< Ezekieli 2 >
1 Iye anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, imirira kuti ndiyankhule nawe.”
“Son of man,” He said to me, “stand up on your feet and I will speak to you.”
2 Pamene ankayankhula nane, Mzimu wa Mulungu unalowa mwa ine ndipo unandiyimiritsa, ndipo ndinamva Iye akundiyankhula.
And as He spoke to me, the Spirit entered me and set me on my feet, and I heard Him speaking to me.
3 Iye anati, “Iwe mwana wa munthu, Ine ndikukutuma kwa Aisraeli, mtundu wa anthu owukira umene wandiwukira Ine; Iwo ndi makolo awo akhala akundiwukira Ine mpaka lero lino.
“Son of man,” He said to me, “I am sending you to the Israelites, to a rebellious nation that has rebelled against Me. To this very day they and their fathers have rebelled against Me.
4 Ndikukutuma kwa anthu okanika ndiponso nkhutukumve. Ndikukutuma kuti akawawuze zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena.
They are obstinate and stubborn children. I am sending you to them, and you are to say to them, ‘This is what the Lord GOD says.’
5 Kaya akamva kaya sakamvera, pakuti iwo ndi anthu opanduka, komabe adzadziwa kuti mneneri ali pakati pawo.
And whether they listen or refuse to listen—for they are a rebellious house—they will know that a prophet has been among them.
6 Tsono iwe mwana wa munthu, usachite nawo mantha kapena kuopa zimene azikanena. Usachite mantha, ngakhale minga ndi mkandankhuku zikuzinge ndipo ukukhala pakati pa zinkhanira. Usachite mantha ndi zimene akunena kapena kuopsedwa ndi nkhope zawo, popeza anthuwa ndi awupandu.
But you, son of man, do not be afraid of them or their words. Do not be afraid, though briers and thorns surround you, and you dwell among scorpions. Do not be afraid of their words or dismayed by their presence, though they are a rebellious house.
7 Ukawawuze ndithu mawu anga, kaya akamva kaya sakamva. Paja anthuwa ndi awupandu.
But speak My words to them, whether they listen or refuse to listen, for they are rebellious.
8 Koma iwe mwana wa munthu, mvetsera zimene ndikukuwuza. Usakhale wowukira ngati iwowo. Tsono yasama pakamwa pako kuti udye chimene ndikukupatsa.”
And you, son of man, listen to what I tell you. Do not be rebellious like that rebellious house. Open your mouth and eat what I give you.”
9 Nditayangʼana ndinangoona dzanja litaloza ine, litagwira mpukutu wolembedwa.
Then I looked and saw a hand reaching out to me, and in it was a scroll,
10 Anawufunyulura pamaso panga. Mpukutu wonse unali wolembedwa kuseri nʼkuseri. Ndipo mawu amene analembedwa mʼmenemo anali a madandawulo, maliro ndi matemberero.
which He unrolled before me. And written on the front and back of it were words of lamentation, mourning, and woe.