< Ezekieli 25 >
1 Yehova anandiyankhula kuti:
主の言葉がわたしに臨んだ、
2 “Iwe mwana wa munthu, tembenukira anthu a ku Amoni ndipo unenere mowadzudzula.
「人の子よ、あなたの顔をアンモンの人々に向け、これに向かって預言し、
3 Awawuze kuti, ‘Inu anthu a ku Amoni, imvani zimene Ambuye Yehova akunena. Iye akuti: Inu munanena mawu onyoza pamene Nyumba yanga yopatulika inkayipitsidwa. Munanyozanso dziko la Israeli pamene linaguga ndiponso anthu a ku Yuda pamene anatengedwa ukapolo.
アンモンの人々に言え。主なる神の言葉を聞け。主なる神はこう言われる、あなたはわが聖所の汚された時、またイスラエルの地の荒された時、またユダの家が捕え移された時、ああ、それはよい気味であると言った。
4 Nʼchifukwa chake Ine ndidzakuperekani mʼmanja mwa anthu akummawa ngati cholowa chawo. Iwo adzamanga misasa yawo ndi kukhoma matenti awo pakati panu. Adzadya zipatso zanu ndi kumwa mkaka wanu.
それゆえ、わたしはあなたを、東の人々に渡して彼らの所有とする。彼らはあなたのうちに陣営を設け、あなたのうちに住居を造り、あなたのくだものを食べ、あなたの乳を飲む。
5 Ndidzasandutsa Raba kuti akhale busa la ngamira ndi mizinda ya Aamoni kuti ikhale makola a nkhosa. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
わたしはラバを、らくだを飼う所とし、アンモンびとの町々を、羊の伏す所とする。そしてあなたがたは、わたしが主であることを知るようになる。
6 Zimene ndikunena Ine Ambuye Yehova ndi izi: Inu munawomba mʼmanja ndi kumalumphalumpha. Munkakondwa mu mtima mwanu pamene munkanyoza dziko la Israeli.
主なる神はこう言われる、あなたはイスラエルの地に向かって手をうち、足を踏み、心に悪意を満たして喜んだ。
7 Nʼchifukwa chake ndidzatambasula dzanja langa kuti ndikulangeni, ndipo ndidzakuperekani kuti mukhale chofunkha cha anthu a mitundu ina. Ndidzakuchotsani pakati pa anthu a mitundu ina ndi kukufafanizani mʼmayiko onse. Ndidzakuwonongani, ndipo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova!’”
それゆえ、見よ、わたしはわが手をあなたに向けて伸べ、あなたを、もろもろの国民に渡して略奪にあわせ、あなたを、もろもろの民の中から断ち、諸国の中から滅ぼし絶やす。そしてあなたは、わたしが主であることを知るようになる。
8 “Ambuye Yehova akuti, ‘Anthu a ku Mowabu ndi a ku Seiri ananena kuti anthu a ku Yuda ali ngati mayiko ena onse.’
主なる神はわたしにこう言われる、モアブは言った、見よ、ユダの家は、他のすべての国民と同様であると。
9 Nʼchifukwa chake ndidzagumula mbali ina ya Mowabu, kuyambira ku mizinda yake ya kumalire; mizinda yokongola ya Beti-Yesimoti, Baala-Meoni ndi Kiriataimu.
それゆえ、わたしはモアブの境界の町々、すなわち国の栄えであるベテエシモテ、バアルメオン、キリアタイムの横腹を開き、
10 Ndidzapereka Amowabu pamodzi ndi Aamoni mʼmanja mwa anthu akummawa kotero kuti Aamoni adzayiwalikiratu pakati pa anthu a mitundu ina.
これをアンモンの人々と共に、東方の人々に与えて、その所有とし、モアブの人々をもろもろの国民の中に記憶させない。
11 Ndidzawalangadi Amowabuwo. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
わたしはモアブの上にさばきを行う。そのとき、彼らはわたしが主であることを知る。
12 “Ambuye Yehova akuti, ‘Pakuti Edomu analipsira Ayuda, ndiye kuti analakwa kwambiri pochita zimenezi.
主なる神はこう言われる、エドムは恨みをふくんでユダの家に敵対し、これに恨みを返して、はなはだしく罪を犯した。
13 Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzatambasula dzanja langa kulanga Edomu ndi kupha anthu ake ndiponso nyama zawo. Ndidzawonongeratu Edomu ndipo adzaphedwa ndi lupanga kuchokera ku Temani mpaka ku Dedani.
それゆえ、主なる神はこう言われる、わたしはエドムの上に手を伸べて、その中から人と獣とを断ち、これを荒れ地とする。テマンからデダンまで人々はつるぎに倒れる。
14 Ndidzalanga Edomu ndi dzanja la anthu anga Aisraeli. Adzalanga anthu a ku Edomu molingana ndi mkwiyo ndi ukali wanga. Choncho adzaona kulipsira kwanga akutero Ambuye Yehova.’”
わたしはわが民イスラエルの手をもって、エドムにわがあだを報いる。彼らがわが怒り、わが憤りに従ってエドムに行う時、エドムの人々は、わたしがあだを返すことを知るようになると、主なる神は言われる。
15 “Ambuye Yehova akuti, ‘Afilisti analanga anthu anga mwankhanza ndi kuwalipsira.
主なる神はこう言われる、ペリシテびとは恨みをふくんで行動し、心に悪意をもってあだを返し、深い敵意をもって、滅ぼすことをした。
16 Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzatambasula dzanja langa kukantha Afilistiwo. Ndidzafafaniza Akereti ndi kuwononga iwo amene amakhala mʼmbali mwa nyanja.
それゆえ、主なる神はこう言われる、見よ、わたしは手をペリシテびとの上に伸べ、ケレテびとを断ち、海べの残りの者を滅ぼす。
17 Ndidzawabwezera chilango choopsa ndipo ndidzawalanga mu mkwiyo wanga. Ndikadzawalipsira ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’”
わたしは怒りに満ちた懲罰をもって、大いなる復讐を彼らになす。わたしが彼らにあだを返す時、彼らはわたしが主であることを知るようになる」。