< Ezekieli 24 >

1 Pa tsiku lakhumi la mwezi wakhumi chaka chachisanu ndi chinayi, Yehova anandiyankhula kuti:
Again, in the ninth year, in the tenth month, in the tenth day of the month, the word of the LORD came to me, saying,
2 “Iwe mwana wa munthu lemba dzina la tsiku lalero, lero lomwe lino, chifukwa mfumu ya Babuloni yazungulira Yerusalemu lero lino.
"Son of man, write the name of the day, even of this same day: the king of Babylon drew close to Jerusalem this same day.
3 Uwaphere mwambi anthu owukirawa ndi kuwawuza kuti: ‘Ambuye Yehova akuti, “‘Ikani mʼphika pa moto, ndipo mu mʼphikamo muthiremo madzi.
Utter a parable to the rebellious house, and tell them, 'Thus says the LORD, "Set on the caldron, set it on, and also pour water into it:
4 Mu mʼphikamo muyikemo nthuli za nyama, nthuli zonse zabwino kwambiri za mwendo wathako ndi mwendo wamwamba. Mudzadzemo mafupa abwino kwambiri.
gather its pieces into it, even every good piece, the thigh, and the shoulder; fill it with the choice bones.
5 Pa gulu la nkhosa musankhepo nkhosa yabwino kwambiri. Muyike nkhuni pansi pa mʼphikawo. Madzi awire. Kenaka muphike nyamayo pamodzi ndi mafupa omwe.’
Take the choice of the flock, and also a pile of wood for the bones under the caldron; make it boil well; yes, let its bones be boiled in its midst."'
6 “‘Nʼchifukwa chake, Ambuye Yehova akuti, “‘Tsoka kwa mzinda wokhetsa magazi, tsoka kwa mʼphika wadzimbiri; dzimbiri lake losachoka! Mutulutsemo nthuli imodzimodzi osasankhulapo.
"Therefore thus says the LORD: 'Woe to the bloody city, to the caldron whose rust is in it, and whose rust is not gone out of it. Take out of it piece after piece; No lot is fallen on it.
7 “‘Paja magazi amene anakhetsa akanali pakati pake mu mzindamo. Iye awakhuthulira pa thanthwe losalala. Sanawakhutulire pa dothi kuopa kuti fumbi lingawafotsere.
For her blood is in the midst of her; she set it on the bare rock; she didn't pour it on the ground, to cover it with dust.
8 Ndinasiya magaziwo pa mwala wosalala kuti asafotseredwe ndi fumbi chifukwa ndinafuna kuonetsa mkwiyo wanga ndi kulipsira.
That it may cause wrath to come up to take vengeance, I have set her blood on the bare rock, that it should not be covered.'
9 “‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: “‘Tsoka kwa mzinda wokhetsa magazi! Inenso, ndidzawunjika mulu waukulu wa nkhuni.
"Therefore thus says the LORD: 'Woe to the bloody city. I also will make the pile great.
10 Choncho wonjeza nkhuni ndipo muyatse moto. Phikani nyamayo bwinobwino, muthiremo zokometsera, mutsanule msuzi, ndipo mupsereze mafupawo.
Pile on the wood, make the fire hot, boil the meat well, and mix in the spices, and let the bones be burned up.
11 Tsono muyike pa makala mʼphika wopanda kanthuwo mpaka utenthe kuchita kuti psuu kuti zonyansa zake zisungunuke ndi kuti dzimbiri lake lichoke.
Then set it empty on its coals, that it may be hot, and its bronze may burn, and that its filthiness may be molten in it, that its rust may be consumed.
12 Koma mʼphikawo walephereka kuyeretsedwa. Dzimbiri lake linalowerera silingatheke kuchoka ngakhale ndi moto womwe.
She has wearied herself with toil; yet her great rust doesn't go forth out of her; her rust doesn't go forth by fire.
13 “‘Tsono dzimbiri limeneli ndi zilakolako za dama lako. Pakuti ine ndinayesa kukutsuka koma iwe sunayere, ndipo sudzayeranso mpaka ukali wanga utakwaniratu pa iwe.
In your filthiness is lewdness: because I have cleansed you and you weren't cleansed, you shall not be cleansed from your filthiness any more, until I have caused my wrath toward you to rest.
14 “‘Ine Yehova ndayankhula. Zimenezi zikubwera ndipo ndidzazichitadi. Sindidzabwerera mʼmbuyo. Sindidzakulekerera kapena kukuchitira chifundo. Ndidzakulanga molingana ndi makhalidwe ndi machitidwe ako, akutero Ambuye Yehova.’”
I, the LORD, have spoken it: it shall happen, and I will do it: I will not go back, neither will I spare, neither will I repent; according to your ways and according to your deeds I will judge you,' says the LORD."
15 Yehova anandiyankhula kuti:
Also the word of the LORD came to me, saying,
16 “Iwe mwana wa munthu, Ine ndikulanda mwadzidzidzi mkazi amene amakukomera mʼmaso kwambiri. Koma usadandaule, usalire kapena kukhetsa misozi.
"Son of man, look, I will take away from you the desire of your eyes with a stroke: yet you shall neither mourn nor weep, neither shall your tears run down.
17 Ubuwule koma mwakachetechete. Usamulire wakufayo. Uvale nduwira yako ndithu, nsapato zakonso usavule. Usaphimbe nkhope kapena kudya chakudya cha anamfedwa.”
Sigh, but not aloud, make no mourning for the dead; bind your headdress on you, and put your shoes on your feet, and do not cover your lips, and do not eat men's bread."
18 Choncho ndinayankhula ndi anthu mmawa, ndipo madzulo mkazi wanga anamwalira. Mmawa mwake ndinachita monga momwe anandilamulira.
So I spoke to the people in the morning; and at even my wife died; and I did in the morning as I was commanded.
19 Ndipo anthu anandifunsa kuti, “Kodi sutifotokozera tanthauzo la zimene ukuchitazi?”
The people said to me, "Won't you tell us what these things are to us, that you do so?"
20 Ndinawayankha kuti, “Yehova anandipatsa uthenga wakuti,
Then I said to them, "The word of the LORD came to me, saying,
21 ‘Awuze Aisraeli kuti: Ine Ambuye Yehova ndikuti: ndidzayipitsa Nyumba yanga yopatulika, nyumba imene mwakhala mukuyinyadira. Mumakondwa kwambiri poyiona, ndipo mumayikonda ndi mtima onse. Ana aamuna ndi aakazi amene munawasiya mʼmbuyo adzaphedwa ndi lupanga.
'Speak to the house of Israel, "Thus says the LORD: Look, I will profane my sanctuary, the pride of your power, the desire of your eyes, and that which your soul pities; and your sons and your daughters whom you have left behind shall fall by the sword.
22 Ndipo mudzachita monga ndachitira inemu. Inu simudzaphimba nkhope zanu kapena kudya chakudya cha anamfedwa.
You shall do as I have done: you shall not cover your lips, nor eat the bread of men.
23 Mudzavala nduwira zanu kumutu ndi nsapato zanu ku mapazi anu. Simudzabuma maliro kapena kukhetsa misozi koma mudzavutika kwambiri chifukwa cha machimo anu ndipo mudzabuwula pakati panu.
Your turbans shall be on your heads, and your shoes on your feet: you shall not mourn nor weep; but you shall pine away in your iniquities, and moan one toward another.
24 Ine Ezekieli ndidzakhala chitsanzo chanu. Mudzachita monga momwe ndachitira. Izi zikadzachitika, akutero Yehova, ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Wamphamvuzonse.’
Thus Ezekiel shall be a sign to you; according to all that he has done, you will do. When this comes, then you will know that I am the LORD."'"
25 “Ndipo Yehova anandiyankhula nati: Iwe mwana wa munthu, tsiku lina ndidzawachotsera anthuwa linga lawo limene ankakondwerera kukongola kwake, limene linkawakomera mʼmaso mwawo, limenenso anayikapo mtima wawo kwambiri. Ndidzawachotsera ana awo aamuna ndi aakazi.
"You, son of man, shall it not be in the day when I take from them their strength, the joy of their glory, the desire of their eyes, and that whereupon they set their heart, their sons and their daughters,
26 Pa tsiku limenelo wothawa nkhondo adzabwera kudzakuwuzani zimenezo.
that in that day he who escapes shall come to you, to cause you to hear it with your ears?
27 Pa tsiku limenelo pakamwa pako padzatsekuka. Udzatha kuyankhula naye ndipo sudzakhalanso chete. Motero udzakhala chizindikiro kwa iwo, ndipo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
In that day your mouth will be opened to him who has escaped, and you shall speak, and be no more mute: so you will be a sign to them; and they shall know that I am the LORD."

< Ezekieli 24 >