< Ezekieli 20 >
1 Tsiku lakhumi la mwezi wachisanu, chaka chachisanu ndi chiwiri, ena mwa akuluakulu a Israeli anabwera kudzapempha nzeru kwa Yehova, ndipo anakhala pansi pamaso panga.
Et factum est in anno septimo, in quinto, in decima mensis: venerunt viri de senioribus Israel ut interrogarent Dominum, et sederunt coram me.
2 Tsono Yehova anandiyankhula nati:
Et factus est sermo Domini ad me, dicens:
3 “Iwe mwana wa munthu, ayankhule akuluakulu a Israeli ndi kuwawuza kuti, ‘Ambuye Yehova akuti: Kodi mwabwera kudzapempha nzeru kwa Ine? Ndithu pali Ine wamoyo, Ine sindidzakulolani kupempha nzeru kwa Ine, akutero Ambuye Yehova.’
Fili hominis loquere senioribus Israel, et dices ad eos: Haec dicit Dominus Deus: Numquid ad interrogandum me vos venistis? vivo ego quia non respondebo vobis, ait Dominus Deus.
4 “Kodi uwaweruza? Iwe mwana wa munthu, kodi ugamula mlandu wawo? Uwadziwitse tsono zonyansa zimene anachita makolo awo, uwawuze kuti,
Si iudicas eos, si iudicas fili hominis, abominationes patrum eorum ostende eis.
5 ‘Ambuye Yehova akuti: Pa tsiku limene ndinasankha Israeli, ndinalumbira kwa zidzukulu za nyumba ya Yakobo ndipo ndinadziwulula kwa iwo ku Igupto. Ndinalumbira ndi kuwawuza kuti: Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
Et dices ad eos: Haec dicit Dominus Deus: In die, qua elegi Israel, et levavi manum meam pro stirpe domus Iacob, et apparui eis in Terra Aegypti, et levavi manum meam pro eis, dicens: Ego Dominus Deus vester:
6 Pa tsiku limenelo ndinalumbira kwa iwo kuti ndidzawatulutsa mʼdziko la Igupto ndi kupita nawo ku dziko limene ndinawapezera, dziko la mwana alirenji, dziko lokongola kwambiri kupambana mayiko ena.
in die illa levavi manum meam pro eis, ut educerem eos de Terra Aegypti, in Terram, quam provideram eis, fluentem lacte, et melle: quae est egregia inter omnes terras.
7 Ndipo ndinawawuza kuti, ‘Aliyense ataye zinthu zonse zonyansa zimene ankasangalala nazo, ndipo musadziyipitse ndi mafano a Igupto, Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’
Et dixi ad eos: Unusquisque offensiones oculorum suorum abiiciat, et in idolis Aegypti nolite pollui: ego Dominus Deus vester.
8 “‘Koma iwo anandiwukira ndipo sanafune kundimvera. Palibe amene anataya zonyansa zonse zimene ankasangalala nazo. Panalibenso amene anasiya mafano a ku Igupto. Tsono ndinaganiza zowakhuthulira ukali wanga ndi kuwaonetsa mkwiyo wanga mʼdziko la Igupto momwemo.
Et irritaverunt me, nolueruntque me audire: unusquisque abominationes oculorum suorum non proiecit, nec idola Aegypti reliquerunt: et dixi ut effunderem indignationem meam super eos, et implerem iram meam in eis, in medio Terrae Aegypti.
9 Koma sindinachite zimenezi chifukwa cha dzina langa, kuti lisayipitsidwe pakati pa anthu a mitundu ina amene ankakhala pakati pawo. Paja ndinali nditaonetsa mphamvu zanga pamaso pa mitunduyo potulutsa Aisraeli mʼdziko la Igupto.
Et feci propter nomen meum, ut non violaretur coram Gentibus, in quarum medio erant, et inter quas apparui eis ut educerem eos de Terra Aegypti.
10 Choncho ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto ndi kubwera nawo mʼchipululu.
Eieci ergo eos de Terra Aegypti, et eduxi eos in desertum.
11 Ndinawapatsa malangizo anga ndi kuwadziwitsa malamulo anga amene munthu aliyense akawamvera adzakhala ndi moyo.
Et dedi eis praecepta mea, et iudicia mea ostendi eis, quae faciens homo, vivet in eis.
12 Ndinawapatsanso Masabata ngati chizindikiro pakati pathu, kuti adziwe kuti Ine Yehova ndinawapatula.
Insuper et sabbata mea dedi eis, ut essent signum inter me et eos: et scirent quia ego Dominus sanctificans eos.
13 “‘Komabe anthu a Israeli anandiwukira mʼchipululu. Iwo sanatsatire malangizo anga koma anakana malamulo anga amene munthu aliyense akawamvera adzakhala ndi moyo. Ndipo anayipitsa kotheratu Masabata anga. Choncho, ndinaganiza zowakhuthulira ukali wanga ndi kuwawononga mʼchipululu.
Et irritaverunt me domus Israel in deserto, in praeceptis meis non ambulaverunt, et iudicia mea proiecerunt, quae faciens homo vivet in eis: et sabbata mea violaverunt vehementer: dixi ergo ut effunderem furorem meum super eos in deserto, et consumerem eos.
14 Koma sindinachite zimenezi chifukwa cha dzina langa, kuti lisayipitsidwe pakati pa anthu a mitundu ina amene anandiona ndikutulutsa Aisraeliwo mu Igupto.
Et feci propter nomen meum, ne violaretur coram Gentibus de quibus eieci eos in conspectu earum.
15 Ndinalumbiranso kwa iwo mʼchipululu muja, nditakweza dzanja, kuti sindidzawalowetsanso mʼdziko limene ndinawapatsa, dziko la mwana alirenji, lokoma kwambiri kuposa mayiko ena onse.
Ego igitur levavi manum meam super eos in deserto, ne inducerem eos in Terram, quam dedi eis fluentem lacte, et melle, praecipuam terrarum omnium:
16 Paja anakana malamulo anga, sanatsatire malangizo anga ndipo anayipitsa masabata anga. Mitima yawo inakonda mafano.
Quia iudicia mea proiecerunt, et in praeceptis meis non ambulaverunt, et sabbata mea violaverunt: post idola enim cor eorum gradiebatur.
17 Komabe ndinawamvera chisoni ndipo sindinawawononge kapena kuwatheratu mʼchipululu.
Et pepercit oculus meus super eos ut non interficerem eos: nec consumpsi eos in deserto.
18 Tsono kwa ana awo mʼchipululu ndinati, ‘Musatsatire malangizo a makolo anu kapena kusunga malamulo awo kapena kudziyipitsa ndi mafano awo.
Dixi autem ad filios eorum in solitudine: In praeceptis patrum vestrorum nolite incedere, nec iudicia eorum custodiatis, nec in idolis eorum polluamini:
19 Ine ndine Yehova Mulungu wanu; tsatirani malangizo anga ndipo sungani malamulo anga.
Ego Dominus Deus vester: in praeceptis meis ambulate, iudicia mea custodite, et facite ea:
20 Masabata anga muziwasunga ngati opatulika kuti akhale chizindikiro pakati pa Ine ndi inu. Mukatero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’
Et sabbata mea sanctificate ut sint signum inter me et vos, et sciatis quia ego sum Dominus Deus vester.
21 “‘Koma ana awo anandiwukira. Iwo sanatsatire malangizo anga, sanamvere malamulo anga, ngakhale kuti amapereka moyo kwa munthu amene amawamvera. Ndiponso anayipitsa Masabata anga. Choncho ndinaganiza zowakhuthulira ukali wanga ndi kuwawonongeratu mʼchipululu momwemo.
Et exacerbaverunt me filii, in praeceptis meis non ambulaverunt: et iudicia mea non custodierunt ut facerent ea: quae cum fecerit homo, vivet in eis: et sabbata mea violaverunt: et comminatus sum ut effunderem furorem meum super eos, et implerem iram meam in eis in deserto.
22 Koma sindinatero chifukwa cha dzina langa kuti lisayipitsidwe pakati pa anthu a mitundu ina amene anandiona ndikutulutsa Aisraeliwo mu Iguptomo.
Averti autem manum meam, et feci propter nomen meum, ut non violaretur coram Gentibus, de quibus eieci eos in oculis earum.
23 Choncho ndinalumbira mʼchipululu, nditakweza dzanja langa, kuti ndidzawabalalitsa pakati pa anthu a mitundu ina ndi kuwamwazira ku mayiko akutali,
Iterum levavi manum meam in eos in solitudine, ut dispergerem illos in nationes, et ventilarem in terras:
24 chifukwa sanamvere malamulo anga, anakana malangizo anga, nayipitsa masabata anga, ndi kupembedza mafano a makolo awo.
eo quod iudicia mea non fecissent, et praecepta mea reprobassent, et sabbata mea violassent, et post idola patrum suorum fuissent oculi eorum.
25 Ine ndinawapatsanso malangizo amene sanali abwino ndi malamulo amene sakanatha kupeza nawo moyo.
Ergo et ego dedi eis praecepta non bona, et iudicia, in quibus non vivent:
26 Ndinawalekerera kuti adziyipitse ndi mphatso zawo zomwe, makamaka popereka ana awo oyamba kubadwa ngati nsembe zopsereza. Ndinatero kuti ndiwadetse nkhawa ndi kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova.’
Et pollui eos in muneribus suis cum offerrent omne, quod aperit vulvam, propter delicta sua: et scient quia ego Dominus.
27 “Tsono iwe mwana wa munthu, yankhula nawo Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Ambuye Yehova akuti makolo anu anandinyozanso posaonetsa moyo wokhulupirika.
Quamobrem loquere ad domum Israel, fili hominis: et dices ad eos: Haec dicit Dominus Deus: Adhuc et in hoc blasphemaverunt me patres vestri, cum sprevissent me contemnentes:
28 Nditawalowetsa mʼdziko limene ndinachita kulumbirira kuti ndidzawapatsa, iwo tsono ankapita kulikonse kumene anaona chitunda chachitali ndi mtengo wa masamba ambiri kukapereka kumeneko nsembe ndi zopereka zawo zimene zinkandikwiyitsa. Kumeneko ankapereka nsembe za fungo lokoma ndiponso nsembe za zakumwa.
et induxissem eos in Terram, super quam levavi manum meam ut darem eis: viderunt omnem collem excelsum, et omne lignum nemorosum, et immolaverunt ibi victimas suas: et dederunt ibi irritationem oblationis suae, et posuerunt ibi odorem suavitatis suae, et libaverunt libationes suas.
29 Tsono ndinawafunsa kuti: Kodi chitunda chimene mukupitako nʼchotani? Chitundachi chakhala chikutchedwa mpaka lero kuti ‘Chitunda cha Chipembedzo.’
Et dixi ad eos: Quid est excelsum, ad quod vos ingredimini? et vocatum est nomen eius Excelsum usque ad hanc diem.
30 “Tsono uwawuze Aisraeli kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Kodi mudzadziyipitsa nokha monga anachitira makolo anu ndi kuchita chigololo ndi milungu yawo yonyansa?
Propterea dic ad domum Israel: Haec dicit Dominus Deus: Certe in via patrum vestrorum vos polluimini, et post offendicula eorum vos fornicamini:
31 Pamene mubwera kudzapereka mphatso zanu ndi kudzapereka ana kuti akhale ngati nsembe zopsereza mumadziyipitsa ndi mafano anu mpaka lero. Kodi Aisraeli, ndingathe kukulolani bwanji kuti mulandire malangizo kwa Ine? Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, sindidzalola kuti mupemphe nzeru kwa Ine.
et in oblatione donorum vestrorum, cum traducitis filios vestros per ignem, vos polluimini in omnibus idolis vestris usque hodie: et ego respondebo vobis domus Israel? Vivo ego, dicit Dominus Deus, quia non respondebo vobis.
32 “‘Inu munanena kuti, ‘Tikufuna tikhale ngati anthu a mitundu ina, ngati anthu adziko lapansi, amene amapembedza mtengo ndi mwala.’ Koma zimene mukuganizazo sizidzachitika.
Neque cogitatio mentis vestrae fiet, dicentium: Erimus sicut Gentes, et sicut cognationes terrae ut colamus ligna, et lapides.
33 Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, ndi dzanja langa lamphamvu, nditasamula mkono wanga mokwiya kwambiri, Ine ndidzakhala wokulamulani.
Vivo ego, dicit Dominus Deus, quoniam in manu forti, et in brachio extento, et in furore effuso regnabo super vos.
34 Ndidzakuchotsani pakati pa anthu a mitundu ina ndikukusonkhanitsani kuchokera ku mayiko kumene munamwazikirako, ndi dzanja langa lamphamvu ndi lotambasuka ndili wokwiya kwambiri.
Et educam vos de populis: et congregabo vos de terris, in quibus dispersi estis, in manu valida, et in brachio extento, et in furore effuso regnabo super vos.
35 Ndidzakulowetsani mʼchipululu cha anthu a mitundu ina ndipo kumeneko, moonana maso ndi maso, ndidzakuzengani mlandu.
Et adducam vos in desertum populorum, et iudicabor vobiscum ibi facie ad faciem.
36 Monga ndinawalangira makolo anu mʼchipululu cha dziko la Igupto, motero ndidzakulangani, akutero Ambuye Yehova.
Sicut iudicio contendi adversum patres vestros in deserto Terrae Aegypti, sic iudicabo vos, dicit Dominus.
37 Ndidzakuwerengani ndi ndodo ya mʼbusa, kukulowetsani mʼchimango cha pangano langa.
Et subiiciam vos sceptro meo, et inducam vos in vinculis foederis.
38 Ndidzakuchotserani anthu amene anandigalukira ndi kundiwukira. Ngakhale ndidzawatulutsa mʼdziko limene akukhalamo, koma sadzalowamo mʼdziko la Israeli. Pamenepo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Et eligam de vobis transgressores, et impios, et de terra incolatus eorum educam eos, et in terram Israel non ingredientur: et scietis quia ego Dominus.
39 “‘Koma inu Aisraeli, zimene ndikunena Ine Ambuye Yehova ndi izi: Pitani katumikireni mafano anu onse, aliyense wa inu! Koma mʼtsogolo mwake mudzandimvera ndithu ndipo simudzayipitsa dzina langa lopatulika popereka mphatso zanu kwa mafano.
Et vos domus Israel, Haec dicit Dominus Deus: Singuli post idola vestra ambulate, et servite eis. Quod si et in hoc non audieritis me, et nomen meum sanctum pollueritis ultra in muneribus vestris, et in idolis vestris:
40 Pakuti pa phiri langa lopatulika, phiri lalitali la ku Israeli, akutero Ambuye Yehova, Aisraeli onse adzanditumikira, ndipo kumeneko Ine ndidzawalandira. Kumeneko ndidzayembekeza zopereka zanu ndi mphatso zanu zopambana, pamodzi ndi nsembe zanu zonse zopatulika.
in monte sancto meo, in monte excelso Israel, ait Dominus Deus, ibi serviet mihi omnis domus Israel; omnes, inquam, in terra, in qua placebunt mihi, et ibi quaeram primitias vestras, et initium decimarum vestrarum in omnibus sanctificationibus vestris.
41 Ndidzakulandirani ngati nsembe ya fungo lokoma ndikadzakutulutsani pakati pa anthu a mitundu ina ndi kukusokhanitsani kuchokera ku mayiko kumene munabalalitsidwirako. Motero ndidzadzionetsa pakati panu kuti ndine woyera ndipo mitundu ya anthu idzaona.
In odorem suavitatis suscipiam vos, cum eduxero vos de populis, et congregavero vos de terris, in quas dispersi estis, et sanctificabor in vobis in oculis nationum.
42 Tsono mudzadziwa kuti ndine Yehova ndikadzabwera nanu ku dziko la Israeli, dziko limene ndinalumbira kuti ndidzapereka kwa makolo anu.
Et scietis quia ego Dominus, cum induxero vos ad terram Israel, in Terram, pro qua levavi manum meam, ut darem eam patribus vestris.
43 Kumeneko mudzakumbukira makhalidwe anu ndi machitidwe anu onse amene munadziyipitsa nawo, ndipo mudzanyansidwa nokha chifukwa cha zoyipa zimene munachita.
Et recordabimini ibi viarum vestrarum, et omnium scelerum vestrorum, quibus polluti estis in eis: et displicebitis vobis in conspectu vestro in omnibus malitiis vestris, quas fecistis.
44 Inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzakuchitirani zabwino chifukwa cha dzina langa koma osati molingana ndi njira zanu zoyipa ndi machitidwe anu okhota, inu Aisraeli, akutero Ambuye Yehova.’”
Et scietis quia ego Dominus, cum benefecero vobis propter nomen meum, et non secundum vias vestras malas, neque secundum scelera vestra pessima domus Israel, ait Dominus Deus.
45 Yehova anandiyankhula nati:
Et factus est sermo Domini ad me, dicens:
46 “Iwe mwana wa munthu, tembenuka uyangʼane kummwera; ndipo lalika mawu odzudzula anthu akummwera ndipo unenere zodzudzula dziko la nkhalango ya kummwera.
Fili hominis, pone faciem tuam contra viam Austri, et stilla ad Aphricum, et propheta ad saltum agri meridiani.
47 Iwuze nkhalango yakummwera kuti, ‘Imvani mawu a Yehova! Ambuye Yehova akuti: Ndikuyatsa moto ndipo motowo udzapsereza mitengo yako yonse yayiwisi ndi yowuma yomwe. Malawi ake sadzazimitsika ndipo aliyense kuchokera kummwera mpaka kumpoto adzapsa nawo.
Et dices saltui meridiano: Audi verbum Domini: haec dicit Dominus Deus: Ecce ego succendam in te ignem, et comburam in te omne lignum viride, et omne lignum aridum: non extinguetur flamma succensionis: et comburetur in ea omnis facies ab Austro usque ad Aquilonem.
48 Aliyense adzadziwa kuti Ine Yehova ndi amene ndayatsa motowo, ndipo sudzazimitsidwa.’”
Et videbit universa caro quia ego Dominus succendi eam, nec extinguetur.
49 Ndipo ine ndinati, “Aa, Ambuye Yehova! Anthu akungondinena kuti, ‘Kodi suja amangonena nthano chabe ameneyu!’”
Et dixi: Ah, ah, ah, Domine Deus: ipsi dicunt de me: Numquid non per parabolas loquitur iste?