi katundu wako.
14 “Anthu a ku Beti Togarima ankapereka akavalo antchito, akavalo ankhondo ndi abulu mosinthanitsa ndi katundu wako.
15 “Anthu a ku Dedani ankachita nawe malonda, ndipo anthu ambiri a mʼmbali mwa nyanja anali ogula malonda ako. Ankakupatsa minyanga ya njovu ndi phingo.
16 “Anthu a ku Aramu ankachita nawe malonda chifukwa cha kuchuluka kwa zinthu zako. Iwo ankapereka miyala ya emeradi, nsalu zapepo, nsalu zopetapeta, nsalu zabafuta, korali ndi miyala ya rubi mosinthanitsa ndi katundu wako.
17 “Yuda ndi Israeli ankachita nawe malonda. Iwo ankapereka tirigu ochokera ku Miniti ndi zokometsera zakudya, uchi, mafuta ndi mankhwala mosinthanitsa ndi katundu wako.
18 “Anthu a ku Damasiko, chifukwa cha zinthu zako za malonda zambiri ndi katundu wako wosiyanasiyana, ankachita nawe malonda a vinyo wochokera ku Heliboni ndi ubweya wankhosa ochokera ku Zahari.
19 Adani ndi Agriki ochokera ku Uzala ankagula katundu wako. Iwo ankapereka chitsulo chosalala, kasiya ndi bango lonunkhira mosinthanitsa ndi katundu wako.
20 “Anthu a ku Dedani ankakugulitsa nsalu zoyika pa zishalo za akavalo.
21 “Arabiya ndi mafumu onse a ku Kedara anali ogula malonda ako. Iwo ankachita nawe malonda a ana ankhosa onenepa, nkhosa zazimuna ndi mbuzi.
22 “Anthu amalonda a ku Seba ndi Raama ankachita nawe malonda. Iwo ankapereka zonunkhira zosiyanasiyana zabwino kwambiri, miyala yokongola ndi golide mosinthanitsa ndi katundu wako.
23 “Amalonda a ku Harani, Kane, Edeni, Seba, Asuri ndi Kilimadi ankachita nawe malonda.
24 Iwowa ankasinthanitsana nawe zovala zokongola, nsalu zopetapeta, zoyala pansi za mawangamawanga, atazimanga bwino ndi zingwe zolimba.
25 “Sitima za pa madzi za ku Tarisisi zinali zonyamula malonda ako. Motero iwe uli ngati sitima yapamadzi yodzaza ndi katundu wolemera.
26 Anthu opalasa ako amakupititsa pa nyanja yozama. Koma mphepo yakummawa idzakuthyolathyola pakati pa nyanja.
27 Chuma chako, katundu wako, malonda ako, okuyendetsa ako, okuwongolera ako ndi opanga sitima za pa madzi, anthu ako amalonda ndi asilikali ako onse ndiponso aliyense amene ali mʼmenemo adzamira mʼnyanja tsiku limene udzawonongeka.
28 Madera a mʼmbali mwa nyanja adzagwedezeka chifukwa cha kufuwula kwa oyendetsa sitimawo.
29 Onse amene amapalasa sitima zapamadzi, adzatuluka mʼsitima zawo; oyendetsa ndi onse owongolera sitima zapamadzi adzayimirira mʼmbali mwa nyanja.
30 Iwo akufuwula, kukulira iwe kwambiri; akudzithira fumbi kumutu, ndi kudzigubuduza pa phulusa.
31 Akumeta mpala mitu yawo chifukwa cha iwe ndipo akuvala ziguduli. Akukulira iweyo ndi mitima yowawa kwambiri.
32 Akuyimba nyimbo yokudandaulira nʼkumati: ‘Ndani anawonongedwapo ngati Turo pakati pa nyanja?’
33 Pamene malonda ako ankawoloka nyanja unakhutitsa mitundu yambiri ya anthu. Mafumu a dziko lapansi analemera ndi chuma chako komanso ndi malonda ako.
34 Koma tsopano wathyokera mʼnyanja, pansi penipeni pa nyanja. Katundu wako ndi onse amene anali nawe amira pamodzi nawe.
35 Onse amene amakhala mʼmbali mwa nyanja aopsedwa ndi zimene zakuchitikira. Mafumu awo akuchita mantha ndipo nkhope zangoti khululu.
36 Anthu amalonda a mitundu ina akukunyogodola. Watha mochititsa mantha ndipo sudzakhalaponso mpaka muyaya.”