< Ezekieli 21 >
1 Yehova anandiyankhula nati:
2 “Iwe mwana wa munthu, tembenuka uyangʼane ku Yerusalemu ndipo ulalike mawu odzudzula malo ake opatulika. Unenere zodzudzula anthu a ku Yerusalemu.
3 Uwawuze kuti, Ambuye Yehova akuti, ‘Taona, Ine ndidzalimbana nawe. Ndidzasolola lupanga langa mʼchimake ndi kuwononga anthu olungama ndi ochimwa omwe.
4 Motero ndidzapha aliyense kuchokera kummawa mpaka kumpoto.
5 Pamenepo anthu onse adzadziwa kuti Ine Yehova ndi amene ndasolola lupanga langa mʼchimake; sindidzalilowetsanso mʼchimakemo.’
6 “Tsono iwe mwana wa munthu, buwula. Buwula pamaso pawo ndi mtima wosweka ndi wachisoni chachikulu.
7 Ndipo akadzakufunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani ukubuwula?’ Iwe udzayankhe kuti, ‘Ndikubuwula chifukwa cha nkhani imene ndamva. Zikadzachitika zimenezi, mitima yonse idzangoti fumu, manja onse adzangolefuka, mpweya wawo udzawathera, ndipo mawondo onse adzangoti zii.’ Izi zikubwera! Ndipo zidzachitika ndithu, akutero Ambuye Yehova.”
8 Yehova anandiyankhulanso kuti,
9 “Iwe mwana wa munthu, unenere ndipo unene kuti, Ambuye Yehova akuti, “Izi ndi zimene Yehova akunena: Lupanga, lupanga, lanoledwa ndipo lapukutidwa.
10 Lanoledwa kuti likaphe, lapukutidwa kuti lingʼanime ngati mphenzi! “‘Kodi tingakondwere bwanji? Wanyoza ndodo, mwana wanga ndi chilichonse cha mtengo.
11 “‘Lupanga laperekedwa kuti lipukutidwe, ndi kuti linyamulidwe, lanoledwa ndi kupukutidwa, kuti liperekedwe mʼmanja mwa munthu amene amapha.
12 Fuwula ndi kulira, iwe mwana wa munthu, pakuti zimenezi zidzagwera anthu anga; zidzagweranso akalonga onse a Israeli. Adzaphedwa ndi lupanga pamodzi ndi anthu anga. Chifukwa chake udzigugude pa chifuwa ndi chisoni.
13 “‘Ambuye Wamphamvuzonse akuti: Ndikuwayesa anthu anga, ndipo ngati satembenuka mtima, ndiye kuti zimenezi sizidzalephera kuwagwera.’
14 “Tsono mwana wa munthu, nenera ndipo uwombe mʼmanja. Lupanga likanthe kawiri ngakhale katatu. Limenelo ndilo lupanga lophera anthu. Inde ndilodi lupanga lophera anthu koopsa limene likuwazungulira.
15 Ndawayikira pa zipata zawo zonse lupanga laphuliphuli kuti ataye mtima ndiponso kuti anthu ambiri agwe. Aa! Lapangidwa lupanga kuti lizingʼanima ngati mphenzi ndi kuti azilisolola kuphera anthu.
16 Iwe lupanga, ipha anthu kumanja, kenaka kumanzere, kulikonse kumene msonga yako yaloza.
17 Inenso ndidzawomba mʼmanja mwanga, ndipo ndidzaziziritsa ukali wanga Ine Yehova ndayankhula.”
18 Yehova anandiyankhulanso kuti,
19 “Iwe mwana wa munthu, ulembe zizindikiro za misewu iwiri imene lupanga la mfumu ya ku Babuloni lingathe kudzeramo. Misewu yonse ikhale yochokera mʼdziko limodzi. Ika chikwangwani pa mphambano yopita mu mzinda.
20 Ulembe chizindikiro pa msewu umene lupanga lidzadzere popita ku Raba wa ku Amoni, ndiponso ku Yuda ndi ku Yerusalemu, mzinda wotetezedwa.
21 Pakuti mfumu ya ku Babuloni yayima pa msewu, pa mphambano ya misewu iwiriyo. Ikuwombeza ndi mivi yake kuti idziwe njira yoyenera kudzeramo. Ikupempha nzeru kwa milungu yake ndipo ikuyangʼana chiwindi cha nyama yoperekedwa ku nsembe.
22 Mʼdzanja lake lamanja muli muvi waula wolembedwa Yerusalemu. Kumeneko mfumuyo idzayika zida zogumulira, idzalamula kupha anthu ndiponso kufuwula mfuwu wa nkhondo. Mfumuyo idzapanga zida zogumulira makoma, kuwunda mitumbira ya nkhondo ndi kumanga nsanja za nkhondo.
23 Koma kwa anthu a ku Yerusalemu zidzaoneka ngati zowombeza zabodza chifukwa cha malumbiro amene anachita kwa mfumuyo. Koma mfumuyo idzawakumbutsa za zolakwa zawo kuti atengedwe ku ukapolo.
24 “Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti, ‘Popeza mwandikumbutsa zolakwa, moti kundiwukira kwanu kwaonekera poyera ndi kuti mu zochita zanu zonse mukuonetsa machimo anu, nʼchifukwa chake mudzagwidwa ndi kutengedwa ukapolo.
25 “‘Tsono iwe kalonga wonyozedwa ndi woyipa wa Israeli, amene tsiku lako lafika, amene nthawi yako yolangidwa yafika penipeni,
26 Ambuye Yehova akuti: Vula nduwira, chotsa chipewa chaufumu. Zinthu sizidzakhala monga zinalili: anthu wamba adzakwezedwa ndipo okwezedwa adzatsitsidwa.
27 Chipasupasu! Chipasupasu! Ine ndidzawupasula mzindawo! Ndipo sadzawumanganso mpaka atafika amene ali woyenera kuwulandira; Ine ndidzawupereka kwa iyeyo.’
28 “Ndipo iwe mwana wa munthu, nenera kuti, ponena za Aamoni ndi zonyoza zawo, Ambuye Yehova akuti, “‘Lupanga, lupanga, alisolola kuti liphe anthu, alipukuta kuti liwononge ndi kuti lingʼanime ngati mphenzi.
29 Zimene akuti akuona mʼmasomphenya zokhudza inu ndi zabodza. Mawula awo okhudza inu ndi abodzanso. Mudzakhala pamodzi ndi anthu oyipa amene tsiku lawo lafika, ndiye kuti nthawi ya kulangidwa kwawo komaliza.
30 “‘Bwezerani lupanga mʼchimake. Ku malo kumene inu munabadwira, mʼdziko la makolo anu, ndidzakuweruzani.
31 Ndidzakhuthula ukali wanga pa inu, ndipo mkwiyo wanga udzakuyakirani. Ndidzakuperekani mʼmanja mwa anthu ankhanza; anthu odziwa bwino kuwononga zinthu.
32 Mudzakhala ngati nkhuni pa moto. Ena adzakhetsa magazi anu mʼdziko lanu lomwe. Simudzakumbukiridwanso pakuti Ine Yehova ndayankhula.’”